Surah Al-Baqarah ( The Cow )

Surah Al-Baqarah ( The Cow ) - Chewa Aya count 286

Alif-Lâm-Mîm.[1]
Omwe amakhulupirira zosaoneka ndi maso (monga Munda wamtendere, Moto, Angelo ndi zina zotere zomwe Allah ndi Mtumiki (s.a.w) adazifotokoza, amapemphera Swala moyenera, ndiponso amapereka m’zimene tawapatsa.
Ndi amene akukhulupirira zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwe, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kale iwe usadadze, nakhulupiriranso motsimikiza kuti lilipo tsiku lachimaliziro.
Iwowo (omwe ali ndi chikhalidwe chotere), ali pachiongoko chochokera kwa Mbuye wawo (Allah), ndipo iwowo ndi omwe ali opambana (pokapeza ulemelero wapamwamba ku Minda ya mtendere).
(Ali ngati kuti) Allah wawadinda chidindo chotseka mitima yawo ndi makutu awo (kotero kuti kuunika kwa chikhulupiliro sikungalowemo), ndipo m’maso mwawo muli chophimba (sangathe kuona zozizwitsa za Allah); choncho iwo adzalandira chilango chachikulu.
Pakati pa anthu alipo (anthu achinyengo) amene akunena: “Takhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro,” pomwe iwo sali okhulupirira.
Allah adzawalipira chipongwe chawocho, ndipo akuwalekelera akungoyumbayumba (kugwira njakata) m’kusokera kwawo.
Fanizo lawo lili ngati (munthu wa paulendo wafungatiridwa ndi mdima) yemwe wayatsa moto; ndipo pamene udaunika zomwe zidali m’mphepete mwake, Allah nkuwachotsera kuunika kwawoko nawasiya mu mdima osatha kuona.
(Nakhala ngati) agonthi, abubu, akhungu; ndipo sangabwelerenso (ku chiwongoko).
Kapena (fanizo lawonso) lili ngati chimvula chochokera ku mitambo m’kati mwake muukhala mdima, mphenzi ndi kung’anima, naika zala zawo m’makutu mwawo chifukwa chamkokomo ndikuopa imfa (pomwe kutero sikungawathandize chilichonse). Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za osakhulupirira.
(Allah) Yemwe adakupangirani nthaka kukhala ngati mphasa, ndi thambo kukhala ngati denga; ndipo adatsitsa madzi kuchokera ku mitambo natulutsa ndi madziwo zipatso zosiyanasiyana kuti zikhale chakudya chanu. Choncho Allah musampangire anzake uku inu mukudziwa (kuti alibe wothandizana naye).
Ndipo ngati muli m’chikaiko ndi zomwe tamvumbulutsira kapolo wathu (kuti sizinachokere kwa Ife,) tabweretsani sura imodzi yolingana ndi Quraniyi (m’kayankhulidwe ka nzeru ndi kayalidwe ka malamulo ake). Ndipo itanani athandizi anu (kuti akuthandizeni) osakhala Allah; ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’an njopekedwa).
Choncho ngati simutha (kubweretsa sura imodzi yonga ya m’Qurani) ndiye kuti simudzatha. Choncho opani Moto omwe nkhuni zake ndi anthu ndi miyala umene wakonzedwera kwa osakhulupirira.
Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira nachita ntchito zabwino (molungama) kuti ndithu adzalandira minda ya mtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi pake (ndi patsogolo pake). Nthawi iliyonse kumeneko akapatsidwa zipatso ngati chakudya, adzakhala akunena: “Izi ndizomwe tidapatsidwa kale,” (chifukwa chakuti) adzapatsidwa zipatso zofanana (m’maonekedwe ake ndi zimene adapatsidwapo kale. Koma makomedwe ake ngosiyana). Ndiponso akalandira m’menemo akazi oyeretsedwa (kuuve wamtundu uliwonse); ndipo iwo adzakhala m’menemo nthawi yaitali.
Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake).
Omwe akuswa chipangano cha Allah pambuyo pochimanga (kuti adzachikwaniritsa; ndi kutsatira malamulo a Allah), ndiponso amadula (chibale) chomwe Allah adalamula kuti chilumikizidwe, naononga pa dziko (poyambitsa nkhondo ndi ziwawa); iwo ndiamene ali otayika.
Kodi mungamkane chotani Allah chikhalirecho inu mudali akufa ndipo adakupatsani moyo (nakuikani pa dziko lapansi)? Kenako adzakupatsani imfa (ikakwana nthawi yanu yofera). Kenako adzakuukitsani (ndikukutulutsani m’manda). Ndipo kenako mudzabwezedwa kwa Iye (kuti mukaweruzidwe pa zomwe mudali kuchita).
Akumbutse (anthu ako nkhani iyi) panthawi yomwe Mbuye wako anati kwa Angelo: “Ine ndikufuna kuika m’dziko lapansi wondiimilira.” (Angelo) adati: “Kodi muika m’menemo amene azidzaonongamo ndi kukhetsa mwazi, pomwe ife tikukulemekezani ndi kukutamandani mokuyeretsani?” (Allah) adati: “Ndithudi, Ine ndikudziwa zimene simukuzidziwa.”
Ndipo (Allah) adaphunzitsa Adam mayina a (zinthu) zonse; nazibweretsa (zinthuzo) pamaso pa Angelo, naati (kwa Angelo): “Ndiuzeni mayina a zinthu izi ngati mukunena zoona (kuti inu ndinu ozindikira zinthu).”
(Angelo) adati: “Kuyeretsedwa Nkwanu! Ife tilibe kuzindikira kupatula chimene mwatiphunzitsa. Ndithudi, Inu Ngodziwa kwambiri, Anzeru zakuya.”
Ndipo (akumbutse anthu ako nkhani iyi) parnene tidawauza Angelo: “Mgwadireni Adam.” Onse adamugwadira kupatula Iblisi (Satana); anakana nadzitukumula. Tero adali m’modzi mwa osakhulupirira.
Ndipo tidati: “E iwe Adam! Khala iwe ndi mkazi wako m’mundamo (mu Edeni); idyani m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; koma musauyandikire Mtengo uwu kuopera kuti mungakhale mwa odzichitira okha zoipa.”
Koma Satana (Iblisi yemwe uja) adawalakwitsa onse awiriwo (nanyoza lamulo la Allah ndikudya mtengo woletsedwawo), nawatulutsa (mu Mtendere) momwe adaalimo. Ndipo tidawauza: “Tsikani (mukakhale pa dziko lapansi) pakati panu pali chidani. Tsopano pokhala panu ndi pa dziko lapansi, ndipo mukapeza chisangalalo pamenepo kwakanthawi.”
Ndipo Adam adalandira mawu kuchokera kwa Mbuye wake, (napempha chikhululuko cha Allah kupyolera m’mawuwo), ndipo (Mbuye wake) adavomera kulapa kwake. Ndithudi, Iyeyo Ngolandira kwambiri kulapa, Wachisoni chosatha.
Tidati: “Tsikani m’menemo nonsenu. Ngati chitakufikani chiongoko chochokera kwa Ine, choncho amene adzatsate chiongoko Changacho, pa iwo sipadzakhala mantha. Ndiponso iwo sadzadandaula.”
Ndipo dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira ndi popemphera Swala. Ndithudi, Swala yo ndiyolemera kupatula kwa odzichepetsa (kwa Allah).
Choncho opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza mnzake ndi chilichonse, ndipo sikudzavomerezedwa kwa iye (munthuyo) dandaulo lililonse, ndiponso silidzalandiridwa dipo kwa iye; ndipo iwo sadzapulumutsidwa.
Ndipo (kumbukiraninso) pamene tidailekanitsa nyanja chifukwa cha inu (kuti muoloke pa mchenga wouma), potero tidakupulumutsani ndi kuwamiza anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini) uku inu mukuona; (chomwe chidali chizizwa choonekera).
(Kumbukiraninso) pamene tidamulonjeza Mûsa masiku makumi anayi (kuti tidzampatsa buku la Taurat patapita masiku makumi anayi pambuyo pa kupulumuka kwanu ndi kuonongeka kwa Farawo); kenako inu mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe) pambuyo pake, (iye kulibe, atapita ku chipangano cha Mbuye wake). Ndipo inu muli ochita zoipa.
Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa tidampatsa buku lolekanitsa choonadi ndi chonama kuti inu muongoke (polilingalira ndi kutsatira malamulo ake).
Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti “E inu anthu anga! Ndithudi, inu mwadzichitira nokha zoipa pompembedza thole (mwana wa ng’ombe). Choncho lapani kwa Mlengi wanu, ndipo iphanani nokha (amene ali abwino aphe oipa). Kutero ndi bwino kwa inu pamaso pa Mlengi wanu.” Choncho (Allah) wavomera kulapa kwanu. Ndithudi, Iye Ngovomera kulapa mochuluka, Wachisoni chosatha.
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona.
Ndipo tidakuphimbani ndi mthunzi wa mitambo (pamene mudali kuoloka chipululu cha mchenga), ndipo tidakutsitsirani Mana (zakumwa zotsekemera ngati uchi) ndi Salwa (zinziri), ndi kukuuzani: “Idyani zinthu zabwino izi zimene takupatsani.” Komatu sadatichitire Ife choipa koma adali kudzichitira okha zoipa.
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene tidati: “Lowani m’mudzi uwu, ndikudya m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; ndipo lowerani pachipata chake uku mutawerama (kusonyeza kuthokoza Allah) ndipo nenani: “E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu.” “Tikukhululukirani machimo anu ndipo tiwaonjezera (mphoto yaikulu) ochita zabwino.”
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mûsa adapemphera anthu ake madzi kwa Allah (atagwidwa ndi ludzu loopsa m’chipululu), tidati: “Menya mwala ndi ndodo yakoyo.” (Atamenya), anatulukadi m’menemo akasupe khumi ndi awiri. Potero fuko lililonse lidadziwa malo awo omwera. (Izi zidachitika kuti asakangane). Choncho idyani, ndiponso imwani mu zopatsa za Allah (popanda inu kuzivutikira), ndipo musasimbwe pa dziko uku mukuononga.
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudati: “E iwe Mûsa! Sitingathe kupirira ndi chakudya chamtundu umodzi (chomwe ndi Mana ndi Salwa); choncho tipemphere kwa Mbuye wako kuti atitulutsire (atipatse) ife zimene nthaka imameretsa, monga masamba, nkhaka, adyo, nyemba za mtundu wa chana ndi anyezi.” Iye adati: “Kodi mukufuna kusinthitsa chonyozeka ndi chabwino? Pitani m’midzi, ndipo kumeneko mukapeza zimene mwapemphazi.” Potero adapatsidwa kunyozeka ndi kusauka; nabwerera ndi mkwiyo wa Allah. Zimenezo n’chifukwa chakuti iwo sadali okhulupirira zisonyezo za Allah, ndikuti adali kupha aneneri a Allah popanda chifukwa. Zidali tero chifukwa cha kunyoza kwawo, ndipo adali olumpha malire.
Ndithu amene akhulupirira (aneneri akale), ndi Ayuda, ndi Akhirisitu ndi Asabayi[3]; aliyense wa iwo amene akhulupirire Allah (tsopano, monga momwe akunenera Mneneri Muhammad (s.a.w) nakhulupiriranso za tsiku lachimaliziro, uku akuchita ntchito zabwino, akalandira mphoto yawo kwa Mbuye wawo. Pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula.
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene tidalandira chipangano chanu (kuti mudzagwiritsa ntchito zomwe zili m’buku la Taurat), ndipo tidakweza pamwamba panu phiri (la Sinai; tidati kwa inu): “Gwirani mwamphamvu chimene takupatsani, ndipo kumbukirani zili m’menemo (pozigwiritsa ntchito. Ndiponso musazinyozere) kuti mukhale oopa Allah.”
Ndithudi mudawadziwa (anthu) amene adapyola malire mwa inu pakuswa kupatulika kwa tsiku la Sabata (m’mene tidawalangira chifukwa chosodza nsomba pa tsiku loletsedwa). Ndipo tidati kwa iwo: “Khalani anyani onyozeka.”
Ndipo tidakuchita kukhala anyaniko, chilango chochenjeza amene adalipo pa nthawiyo ndi akudza pambuyo pawo, ndiponso phunziro kwa oopa Allah.
(Kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Ndithudi, Allah akukulamulani kuti muzinge ng’ombe.” Iwo adati: “Kodi ukutichitira zachipongwe?” Iye adati: “(Sichoncho), ndikudzitchinjiriza ndi Allah kukhala mwa anthu aumbuli.”
Iwo adatinso: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atilongosolere mmene kakhalidwe kake kalili. Ndithudi, ng’ombe zimene wafotokozazo n’zofanana kwa ife. Ndipo ndithudi, Allah akafuna tikhala oongoka.”
Adati: “Ndithudi Iye akuti, imeneyo ndi n’gombe yosaigwiritsa ntchito yolima m’nthaka, ndiponso yosathilira mbewu; yabwinobwino yopanda banga.” Iwo adati: “Tsopano wabweretsa (mawu a) choonadi.” Choncho adaizinga, koma padatsala pang’ono kuti asachite (lamulolo).
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudapha munthu, kenako mudakangana ndi kukankhirana za munthuyo, (ena ankati uje ndiye wapha, pomwe ena ankati koma uje ndiye wapha). Ndipo Allah atulutsira poyera zimene mudali kubisa.
Choncho tidati: “Mmenyeni (wakufayo) ndi gawo la nyamayo. (Potero auka ndikunena za amene adamupha).” Momwemo Allah adzawaukitsa akufa (m’manda monga adamuukitsira wakufayo pamaso panu), ndipo akukusonyezani zizindikiro Zake kuti mukhale ndi nzeru.
Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: Takhulupirira (kuti uyu, Muhammad (s.a.w) ndi mneneri woona, ndipo watchulidwa m’mabuku athu).” Koma akakhala kwaokha kuseli, amati: “Mukuwauza iwo (Asilamu) zimene Allah anakufotokozerani (m’buku la Taurat) kuti adzakhale ndi mtsutso pa inu kwa Mbuye wanu? Kodi mulibe nzeru?
“Kodi sadziwa kuti Allah akudziwa zomwe akubisa ndi zomwe akuonetsera poyera? (Kwa Allah palibe chobisika).
Ndipo mwa iwo (Ayudawo) zilipo mbuli zosadziwa kuwerenga buku (la Allah), koma ziyembekezero zabodza basi, ndipo iwo alibe china koma kungoganizira.
Chilango cha ukali chili pa amene akulemba buku ndi manja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” (akunena bodzalo) kuti apeze zinthu za mtengo wochepa (za m’dziko lapansi); choncho kuonongeka kuli pa iwo chifukwa cha zomwe manja awo alemba, ndiponso kuonongeka n’kwawo chifukwa cha zomwe akupeza.
Ndipo kumbukirani pamene tidalandira pangano lanu kuti simukhetsa mwazi wanu, ndikutinso simudzatulutsana nokha m’nyumba zanu, ndipo inu munavomereza zimenezi, ndipo inu mukuikira umboni zimenezi (koma simudatsate malamulowo).
(Iwo) adati: “Mitima yathu yakutidwa, (potero tikulephera kumvetsa ulaliki wako, iwe Muhammad (s.a.w).’’ Iwo ngabodza pa zimene akunenazi. Koma Allah wawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Tero n’zochepa zimene akuzikhulupirira.
Ndipo pamene buku lidawadzera (m’nyengo ya mtumiki Muhammad {s.a.w}) lochokera kwa Allah, loikira umboni zomwe zili pamodzi ndi iwo (adalikana), pomwe kale (lisadadze bukulo) adali kupempha chithandizo (kupyolera kwa mtumiki wolonjezedwa) chogonjetsera amene sadakhulupirire. Koma pamene chidawadzera chimene adachidziwa, (Qur’an) adachikana. Choncho matembelero a Allah ali pa osakhulupirira.
N’choipa zedi chimene asinthanitsira (chisangalalo cha tsiku lachimaliziro cha) mitima yawo pa kukana kwao zimene Allah adavumbulutsa, chifukwa cha njiru basi kuti Allah watsitsira chifundo chake amene wamfuna mwa akapolo Ake (amene sali Myuda). Potero adabwerera ndi mkwiyo wa Allah kuonjezera pa mkwiyo wakale. Ndipo osakhulupirira adzakhala ndi chilango chosambula.
Ndipo akauzidwa (Ayuda): “Khulupirirani zimene Allah wavumbulutsa (kwa mtumiki Muhammad {s.a.w}).” Amanena: “Tikukhulupirira zimene zidavumbulitsidwa kwa ife,” ndipo amazikana zomwe sizili zimenezo ngakhale izo zili zoona, zomwe zikutsimikizira pa zimene ali nazo pamodzi. Nena: “Nanga bwanji mudapha aneneri a Allah kalelo ngati muli okhulupiriradi?”
Ndipo adakudzerani Mûsa ndi zisonyezo zoonekera, koma pambuyo pake mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe), ndipo potero mudali anthu ochita zoipa kwabasi.
