Surah At-Taubah ( The Repentance )

Surah At-Taubah ( The Repentance ) - Chewa Aya count 129

Uku ndikudzipatula kochokera kwa Allah ndi Mtumiki wake ku (mapangano) amene mudapangana nawo (kenako nkuswa mapangano awowo) a m’gulu la Amushirikina.[204]
(Auze Amushirikina kuti): Yendani pa dziko miyezi inayi basi. (Pambuyo pake sipadzakhala chitetezo pakati pawo ndi ife). Ndipo dziwani kuti inu simungathe kumpambana Allah. Ndipo Allah Ngosambula osakhulupirira.
Ndipo miyezi yopatulika ikatha (yomwe njoletsedwa kuchitamo nkhondo), apheni Amushirikina paliponse pamene mwawapeza (menyanani nawo), ndipo agwireni (monga momwe iwo akukuchitirani). Ndipo azungulireni ndi kuwakhalira pa njira zonse. Koma akalapa nayamba kupemphera Swala, ndikupereka chopereka (Zakaat), ilekeni njira yawoyo (asiyeni). Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo ngati mmodzi wa Amushirikina Atakupempha chitetezo (kuti amvere mawu a Allah), mtetezeni kuti amve mawu a Allah. Kenako (ngati sadakhutitsidwe nawo), mpititseni kumalo kwake mwamtendere (ngati safuna kulowa m’Chisilamu). Izi nchifukwa chakuti iwo ndi anthu osadziwa.
Chingakhalepo bwanji chipangano pakati pa Amushirikina (oswa mapangano nthawi ndi nthawi) ndi Allah ndi Mthenga Wake, kupatula okhawo amene mudapangana nawo mapangano pa Msikiti Wopatulika? (Amene adakwaniritsa mapangano awo). Ngati iwo akupitiriza kulungama (posunga mapanganowo) kwa inu, nanunso pitirizani kulungama kwa iwo. Ndithu Allah akukonda amene akumuopa.
(Kodi inu ndiye osunga malonjezo?) Bwanji? Pomwe iwo akakhala ndi mphamvu pa inu sakusungirani chibale kapena pangano? Amakusangalatsani ndi pakamwa pawo pomwe mitima yawo ikukana (kukukondani). Ndipo ambiri a iwo ngoukira malamulo (a Allah).[205]
Asinthanitsa Ayah za Allah (ndi zinthu za dziko lapansi) ndi mtengo wochepa, ndipo atsekereza (anthu) kunjira Yake. Ndithu nzoipa kwabasi zomwe iwo akhala akuchita.
Ndipo ngati aswa malumbiro awo pambuyo pomanga chipangano chawo, ndi kuyamba kutukwana chipembedzo chanu, menyanani nawo atsogoleri a kusakhulupirira. Ndithu iwo alibe mapangano, (sasunga mapangano. Menyanani nawo) kuti iwo aleke (machitidwe awo oipa).
Kodi nchotani kuti musamenyane nawo anthu omwe aswa malonjezo awo, natsimikiza kumtulutsa (kumpirikitsa mu mzinda wa Makka, kapena kumupha) Mtumiki? Iwo ndi amene adayamba kukuputani pachiyambi, nanga mukuwaopa chotani? Allah ndiye wofunika kumuopa, ngati inu mulidi okhulupirira.
Menyanani nao; Allah awalanga kupyolera m’manja anu, ndipo awasambula ndi kukupulumutsani kwa iwo ndi kuchiritsa kuwawidwa (komwe kudali) m’mitima mwa anthu okhulupirira (chifukwa cha masautso omwe adawapeza kwa iwo).
Ndi kuchotsa mkwiyo wa m’mitima mwawo (Asilamu). Ndi kuti Allah Alandire kulapa kwa amene wamfuna. Ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.
Nkosayenera kwa Amushirikina kukhala (ndi udindo) woyang’anira Misikiti ya Allah pomwe iwo akudzichitira okha umboni kuti ngosakhulupirira. Awo (ndi omwe) zochita zawo zabwino zapita pachabe. Ndipo iwo ku Moto adzakhala nthawi yaitali.
Mbuye wawo akuwauza nkhani yabwino ya chifundo chochokera kwa Iye, ndi chiyanjo (Chake) ndi Minda yomwe mkati mwake adzapezamo mtendere wamuyaya.
