E inu anthu! Opani Mbuye wanu yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi (Adam) ndipo adalenga mmenemo mkazi wake (Hawa), ndipo adafalitsa amuna ndi akazi ambiri kuchokera mwa awiriwo. Ndipo opani Allah yemwe kupyolera mwa Iye mumapemphana. Ndipo (sungani) chibale. Ndithudi Allah Ndimyang’aniri pa inu (akuona chilichonse chimene muchita).[105]
Ndipo apatseni ana amasiye chuma chawo; musasinthanitse choipa ndi chabwino. Ndipo musadye chuma chawo pochiphatikiza ndi chuma chanu. Ndithudi, (zonsezo) ndiuchimo waukulu.
Ngati mwaopa kuti simungachite chilungamo pa amasiye (opaninso kusawachitira chilungamo akazi pamitala), choncho kwatirani amene mukuwafuna mwa akazi; awiri, kapena atatu, kapena anayi (basi). Koma ngati mukuopa kuti simungathe kuchita chilungamo, (kwatirani) mmodzi basi kapena amene manja anu akumanja adapeza (mdzakazi). Kutero kudzakuchititsani kuti musapendekere (kumbali yosalungama).[106]
Ndipo akazi apatseni chiwongo chawo monga mphatso. Koma (akazi anuwo) ngati atakupatsani mokoma mtima chilichonse (m’chiwongocho), idyani mokondwa ndi mothandizika nacho.[107]
Ozerezeka musawapatse chuma chanu chomwe Allah wachichita kukhala cholimbitsa matupi anu ndi moyo wanu. Koma adyetseni nacho ndikuwaveka nacho ndikuwauza mawu abwino (monga kuti: Mukadzakula ndikukhala olungama, tidzakupatsani chuma chanu).[108]
Ayeseni amasiye (akayandikira kukula nsinkhu kuti muone kuti atha kuchita ntchito yabwino ndi chuma chawo mukawapatsa), kufikira atafika nthawi yokwatira/kukwatiwa. Ndipo ngati mutawaona kuti ali ndi nzeru zabwino, apatseni chuma chawo. Musachidye mosasamala ndi mwachangu poopa kuti angakule. Ndipo amene ali opeza bwino adziletse (kulandira mphoto yolelera ana amasiyewo). Koma amene ali wosauka adye mwa ubwino (osati moononga). Ndipo pamene mukuwapatsa chuma chawo, funani mboni (zoonelera kuperekedwa kwa chumacho). Ndipo Allah ali Wokwana kukhala Muwelengeri (ndi Woyang’anira).[109]
Amuna m’chuma chimene makolo ndi achibale asiya ali ndi gawo. Naonso akazi ali ndigawo m’chuma chimene asiya makolo ndi achibale (chapafupi), ngakhale chitakhala chochepa kapena chochuluka ndigawo logawidwa (ndi Allah)[110]
Ndipo panthawi yogawa, ngati angabwere achibale, amasiye ndi osauka (omwe alibe gawo pa chumacho), apatseniko kanthu ndi kunena nawo mawu abwino.[111]
Ndipo (wowasiirawo) aope (kusachita chilungamo), kuti naonso ngati atasiya ana awo ofooka pambuyo, akadawaopera (kuchenjeleredwa). Choncho aope Allah ndipo anene mawu olingana (kwa ana amasiyewo).
Ndithu amene akudya churna cha ana amasiye mopondereza, akudya ndi kuthira moto m’mimba zawo. Ndipo adzalowa ku Moto woyaka!
Allah akukulamulani za ana anu achimuna apate gawo lolingana ndi gawo la akazi awiri. Ngati akaziwo ali (opitilira) awiri, ndiye kuti adzalandira zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu (2/3) za (chumacho) chimene wasiya (womwalira), ngati mwana wamkazi ndi mmodzi, apatsidwe gawo limodzi mwa magawo awiri (1/2), naonso makolo ake awiri aliyense wa iwo alandile gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) achuma chosiidwacho, ngati (womwalirayo) wasiya mwana (kapena mdzukulu). Koma ngati sadasiye mwana, ndipo makolo ake awiri ndiwo awasiira, ndiye kuti mayi wake alandire gawo limodzi mwamagawo atatu (1/3) achumacho, (ndipo bambo alandire 2/3). Ngati wakufayo wasiya abale, ndiye kuti mayi wake apeza gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) achumacho. (Kugawa chumaku kuchitike) atachotsapo chimene iye adalamulira kuti adzachipereke kwakutikwakuti, kapena kulipira ngongole (zake). Atate anu ndi ana anu, simudziwa inu kuti ndani mwa iwo amene ali ndi chithandizo chapafupi kwa inu. Amenewa ndi malamulo omwe akhazikitsidwa ndi Allah. Ndithudi, Allah ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya.[112]
Inunso mupata gawo limodzi mwa magawo awiri (1/2) achuma chimene akazi anu asiya ngati alibe mwana (kapena mdzukulu), ngati asiya mwana ndiye kuti inu mupata gawo limodzi m’magawo anayi (1/4) achuma chosiidwacho mutachotsapo zomwe adalamula kuti zipite kwakutikwakuti kapena ngongole zake, naonso akazi anu apata gawo limodzi m’magawo anayi (1/4) pa chuma chomwe mwasiya, ngati mulibe mwana (ndi mdzukulu). Koma ngati mwasiya mwana (ndi mdzukulu), (akaziwo) apata gawo limodzi m’magawo asanu ndi atatu (1/8) pa chuma chomwe mwasiya mutachotsapo chomwe mudanena kuti chipite kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole (zanu). Ngati mwamuna kapena mkazi alowedwa m’malo pachuma pomwe alibe mwana (ndi mdzukulu) ngakhale makolo awiri, koma ali naye m’bale wake (wakuchikazi) kapena mlongo wake (wakuchikazinso) aliyense wa iwo apata gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi (1/6). Ndipo ngati ali ochulukirapo, ndiye kuti agawirana gawo limodzi m’magawo atatu (1/3) a chumacho pambuyo pochotsapo chomwe chidanenedwa kuti chipita kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole, popanda kupereka mavuto. Awa ndi malamulo ofunika omwe achokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri (pokhazikitsa malamulo); Woleza (pa akapolo Ake).[113]
Amenewo ndiwo malire a Allah; (musawalumphe). Ndipo amene angamvere Allah ndi Mtumiki Wake adzamulowetsa m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
Koma amene anganyoze Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kulumpha malire ake, (Allah) adzamulowetsa ku Moto; nadzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ndipo adzapeza chilango chosambula.