Ndipo (kumbukirani nkhani iyi, inu ana a Israyeli) pamene tidalandira kwa inu pangano lamphamvu, ndipo tidakukwezerani phiri pamwamba panu (uku tikuti): “Gwiritsani mwamphamvu (malamulo) amene takupatsani, ndipo mverani.” (Iwo) adati: “Tamva (mawu anu), koma tanyozera.” Ndipo adamwetsedwa m’mitima mwawo kukonda kupembedza thole (mwana wang’ombe) chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Nena: “N’choipa zedi chimene chikhulupiliro chanu chikukulamulirani ngati inu mulidi okhulupirira.”
Koma sadzailakalaka (imfa) ngakhale pang’ono, chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza (chifukwa cha machimo omwe adadzichitira). Ndipo Allah akudziwa bwino za anthu oipa.
Ndipo muwapeza (Ayuda) kuti ngokondetsetsa kukhala ndi moyo wautali kuposa anthu ena, kuposanso anthu amene akuphatikiza (Allah ndi mafano). Aliyense wa iwo amafuna atapatsidwa moyo wokwana zaka chikwi chimodzi. Pomwe kupatsidwa kwake moyo wautali sikungamuike kutali ndi chilango. Ndipo Allah akuona zonse zimene akuchita.
Nena: “Amene akhale mdani wa Gaburieli (chifukwa chobweretsa chivumbulutso kwa Muhammad {s.a.w}, iyeyo ndi mdani wa Allah). Ndithudi, iye waivumbulutsa Qur’an mumtima mwako mwachilolezo cha Allah. Kudzatsimikidzira zomwe zidali patsogolo pake, ndiponso ndi chiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira.
Ndipo adatsatira njira za afiti zomwe asatana adali kuwafotokozera m’nthawi ya ufumu wa Sulaiman. Ndipo Sulaiman sadamkane Allah (sadali mfiti), koma asatana ndi amene adamkana, naphunzitsa anthu ufiti (umene adaudziwa kuyambira kale); natsatiranso (njira za ufiti) zimene zinatsitsidwa kwa Angelo awiri Haruta ndi Maruta (ku midzi ya) ku Babulo. Koma Angelowo sadaphunzitse aliyense pokhapokha atamuuza kuti: “Ife ndife mayeso (ofuna kuona kugonjera kwanu malamulo a Allah); choncho musamkane (Allah).” Komabe ankaphunzira kwa iwo njira zolekanitsira pakati pa munthu ndi mkazi wake, (ndi zina zotero). Ndipo sadavutitse aliyense ndi zimenezo koma mwachilolezo cha Allah. Ndipo akuphunzira zomwe zingawavutitse pomwe sizingawathandize. Ndithudi, akudziwa kuti yemwe wausankha (ufitiwo) sadzakhala ndi gawo lililonse (la zinthu zabwino) tsiku lachimaliziro. Ndithudi, nchoipitsitsa chimene adzisankhira okha akadakhala akudziwa.
E inu amene mwakhulupirira! Musam’nenere (Mneneri liwu lakuti) “raina” (ndicholinga chomunenera kuti iye ndi mbutuma), koma mnenereni (liwu lakuti) “utiyang’anire,” ndipo mverani malamulo. Kwa osakhulupirira kuli chilango chopweteka.
Kodi mukufuna kumfunsa Mtumiki wanu (inu Asilamu) monga momwe Mûsa adafunsidwira kale (mafunso achipongwe)? Ndipo amene angasinthitse chikhulupiliro ndi kusakhulupirira, ndithudi wasokera njira yolingana (yopanda majiga).
Ayi, koma amene nkhope yake yagonjera kwa Allah uku akuchita zabwino (kwa anthu anzawo) iye ndi amene adzapeza mphoto yake kwa Mbuye wake. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso iwo sadzadandaula.
Ndipo Ayuda akumanena: “Akhrisitu alibe chilichonse (chotsamira pa chipembedzo chawo);” naonso Akhrisitu akumanena: “Ayuda alibe chilichonse (chotsamira pa chipembedzo chawo),” pomwe onsewa akuwerenga buku (lomwe adawavumbulutsira popanda kutsatira zili m’bukulo). Momwemonso akunena amene sali odziwa (Arabu opembedza mafano) monga zonena zawo (Ayuda). Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chimaliziro pa zomwe adali kusiyana.
Kodi alipo woipitsitsa woposa amene akutsekereza (anthu kulowa) m’misikiti ya Allah kuti lisatchulidwe m’menemo dzina Lake nalimbika kuiononga (misikitiyo)? - Kotero kuti sikunali koyenera kwa iwo kulowa mmenemo koma mwa mantha. Kuyaluka kwa pa dziko lapansi nkwawo ndipo tsiku lachimaliziro iwo adzapeza chilango chachikulu.
Ndipo kuvuma ndi kuzambwe nkwa Allah; ndipo pamalo paliponse pamene mwatembenukira, (pomwe Allah wakulamulirani kuti mutembenukire), pamenepo mupezapo chiyanjo cha Allah. Ndithudi Allah Ngokwanira ponseponse, Wodziwa chilichonse.
Ndipo (osakhulupirira) akumanena: “Allah wadzipangira mwana.” (Allah) wapatukana ndi zimenezo. Koma (zolengedwa) zonse za kumwamba ndi pansi Nzake. Zonse zikumumvera Iye.
(Iye ndi) Mlengi wa thambo ndi nthaka popanda chofanizira. Ndipo akafuna chinthu kuti chichitike amangoti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi.
Ndithudi, Ife takutumiza (iwe Mtumiki {s.a.w}) ndi choonadi kuti ukhale wouza nkhani zabwino ndi wochenjeza. Ndipo siudzafunsidwa za anthu a ku Moto.
Anthu omwe tidawapatsa buku naliwerenga kuwerenga koyenera (kopanda kusintha mawu ake ndi matanthauzo ake), iwo ndi amene akulikhulupirira (bukuli la Qur’an). Koma amene angalikane iwowa ndi omwe ali oonongeka.
Ndipo opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza munthu mnzake ndi chilichonse, ndipo dipo silidzalandiridwa, ngakhale dandaulo lililonse silidzamthandiza, ndiponso iwo sadzapulumutsidwa.
Ndipo kumbukirani pamene Ibrahim Mbuye wake (Allah) adamuyesa iye mayeso ndi malamulo ambiri; ndipo iye adakwaniritsa. Adamuuza: “Ndithudi, Ine ndichita iwe kukhala mtsogoleri wa anthu.” (Ibrahim adayankha kuti): “Kodi ndi ana anga omwe?” Adati: “(Inde; koma) lonjezo langa silingawafike ochita zoipa.”
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene tidapanga nyumba (ya Al-Kaaba) kuti pakhale pamalo pobwererapo anthu (poyendera anthu) ndikukhalanso malo achitetezo. Ndipo pachiteni kukhala popemphelera Swala pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira (pomamga nyumbayo). Ndipo tidalamula Ibrahim ndi Ismail kuti: “Ayeretsereni nyumba Yanga oizungulira (pochita twawaf) ndi amene akuchita m’bindikiro, owerama ndi kulambira (kuswali mmememo).
Ndipo (kumbukirani nkhani iyi) pamene Ibrahim adanena: “E Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa chitetezo, ndipo zipatseni nzika zake zipatso, amene akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro mwa iwo. Allah adati: “Nayenso wosakhulupirira ndinkondweretsa pang’ono; kenako ndidzamkankhira ku chilango cha Moto. Taonani kunyansa malo obwerera.
Ndipo (kumbukiraninso) pamene Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Allah): “E Mbuye wathu! Tilandireni (ntchito yathuyi), ndithudi, Inu ndinu Akumva; Odziwa.”
“E Mbuye wathu! Tichiteni Kukhalala Asilamu (ogonjera Inu), pamodzinso ndi ana athu muwachite kukhala fuko la Chisilamu (logonjera Inu). Ndipo tidziwitseni (njira) za mapemphero athu; ndipo landirani kulapa kwathu, ndithudi, Inu Ndinu Wolandira kulapa mochuluka; Wachisoni chosatha.”
(Kumbukiraninso) pamene Mbuye wake adamuuza kuti: “Khala Msilamu (gonjera).” (Iye) adati: “Ndili Msilamu (ndagonjera) kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.”
Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi, chonchonso Ya’qub (adalangizanso ana ake kuti): “E inu ana anga! Ndithudi, Allah wakusankhirani chipembedzo; choncho musafe pokhapokha muli Asilamu (ogonjera Mulungu).”
Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita.
Ndipo (Ayuda ndi Akhrisitu) adati (kwa Asilamu): “Khalani Ayuda kapena Akhrisitu mukhala oongoka.” Nena: “Koma (tikutsata) chipembedzo cha Ibrahim yemwe adaleka zipembedzo zopotoka, ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).”