Ndithu Allah wakhala akukupulumutsani (kwa adani anu) m’malo ambiri omenyanira nkhondo, ndi pa tsiku la Hunaini, pamene kudakunyengani kuchuluka kwanu. Koma sikudakuthandizeni chilichonse. Ndipo dziko lidakupanani ngakhale kuti lidali lotambasuka ndipo kenako mudatembenukira kumbuyo (kuthawa).[206]
Ndipo pambuyo pa izi, Allah alandira kulapa kwa amene wamfuna (mwa osakhulupirira powalowetsa m’Chisilamu). Ndipo Allah Ngokhululuka Ngwachisoni chosatha.
Ndipo Ayuda akunena kuti Uzairi ndimwana wa Mulungu, naonso Akhrisitu akunena kuti Mesiya (Isa {Yesu}) ndimwana wa Mulungu. Awa ndi mawu amene akunena ndi pakamwa pawo (popanda umboni wochokera kwa Allah); akutsanzira zonena za omwe sadakhulupirire kale. Allah awaononge; kodi iwo akusokera chotani (kusiya choonadi)?
Awachita ophunzira a za chipembedzo chawo ndi ansembe awo kukhala milungu kusiya Allah (powatsata pa zimene akuwalamula popanda umboni wa Allah). (Amsandutsanso) Mesiya (Isa {Yesu}) mwana wa Mariya (kukhala mulungu); chikhalirecho sadalamulidwe china koma kupembedza Mulungu Mmodzi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, wapatukana ndi zimene akumphatikiza nazozo.
Pa tsiku lomwe (chuma chawo) chidzatenthedwa ku moto wa Jahannam, ndipo ndi chumacho zidzatenthedwa nkhope zawo, nthiti zawo ndi misana yawo (ali kuwuzidwa kuti): “Izi ndi zija zomwe mudadzisungira nokha. Choncho lawani (chilango) cha zomwe mudali kuzisunga.[207]
Ndithu kutalikitsa ndi kuchedwetsa (mwezi wopatulika kuti usafike mwamsanga), kumaonjezera kusakhulupirira (mwa Allah), zoterozo akusokerezedwa nazo amene sadakhulupirire. Chaka china amauyesa wosapatulika pomwe chaka china amauyesa wopatulika ndi cholinga chokwaniritsa chiwerengero cholingana ndi miyezi yomwe Allah adaipatula kukhala yopatulika. Choncho, chimene Allah adaletsa, amachiyesa chololedwa. Zakometsedwa kwa iwo zochita zawo zoipa. Ndipo Allah sawatsogolera anthu osakhulupirira.[209]
E inu amene mwakhulupirira! Mwatani; mukauzidwa (kuti): “Pitani mukachite Jihâd pa njira ya Allah,” mukudziremetsa pa nthaka (polemedwa ndi kutulukako)? Kodi mwasangalatsidwa ndi moyo wa pa dziko lapansi kuposa moyo wa tsiku lachimaliziro? Koma zosangalatsa za m’moyo wa dziko lapansi poyerekeza ndi (moyo wa) tsiku lachimaliziro, ndi zochepa kwambiri.
Ngati simupita (ku nkhondoko), (Allah) akulangani ndi chilango chowawa, ndipo abweretsa anthu ena m’malo mwa inu; ndipo simungamuvutitse ndi chilichonse (ngati musiya kupita kukamenyera chipembedzo Chake). Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.
Ngati simumthandiza (Mtumuki Muhammad {s.a.w} palibe kanthu), ndithu Allah adamthandiza pamene adamtulutsa aja amene sadakhulupirire. Pamene adali awiriwiri kuphanga, pamene ankanena kwa mnzake: “Usadandaule. Ndithu Allah ali nafe pamodzi.” Ndipo Allah adatsitsa mpumulo Wake pa iye, ndipo adaamthangata ndi asilikali a nkhondo omwe simudawaone. Ndipo mawu a amene sadakhulupirire adawachita kukhala apansi ndipo mawu a Allah ndiwo apamwamba. Ndipo Allah Ngopambana, Ngwanzeru zakuya.
