وَلَن تَرْضَىٰ عَنكَ ٱلْيَهُودُ وَلَا ٱلنَّصَٰرَىٰ حَتَّىٰ تَتَّبِعَ مِلَّتَهُمْ ۗ قُلْ إِنَّ هُدَى ٱللَّهِ هُوَ ٱلْهُدَىٰ ۗ وَلَئِنِ ٱتَّبَعْتَ أَهْوَآءَهُم بَعْدَ ٱلَّذِى جَآءَكَ مِنَ ٱلْعِلْمِ ۙ مَا لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن وَلِىٍّۢ وَلَا نَصِيرٍ ﴿١٢٠﴾
Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu sangakondwere nawe pokhapokha utatsatira chipembedzo chawo. Nena: “Ndithudi, chiongoko cha Allah ndichomwe chili chiongoko chenicheni.” Ngati utsata zilakolako zawo pambuyo pa zomwe zakudzera, monga kuzindikira (kwenikweni), sudzapeza mtetezi aliyense ngakhale mthandizi kwa Allah.