Ndipo omwe achite cha uve (chigololo) mwa akazi anu, afunireni mboni zinayi za mwa inu zoikira umboni pa iwo. Ngati ataikira umboni (kuti achitadi cha uvecho), atsekereni m’nyumba kufikira imfa idzawapeze, kapena Allah adzawaikire njira ina (monga kuphedwa).[114]
Ndipo amuna awiri mwa inu amene akuchita zauve (monga kuchitana ukwati amuna okhaokha ‘matanyula’), akhaulitseni (powalanga). Tsono ngati atalapa ndikukonza bwino (mkhalidwe wawowo) asiyeni. Ndithudi, Allah Ngolandira kulapa, ndiponso Ngwachisoni chambiri.
Ndithudi kulapa kovomerezeka ndi Allah nkwa omwe amachita zoipa mwa umbuli kenako nkulapa mwachangu. Amenewo ndiomwe Allah amawalandira kulapa kwawo. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri Ngwanzeru zakuya.[115]
Kulapa sikungalandiridwe pa omwe akuchita zoipa mpaka imfa kumfikira m’modzi wa iwo (pamenepo) nkunena: “Ndithudi ine ndikulapa tsopano.” Ngakhalenso pa omwe akufa ali osakhulupirira. Iwo tawakonzera chilango chopweteka.
E inu amene mwakhulupirira! Sikovomerezedwa kwa inu kuwalowa chokolo akazi mowakakamiza. Ndipo musawaletse (kukwatiwa ndi amuna ena) ndi cholinga choti muwalande zina mwa zomwe mudawapatsa, (nkosaloledwa kutero) kupatula ngati atachita choipa choonekera. Ndipo khalani nawo mwa ubwino. Ngati mutawada (musalekane nawo), mwina mungade chinthu chomwe Allah waika zabwino zambiri mkati mwake.[116]
Ndipo ngati mufuna kusintha mkazi wina m’malo mwa wina (pokwatira wina kusiya wakale) pomwe mmodzi wa iwo (woyambayo) mudampatsa milumilu ya chuma, musatenge (kulanda) chilichonse. Kodi mungachitenge mwa chinyengo ndi uchimo woonekera?
Kodi mungachitenge bwanji pomwe mudalowana wina ndi mnzake, ndipo (akazi) adalandira kwa inu chipangano cholimba?
Ndipo musakwatire akazi amene adakwatiwapo ndi atate anu, kupatula zomwe zidapita, (musabwerezenso kuzichita). Ndithudi, chinthu ichi nchauve ndipo nchodedwa ndiponso ndinjira yoipa.[117]
Kwaletsedwa kwa inu kukwatira amayi anu, ana anu, alongo anu, azakhali anu, amayi anu aang’ono kapena aakulu, ana achikazi am’bale wanu, ana achikazi a mlongo wanu, amayi anu amene adakuyamwitsani, alongo anu oberekedwa ndi amene adakuyamwitsanipo. Mayi a akazi anu, ana achikazi owapeza amene mukuwasunga woberekedwa ndi akazi anu omwe mwalowana nawo. Koma ngati simudalowane nawo, nkosaletsedwa kwa inu kukwatira ana awowo; ndi akazi a ana amuna omwe ngochokera kumisana yanu. Ndiponso nkoletsedwa kwa inu kukwatira mophatikiza mkazi ndi mchemwali wake obadwa naye, kupatula zomwe zidapita. Ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni zedi.
۞ Ndiponso (nkoletsedwa kwa inu kukwatira) akazi okwatiwa kupatula chimene manja anu akumanja apeza (mdzakazi). Ili ndi lamulo la Allah lomwe lili pa inu. Ndipo kwalolezedwa kwa inu (kukwatira akazi) omwe sali m’gulu ili. Afunefuneni ndi chuma chanu m’njira ya ukwati, osati chiwerewere. Choncho, amene mwawakwatira mwa iwo nkusangalala nawo, apatseni chiwongo chawo chomwe chakakamizidwa. Palibe kuipa kwa inu (kupereka) chomwe mwagwirizana m’malo mwa chomwe chidatchulidwa. Ndithudi, Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya (pokhazikitsa malamulo Ake).
Ndipo amene sangathe mwa inu kupeza chuma chokwatilira mkazi amene ali mfulu wokhulupirira, (akwatireni adzakazi) achisungwana okhulupirira, mwa omwe manja anu akumanja apeza, Allah akudziwa kwambiri chikhulupiliro chanu. Ndinu amodzi kuchokera kwa wina ndi mnzake (nonsenu ndinu ana a Adam). Akwatireni ndi chilolezo cha mabwana awo, ndipo apatseni chiwongo chawo mwachilamulo. (Akwatireni) omwe ali akazi odzisunga, osati achiwerewere kapena ochita zibwenzi. Ndipo akakwatiwa, kenako nkuchita chauve, chilango chawo nditheka lachilango cha mfulu. Kumeneko (kukwatira akapoloko) ndilamulo kwa yemwe mwa inu akuopa kuti angachite chiwerewere. Koma ngati mutapirira (posiya kukwatira akapolo) ndibwino kwa inu kutero. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
Allah akufuna kukufotokozerani ndi kukutsogolerani kunjira za omwe adalipo patsogolo panu; ndiponso akufuna kulandira kulapa kwanu. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya.