Nenani (inu Asilamu kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu); “Takhulupirira Allah ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi zidzukulu (zake) ndi zimene adapatsidwa Mûsa, Isa (Yesu), ndiponso zimene adapatsidwa aneneri (ena) kuchokera kwa Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati pa mmodzi wa iwo (koma onse tikuwakhulupirira). Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”
Choncho ngati akhulupirira (Ayuda ndi Akhrisitu) monga mmene mwakhulupirira inu, ndiye kuti awongoka. Koma ngati akutembenuka (posakhulupirira) ndiye kuti iwo ali m’kutsutsana. Choncho Allah akuteteza ku zoipa zawo, ndipo Iye Ngwakumva; Wodziwa.
(Tsatirani) chiongoko cha Allah (Chisilamu). Kodi ndi ndani amene ali ndi chiongoko chabwino kuposa Allah? Ndipo ife Iye Yekha timupembedza.
Nena (iwe Muhammad {s.a.w} kwa Ayuda ndi Akhrisitu): “Ha! Mukutsutsana nafe za Allah (ponena kuti bwanji wapereka uneneri kumbali ya ife), pomwe Iye ndi Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu? (Pamene mudali olungama adakupatsani uneneri, ndipo pamene mudakhota adakulandani natipatsa ife). Ife tili ndi zochita zathu; inunso muli ndi zochita zanu, ndipo ife tikudzipereka kwathunthu kwa Iye (Allah).”
Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita.
۞ Posachedwapa mbutuma za anthu zikhala zikunena: “Nchiyani chimene chawatembenuza ku chibula (mbali yoyang’ana popemphera) chawo chomwe akhala akulunjika nkhope zawo.” Nena: “Kuvuma ndi kuzambwe ndi kwa Allah amamuongolera amene wamfuna kunjira yolunjika.”
Choncho takusankhani (inu Asilamu) kukhala mpingo wabwino (wapakatikati) kuti mukhale mboni pa anthu ndi kuti Mtumiki (s.a.w) akhale mboni pa inu. Ndipo chibula (choyang’ana mbali ya ku Yerusalemu) chomwe udali nacho sitidachichite koma kuti timdziwitse (adziwike kwa anthu) amene akutsata Mtumiki (s.a.w), ndi yemwe akutembenukira m’mbuyo. Ndipo ndithudi, chidali chinthu chovuta kupatula kwa omwe Allah wawaongola. Ndipo nkosayenera kwa Allah kusokoneza Swala zanu, pakuti Allah Ngoleza kwabasi kwa anthu, Ngwachifundo chambiri. [6]
Ndithudi, taona kutembenukatembenuka kwa nkhope yako (kuyang’ana) kumwamba. Choncho tikutembenuzira ku chibula chimene ukuchifunacho. Tero tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (Al-Kaaba). Ndipo paliponse pamene mulipo yang’anitsani nkhope zanu kumene kuli (msikitiwo). Ndithudi amene adapatsidwa buku akudziwitsitsa kuti chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wawo. Ndipo Allah siwonyalanyaza zimene akuchita. (Koma chilichonse chikulembedwa m’kaundula).
(Kuyang’ana ku Al-Kaaba popemphera Swala ndicho) choonadi chomwe chachokera kwa Mbuye wako, choncho usakhale mmodzi mwa openekera.
Ndipo (mpingo) uliwonse udali ndi chibula chimene udali kuchilunjika. Choncho pikisanani pochita zabwino. Paliponse pamene mungakhale Allah adzakubweretsani nonsenu pamodzi (pa tsiku la chimaliziro). Ndithudi, Allah Ngokhoza chinthu chilichonse.
Ndipo paliponse pomwe wapita tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (panthawi yopemphera). Chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita.
Choncho ndikumbukireni (pondithokoza pa mtendere umene ndakupatsaniwu). Nanenso ndikukumbukirani (pokulipirani mphoto yaikulu). Ndipo ndiyamikeni; musandikane.
Ndithudi, Safaa ndi Marwa ndizizindikiro zolemekezera chipembedzo cha Allah. Choncho, amene akukachita mapemphero a Hajj ku nyumbayo, kapena kuchita Umrah, sikulakwa kwa iye kuzungulira pamenepo (pakati pamapiri amenewo). Ndipo amene achite chabwino modzipereka (adzalipidwa). Ndithudi Allah Ngothokoza; Ngodziwa.[8]
Kupatula amene alapa ndi kukonza (zolakwika) nachilongosola (choonadicho kwa anthu), iwowo ndi amene ndiwalandira kulapa kwao. Ndipo ine Ngolandira kulapa kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
M’menemo (m’chilango cha matembelero) adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo chilango sichidzapeputsidwa kwa iwo, ndipo sadzapatsidwa nthawi (yopumula).
Ndipo mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi basi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha.[10]
Ndithudi, m’kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu-zikulu zomwe zikuyenda pa nyanja (zitasenza zinthu) zothandiza anthu, ndi madzi amene Allah wawatsitsa kuchokera ku mitambo, naukitsira nawo nthaka pambuyo pokhala youma, nawanditsa m’menemo mtundu uliwonse wa nyama (chifukwa cha madziwo), ndi m’kusinthanasinthana kwa mphepo, ndi mitambo yomwe yalamulidwa kuyenda pakati pa thambo ndi nthaka; ndithudi, (m’mzimenezo) muli zisonyezo kwa anthu anzeru, (kuti Allah alipo).
Ndipo fanizo la amene sadakhulupirire (omwe akulalikidwa mawu a Allah, ndi makani awo) lili ngati (mbusa) yemwe akukuwira ziweto zake ndi kuzikalipira pomwe izo sizimva tanthauzo la mawu oitanawo, koma kuitana (chabe) ndi kufuula. (Iwo) ndi agonthi, abubu ndi akhungu. Tero iwo sangazindikire.
Iye akukuletsani (kudya) nyama yofa yokha, liwende, nyama yankhumba ndi nyama yodulidwa poikuwira mayina a mafano kusiya Allah. Koma amene wasimidwa (nadya) popanda kuchikhumba choletsedwacho ndi mosapyoza muyeso palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.[13]
Zimenezo nchifukwa chakuti Allah adavumbulutsa buku Lake mwa choonadi (ndipo iwo adalikana). Koma amene asemphana pa zabukuli ali mu nkangano wonkera nawo kutali kusiya choonadi.
Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali yakuvuma ndi kuzambwe (popemphera Swala); koma ubwino weniweni ndi (wa omwe) akukhulupirira Allah, tsiku lachimaliziro, angelo, buku ndi aneneri; napereka chuma - uku eni akuchifunabe - kwa achibale ndi amasiye, ndi masikini ndi a paulendo (omwe alibe choyendera), ndi opempha, ndi kuombolera akapolo; napemphera Swala, napereka chopereka (Zakaat); ndi okwaniritsa malonjezo awo akalonjeza, ndi opirira ndi umphawi ndi matenda ndi panthawi yankhondo. Iwowo ndi amene atsimikiza (Chisilamu chawo). Ndiponso iwowo ndi omwe ali oopa Allah.
Mu Qiswas (kubwezerana kofanana) muli kusunga moyo kwa inu, E, inu eni nzeru! Kuti mudzitchinjirize (ku mchitidwe ophana).[16]
Ndipo amene waopa kuti wopereka wasiya angapendekere kumbali yokhota kapena ku uchimo, nalinganiza pakati pawo, palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah ngokhululuka zedi, Ngwachifundo chambiri.
E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu kusala (m’mwezi wa Ramadan) monga momwe kudalamulidwira kwa anthu akale, inu musadabwere kuti muope Allah (popewa zoletsedwa).
