ثُمَّ قَسَتْ قُلُوبُكُم مِّنۢ بَعْدِ ذَٰلِكَ فَهِىَ كَٱلْحِجَارَةِ أَوْ أَشَدُّ قَسْوَةًۭ ۚ وَإِنَّ مِنَ ٱلْحِجَارَةِ لَمَا يَتَفَجَّرُ مِنْهُ ٱلْأَنْهَٰرُ ۚ وَإِنَّ مِنْهَا لَمَا يَشَّقَّقُ فَيَخْرُجُ مِنْهُ ٱلْمَآءُ ۚ وَإِنَّ مِنْهَا لَمَا يَهْبِطُ مِنْ خَشْيَةِ ٱللَّهِ ۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ ﴿٧٤﴾
Koma mitima yanu idauma pa mbuyo pa zimenezo; (nkukhala gwa!) ngati mwala kapena kuposerapo. Ndithudi pali miyala ina yomwe ikutuluka mkati mwake mitsinje; ndipo pali ina imene imang’ambika nkutuluka madzi mkati mwake; ndipo pali ina imene imagudubuzika chifukwa cha kuopa Allah. (Koma inu Ayuda simulalikika ngakhale mpang’ono pomwe). Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita.