Surah Ash-Shuara ( The Poets )

Surah Ash-Shuara ( The Poets ) - Chewa Aya count 227

Tâ-Sîn-Mîm.
Izi ndi Ayah (ndime) za buku (la Qur’an) lofotokoza chilichonse (chofunika m’chipembedzo).
Mwina iwe (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) udziononga wekha (ndi madandaulo) chifukwa chakuti (iwo) sadakhale okhulupirira.
Tikadafuna, tikadawatsitsira chizizwa kuchokera kumwamba; kotero kuti makosi awo akadadzichepetsa ndi chizizwacho, (sakadatha kucheukira kwina koma sitifuna kukakamiza anthu kuti akhale Asilamu).[295]
Ndipo palibe pamene chikuwadzera chivumbulutso chatsopano chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri koma amazipatula ku icho (chivumbulutso).
Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro (zosonyeza mphamvu za Allah). Koma ambiri a iwo sali okhulupirira.
Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako adaitana (m’neneri) Mûsa; adamuuza: “Pita kwa anthu ochita zoipa.”
(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ine ndikuopa kuti anganditsutse.
Ndipo chingabanike chifuwa changa (ndi maganizo, chifukwa chakunditsutsa kwawo); ndiponso lirime langa siliyankhula momveka bwino. Choncho tumizaninso uthengawu kwa Harun (kuti tikhale awiri ndipo azikandithangata pantchito yangayi).
Ndipo iwowo ndili nawo mlandu ndipo ndikuopa kuti angandiphe (pobwezera chimene ndidawalakwira powaphera munthu wawo).
(Allah) adati: “Iyayi! Pitani pamodzi ndi zozizwa Zathu; ndithu Ife tikakhala nanu limodzi (pokuthangatani) uku tikumvetsera (zimene azikanena).”
“Choncho mpitireni Farawo, ndipo kamuuzeni kuti: “Ife ndi atumiki a Mbuye wa zolengedwa zonse.”
“(Tatumidwa) kuti uwapereke kwa ife ana a Israyeli (kuti tinke nawo ku Sham).”
(Farawo) adati (kwa Mûsa): “Kodi sitidakulere kwathu uli mwana, ndi kukhala nafe pa moyo wako zaka zambiri?”
“Ndipo udachita chochita chako chimene udachichita, ndipo iwe ndiwe mmodzi wa osathokoza!”
(Mûsa) adati: “Ndidachita zimenezo pomwe ine ndidali mmodzi wa osazindikira zinthu.”
“Choncho ndidakuthawani pomwe ndidakuopani; tsono Mbuye wanga wandipatsa nzeru zoweruzira (zinthu), ndi kundisankha kukhala mmodzi wa atumiki.”
(Mûsa) adati: “Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli ndi chitsimikizo. (Amachita chilichonse m’menemo mmene wafunira; kupereka moyo ndi imfa).”
(Farawo) adauza omwe adali m’mphepete mwake (mwachipongwe): “Kodi simukumva (mawu achibwanawa)?”
(Mûsa adapitiriza kunena) adati: “Allah ndi Mbuye wanu komanso Mbuye wamakolo anu oyamba.”
(Farawo) adati (kwa anthu ake pofuna kuwakwiitsa): “Ndithu Mtumiki wanu amene watumidwa kwa inu, ngwamisala.”
(Mûsa) adati: “Mbuye wakuvuma ndi kuzambwe, ndi zomwe ziri pakati pake ngati mumazindikira (zinthu, muzindikira izi).”
(Farawo) adati: “Ngati udzipangira mulungu wina kusiya ine, ndikuchita kukhala mmodzi wa omangidwa kundende.”
(Mûsa) adati: “Kodi ngakhale nditakubweretsera chinthu choonekera poyera (chosonyeza kuti zimene ndikunenazi ndizoona ndatumidwa ndi Allah)?”