(Kusalaku nkwa) masiku owerengeka. Koma amene akhale odwala mwa inu kapena akhale paulendo, (namasula masiku ena), akwaniritse chiwerengerocho m’masiku ena. Ndipo kwa amene sangathe kusala apereke dipo lodyetsa masikini. Ndipo amene achite zabwino mwa chifuniro chake, kutero ndibwino kwa iye. Ndipo kusala (pamene kukulolezedwa kumasula) ndibwino kwa inu, ngati muli odziwadi (kufunika kwa kusala).[19]
(Mwezi mwalamulidwa kusalawu ndi) mwezi wa Ramadan womwe mkati mwake Qur’an idavumbulutsidwa kuti ikhale chiongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera za chiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa (pakati pa choonadi ndi bodza). Ndipo mwa inu amene akhalepo (pa mudzi) m’mweziwu, asale. Koma amene ali wodwala, kapena ali pa ulendo, akwaniritse chiwerengero m’masiku ena (cha masiku amene sadasale). Allah akukufunirani zopepuka ndipo samakufunirani zovuta, ndiponso (akufuna) kuti mukwaniritse chiwerengerocho ndi kumlemekeza Allah chifukwa chakuti wakutsogolerani, ndikutinso mukhale othokoza.[20]
Kwaloledwa kwa inu mu usiku wosala kukumana ndi akazi anu. Iwo ali ngati chovala chanu, inunso muli ngati chovala chawo. Allah wadziwa kuti mudali kudzichitira chinyengo nokha. Choncho walandira kulapa kwanu ndipo wakukhululukirani. Tsopano khudzanani nawo ndipo funani chimene Allah wakulamulirani, ndipo idyani ndi kumwa mpaka udziwike bwinobwino kwa inu ulusi woyera kuchokera ku ulusi wakuda kum’bandakucha (kufikira mudziwe kuti kucha kwalowa, usiku watha). Kenako kwaniritsani kusala mpaka dzuwa litalowa. Ndipo musakhudzane nawo (akazi anu) pamene inu mukuchita mbindikiro m’misikiti. Amenewo ndi malire a Allah; choncho musaayandikire. Motere ndimo Allah akulongosolera mwatsatanetsatane zisonyezo zake kwa anthu kuti akhale oopa Allah (potsatira malamulo ake ndi kusiya zoletsedwa). [22]
Ndipo menyanani nao nkhondo pa njira ya Allah (modziteteza) amene akukuthirani nkhondo. Koma musalumphe malire (powamenya amene sadakuputeni), ndithu Allah sakonda olumpha malire.[24]
Ndipo athireni nkhondo (amene akukuthirani nkhondo popanda chifukwa) paliponse pamene mwawapeza; ndipo atulutseni paliponse pamene adakutulutsani; chifukwa kusokoneza anthu pa chipembedzo chawo nkoipitsitsa kuposa kupha. Koma musamenyane nawo pafupi ndi Msikiti Wopatulika pokhapokha atayamba ndiwo kukumenyani pamenepo. Chomwecho ngati atamenyana nanu pamenepo inunso amenyeni. Motero ndi momwe ilili mphoto ya osakhulupirira.
Koma ngati asiya, ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo menyanani nao kufikira pasakhale masautso (ochokera kwa iwo powasautsa asilamu popanda chifukwa). Ndipo chipembedzo chikhale cha Allah (osati kupembedza anthu). Koma ngati asiya, pasakhale mtopola kupatula kwa okhawo amene ali ochita zoipa.
Mwezi wopatulika kwa mwezi wopatulika; ndipo zinthu zopatulika paikidwa kubwezerana. Ndipo amene wakuchitirani mtopola, inunso mchitireni mtopola molingana ndi momwe wakuchitirani mtopola, ndipo opani Allah (musapyoze kuposa momwe wakuchitirani). Ndipo dziwani kuti Allah ali pamodzi ndi oopa.
Ndipo kwaniritsani Hajj ndi Umrah chifukwa chofuna kukondweretsa Allah. (Izi zili mkutsimikiza kulowa m’mapemphero a Hajj). Ndipo ngati mutatsekerezedwa (kukwaniritsa mapempherowo), choncho zingani nyama zimene zili zosavuta kuzipeza (monga mbuzi), ndipo musamete mitu yanu kufikira nsembeyo ifike pamalo pake pozingirapo (pomwe ndi pamalo pamene mwatsekerezedwapo). Ndipo amene mwa inu ali odwala kapena ali ndi zovutitsa ku mutu kwake, (nachita zomwe zidali zoletsedwa monga kumeta) apereke dipo la kusala kapena kupereka sadaka (chopereka chaulere), kapena kuzinga chinyama. Ndipo ngati muli pa mtendere, choncho amene angadzisangalatse pochita Umrah kenako nkuchita Hajj, azinge nyama imene ili yosavuta kupezeka (monga mbuzi). Ndipo Amene sadapeze, asale masiku atatu konko ku hajjiko ndipo asalenso masiku asanu ndi awiri mutabwerera (kwanu). Amenewo ndi masiku khumi okwanira. Lamuloli ndi la yemwe banja lake silili pafupi ndi Msikiti Wopatulika. Ndipo opani Allah, dziwani kuti Allah Ngwaukali polanga.
(Mapemphero a) Hajj ali ndi miyezi yodziwika, (yomwe ndi: Shawwal, Dhul Qa’da ndi Dhul Hijjah). Amene watsimikiza kuchita Hajj m’miyezi imeneyo, asachite ndi kuyankhula zauve, ndiponso asapandukire malamulo (pochita zoletsedwa uku iye ali m’mapemphero a Hajj), ndiponso asakangane ali m’Hajjimo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, Allah achidziwa. Ndipo dzikonzereni kamba wa paulendo, ndithu kamba wabwino (wadziko lapansi) ndi amene angakupewetseni kupemphapempha, (koma kamba wabwino wa tsiku lachimaliziro ndiko kuopa Allah). Choncho ndiopeni inu eni nzeru.
Sikulakwa kwa inu kufunafuna zabwino kwa Mbuye wanu (pogulitsa zinthu zanu uku muli m’mapemphero a Hajj, kapena kugula). Ndipo mukabwerera kuchokera ku Arafat, tamandani Allah pamalo otchedwa Masha’r Harâm (Muzdalifa). Ndipo mkumbukireni monga momwe adakutsogolerani, chikhalirecho kale mudali mwa osokera.
Kenako yendani limodzi kuchokera pamalo pamene akuchokerapo anthu onse (pomwe ndi pa Arafat), ndipo pemphani chikhululuko kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo mukamaliza mapemphero anu (tsiku la Idi komwe ndikuponya sangalawe, kuzinga nyama za nsembe, kumeta ndi kuzungulira Ka’aba (Tawaful Ifâda), mtamandeni Allah monga momwe mudali kutamandira makolo anu kapena mtamandeni koposa. Ndipo alipo ena mwa anthu amene akunena (kuti): “E Mbuye wathu! Tipatseni padziko lapansi.” Ndipo iwo alibe gawo lililonse pa tsiku lachimaliziro.
Ndipo alipo ena mwa iwo omwe akunena kuti: “E Mbuye wathu! tipatseni zabwino pa dziko lapansi komanso pa tsiku lachimaliziro mudzatipatsenso zabwino, ndi kutitchinjiriza ku chilango cha Moto.”
Ndipo mwa anthu alipo amene zoyankhula zake zikukondweretsa (iwe) pano pa dziko la pansi, (koma tsiku lachimaliziro kuipa kwake kudzadziwika). Ndipo iye akutsimikizira Allah kuti akhale mboni pa zomwe zili mu mtima mwake pomwe iye ndi wa makani kwambiri.[25]
Ndipo akauzidwa kuti: “Opa Allah”, Akugwidwa ndi mwano womupititsa ku machimo, choncho Jahannam ikukwana kwa iye (kuwuchotsa mwano wakewo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!
Ndipo ngati mutaterezuka (kuchimwa) pambuyo pokudzerani zisonyezo (za Allah) zoonekera poyera, dziwani kuti Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.
Kodi pali china chimene akuyembekeza posakhala kuwadzera Allah m’mithunzi ya mitambo ndi (kuwadzera) angelo; nkuweruzidwa chilamulo (chakuonongeka kwawo)? Komatu zinthu zonse zimabwezedwa kwa Allah.
Anthu onse adali a chipembedzo chimodzi (cha Chisilamu panthawi ya Adam kufikira Nuh kenako adayamba kupatukana), ndipo Allah adatumiza aneneri onena nkhani zabwino ndi ochenjeza; ndipo pamodzi nawo adavumbulutsa mabuku achoonadi kuti aweruzire pakati pa anthu pa zimene adasemphana. Ndipo sadasemphane pa zimenezo koma aja amene adapatsidwa mabukuwo pambuyo powadzera zizindikiro zoonekera poyera, chifukwa chakuchitirana dumbo pakati pawo. Koma Allah adawaongolera amene adakhulupirira kuchoonadi cha zomwe adasempaniranazo, mwachifuniro chake. Ndipo Allah amamutsogolera ku njira yolunjika amene wamfuna.
Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe sanakudzereni masautso olingana (ndi omwe) adawapeza amene adamuka kale inu musanabadwe? Kusauka ndi matenda zidawakhudza, ndipo adanjenjemeretsedwa koopsa kufikira mtumiki pamodzi ndi amene adakhulupirira naye adati: “Chipulumutso cha Allah chibwera liti?” Dziwani kuti ndithu chipulumutso cha Allah chili pafupi![28]
Kwalamulidwa kwa inu kumenya nkhondo (yotetezera chipembedzo cha Allah ) pomwe iyo (nkhondoyo) njodedwa ndi inu. Komatu mwina mungachide chinthu pomwe icho chili chahwino kwa inu. Mwinanso mungakonde chinthu pomwe icho chili choipa kwa inu. Koma Allah ndiyemwe akudziwa, ndipo inu simudziwa.
Akukufunsa za (lamulo la) kumenya nkhondo m’miyezi yopatulika. nena: “Kumenya nkhondo m’miyeziyo ndi tchimo lalikulu. Komatu kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kumkana Allah, (ndi kuletsa anthu) ku Msikiti Wopatulikawo, ndi kutulutsa anthu m’menemo nditchimo loposa kwa Allah. Ndipo kutsekereza anthu kuchipembedzo chawo nzoipa kwabasi kuposa kupha. Ndipo sasiya kumenyana nanu kufikira akuchotseni m’chipembedzo chanu ngati angathe. Ndipo mwa inu amene atuluke m’chipembedzo chake, kenako namwalira uku ali osakhulipirira, iwo ndi omwe ntchito zawo zaonongeka pa dziko lapansi mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali.[30]
Za m’dziko lapansi ndi (zinthu) za tsiku lachimaliziro. Ndipo akukufunsa za ana amasiye, nena: “Kuwachitira zabwino ndiwo ubwino; ngati mutasakanikirana nawo, (ndibwinonso). Iwo ndi abale anu; ndipo Allah akumdziwa woononga ndi wochita zabwino. Ndipo Allah akadafuna, akadakukhwimitsirani malamulo. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.”
Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu ya chikazi yopembedza mafano, ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) musawakwatitse kwa amuna osakhulupirira, mpaka akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yopembedza mafano, ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira ku Moto. Koma Allah akuitanira ku Munda wamtendere ndi ku chikhululuko mwa lamulo lake. Ndipo Iye akulongosola mwatsatanetsatane ndime za mawu ake kwa anthu, kuti athe kukumbukira.[32]
Ndipo (iwo) akukufunsa za kukhala malo amodzi ndi azimayi panthawi imene akusamba, auze (kuti): “Zimenezo ndizovulaza (ndiponso ndiuve). Choncho apatukireni akazi m’nthawi ya matenda akumwezi, ndipo musawayandikire mpaka ayere. Ngati atayera, kumananaoni kupyolera m’njira yomwe Allah wakulamulani. Ndithu Allah amakonda olapa, ndiponso amakonda odziyeretsa. ”
Ndipo kulumbilira kwanu dzina la Allah musakuchite kukhala chokuletsani kuchita zinthu zabwino (za m’Chisilamu) ndi kuopa Allah, ndi kuyanjanitsa pakati pa anthu. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[33]
Allah sangakulangeni pa kulumbira kwanu kopanda pake, koma adzakulangani chifukwa cha malumbiro anu amene mitima yanu yatsimikiza mwa mphamvu. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza.
Kwa omwe akulumbilira kuti adzipatula kwa akazi awo, (nyengo yawo) ayembekezere miyezi inayi. Koma ngati atabwerera (nakhala pamodzi ndi akazi awo), ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi. [34]
Ndipo akazi osiidwa (asakwatiwe) ayembekezere mpaka kuyeretsedwa kutatu kukwanire. Ndipo nkosafunika kwa iwo kubisa chimene Allah walenga m’mimba zawo, ngati akukhulupiriradi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amuna awo ali ndi udindo wowayenereza kuwabwerera m’nthawi imeneyi ngati akufuna kuchita chimvano. Nawonso azimayi ali ndi zofunika kuchitiridwa (ndi amuna awo) monga m’mene ziliri kwa azimayiwo kuchitira amuna awo mwachilamulo cha Shariya. Koma amuna ali ndi udindo okulirapo kuposa iwo. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya. [35]
Twalaq (mawu achilekaniro cha ukwati omwe akupereka mwayi kwa mwamuna kubwereranso kwa mkazi wake), ndi omwe anenedwa kawiri. Kenako amkhazike (mkaziyo) mwa ubwino (ngati afuna kubwererana naye) kapena alekane mwa ubwino (ngati atafunadi kumleka. Ndipo sangathe kubwererana naye ngati atamunenera kachitatu mawu achilekano pokhapokha atakwatiwa kaye ndi mwamuna wina ndi kusiidwa ndi mwamunayo). Ndipo sizili zololedwa kwa inu kuti mutenge (kulanda) chilichonse chimene mudawapatsa (akazi anu) pokhapokha (onse awiri) ngati akuopa kuti satha kusunga malire a Allah (malamulo a Allah). Ngati muopa kuti sasunga malire a Allah, ndiye kuti pamenepo pakhala popanda tchimo kwa iwo (mwamuna woyamba ndi mkaziyu) kulandira (kapena kupereka) chodziombolera mkazi. Awa ndiwo malire a Allah; choncho musawalumphe. Ndipo amene alumphe malire a Allah (powaswa), iwowo ndiwo anthu ochita zoipa.[36]
Tero ngati atamuleka (ndi kunena katatu mawu achilekaniro, choncho mkazi ameneyo) ngosaloledwa kwa iye pambuyo pakutero, kufikira akwatiwe ndi mwamuna wina. (Ngati mwamuna winayo atamusiya), palibe kulakwa kwa awiriwo kubwererana ngati akuona kuti adzasunga malire a Allah. Ndipo awa ndi malire a Allah omwe akuwalongosola kwa anthu odziwa.
Ndipo pamene musiya akazi powanenera mawu achilekaniro, niiyandikira kukwana nyengo ya edda yawo (chiyembekezero chawo), abwelereni mwa ubwino; kapena lekananaoni mwa ubwino, ndipo musawabwelere mowavutitsa kuti mupyole malire a Allah (poswa malamulo ake). Ndipo amene achite zimenezo ndiye kuti wadzichitira yekha zoipa. Ndipo ndime za mawu a Allah musazichitire chibwana. Ndipo kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu; makamaka chisomo chokuvumbulutsirani buku (la Qur’an) ndi kudziwitsidwa nzeru zomwe akukulangizani nazo. Ndipo opani Allah, ndithudi dziwani kuti Allah Ngodziwa chirichonse.[37]
Ndipo akazi omwe angobereka kumene ayamwitse ana awo zaka ziwiri zathunthu kwa yemwe akufuna kukwaniritsa kuyamwitsa. Ndiudindo wa abambo kuwapezera chakudya chawo ndi chovala chawo (ana awo ndi ) amayiwo, motsatira malamulo a Shariya. Ndipo mzimu wa munthu aliyense sukakamizidwa, koma m’mene ungathere. Ndipo mayi wa mwanayo asazunzidwe chifukwa cha mwana wakeyo. Nayenso bambo wa mwanayo asazunzike chifukwa cha mwana wakeyo. Ndipo lamuloli lilinso chimodzimodzi pa mlowam’malo (ngati bambo atamwalira). Ndipo onse awiri ngati atafuna kumletsa kuyamwa, mogwirizana pakati pa awiriwo, ndi mokambirana palibe kulakwa pa iwo awiriwo. Ndipo ngati mutafuna kuwapezera ana anu akazi ena owayamwitsa (omwe si amayi awo), palibe uchimo mwa inu ngati mwapereka chimene udalonjeza kuwapatsa (oyamwitsawo) mwa ubwino. Ndipo opani Allah; dziwaninso kuti Allah akuona zonse zimene mukuchita.[38]
234, Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi, choncho (akaziwo) ayembekezere (asakwatiwe) miyezi inayi ndi masiku khumi. Ndipo akakwanitsa nyengo ya chiyembekezero chawo cha edda, sitchimo kwa inu pazimene akaziwo adzichitira okha (monga kudzikongoletsa ndi kudziwonetsa kwa ofunsira ukwati); motsatira malamulo a Shariya. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita.
Ndipo sitchimo kwa inu kupereka mawu okuluwika ofunsira ukwati kwa akaziwo (pamene chiyembekezero cha edda yawo chisanathe. Ndiponso palibe uchimo) kapena kubisa mu mtima mwanu, kuwakwatira (chiyembekezo chawo chikadzatha). Allah wadziwa kuti mukhala mukuwakumbukira akaziwo. Koma musawalonjeze mobisa (kuti: “Ikatha edda ndidzakukwatira).” Koma nenani mawu abwino. Ndipo musatsimikize kumanga ukwati mpaka nyengo yolembedwayo ikwanire. Ndipo dziwani kuti Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwanu. Tero muopeni (Allah), dziwaninso kuti Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza.