Ukadakhala ulendo wokafuna za m’dziko zopepuka kuzipeza, ndi ulendo wofupika, ndithu akadakutsata (achiphamaso). Koma ulendo wamavutowu wakhala wautali kwa iwo. Ndipo iwo alumbilira Allah (ponena kuti): “Kukadakhala kotheka kwa ife, tikadapita nanu.” (Pa mawu awa), akudziononga okha. Ndipo Allah akudziwa kuti iwo Ngabodza.
Sangakupemphe chilolezo (chotsala ku nkhondo) amene akhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro kuti asapite kukamenyera (chipembedzo cha Allah) ndi chuma chawo ndi Matupi awo. Ndipo Allah akuwadziwa amene akumuopa.
Akadafunadi kuti atuluke (kupita ku nkhondo) akadakonzekera zokonzekera za ku nkhondo; koma Allah sadafune kuti iwo apiteko; choncho adawatsekereza, ndipo kudanenedwa: “Khalani pamodzi ndi Otsalira.”
Ndithudi, akhala akukufunirani chisokonezo kuyambira kale, akusanthulirasanthulira zinthu (n’cholinga choti athane nawe) kufikira choonadi chadza ndi kuonekera poyera lamulo la Allah (lowakhaulitsa Ayuda) iwo asakufuna.
Ndipo mwa iwo pali yemwe akuti: “Ndiloreni ine (kuti nditsale ku nkhondo) ndipo musandiponye m’mayeso (kuopa kuti ndingalakwe ndikaona akazi akumeneko).” Dziwani kuti iwo agwera kale m’mayesero. Ndipo, ndithu Jahannam ikawazinga mbali zonse osakhulupirira.
Chikakupeza chabwino, (iwe Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndi okutsatira) zimawanyansa, ndipo vuto likakupeza amanena: “Tidalingalira zinthu zathu kale. (Nchifukwa chake mavuto atizemba).” Ndipo amatembenuka nkupita uku akukondwa.[210]
Nena: “Kodi chilipo chimene mukuyembekezera mwa ife posakhala chimodzi mwa zinthu ziwiri zabwino, (kupambana pa nkhondo ndi kupeza zotolatola zake, kapena kufa ndikukalowa ku Munda wamtendere)? Ndipo nafe tikukuyembekezerani kuti Allah akupatsani chilango chochokera kwa Iye, kapena kupyolera m’manja mwathu. Choncho bayembekezerani; nafenso tikuyembekezera nanu limodzi.”
Nena (kwa achiphamaso): “Perekani (chuma chanu) mwa chifuniro kapena mosafuna sichizalandiridwa kwa inu. Ndithu inu ndinu anthu otuluka m’chilamulo cha Allah.”
Ndipo ngati iwo akadakondwera ndi chimene Allah ndi Mtumiki Wake wawapatsa, nanena: “Allah watikwanira. Posachedwapa Allah ndi Mtumiki Wake atipatsa zabwino Zake. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Allah.” (Ndiye kuti Allah akadawapatsa zambiri).
Ndithu sadaka (za Zakaati) ndi za mafukara, masikini, ogwira ntchito yosonkhetsa sadakazo, owalimbitsa mitima yawo (pa Chisilamu amene alowa kumene), kuombolera akapolo (kuti akhale afulu), kuthandizira amene ali m’ngongole; kuzipereka pa njira ya Allah; ndi kuwapatsa a paulendo (omwe alibe choyendera). Ili ndi lamulo lochokera kwa Allah, ndipo Allah Ngodziwa kwabasi, Ngwanzeru zakuya.[211]
Ndipo alipo ena mwa iwo amene akuzunza Mneneri ponena kuti: “Uyu ndi khutu (lomvetsera nkhani iliyonse popanda kuiganizira).” Nena: “Ndi khutu labwino kwa inu.” (Mwini khutulo) amakhulupirira Allah, amakhulupirira (zonena) za okhulupirira, ndipo (iye) ndichifundo kwa amene akhulupirira mwa inu. Ndipo amene akuvutitsa Mtumiki wa Allah adzakhala ndi chilango chopweteka.
Akulumbira kwa inu potchula dzina la Allah kuti akukondweretseni (chikhalirecho akunyoza Allah ndi Mtumiki Wake), pomwe Allah ndi Mtumiki Wake ndiye wofunika kuti amkondweretse ngati iwo ngokhulupiriradi (mwachoonadi).