Ndipo (Mûsa) adaponya (pansi) ndodo yake, mwadzidzidzi idasanduka njoka yopenyeka.
Ndipo adatulutsa dzanja lake; pompo lidali loyera (kwambiri) kwa (onse) openya.
(Farawo) adauza akuluakulu omwe adali m’mphepete mwake: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa kwambiri.”
(Anthu) adati (kwa Farawo): “Mpatse nthawi ndi m’bale wakeyo, ndipo tumiza (amithenga) m’mizinda yonse osonkhanitsa anthu.”
“Ndipo akubweretsera amatsenga onse odziwa kwabasi (kotero kuti adzampambana Mûsa).”
Ndipo anthu adauzidwa: “Kodi inu musonkhana? (Choncho, sonkhanani).”
(Farawo) adati: “Inde, (ndipo kuonjezera apo) ndithu inu mudzakhala mwa amene amakhala pafupi (ndi ine, monga nduna zanga).”
Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zimene mufuna kuponya (zosonyeza kuya kwa matsenga anu).”
(Farawo) adati: “Ha! Mwamkhulupirira chotani ndisanakulolezeni? Ndithu iyeyu ndimkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Choncho posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni) ndithu ndidula manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa (podula mkono wakumanja ndi mwendo wakumanzere; kapena kudula mkono wakumanzere ndi mwendo wakumanja), ndipo kenako ndikupachikani nonsenu.”
(Amatsenga) adati: “Palibe vuto, ndithu ife (tonse) tibwerera kwa Mbuye wathu.”
Ndipo tidamvumbulutsira Mûsa (kuti): “Pita ndi anthu anga m’nthawi yausiku (musamuke m’dziko la Iguputo); ndithu inu mutsatidwa.”
Choncho Farawo adatuma (owatuma) kuti asonkhanitse anthu m’mizinda (kuti aletse ana a Israyeli kutuluka).
(Adawauza otumidwa aja kuti auze anthu kuti): “Ndithu awa (ana a Israyeli) ndikagulu kochepa.
Koma ndithu ife tonse (ndife ochuluka komabe ngakhale zili choncho) tikuwaopa.”
Ndi m’nkhokwe za chuma ndi m’malo okongola.
Momwemo ndi mmene tidawachitira ndipo tidawalowetsera chokolo zinthu zawo zonse kwa ana a Israyeli.
Choncho (anthu a Farawo ndi iye mwini) adawatsatira (ana a Israyeli) dzuwa litatuluka.
Ndipo pamene magulu awiri adaonana (anthu a Farawo ndi anthu a Mûsa), anthu a Mûsa adati: “Ndithu ife tigwidwa.”
(Mûsa) adati: “Iyayi! Ndithu Mbuye wanga ali nane pamodzi. Andiongolera (kuti ife tonse tipulumuke).”
Ndipo tidawayandikitsa pamenepo anthu enawo, (Farawo ndi anthu ake nalowa pa njira yomweyo pambuyo pa Mûsa ndi anthu ake).
Ndipo tidapulumutsa Mûsa ndi onse amene adali nawo (mpaka adaoloka nyanjayo, madzi ali chiimire mbali iyi ndi iyi).
Kenako tidawamiza enawo, (Farawo ndi anthu ake).
Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa (amalanga ndi chilango choopsa omwe amunyoza); Wachisoni (kwa omkhulupirira ndi kumumvera).
Ndipo awerengere (osakhulupirira) nkhani ya (M’neneri) Ibrahim.
Pamene adafunsa bambo wake ndi anthu ake (kuti); “Kodi mukupembedza chiyani?”
“Kapena amakuthandizani (mukawapembedza) kapena amapereka masautso kwa inu (mukasiya kuwapembedza)?”