Palibe tchimo pa inu mutawapatsa akazi mawu achilekaniro pomwe simudakhudzane nawo; pomwenso simudawadziwitse gawo la chiwongo chawo; koma asangalatseni (powapatsa chilekaniro). Wopeza bwino apereke malinga ndikupeza bwino kwake; wochepekedwa apereke malingana ndikuchepekedwa kwake. Chilekaniro chosangalatsacho chikhale molingana ndi malamulo a Shariya, ndipo ndilamulo kwa ochita zabwino.[39]
Ndipo ngati mwalekana nawo (akaziwo) musanakhudzane nawo mutawadziwitsa gawo la chiwongo chawo, apatseni theka la chimene mudagwirizana kuwapatsa pokhapokha ngati akaziwo atakana okha (theka la chiwongocho), kapena (mwamuna) uja yemwe kumangitsa kwa ukwati kuli m’manja mwake amusiire (chiwongo chonsecho mkaziyo). Ndipo ngati mutasiirana (zimenezo) zingakuyandikitseni kumbali yoopa Allah. Ndipo musaiwale kuchitirana zabwino pakati panu (ngakhale kuti mukulekana). Ndithudi Allah akuona zonse zimene mukuchita.[40]
Ndipo ngati muli ndi mantha (kupemphera mwalamulo pamene mukumenyana ndi adani anu), pempherani uku mukuyenda, kapena mutakwera chokwera. Ndipo mukakhala pachitetezo mkumbukireni Allah (pempherani) monga momwe wakuphunzitsirani zomwe simudali kuzidziwa.
Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi awo, alangize (amlowam’malo awo, monga makolo ndi achibale) za akazi awo kuti awapatse zodyera m’nyengo ya chaka chimodzi popanda kutulutsidwa (m’nyumba zomwe ankakhala ndi amuna awo). Koma ngati akaziwo atuluka (okha), palibe kulakwa pa inu pa zimene adzichitira okha zomwe nzogwirizana ndi chilamulo cha Shariya. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.
Ndipo akazi osiidwa ukwati, apatsidwe chilekaniro chowasangalatsa m’chilamulo cha Shariya. Ili ndi lamulo kwa amene akuopa Allah.[42]
Kodi sudamve (nkhani za) amene adatuluka m’nyumba zawo ali zikwizikwi kuopa imfa? Ndipo Allah adawauza: “Mwalirani,” (ndipo adamwalira chabe popanda chifukwa chilichonse). Kenako Adawaukitsa (kuti adziwe kuti imfa njosathawika). Ndithudi, Allah Ndimwini kuchita zabwino pa anthu, koma anthu ambiri sathokoza.[43]
Kodi ndani angamkongoze Allah ngongole yabwino (yochokera m’chuma chake powapatsa amphawi ndi kupereka pa njira ya Allah) kuti amuonjezere zoonjezera zambiri? Ndipo Allah ndi yemwe amafumbata ndi kutambasula, ndipo kwa Iye nkumene mudzabwezedwa.[44]
Ndipo mneneri wawo adawauza (kuti): “Ndithu chizindikiro cha ufumu wake, ndikukudzerani bokosi lomwe mkati mwake muli mpumulo wa miyoyo yanu wochokera kwa Mbuye wanu, ndi zotsalira zomwe adazisiya anthu a Mûsa ndi anthu a Harun, atanyamula angelo. Ndithu m’zimenezo muli chisonyezo kwa inu (chosonyeza kuyenera kwa ufumu wake pa inu) ngati mulidi okhulupirira.”
Choncho, Taluti pamene adapita ndi magulu (ake) a nkhondo, adati: “Allah akuyesani mayeso ndi mtsinje (womwe mukumane nawo panjira komwe mukupitako). Choncho amene akamwe mmenemo sali nane. Koma amene sakamwa adzakhala pamodzi nane kupatula amene watunga ndi dzanja lake (ndikumwa; iyeyo ndiye kuti sadalakwe). Koma (iwo) adamwa m’menemo kupatula ochepa mwa iwo. Choncho pamene adaoloka iye pamodzi ndi aja omwe adakhulupirira limodzi naye, (iwo) adati: “Lero sitingamuthe Jaluti ndi magulu ake a nkhondo.” Omwe adali ndi chitsimikizo chokumana ndi Allah adati: “Kodi ndimagulu angati ochepa amene adagonjetsa magulu ambiri mwa chilolezo cha Allah! Ndipo Allah Ali pamodzi ndi opirira.[45]
Ndipo pamene adapita kukalimbana ndi Jaluti (mfumu ya adaniwo), pamodzi ndi magulu ake a nkhondo (anthu a Taluti) adati: “E Mbuye wathu! Titsanulireni chipiliro, ndipo limbikitsani mapazi athu: Tithangateni kwa anthu osakhulupirira.”
Awa ndi ma Ayah (ndime) a Allah; tikuwawerenga kwa iwe (Mtumiki s.a.w) mwachoonadi. Ndithudi, iwe ndiwe mmodzi mwa atumiki.
Allah palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chilichonse. Kusinza sikumgwira ngakhale tulo. Zonse za kumwamba ndi za pansi nza Iye. Kodi ndani angathe kuombola kwa Iye popanda chilolezo chake? Akudziwa za patsogolo ndi zomwe zili pambuyo pawo ndipo zolengedwazo sizidziwa chilichonse pa zomwe zili m’kudziwa Kwake kupatula chimene wafuna. Mpando wake wachifumu wakwanira kumwamba ndi pansi ndipo sizimamvuta kuzisunga zimenezo. Ndipo Iye (Yekha) Njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, (Ngolemekezeka kwambiri).[48]
Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu) adati: “Kodi Allah adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo pakufa kwake?” Ndipo Allah adampatsa imfa kwa nthawi yokwana zaka zana limodzi (100), kenako adamuukitsa namufunsa: “Kodi wakhala nyengo yaitali bwanji?” Adati: “Ndakhala nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku.” (Allah) adati: “Korna wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona chakudya chako ndi zakumwa zako, sizinaonongeke (sizinavunde). Ndipo yang’ana bulu wako (ali mafupa okhaokha oyoyoka); ndi kuti ukhale chisonyezo kwa anthu, (nchifukwa chake takuukitsa ku imfa). Ndipo yang’ana mafupa (a bulu wako) momwe tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu.” Choncho pamene zidazindikirika (kwa iye, woukitsidwayo), adati: “Ndikudziwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse.”[51]
Ndipo (kumbukira) pamene Ibrahim adati: “E Mbuye wanga!, Ndionetseni mmene mudzaaukitsire akufa.” (Allah) adati: “Kodi sunakhulupirirebe?” Adati: “Iyayi, (ndikukhulupirira), koma (ndikufuna kuona zimenezo) kuti mtima wanga ukhazikike.” (Allah) adati: “Choncho katenge mbalame zinayi; uzisonkhanitse kwa iwe (mpaka uyizindikire mbalame iliyonse mmene ilili, ndipo kenako uziduledule zonsezo zidutswazidutswa ndikuzisakaniza ndi kuzigawa mzigawo zinayi). Ndipo paphiri lililonse ukaikepo gawo limodzi la zimenezo, ndipo kenako uziitane. Zikudzera zikuthamanga. Ndipo dziwa kuti Allah ndi Mwini mphamvu zoposa, Ngwanzem zakuya.”[52]
Fanizo la amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah lili ngati fanizo la njere imodzi yomwe yatulutsa ngala zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala iliyonse nkukhalamo njere zana limodzi. Ndipo Allah amamuonjezera amene wamfuna (kuposera pamenepa). Ndipo Allah alinazo zambiri, Ngodziwa.[53]
Mawu abwino, ndi kukhululukira (amene wakulakwira) nzabwino zedi kuposa sadaka yotsatizidwa ndi masautso. Ndipo Allah ndiyemwe ali Wolemera kwambiri ndiponso Woleza (kwa zolengedwa Zake).
Ndipo fanizo la anthu amene akupereka chuma chawo chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah ndi kulimbikitsa mitima yawo (pa chipembedzo cha Allah) lili ngati fanizo la munda umene uli pachitunda, chiufikira chimvula tero nubweretsa zinthu zake dzochuluka moonjeza kawiri (kuposera pachikhalidwe chake). Ndipo ngati chimvula sichidaudzere, ndiye kuti yamawawa (nkuukwanira mundawo). Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita.
Satana amakuopsezani ndi umphawi ndi kukulamulirani kuchita zoipa (monga umbombo), pomwe Allah akukulonjezani chikhululuko kuchokera kwa Iye ndi ubwino (waukulu ngati mupereka); ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngodziwa.[54]
Ndipo chilichonse chomwe mungapereke kapena naziri (lonjezo) iliyonse yomwe mwalonjeza Allah, ndithudi, Allah akudziwa zonsezi. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi.