Achiphamaso akuopa kuwatsikira Sura yomwe ingawafotokozere (zachinyengo chawo) chomwe chili m’mitima mwawo. Nena: “Chitani zachipongwe. Ndithu Allah atulutsira poyera zomwe mukuziopazo (kuti Asilamu asazidziwe).”
Ndipo utawafunsa (chifukwa ninji chipembedzo akuchichitira chipongwe)? Anena: “Ife timangosereula ndi kusewera basi (palibe china).” Nena: “Mumachitira Allah ndi Ayah (ndime) Zake ndi Mtumiki Wake zachipongwe?”
Musapereke madandaulo (abodza), ndithu mwaonetsera ukafiri wanu poyera, pambuyo pa kukhulupirira kwanu (kwabodza). Ngati gulu lina mwa inu tilikhululukira (litalapa), gulu lina tililanga chifukwa cha kupitiriza kulakwa kwawo.
Achiphamaso aamuna ndi achiphamaso aakazi onse khalidwe lawo ndi limodzi. Amalamulira zoipa ndikuletsa zabwino, ndipo amafumbata manja awo (sathandiza pa zabwino). Amuiwala Allah (ponyozera malamulo Ake). Iyenso wawaiwala (powanyozera). Ndithu achiphamaso ngotuluka mchilamulo (cha Allah).
Allah walonjeza achiphamaso aamuna ndi achiphamaso aakazi ndi akafiri moto wa Jahannam, akakhala m’menemo nthawi yaitali. Umenewo ukukwanira kwa iwo (kuwalanga). Ndipo Allah wawatembelera, ndipo iwo adzapeza chilango cha nthawi zonse.
(Inu osakhulupirira) ndinu ofanana ndi amene adalipo patsogolo panu. (Tikuonongani monga tidawaonongera iwo; koma) iwo adali ndi nyonga zambiri kuposa inu; adalinso ndi chuma chambiri ndi ana ambiri kuposa inu. Choncho, adasangalalira gawo lawo, inunso mukusangalalira gawo lanu monga momwe adasangalalira gawo lawo omwe adalipo patsogolo panu, ndipo mwamira m’zoipa monga momwe adamilira iwo. Awo ndi amene zochita zawo zidapita pachabe padziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Awo ndi omwe ali otaika (oluza).
Kodi siidawadzere nkhani ya amene adalipo patsogolo pawo anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu; anthu a Ibrahim ndi anthu a ku Madiyan ndi (anthu) a m’midzi imene idatembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba? Atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera (koma adakana kuwatsata. Choncho, Allah adawaononga). Allah sadawachitire choipa, koma ankadzichitira okha zoipa.
Allah waalonjeza okhulupirira aamuna ndi okhulupirira aakazi Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda, adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ndi mokhala mwabwino m’Minda ya Edeni. Ndipo chiyanjo chochokera kwa Allah ndichachikulu (omwe ndi mtendere waukulu kwambiri kuposa zonse). Kumeneko ndiko kupambana zedi.
(Achiphamaso pambuyo pomunenera Allah ndi Mtumiki Wake mawu oipa), akulumbira potchula dzina la Allah (kuti) sadanene (zonyoza), pomwe adanenadi mawu aukafiri, ndipo akana chikhulupiliro pambuyo posonyeza Chisilamu chawo (chabodza); ndipo adatsimikiza (kuchita) zomwe sadathe kuzifika. Komatu sadaone choipa (m’kudza kwa Chisilamu), koma kuti Allah ndi Mtumiki Wake adawalemeretsa ndi zabwino zake. Choncho Ngati alapa, zikhala zabwino kwa iwo. Ndipo ngati anyoza, Allah awalanga ndi chilango chowawa pa moyo wa pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro. Ndipo sadzakhala ndi mtetezi ngakhale aliyense wowapulumutsa pa dziko.
Choncho, chotsatira chake adawaika chinyengo m’mitima mwawo kufikira tsiku lokumana naye (Allah), chifukwa cha kuphwanya kwawo zomwe adamulonjeza Allah. Ndiponso chifukwa cha zabodza zomwe ankanena.