Ndiponso Allah akufuna kulandira kulapa kwanu. Koma amene akutsata zilakolako zawo akufuna mupotoke; kupotoka kwakukulu.
Allah akufuna kukupeputsirani, pakuti munthu adalengedwa wofooka (alibe mphamvu za thupi ngakhale zolimbana ndi zilakolako za moyo).
E inu amene mwakhulupirira! Musadye chuma chanu mwachinyengo koma m’njira yamalonda ndi moyanjana pakati panu. Ndipo musadziphe nokha (ngakhale kupha anzanu). Ndithudi, Allah ali Wachisoni pa inu.[118]
Ndipo amene achite izi molumpha malire ndi mopanda chilungamo, iyeyo tidzamulowetsa kumoto. Ndipo zimenezo nzopepuka kwa Allah.
Ngati mudzitalikitsa kumachimo akuluakulu omwe mukuletsedwa, ndiye kuti tikufafanizirani zolakwa zanu (zing’onozing’ono) ndipo tidzakulowetsani malo aulemu.[119]
Ndipo musazilakelake (mwadumbo) zomwe Allah wawadalitsa nazo ena mwa inu. Amuna ali ndi gawo (lokwanira) la zomwe apeza. Nawonso akazi ali ndi gawo (lokwanira) la zomwe apeza. Ndipo mpempheni Allah zabwino zake. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse.[120]
Ndipo anthu tawaikira alowa mmalo pa zomwe asiya makolo awiri ndi achibale. Ndipo amene mudagwirizana nawo chipangano, apatseni gawo lawo. Ndithudi, Allah Ndimboni pa chilichonse.[121]
Amuna ndiayang’aniri pa akazi chifukwa choti Allah watukula ena pa ulemelero pamwamba pa ena, chifukwa cha chuma chawo chimene apereka. Choncho, akazi abwino ndi omwe ali omvera, odzisunga ngakhale amuna awo palibe pakuti Allah wawalamula kudzisunga. Ndipo akazi omwe mukuopa mnyozo wawo, achenjezeni; ndipo kenako achokereni pamphasa, (apo ayi), akwapuleni (kukwapula kosavulaza), koma ngati akukumverani, musawafunire njira yowavutitsira. Ndithu Allah ndi yemwe ali Wapamwamba, Wamkulu (kuposa inu nonse).[122]
Ndipo (inu aweruzi) ngati muopa mkangano pakati pawo (pa mwamuna ndi mkazi wake), tumizani nkhoswe ya kuchimuna ndi nkhoswe ya kuchikazi. Ngati iwo atafuna kuyanjanitsa, Allah awapatsa mphamvu zoyanjanitsira pakati pawo (okanganawo). Allah Ngodziwa nkhani zobisika, ndiponso Ngodziwa nkhani zoonekera.
Ndipo mpembedzeni Allah, ndipo musamphatikize ndi chilichonse; ndipo achitireni zabwino makolo awiri, ndi achibale, ndi ana amasiye ndi masikini ndi mnansi woyandikana naye nyumba, ndi wapadera wogundizana naye nyumba, ndi mnzako wokhala naye limodzi, ndi wapaulendo yemwe alibe choyendera, ndi omwe manja anu akumanja apeza (adzakazi). Ndithudi, Allah sakonda wodzitukumula ndi wodzitama.[123]
Omwe amachita umbombo ndi kulamula anthu kuchita umbombo ndi kubisa zabwino zomwe Allah wawapatsa. Komatu osakhulupirira tawakonzera chilango choyalutsa.[124]
Ndi omwe akupereka chuma chawo modzionetsera kwa anthu ndipo sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndiponso yemwe satana angakhale bwenzi lake, ndithudi ali ndi bwenzi loipa.
Kodi pakadakhala vuto lanji kwa iwo ngati akadakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro napereka zina mwa zomwe Allah wawapatsa? Ndipo Allah ali Wodziwa bwino za iwo.
Ndithudi, Allah sachitira (anthu) zosalungama ngakhale kanthu kolemera ngati kanyelere; ngati kanthuko kali kabwino amakachulukitsa ndi kupereka malipiro aakulu kuchokera kwa Iye.
Nanga zidzakhala bwanji tikadzabweretsa mboni pa m’badwo uliwonse ndikukubweretsa iwe (Mneneri Muhammad{s.a.w}) kuti ukhale mboni pa m’badwo uwu.
Tsiku limenelo aja omwe sadakhulupirire namunyoza Mtumiki, adzakhumba kuti nthaka ikadafafanizidwa pa iwo (akwiliridwe, asaukitsidwe). Ndipo sadzatha kum’bisira Allah nkhani iliyonse (m’zomwe adachita m’moyo wa pa dziko).
E inu amene mwakhulupirira! Musayandikire Swala uku muli oledzera, mpaka mudziwe chimene mukunena; ngakhalenso pamene muli ndi janaba (musapemphere kufikira mutasamba) kupatula amene ali pa ulendo (achite Tayammam). Ndipo ngati muli odwala, kapena muli pa ulendo, kapena m’modzi wanu wadza kuchokera kuchimbudzi, kapena mwakhudza akazi (m’njira ya ukwati) ndipo simunapeze madzi (osamba) chitani Tayammam ndi dothi labwino; lipakeni kunkhope kwanu ndi m’mikono mwanu. Ndithudi, Allah Ngofafaniza machimo, Ngokhululuka kwambiri.