(Ibrahim) adati: “Kodi mukuwaona awa amene mwakhala mukuwapembedza,”
“Yemwe adandilenga, ndiponso Yemwe akundiongolera (kunjira yolungama);”
“Ndi Amene adzandipatsa imfa, ndipo (tsiku la Qiyâma) adzandidzutsa;”
“E Mbuye wanga! Ndipatseni nzeru zoweruzira (zinthu), ndikundilumikiza ndi anthu abwino;”
“Ndipo khululukirani bambo wanga; ndithu iye adali mmodzi wa osokera;”
“Ndipo musadzandiyalutse pa tsiku loukitsidwa anthu (ku imfa);”
“Tsiku lomwe chuma ndi ana sizidzathandiza (aliyense).”
“Kupatula yemwe adzadza kwa Allah ndi mtima woyera (iye ndiamene adzathandizidwa patsikulo).”
Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa kwa oopa (Allah),
Ndipo kudzanenedwa kwa iwo: “Ali kuti amene mudali kuwapembedza aja,
M’malo mwa Allah? Kodi angathe kukuthandizani kapena kudzithandiza okha?”
Ndipo iwo ndi opotoka ena adzaponyedwa ndi nkhope zawo m’menemo (mu Jahannam).
Ndi magulu onse ankhondo a Iblis (omwe adali kukometsa kwa anthu zoipa ndi machimo).
Adzanena (movomereza kulakwa kwawo) uku naonso ali m’menemo, akukangana (ndi anzawo omwe adawasokeretsa):
Ngakhalenso bwenzi wapamtima (woti angatipulumutse kumasautsowa).
Tikadapeza mwayi wobwerera (ku moyo wa padziko), tikadakhala mwa okhulupirira.”
Ndipo ndithu Mbuye wako, ndiye Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
Pamene adawauza Nuh m’bale wawo kuti: “Kodi simukuopa (Allah ngakhale nditakuuzani zoopsa zimene zikukudikirani)?”
“Ndithu ine kwa inu ndine Mtumiki wokhulupirika;”
(Iwo) adati: “Nchotani kuti tikukhulupirire iwe chikhalirecho anthu wamba ndi amene akukutsatira?”
(Nuh) adati: “Sindikudziwa zimene adali kuchita (zomwe zachititsa kuti Allah awaongolere kunjira yoongoka).”
“Chiwerengero chawo sichili kwina koma kwa Mbuye wanga, mukadakhala mukuzindikira.”
“Ndipo sindine wopirikitsa okhulupirira (ku chipembedzo cha Allah kuti inu olemekezeka muchikhulupirire).”
(Iwo) adati: “Ngati susiya, iwe Nuh, (zonena zakozi) ndithu ukhala mmodzi mwa ogendedwa (miyala mpaka ufe).”
(Nuh) adati (kwa Allah): “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga anditsutsa.”
Choncho weruzani pakati panga ndi pakati pa iwo (chiweruzo chabwino), ndipo ndipulumutseni pamodzi ndi amene alinane mwa okhulupirira.”
Choncho, tidampulumutsa pamodzi ndi omwe adali naye m’chombo chodzadza (ndi chilichonse chamoyo chomwe chidalipo m’dziko, chachimuna ndi chachikazi chidaikidwa m’menemo).
Ndipo ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha.
Pamene m’bale wawo (Mneneri) Hûd adawafunsa kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”
“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu;”
“Kodi mukudzimangira nyumba pamalo paliponse pachitunda pokongola, moseweretsa?”
“Ndipo mukudzimangira (nyumba zonga) linga ngati kuti mukuona kuti mudzakhala muyaya?”
“Ndithu kutero (anthu ena kudzitcha atumiki a Allah), sikanthu koma ndi machitidwe a anthu akale.”
“Ndipo ife sitidzalangidwa (monga momwe ukunenera).”
Ndipo ndithu Mbuye wako ndiye Wamphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
“Ndithu ine ndimtumiki wokhulupirika kwa inu.”
“Kodi (mukuganizira kuti) mudzasiidwa mwamtendere pa izi zili pano (popanda imfa kukudzerani?)”
“Ndi (m’minda) yammera ndi mitengo yakanjedza yamikoko yakupsa yofewa?”
Iye adati: “(Ndakubweretserani) ngamira iyi yaikazi; (koma) ili ndi gawo lake lakumwa, ndipo inu muli ndi gawo lanu lakutunga (madzi) patsiku lodziwika. (Tsiku lina lotunga rnadzi anthu).”
“Ndipo musaikhudze ndi choipa chilichonse kuopera kuti chingakupezeni chilango cha tsiku lalikulu.”
Koma iwo adaipha; ndipo adali odzinena (pamene chidadza chilango cha Allah).
Ndipo, ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; wachisoni chosatha.
Pamene m’bale wawo Luti adanena kwa iwo (kuti): “Kodi simuopa (Allah)?”
“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”
Iye adati: “Ndithu ine ndine m’modzi wakuzida izi zochita zanu (choncho Sindisiya kuzidzudzula).”
“E Mbuye wanga! Ndipulumutseni ine ndi banja langa ku (matsoka a) zimene akuchita.”
Kupatula nkhalamba yaikazi idali mwa otsalira m’mbuyo.
Ndipo, ndithu Mbuye wako, Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha.
(Akumbutse) pamene (Mneneri) Shuaib adati kwa iwo: “Kodi simuopa (Allah)?”
“Ndithu ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”
“Kwaniritsani mulingo (pamalonda pamene mukupima), ndipo musakhale mwaopungula (mulingo).”
“Ndipo muopeni amene adalenga inu ndiponso zolengedwa zoyamba (zimene zidanka kale).”
“Ndipo iwe suli kanthu koma munthu ngati ife, ndipo ndithu tikukutsimikizira kuti ndiwe mmodzi wa abodza.”
(Shuaib) adati: “Mbuye wanga Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita. (Akadzaona kuti inu ngoyenera kulangidwa ndizidutswa za thambo, adzakulangani).”
Ndipo, ndithu Mbuye wako Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha.
Ndipo, ndithu iyi (Qur’an) ndiyo chivumbulutso cha Mbuye wazolengedwa zonse.
Ndipo ndithu izi (zomwe zili m’Qur’an) zilipo m’mabuku akale.
Kodi sipadapezeke chisonyezo kwa iwo kuti akuidziwa (Qur’an) odziwa mwa ana a Israyeli (kotero kuti ena alowa m’Chisilamu)?
Tero adzayamba kunena: “Kodi ife tipatsidwa nthawi (yoti tilape)?”
Kodi ukuona bwanji, ngati titawasangalatsa zaka (zankhaninkhani).
(Kuti akhale) chikumbutso. Ndipo sitidali osalungama (powaononga popanda kuwachenjeza).
Ndipo asatana sadaivumbulutse (iyi Qur’an monga osakhulupirira akunenera monyoza).
Ndipo sikoyenera kwa iwo (kuivumbulutsa Qur’an) ndiponso sangathe.
Ndithu iwo ngotsekerezedwa kumvetsera (zimene angelo amalankhula kumwamba).
Ndipo fungatira ndi phiko lako amene akutsata mwa okhulupirira. (Ukhale wachifundo kwa iwo).
Ndipo tsamira kwa (Mbuye wako) Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.
Yemwe akukuona pamene ukuimilira (pamapemphero).
Ndikutembenukatembenuka kwako (pogwetsa mphumi yako pansi ndi kudzuka ndi kuimilira) pamodzi ndi ogwetsa mphumi pansi (polambira Allah).
Amawaponyera (asatana anzawo a mu anthu) zimene azimva. Koma ambiri a iwo ngabodza.
Ndipo alakatuli (olakatula zopanda phindu) amatsatidwa ndi (anthu) opotoka.
Kodi suona kuti iwo akungoyumbayumba m’chigwa chilichonse (chamawu)?
Share