(E iwe Mtumiki!) Uwapemphere chikhululuko (achiphamaso) kapena usawapemphere, (zonsezo nchimodzimodzi). Ngakhale utawapemphera chikhululuko chochuluka kwabasi mokwanira makumi asanu ndi awiri (70) Allah sangawakhululukire. Zimenezo nchifukwa chakuti iwo amkana Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah satsogolera anthu ophwanya malamulo (Ake).
Akondwa amene adasiidwa m’mbuyo (osapita kunkhondo) chifukwa chakukhala kwawo m’mbuyo polekana ndi Mtumiki wa Allah, nakuda kumenyana pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo, nati (kwa anzawo): “Musapite (ku nkhondo) m’nthawi yotenthayi.” Auze: “Moto wa Jahannam ngotentha kwambiri akadakhala akuzindikira.”
Choncho, aseke pang’ono (padziko lapansi). Ndipo adzalira kwambiri (patsiku lachimaliziro); (iyo ndi) mphoto ya zomwe adapeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa).[212]
Ngati Allah akubweza (ku nkhondoko) nkufika kugulu lina la mwa iwo ndipo iwo nkukupempha chilolezo chakutuluka (kupita ku nkhondo zomwe zidzapezeke mtsogolo), nena: “Inu simudzatuluka nane mpaka muyaya, ngakhalenso kumenyana ndi adani pamodzi nane; inu mudakonda kukhala nthawi yoyamba; choncho khalani (nthawi zonse) pamodzi ndi otsalira (pambuyo).”
Ndipo Sura ikavumbulutsidwa (yonena kuti): “Mkhulupirireni Allah ndi kumenya nkhondo (chifukwa cha chipembedzo Chake) pamodzi ndi Mtumiki Wake,” opeza bwino mwa iwo akukupempha chilolezo (kuti asapite ku nkhondo), ndipo akuti: “Tisiye tikhale pamodzi ndi okhala (otsalira m’mbuyo).”
Akondwera pokhala limodzi ndi otsalira m’mbuyo (akazi ndi ana). Ndipo mitima yawo yadindidwa chidindo (yatsekedwa), choncho iwo sazindikira.
Ndipo adza eni madandaulo (owona) mwa anthu akumidzi (omwe ndi Asilamu) kuti awapatse chilolezo (chosapita ku nkhondo). Koma adakhala (popanda kupempha chilolezo kwa Mtumiki) amene amunamiza Allah ndi Mtumiki Wake. (Amenewa ndi achiphamaso omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu pomwe sadali Asilamu). Mwa iwo amene sadakhulupirire Allah chiwapeza chilango chopweteka.
Palibe tchimo (kusapita kunkhondo) kwa amene ali ofooka (pachilengedwe chawo), ngakhale kwa odwala, ngakhale kwa omwe sapeza chothandiza (pa ulendo ngakhale chosiira akubanja lawo) ngati iwo ali ndi cholinga chabwino pa Allah ndi Mtumiki Wake. Palibe njira (yowadzudzulira) amene akuchita zabwino. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni zedi.
۞ Ndithu njira (yodzudzulidwa) ili pa arnene akukupempha chilolezo (choti asapite ku nkhondo ndi kusiyanso kupereka chuma chawo) pomwe iwo ngolemera. Akonda kukhala pamodzi ndi otsala m’mbuyo. Ndipo Allah wadinda chidindo (cha mantha) m’mitima mwawo, tero sadziwa (chilichonse chowathandiza).
Arabu a kumizi ngoyipitsitsa pa kusakhulupirira ndi uchiphamaso ndiponso ngoyenera kusazindikira malire a zomwe Allah wavumbulutsa kwa Mtumiki Wake. Komatu Allah Ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya.
Ndipo alipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe amachichita chimene akupereka pa njira ya Allah ngati dipo (laulere lopanda phindu), ndikumadikira kwa inu kuti miliri ikupezeni. Miliri yoipa ili pa iwo; (iwapeza okha). Ndipo Allah Ngwakumva (nkhani iliyonse), Wodziwa (chilichonse).