Kodi sukuwaona omwe adapatsidwa gawo la (nzeru zozindikira) buku (la Allah, omwe ndi Ayuda ndi Akhrisitu), akudzisankhira kusokera ndiponso akufuna mutasokera kusiya njira (yabwino).[125]
Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za adani anu. Ndipo Allah akukwanira kukhala Mtetezi. Allah akukwananso kukhala Mthandizi.
Mwa Ayuda alipo omwe amasintha mawu kuwachotsa m’malo mwake. Ndipo amanena (chabe ndi milomo yawo): “Tamva;” (pomwe mitima yawo ikunena): “Tanyoza.” (Ndipo akunena kuuza Mtumiki): “Imva koma wosamveredwa (ndipo pakati pakuyankhula kwawo amanena mawu akuti) ‘Raaina’ (ncholinga chomnenera kuti iye ndimbutuma), mokhotetsa malilime awo (mu zoyankhula zawo kuti akhale ngati akumunenera zabwino pomwe akumtembelera) ndi cholinga chotukwana chipembedzo (cha Chisilamu). Akadakhala kuti iwo adanena: “Tamva ndipo tamvera; ndipo imva, utiyang’anire,” (mmalo mwa kunena kwawo kwakuti: ‘Raaina’), zikadakhala zabwino ndizolingana kwa iwo. Koma Allah adawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Sakhulupirira koma pang’ono basi.
E inu amene mwapatsidwa buku! Zikhulupirireni zomwe tavumbulutsa zikutsimikizira zomwe muli nazo tisanazisinthe nkhope zanu ndi kuzitembenuzira kumbuyo kwake, kapena tisanawatembelere monga momwe tidawatembelera omwe sadalemekeze kupatulika kwa tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la Allah ndilochitikadi.
Ndithudi Allah sangakukhululuke kuphatikizidwa (ndi chinachake), koma amakhululuka (machimo ena) osati amenewa kwa amene wamfuna. Ndipo amene angamphatikize Allah, ndithudi, wadzipekera uchimo waukulu.
Kodi sukuwaona omwe akudziyeretsa okha? Koma Allah amamuyeretsa amene wamufuna (pomulimbikitsa kuchita zabwino). Ndipo sadzaponderezedwa ngakhale ndi kachinthu kochepa konga kaulusi kokhala mkati mwakhokho la tende.[126]
Taona, momwe akumpekera Allah bodza! Ndipo izi zikukwana kukhala tchimo loonekera!
Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la nzeru zozindikira buku (la Allah)? Amakhulupirira mafano ndi asatana, ndipo akumati kwa amene sadakhulupirire: “Awa ali panjira yoongoka kwabasi kuposa okhulupirira (Asilamu).”[127]
Iwo ndi omwe Allah wawatembelera. Ndipo amene Allah wamtembelera, simungathe kumpezera wompulumutsa.
Kodi ali ndi gawo la ufumu (wa Allah? Nchifukwa ninji akunyasidwa munthu wina akaninkhidwa utumiki)? Zikadatero ndiye kuti sakadawapatsa anthu ngakhale kochepa kwambiri monga khokho la tende.[128]
Kodi akuchitira anthu dumbo pa zomwe Allah wawapatsa ndi ufulu wake? Choncho tidalipatsa banja la Ibrahim buku ndi nzeru. Ndipo tidawapatsa ufumu waukulu.
Choncho alipo ena mwa iwo amene anazikhulupirira izi, ndiponso alipo ena mwa iwo omwe adziika nazo kutali. Ndipo Jahannam ikukwanira kukhala Moto waukali wowatentha.
Ndithu amene sadakhulupirire zizindikiro Zathu, tidzawalowetsa ku Moto. Nthawi iliyonse yomwe makungu awo adzikapselera tidzidzawasinthira makungu ena kuti adzapitirize kulawa chilango. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.[129]
Ndipo amene akhulupirira ndi kuchita zabwino, Tidzawalowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi patsogolo) pake. Adzakhala mmenemo muyaya. Ndipo iwo adzapeza mmenemo akazi oyeretsedwa (ku uve wamtundu uliwonse) ndi kuwalowetsa ku mithunzi yabwino kwambiri.
Ndithudi, Allah akukulamulani kubweza kwa eni zomwe mwakhulupirika nazo. Ndipo pamene mukuweruza pakati pa anthu, weruzani mwachilungamo. Ndithu malangizo amene Allah akukulangizani, ngabwino kwambiri. Ndithudi, Allah Ngwakumva, Ngoona.[130]
E inu amene mwakhulupirira! Mumvereni Allah ndiponso mumvereni Mtumiki, ndi omwe ali ndi udindo pa inu. Ngati Mutatsutsana pa chinthu chilichonse, chibwezeni kwa Allah ndi Mtumiki Wake, ngatidi mukukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, kutero ndibwino; ndipo zotere zili ndi zotsatira zabwino.[131]
Kodi sukuwaona omwe akungonena chabe kuti akhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zomwe zidavumbulutsidwa patsogolo pako, pomwe iwo akufuna kuti akaweruzidwe ndi maweruzo osagwirizana ndi Shariya, pomwenso alamulidwa kukana njira zotere? Koma satana akufuna kuwasokeretsa, kusokera kwakutali.
Ndipo akauzidwa: “Idzani ku zomwe Allah wavumbulutsa, ndiponso (idzani) kwa Mtumiki.” Uwaona achinyengo akudziika kutali kwabasi ndi iwe.
Kodi zingakhale bwanji litawabwerera vuto chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza? Kenako nkukudzera (iwe Mtumiki) uku akulumbira: “Tikulumbira Allah; sitinafune china chilichonse koma zabwino zokha ndi chimvano.”
Iwo ndi omwe Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwawo. Choncho dzipatule kwa iwo, ndipo alangize ndi kuwauza mawu ogwira mtima.