Siudindo wako kuwaongola, koma Allah amamuongola amene wamfuna, (udindo wako nkulalikira kokha). Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke, (phindu lake) lili pa inu eni, ndipo musapereke pokhapokha pofunafuna chikondi cha Allah. Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke adzakubwezerani mokwanira (mphoto yake), ndipo simudzaponderezedwa.[55]
(Sadakazo ziperekedwe) kwa amphawi amene atsekerezedwa pa njira ya Allah, amene sangathe kuyenda pa dziko (kukachita ntchito yopezera zofunika pamoyo wawo). Amene sadziwa za chikhalidwe chawo, amawaganizira kuti ngolemera chifukwa chakudziletsa kwawo (kupemphapempha). Ungawazindikire (kuti ngosowedwa) ndi zizindikiro zawo. Sapempha anthu mwaliuma. Ndipo chabwino chilichonse chimene mukupereka, ndithudi, Allah ali Wodziwa za icho.
Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali.[56]
Allah amachotsa madalitso pa (chuma cha) katapira ndipo amaika madalitso pa chaulere. Ndipo Allah sakonda aliyense wosakhulupirira, wamachimo ambiri.
Ndipo ngati wokongola ali ndi mavuto, choncho (wokongoza) amdikire mpaka apeze bwino. Koma ngati inu (okongoza mungakhululuke pakusiya kuitanitsa ngongole) muisintha kuti ikhale sadaka, ndibwino kwa inu ngati mukudziwa (zimenezo).
Ndipo liopeni tsiku lomwe inu mudzabwezedwa kwa Allah. Ndipo kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zonse zimene adachita (ndi manja ake), ndipo iwo sadzaponderezedwa.
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا۟ إِذَا تَدَايَنتُم بِدَيْنٍ إِلَىٰٓ أَجَلٍۢ مُّسَمًّۭى فَٱكْتُبُوهُ ۚ وَلْيَكْتُب بَّيْنَكُمْ كَاتِبٌۢ بِٱلْعَدْلِ ۚ وَلَا يَأْبَ كَاتِبٌ أَن يَكْتُبَ كَمَا عَلَّمَهُ ٱللَّهُ ۚ فَلْيَكْتُبْ وَلْيُمْلِلِ ٱلَّذِى عَلَيْهِ ٱلْحَقُّ وَلْيَتَّقِ ٱللَّهَ رَبَّهُۥ وَلَا يَبْخَسْ مِنْهُ شَيْـًۭٔا ۚ فَإِن كَانَ ٱلَّذِى عَلَيْهِ ٱلْحَقُّ سَفِيهًا أَوْ ضَعِيفًا أَوْ لَا يَسْتَطِيعُ أَن يُمِلَّ هُوَ فَلْيُمْلِلْ وَلِيُّهُۥ بِٱلْعَدْلِ ۚ وَٱسْتَشْهِدُوا۟ شَهِيدَيْنِ مِن رِّجَالِكُمْ ۖ فَإِن لَّمْ يَكُونَا رَجُلَيْنِ فَرَجُلٌۭ وَٱمْرَأَتَانِ مِمَّن تَرْضَوْنَ مِنَ ٱلشُّهَدَآءِ أَن تَضِلَّ إِحْدَىٰهُمَا فَتُذَكِّرَ إِحْدَىٰهُمَا ٱلْأُخْرَىٰ ۚ وَلَا يَأْبَ ٱلشُّهَدَآءُ إِذَا مَا دُعُوا۟ ۚ وَلَا تَسْـَٔمُوٓا۟ أَن تَكْتُبُوهُ صَغِيرًا أَوْ كَبِيرًا إِلَىٰٓ أَجَلِهِۦ ۚ ذَٰلِكُمْ أَقْسَطُ عِندَ ٱللَّهِ وَأَقْوَمُ لِلشَّهَٰدَةِ وَأَدْنَىٰٓ أَلَّا تَرْتَابُوٓا۟ ۖ إِلَّآ أَن تَكُونَ تِجَٰرَةً حَاضِرَةًۭ تُدِيرُونَهَا بَيْنَكُمْ فَلَيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ أَلَّا تَكْتُبُوهَا ۗ وَأَشْهِدُوٓا۟ إِذَا تَبَايَعْتُمْ ۚ وَلَا يُضَآرَّ كَاتِبٌۭ وَلَا شَهِيدٌۭ ۚ وَإِن تَفْعَلُوا۟ فَإِنَّهُۥ فُسُوقٌۢ بِكُمْ ۗ وَٱتَّقُوا۟ ٱللَّهَ ۖ وَيُعَلِّمُكُمُ ٱللَّهُ ۗ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَىْءٍ عَلِيمٌۭ ﴿٢٨٢﴾
E inu amene mwakhulupirira! Mukamakongozana ngongole kwa nyengo yodziwika ilembeni. Ndipo mlembi pakati panu alembe mwachilungamo; ndipo mlembi asakane kulemba monga momwe Allah wamphunzitsira; choncho alembe. Ndipo alakatule (mawu olembedwawo ndi wokongolayo) yemwe ngongole ili pa iye. Nayenso aope Allah, Mbuye wake, ndipo asapungule chilichonse m’menemo (m’ngongole). Ndipo ngati wokongola ndiozelezeka kapena wofooka, kapena iye mwini sangathe kulembetsa (momveka), choncho amulembetsere myang’aniri (wakili) wake (yemwe akuyang’anira zinthu zake) mwachilungamo. Ndipo funiraponi mboni ziwiri zochokera mwa anthu anu aamuna (asilamu). Koma ngati amuna awiri palibe, choncho apezeke mwamuna mmodzi ndi akazi awiri (kuti aikire umboniwo), amene mumavomereza kukhala mboni kuti ngati mmodzi mwa iwo (akazi awiriwo) angaiwale mmodzi wawo akumbutse winayo. Ndipo mboni zisakane zikaitanidwa. Ndiponso musanyozere kulemba (ngongoleyo) yaing’ono kapena yaikulu mpaka nyengo yake. Zimenezo (kulembako) ndibwino kwa Allah, ndipo ncholungama zedi kumbali yaumboni, ndiponso nchothandiza kuti musakhale ndi chipeneko. Koma akakhala malonda omwe ali pompo omwe mukupatsana pakati panu (tsintho) sikulakwa kwa inu kusawalemba. Koma funani mboni pamene mukugulitsana. Komatu asavutitsidwe mlembi ndiponso mboni. Ngati mutachita zimenezo (zoletsedwazo) kumeneko ndiko kutuluka (m’chilamulo cha Mulungu wanu), ndipo opani Allah, Allah akukuphunzitsani. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.[57]
Ndipo ngati muli pa ulendo, ndipo simudapeze mlembi, choncho (wokongoza) apatsidwe chikole (pinyolo) m’manja mwake. Ngati wina wasungitsa mmodzi wa inu chinthu (pomudalira wokhulupirika) choncho amene wayesedwa wokhulupirikayo abweze chinthucho kwa mwini wake, ndipo aope Allah, Mbuye wake. Ndipo musabise umboni (ngakhale uli wokuipirani). Ndipo amene abise ndiye kuti mu mtima mwake mwalowa uchimo; ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.[58]
Mtumiki wakhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake. Naonso asilamu (akhulupirira). Onse akhulupirira Allah, angelo Ake, mabuku Ake ndi atumiki Ake. (Iwo pamodzi ndi Mtumiki wawoyo akunena kuti): “Sitingalekanitse aliyense pakati pa atumiki Ake, (onse tikuwakhulupirira).” Ndipo akunena: “Tamva ndiponso tamvera, (choncho tikukupemphani) chikhululuko chanu. E Mbuye wathu! Ndipo kwa Inu nkobwerera.”[59]
Allah sakakamiza mzimu uliwonse koma chimene chili cholingana ndi kukhoza kwake. (Ndipo phindu la) zimene mzimuwo udapeza ndilake ndiponso kuluza kwa zomwe udapeza nkwake. (Asilamuwo amanena) “E Mbuye wathu! Musatilange tikaiwala kapena tikalakwitsa, E Mbuye wathu! Musatisenzetse mtolo (wamalamulo) monga munawasenzetsera amene adalipo patsogolo pathu. E Mbuye wathu! Musatisenzetse chimene sitingachithe. Tifafanizireni machimo athu, tikhululukireni zolakwa zathu, ndiponso tichitireni chifundo. Inu Ndinu Mtetezi wathu. Choncho tithangateni ku anthu osakhulupirira.”
Share