Ndipo alipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro ndipo zomwe akupereka (pa njira ya Allah) amazichita monga chodziyandikitsira nacho kwa Allah, ndi (chowachititsa kuti apeze) mapemphero a Mtumiki. Tamverani! Ndithu zimenezo ndizinthu zowayandikitsa kwa Allah. Allah adzawalowetsa ku Mtendere Wake. Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe akukhala m’mphepete mwanu (m’mphepete mwa mzinda wa Madina) alipo achiphamaso (achinyengo), ndiponso eni mzinda wa Madina aphunzira ukatswiri wachinyengo (kotero kuti) sukuwadziwa, Ife tikuwadziwa. Tiwalanga kawiri (pa dziko lapansi) ndipo kenako adzabwezedwa kuchilango chachikulu (pa tsiku lachimaliziro).
Tenga sadaka (Zakaat) m’chuma chawo kuti uwayeretse nayo (kumachimo ndi umbombo) ndi kuti uwatukulire nayo ulemelero wawo kwa Allah; ndipo apemphere (zabwino ndi chiongoko). Ndithu mapemphero ako kwa iwo ndimpumulo. Ndipo Allah Ngwakumva, Wodziwa (chilichonse).
Ndipo aliponso ena amene (adagwa m’machimo omwe) akuyembekezera lamulo la Allah, (kulapa kwawo sikunavomerezekebe), kapena awalanga kapenanso awavomera kulapa kwawo. Ndipo Allah Ngodziwa (khalidwe lawo ndi zomwe zili m’mitima mwawo), Wanzeru zakuya (pa zonse zomwe akuchita kwa anthu Ake popereka mphoto ndi chilango).
Ndipo (alipo achiphamaso ena) amene adamanga msikiti ndi cholinga chodzetsa masautso ndi (kulimbikitsa) kusakhulupirira Allah ndi kuwagawa okhulupirira (mu umodzi wawo) ndi kuupanga kukhala msasa wa omwe adamthira nkhondo Allah ndi Mtumiki Wake kale. Ndithu alumbira (ndikunena): “Sitidali ncholinga china (pomanga msikitiwo) koma ubwino.” Koma Allah akuikira umboni kuti iwo ngabodza.
Usaimilire (ndi kupemphera) m’menemo mpang’ono pomwe. Ndithu msikiti umene udakhazikitsidwa poyamba ncholinga choopa Allah ndiwo wofunika kuti uimilire m’menemo (ndi kupemphera). M’menemo muli anthu okonda kudziyeretsa (matupi ndi mitima yawo); ndipo Allah amakonda odziyeretsa.
Kodi amene wakhazikitsa maziko a chomanga chake chifukwa choopa Allah ndi kufunafuna chiyanjo (Chake), sindiye wabwino, kapena Yemwe wakhazikitsa maziko a chomanga chake m’mphepete mwa dzenje (lakuya) lomwe dothi lake likugumukira (m’dzenjemo) ndipo nkugwa pamodzi naye m’moto wa Jahannam, (ameneyu ndiye wabwino)? Ndithudi, Allah saongolera anthu ochita zoipa.
Chomanga chawo chomwe adachimanga sichileka kudzetsa chikaiko ndi kusakhazikika m’mitima mwawo kufikira mitima yawo itaduka (ndi madandaulo kapena imfa). Ndipo Allah Ngodziwa (chilichonse), Ngwanzeru zakuya (m’zochitachita Zake).
Ndithu Allah wagula kwa okhulupirira moyo wawo ndi chuma chawo (kuti apereke moyo wawo ndi chuma chawo pomenya nkhondo pa njira ya Allah) kuti iwo alandire Munda wamtendere. Akumenya nkhondo pa njira ya Allah, ndipo akupha ndi kuphedwa. Ili ndi lonjezo loona lokakamizika pa Iye lomwe likupezeka m’buku la Taurati, Injili ndi Qur’an. Kodi ndani wokwaniritsa lonjezo lake kuposa Allah? Choncho kondwerani ndi kugulitsa kwanu komwe mwagulitsana Naye. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
(Awo amene alonjezedwa kupeza izi, ndi) omwe amalapa (akalakwa); ochita mapemphero (awo m’njira yoyenera); otamanda Allah kwambiri; ochulukitsa kusala (Swaumu kapena oyendayenda padziko ncholinga chochitira zabwino anthu), owerama, ogwetsa nkhope zawo pansi; olamula zabwino; oletsa zoipa ndi osunga malire a Allah (malamulo Ake). Choncho, auze nkhani yabwino awo amene akhulupirira.