Ndipo sitidamtumize mtumiki aliyense koma kuti azimveredwa mwa lamulo la Allah. Ngati akadakudzera pamene adadzichitira okha zoipa, (chifukwa chokafuna chiweruzo cha satana) napempha chikhululuko kwa Allah (naye) Mtumiki nkuwapempheranso chikhululuko, ndithudi, akadampeza Allah ali Wolandira kulapa kwawo ali Wachisoni chosatha.
Ndikulumbira (m’choonadi cha) Mbuye wako, iwo sangakhale okhulupirira moona pokhapokha akuyese muweruzi wawo pa zomwe akukangana pakati pawo. Kenako asaone vuto m’mitima yawo pa zomwe waweruza, ndipo adzipereke kwathunthu (pogonjera chiweruzo chako).[132]
Ndipo ngati tikadawalamula kuti: “Dzipheni nokha,” kapena: “Tulukani m’nyumba zanu; (mupite kunkhondo kapena musamuke),” sakadachita zimenezo kupatula ochepa mwa iwo. Koma akadachita zomwe auzidwa, zikadakhala zabwino kwa iwo. Ndipo zikadawalimbikitsa kwambiri (Chisilamu chawo).
Ndipo zikadatero, tikadawapatsa malipiro aakulu ochokera kwa Ife.
Ndiponso tikadawatsogolera ku njira yoongoka (yokawafikitsa ku Munda wamtendere).
Ndipo amene angamvere Allah ndi Mtumiki wake, iwowo ndi omwe adzakhale pamodzi ndi omwe Allah adawadalitsa, kuyambira aneneri, olungama, mashahidi (asilamu ofela ku nkhondo) ndi anthu abwino. Taonani ubwino wokhala nawo pamodzi iwowo!
Umenewo ndiubwino wochokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa mokwanira.
E inu amene mwakhulupirira! Khalani ochenjera (ndi adani anu; musanyengedwe nawo). Pitani (kunkhondo) gulu limodzilimodzi, kapena pitaniko nonsenu pamodzi (monga momwe Mtumiki angakulangizireni).
Ndipo ndithu alipo ena mwa inu otsalira m’mbuyo sapita ku nkhondo, (ndiponso amaletsa anzawo). Ngati vuto litakupezani, (yense wa iwo) amanena: “Allah wandichitira chisomo posakhala m’gulu lawo kumeneko.”
Koma ngati utakupezani ubwino wochokera kwa Allah (monga kupeza chuma chambiri chosiidwa ndi adani, kapena kupambana kumene) amanena ngati kuti padalibe chikondi pakati panu ndi pakati pake: “Kalanga ine! Ndikadakhala nawo pamodzi pa nkhondo imeneyi, (ndiye kuti) ndikadapambana; kupambana kwakukulu.”
Choncho, amenye nkhondo pa njira ya Allah omwe akugulitsa moyo (wawo) wadziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene angamenye nkhondo pa njira ya Allah, kenako ndikuphedwa kapena kupambana tidzampatsa malipiro aakulu.
Mwatani inu osamenyana pa njira ya Allah, ndi (kuwapulumutsa) omwe ali ofooka, aamuna ndi aakazi ndi ana, omwe akunena: “Mbuye wathu! Titulutseni m’mudzi uwu omwe anthu ake ndiopondereza; ndipo tipatseni mtetezi wochokera kwa Inu; ndiponso tipatseni mthandizi wochokera kwa Inu.”[133]
Amene akhulupirira, akumenya nkhondo pa njira ya Allah. Koma amene sadakhulupirire, akumenya nkhondo panjira ya satana. Choncho menyanani ndi abwenzi a satana. Ndithudi, ndale za satana nzofooka.
Kodi sukuwaona omwe adauzidwa kuti: “Aletseni manja anu (kumenyana ndi osakhulupirira mpaka lidze lamulo lakumenyana)? Koma tsono pempherani Swala ndikupereka chopereka basi. Koma pamene adalamulidwa kumenyana, pompo gulu lina la iwo lidaopa anthu (osakhulupirira) ngati likuopa Allah kapena kuposerapo. Ndipo adati: “Mbuye Wathu! chifukwa ninji mwatilamula kumenyana? Ha! Mukadatichedwetsa kufikira nyengo yochepa, (zikadakhala bwino).” Nena: “Chisangalalo cha m’dziko n’chochepa. Koma tsiku lachimaliziro ndilabwino kwambiri kwa amene akuopa (Allah). Ndipo simudzaponderezedwa ngakhale pa chinthu chaching’ono monga ulusi wakhokho la tende!”
Paliponse pamene mungakhale imfa ikupezani ngakhale mutakhala m’malinga olimba, ndipo ngati ubwino utawafika (opembedza mafano ndi achiphamaso) amati: “Ubwinowu, ukuchokera kwa Allah.” Koma choipa chikawafikira, amati: “Ichi chachitika chifukwa cha iwe (Muhammad).” Nena: “Zonse zachokera kwa Allah.” Kodi ngotani anthu awa, sangathe kuzindikira nkhani?
Chabwino chimene chakufikira (iwe munthu) ndiye kuti chachokera kwa Allah. Koma choipa chimene chakufikira ndiye kuti chachokera kwa iwe mwini (chifukwa cha zochita zako zoipa). Ndipo takutumiza (iwe Muhammad) kwa anthu kukhala Mtumiki. Ndipo Allah ndimboni yokwana.
Yemwe angamvere Mtumiki ndiye kuti wamvera Allah, (chifukwa chakuti zonse zomwe iye akulamula nzotumidwa ndi Allah). Ndipo amene atembenukire kutali (kunyoza iwe, ndiye kuti zoipa zili pa iye mwini). Sitidakutumize iweyo kukhala muyang’anili pa iwo.
