Surah Al-Baqarah ( The Cow ) - Aya 150

Surah Al-Baqarah ( The Cow ) - Chewa - Aya 150 Aya count 286

وَمِنْ حَيْثُ خَرَجْتَ فَوَلِّ وَجْهَكَ شَطْرَ ٱلْمَسْجِدِ ٱلْحَرَامِ ۚ وَحَيْثُ مَا كُنتُمْ فَوَلُّوا۟ وُجُوهَكُمْ شَطْرَهُۥ لِئَلَّا يَكُونَ لِلنَّاسِ عَلَيْكُمْ حُجَّةٌ إِلَّا ٱلَّذِينَ ظَلَمُوا۟ مِنْهُمْ فَلَا تَخْشَوْهُمْ وَٱخْشَوْنِى وَلِأُتِمَّ نِعْمَتِى عَلَيْكُمْ وَلَعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ ﴿١٥٠﴾
Paliponse pamene wapita (iwe Mtumiki {s.a.w}) tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika. Ndipo paliponse pamene (inu Asilamu) muli tembenuzirani nkhope zanu kumbali yake (ya Msikitio) kuti anthu asakhale ndi mtsutso pa inu, kupatula amene adzichitira zoipa mwa iwo. Tero musawaope, koma opani Ine, ndipo ndikwaniritsa chisomo Changa pa inu kuti muongoke.
Share