Ndipo sikudali kupempha chikhululuko kwa Ibrahim kuwapemphera bambo wake koma chifukwa cha lonjezo lomwe adamulonjeza. Koma pamene zidaonekera kwa iye poyera kuti iwo (bambo wake) ndi mdani wa Allah, adadzipatula kwa iwo. Ndithudi, Ibrahim adali wochulukitsa kupempha Allah modzichepetsa, woleza mtima.
Ndipo Allah sangasokeretse anthu (ndi kupititsa chilango pa iwo) pambuyo powaongolera ku Chisilamu; koma pokhapokha atawonetsa poyera kwa iwo zimene zingafunike kuzipewa. Ndithu Allah Ngodziwa chilichonse.
Ndithu Allah wafunira zabwino Mtumiki Wake ndi Amuhajirina ndi Answari amene adamtsatira iye (Muhammad {s.a.w}) m’nthawi yamasautso (pokamenyana ndi Aroma pankhondo ya Tabuk), nthawi yomwe mitima ya ena a iwo idatsala pang’ono kupotoka (kutsata machitidwe achikafiri); kenako Allah adawatembenukira ndi chifundo. Ndithu Iye (Allah) kwa iwo Ngodekha, Ngwachisoni chosatha.[213]
Ndiponso (adawatembenukira mwachifundo) aja atatu amene adawadikiritsa (pakusavomera msanga kulapa kwawo), kufikira pamene dziko lidawapana ngakhale lidali lophanuka, nabanika m’mitima mwawo natsimikiza kuti palibe komuthawira Allah (kwina) koma kwa Iye (Allah polapa). Kenako (Allah) adawatsogolera kulapa kuti alape. Ndithu Allah Ngolandira kulapa, Ngwachisoni chosatha.
E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo khalani pamodzi ndi owona (amene akuchitsimikiza Chisilamu chawo ndi zochita zawo, osati kungoyankhula pakamwa pokha).
Nkosayenera kwa anthu a mu mzinda wa Madina ndi amene ali m’mphepete mwawo, mwa Arabu a kuchimizi, kutsalira m’mbuyo mwa Mtumiki wa Allah (poleka kutsagana naye ku nkhondo), ndiponso nkosayenera kwa iwo kudzikonda okha kuposa iye (Mtumiki). Zimenezo nchifukwa chakuti iwo silingaapeze ludzu kapena mavuto kapena njala pa njira ya Allah, ndipo sangaponde malo owakwiitsa osakhulupirira, ndipo sangampatse mdani chompatsa chilichonse chopweteka koma kulembedwa kwa iwo pa zimenezo (kuti achita) ntchito yabwino. Ndithu Allah sawononga malipiro a ochita zabwino.
Nkosafunika kwa okhulupirira kutuluka onse (m’midzi yawo kupita ku Madina ndi kusiya midzi yopanda anthu). Nchifukwa ninji silituluka gulu m’fuko lililonse mwa iwo (ndikupita ku Madina kwa Mtumiki) kukaphunzira bwino za Chipembedzo, ndipo akawachenjeze anthu awo akazabwerera kwa iwo kuti aope.
Ndipo nthawi iliyonse sura yatsopano ikavumbulutsidwa amayang’anana (iwo achiphamaso kuti athawe, asamvere mawu ake, uku akuuzana pakati pawo): “Kodi alipo amene akukuonani?” Kenako amatembenuka nkuthawa. Tero, Allah waikhotetsa mitima yawo chifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira.
Ndithu wakudzerani Mtumiki wochokera mwa inu. Zimamudandaulitsa iye zomwe zikukuvutitsani; iye ngoikira mtima pa inu pokufunirani zabwino; ndipo pa okhulupirira ngodekha ndiponso ngwachisoni.
Koma ngati (iwo osakhulupirira) apitiriza kunyoza, nena: “Allah wandikwanira (palibe vuto lingapezeke kuchokera kwa inu) palibe woti nkupembedzedwa koma Iye basi. Ndatsamira kwa Iye. Ndipo Iye, ndi Bwana wa Arsh (mpando wachifumu) yaikulu!”
Share