Amati: “Tikumvera.” Koma akachoka kwa iwe, gulu lina la iwo limapangana usiku zosagwirizana ndi zomwe ukunena (pamaso pawo). Koma Allah akulemba zonse zomwe akupangana. Choncho apatukire ndipo yadzamira kwa Allah. Ndipo Allah wakwanira kukhala Mtetezi.
Kodi bwanji sakuilingalira Qur’an? Ndipo ikadakhala kuti siikuchokera kwa Allah, ndithudi, mmenemo akadapeza kusiyana kwambiri.[134]
Ndipo chikawadzera chinthu chilichonse chokhuza chitetezo kapena mantha, amachifalitsa. Koma akadachibwezera kwa Mtumiki ndi kwa omwe ali ndi udindo pa iwo, akadachidziwa omwe amafufuzafufuza zinthu mwa iwo (kuti kodi nzoyenera kuzifalitsa kapena ayi). Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, ndithudi, mukadamtsatira satana kupatula ochepa.
Choncho menya nkhondo pa njira ya Allah, suukukakamizidwa (za anthu ena) koma iwe mwini, ndipo akhwirizire Asilamu. Ndithu Allah angatsekereze mtopola wa omwe sadakhulupirire. Ndipo Allah Ngwaukali kwambiri pomenya nkhondo ndiponso Wolanga kwabasi.
Amene angampemphere (mnzake) pempho labwino (lothandizira pa zabwino) adzapeza gawo mmenemo. Ndipo amene angampemphelere pemphero loipa, adzapeza gawo m’zoipazo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.[135]
Ndipo pamene mwalonjeredwa; kulonjeredwa kwamtundu uliwonse (Salam) vomerani ndi malonje abwino oposa amenewo, kapena bwezani ofanana nawo. Ndithudi, Allah Ngowerengera chinthu chilichonse.
Allah! Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi. Ndithudi, adzakusonkhanitsani tsiku la chiweruziro lopanda chikaiko mwa ilo. Kodi ndani ali onena zoona kuposa Allah?
Kodi mwatani inu pokhala magulu awiri pa nkhani ya achiphamaso (achinyengo) pomwe Allah wawatembenuza chifukwa cha (zoipa) zomwe achita? Kodi mukufuna kuti mumuongole amene Allah wamlekelera kusokera? Ndipo amene Allah wamulekelera kusokera, simungathe kumpezera njira (yomuikira ku chilungamo).
Ndipo akufuna kuti mukadakhala osakhulupirira monga momwe iwo sadakhulupirire tero kuti mukhale ofanana. Musawachite kukhala abwenzi mpaka asamukire panjira ya Allah. Koma ngati anyoza, agwireni ndi kuwapha paliponse mwawapeza (monga momwe akukuchitirani inu). Ndipo musamuyese mtetezi ngakhale mthandizi aliyense wa iwo.
Kupatula omwe akugwirizana ndi anthu amene pali pangano pakati panu ndi iwo, kapena omwe akudza kwa inu uku zifuwa zawo zili zobanika kumenyana nanu, kapena kumenyana ndi anthu awo. (Oterewo musamenyane nawo). Ngati Allah akadafuna, akadawapatsa mphamvu yokugonjetserani, choncho akadakumenyani. Ngati atakupewani, osamenyana nanu ndipo nkukupatsani mtendere, ndiye kuti Allah sadakupangireni njira pa iwo (yakuti mumenyane nawo).
Muzawapeza ena omwe akufuna kupeza chitetezo kwa inu ndi kupeza chitetezo kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akabwezedwa ku ukafiri (ndi anzawo osakhulupirira), amagweramo mwamtheradi (nkuyamba kumenyananso ndi inu), ngati sadzipatula kwa inu ndipo osakupatsani mtendere ndi kutsekereza manja awo, agwireni ndi kuwapha paliponse pamene mwawapeza (monga momwe iwo akuchitira kwa inu) ndipo takupangirani chisonyezo choonekera pa iwo
Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira kupha wokhulupilila (mnzake mwadala) pokhapokha mwangozi. Ndipo yemwe wapha wokhulupilila mwangozi, apereke ufulu kwa kapolo wa Chisilamu ndi dipo lomwe alipereke kwa ofedwawo pokhapokha akakana okha (amulowa mmalo a womwalilayo), monga m’njira ya sadaka. Ngati wophedwayo ndi mnansi wa adani anu pomwe ali wokhulupilila, perekani ufulu kwa kapolo wa Chisilamu, (palibenso dipo lina). Ngati wophedwayo ndi mmodzi wa anthu omwe pakati panu ndi iwo pali chipangano (chosamenyana nkhondo), ndiye kuti amulowammalo ake apatsidwe dipo; apatsidwenso ufulu kapolo wa Chisilamu. Ndipo ngati sadapeze (zoterozo), asale miyezi iwiri yotsatana. Iyo ndiyo njira yolapira (pa uchimo wotere) yochokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa Ngwanzeru zakuya.
Ndipo amene angaphe wokhulupilila mwadala, mphoto yake ndi Jahannam; mmenemo adzakhala nthawi yaitali. Ndipo Allah amkwiira ndi kumtembelera ndi kumkonzera chilango chachikulu.
E inu amene mwakhulupirira! Mukayenda pa njira ya Allah, musachite chinthu pokhapokha mutaonetsetsa bwino. Ndipo musanene kwa amene akukulonjerani Salamu (kuti): “Sindiwe wokhulupirira,” (nkumupha). Mukufuna zinthu zamdziko lapansi komatu kwa Allah kuli zopeza zambiri. Umo ndi momwe inunso mudalili kale; koma Allah adakuchitirani chifundo (choncho mudalowa m’Chisilamu. Penyetsetsani bwinobwino). Ndithu Allah Ngodziwa bwinobwino nkhani zonse zimene muchita.
