Surah Al-Baqarah ( The Cow ) - Aya 264

Surah Al-Baqarah ( The Cow ) - Chewa - Aya 264 Aya count 286

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ لَا تُبْطِلُوا۟ صَدَقَٰتِكُم بِٱلْمَنِّ وَٱلْأَذَىٰ كَٱلَّذِى يُنفِقُ مَالَهُۥ رِئَآءَ ٱلنَّاسِ وَلَا يُؤْمِنُ بِٱللَّهِ وَٱلْيَوْمِ ٱلْءَاخِرِ ۖ فَمَثَلُهُۥ كَمَثَلِ صَفْوَانٍ عَلَيْهِ تُرَابٌۭ فَأَصَابَهُۥ وَابِلٌۭ فَتَرَكَهُۥ صَلْدًۭا ۖ لَّا يَقْدِرُونَ عَلَىٰ شَىْءٍۢ مِّمَّا كَسَبُوا۟ ۗ وَٱللَّهُ لَا يَهْدِى ٱلْقَوْمَ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿٢٦٤﴾
E inu amene mwakhulupirira! Musaononge sadaka zanu pokumba ndiponso popereka masautso, monga yemwe akupereka chuma chake modzionetsera kwa anthu, ndipo sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Choncho fanizo lake lili ngati thanthwe lomwe pamwamba pake pali dothi. Kenako nkulifikira chimvula (nkuchotsa dothi lonse lija), nkulisiya lopanda kanthu. Tero sadzatha kupeza chilichonse pazimene adachita. Ndipo Allah satsogolera anthu osakhulupirira.
Share