Sangafanane okhulupirira omwe akukhala osapita kunkhondo pomwe sali ovutika, ndi amene akumenya nkhondo yoyera pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo. Allah wawatukula pa ubwino ndi pa nyota amene akuchita Jihâd ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo kuposa okhala. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino. Koma wawapambanitsa ochita Jihâd malipiro aakulu kuposa ongokhala.
Adzapata nyota zazikulu zochokera kwa Iye ndi chikhululuko ndi chisoni. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.
Ndithudi amene angelo atenga miyoyo yawo, ali odzichitira okha zoipa (posasamuka ku Makka), adzawauza kuti: “Mudachitanji (pachipembedzo chanu?)” Iwo adzati: “Tidali ofooka ndi oponderezedwa padziko; (choncho sitidathe kuchita mapemphero athu).” (Angelo) adzati: “Kodi dziko la Allah silidali lotambasuka kotero kuti inu nkusamukira kwina m’menemo?” Iwowo malo awo ndi Jahannam. Taonani kuipa kwa malo obwerera.[136]
Kupatula omwe adali ofooka kwenikweni amuna, akazi ndi ana omwe sangathe kuchita ndale yamtundu uliwonse, ndipo sangathe kulondola njira (yonkera ku Madina).
Choncho iwo ndithudi Allah angawafafanizire machimo, pakuti Allah Ngofafaniza machimo, Wokhululuka.
Ndipo amene angasamuke pa njira ya Allah (chifukwa cha chipembedzo chake,) apeza malo ambiri m’dzikomo othawira ndikupeza bwino. Ndipo amene angatuluke m’nyumba mwake kuti asamuke chifukwa cha Allah ndi Mtumiki Wake, kenako nkumpeza imfa (m’njira), ndithu malipiro ake atsimikizika kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.[137]
Ndipo ngati mukuyenda pa dziko, sikulakwa kwa inu kufupikitsa Swala ngati mukuopa kuti angakusokonezeni omwe sadakhulupirire. Ndithudi, osakhulupirira ndi adani anu oonekera.[138]
Ndipo ngati uli pamodzi (ndi Asilamu pankhondo) ndikuwatsogolera Swala, ndiye kuti gulu limodzi la iwo liimilire pamodzi ndi iwe ndikupemphera uku atagwirizira zida zawo. Ndipo akamaliza kulambira kwawo, apite kumbuyo kwanu (kuti akulondereni) ndipo lidze gulu lina lomwe silidapemphere, lipemphere nawe pamodzi; nawonso achenjere ndikugwirizira zida zawo (nkupemphera), chifukwa chakuti omwe sadakhulupirire akufuna kuti mutanyalanyaza zida zanu ndi katundu wanu angokuukirani nthawi imodzi. Koma sikulakwa kwa inu mutaika pansi zida zanu chifukwa chakuvutitsidwa ndi mvula kapena ngati mukudwala. Koma chenjeranaoni. Ndithudi Allah wawakonzera chilango choyalutsa osakhulupirira.[139]
Mukamaliza Swala, pitirizani kumkumbukira Allah muli chiimire, chikhalire kapena mutagona chammbali. Ngati mutapeza chitetezo (chifukwa chakuti nkhondo palibe), pempherani Swala zanu mwa chilamulo. Ndithudi, Swala ndilamulo lokhala ndi nthawi kwa okhulupirira.[140]
Ndipo musachite ulesi kutsata anthu (omwe ndi adani), ngati mukumva kupweteka, iwonso akumva kupweteka monga momwe inu mukumvera kupweteka. Koma inu mukuyembekezera kwa Allah chomwe iwo sakuyembekezera. Ndipotu Allah Ngodziwa, Ngwanzeru.[141]
Ndithudi, takuvumbulutsira buku mwa choonadi kuti uweruzire pakati pa anthu, monga momwe Allah wakuphunzitsira. Ndipo usakhale mtetezi wa achinyengo.
Ndipo mpemphe chikhululuko Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo usawaikile kumbuyo omwe akudzichitira okha chinyengo. Allah sakonda yemwe ali wachinyengo, wamachimo.
Akudzibisa kwa anthu (pochita za machimo) koma sakuzibisa kwa Allah pomwe Iye adali nawo pamodzi pamene adali kupangana usiku mawu osakondweretsa. Allah akudziwa bwinobwino zimene akuchita.[142]
Taonani! Inu ndi amene mwaayikira kumbuyo pa moyo wa pa dziko lapansi. Kodi ndani amene adzatsutsana ndi Allah pa iwo tsiku lachimaliziro, kapena ndani adzakhale mtetezi wawo.[143]
Ndipo amene angachite choipa (povutitsa ena), kapena kudzichitira yekha zoipa, kenako nkupempha chikhululuko kwa Allah, adzampeza Allah ali Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha. [144]
Ndipo amene angachite tchimo, ndiye kuti akudzichitira yekha. Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.[145]
Ndipo amene angachite cholakwa (chaching’ono) kapena tchimo (lalikulu) kenako nkumponyera nalo yemwe sadalakwe (momunamizira), ndithudi wasenza bodza lamkunkhuniza ndi uchimo woonekera.[146]
Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chisoni chake pa iwe, ndithudi, gulu limodzi la iwo likadalinga kukusokeretsa. Ndipo iwo palibe yemwe akadamsokeretsa koma iwo okha basi. Ndipo sangathe kukuvutitsa ndi chilichonse. Ndipo Allah wakuvumbulutsira buku, kudzanso luntha. Ndipo wakuphunzitsa zomwe sudali kuzidziwa. Ndipo ubwino wa Allah umene uli pa iwe ngwaukulu zedi.[147]
Palibe ubwino m’zambiri zimene akunong’onezana kupatula amene akulamulira ena kupereka sadaka, kapena kuchita zabwino, kapenanso kuyanjanitsa pakati pa anthu (pakunong’onezana mawu). Amene angachite zimenezi, chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah, tidzampatsa malipiro aakulu.
Ndipo amene anyoza Mtumiki pambuyo pomuonekera chiongoko, nkutsata njira yosakhala ya okhulupirira, timtembenuzira kumene watembenukira mwini wakeko. Ndipo tidzamulowetsa ku Jahannam. Taonani kuipa malo ofikira.
Ndithudi, Allah sakhululuka (uchimo) womphatikiza ndi chinthu china, (pochiyesa kuti ndi mnzake wa Allah). Koma Iye amakhululukira machimo ena omwe sali amenewo kwa yemwe wamfuna. Ndipo yemwe angamphatikize Allah (ndi milungu yabodza), ndithudi, wasokera kusokera konka nako kutali (ndi njira yachoonadi).
Sapembedza Allah koma mafano achikazi, ndiponso sapembedza china koma satana wonyoza (wamachimo)
(Yemwe) Allah adamtembelera. Ndipo iye (satana) adati (kwa Allah): “Ndithudi, ndikadzipezera gawo lodziwika mwa akapolo anu.”[148]
“Ndipo ndikawasokeretsa ndi kuwapatsa ziyembekezo (zabodza) ndithu ndikawalamula kuti azikadula makutu a ziweto, ndipo ndikawalamulanso kuti azikasintha chilengedwe cha Allah.” Ndipo amene angamulole satana kukhala mtetezi wake kusiya Allah, ndiye kuti wataika koonekera.[149]
(Satana) akuwalonjeza ndikuwapatsa chiyembekezo (pa zinthu zomwe sizingachitike). Ndithudi, satana sawalonjeza china koma chinyengo basi.
Iwowo malo awo ndi ku Jahannam ndipo sadzapeza pothawira kutuluka mmenemo.
Ndipo omwe akhulupirira ndi kumachita zabwino, tidzawalowetsa ku Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. Adzakhala m’menemo muyaya. Ili ndilonjezo loona la Allah. Kodi ndani woona ponena kuposa Allah?
(Kulowa ku Munda wamtendere) sikuli pa kukhumba kwanu ngakhalenso pa kukhumba kwa anthu a buku (Ayuda ndi Akhrisitu). Amene angachite choipa, adzalipidwa (nacho), ndipo sadzapeza mtetezi ngakhale mpulumutsi kupatula Allah.
Ndipo amene angachite ntchito zabwino, mwamuna kapena mkazi, pomwe iye ali wokhulupirira, iwo ndiamene adzalowa ku Munda wamtendere. Ndipo sadzaponderezedwa pa chilichonse, ngakhale chochepetsetsa kwambiri ngati kamphako ka nthangala ya tende.
Kodi ndani yemwe ali ndi chipembedzo chabwino choposa yemwe walunjika nkhope yake kwa Allah, iye ali wochita zabwino ndipo akutsata njira ya Ibrahim woona pa chikhulupiliro. Ndipo Allah adasankha Ibrahim kukhala bwenzi.
Ndipo zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah; ndipo Allah ndi amene wazungulira chinthu chilichonse kuchidziwa.
Ndipo akukufunsa zomwe zikukhudza azimayi nena: “Allah akukuuzani nkhani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa kwa inu m’buku (ili) za akazi amasiye omwe simukuwapatsa (chiwongo chawo) chomwe chidalamulidwa kwa iwo, komabe mukufuna kuwakwatira, ndi za ana omwe ali ofooka ndi oponderezedwa; ndipo (akukuuzani) kuti limbikirani kuwayang’anira ana amasiye mwachilungamo. Ndipo chabwino chilichonse chimene muchita, Allah akuchidziwa.[150]
Ndipo ngati mkazi ataona kwa mwamuna wake nkhanza ndi kumusala, palibe kulakwa pa iwo kuyanjana pakati pawo mwachimvano. Ndipo chimvano ndichabwino. (Munthu aliyense amaumilira chimene afuna) chifukwa chakuti mitima ya anthu imaumilira umbombo. Koma ngati muchita zabwino ndi kuopa Allah, ndithudi, Allah Ngodziwa nkhani zanu zonse zomwe muchita.
Ndipo inu simungathe kuchita chilungamo (chenicheni) pakati pa akazi ngakhale mutayesetsa chotani. Koma musapendekere (mbali imodzi); kupendekera kwathunthu kotero kuti nkumusiya (yemwe simukumfunayo) ngati kuti wapachikidwa (osadziwika kuti ngokwatiwa kapena ayi). Ndipo ngati mutayanjana ndi kuopa Allah (zingakhale bwino). Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.
Koma ngati atalekana, Allah angalemeretse aliyense wa iwo kuchokera m’zabwino zake zochuluka ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngwanzeru zakuya.
Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndithudi, tidawalangiza omwe adapatsidwa buku patsogolo panu ndi inunso kuti muopeni Allah. Koma ngati mungakane, ndithudi, zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndipo Allah Ngokhupuka kwabasi Wotamandidwa.
Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Mtetezi (kwa anthu Ake).
Ngati atafuna, akuchotsani, inu anthu, ndi kubweretsa ena. Ndipo Allah ali Wokhoza pazimenezo.
Amene afuna mphoto ya dziko lapansi, (afunefune kwa Allah). Kwa Allah ndikumene kuli mphoto ya pa dziko lapansi ndi ya tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngopenya.
E inu amene mwakhulupirira! Khalani oimiritsa chilungamo, opereka umboni chifukwa cha Allah; ngakhale kuti ubwere ndi masautso kwa inu, kapena kwa makolo anu, kapena kwa abale anu, ngakhale ali olemera kapena osauka, (musayang’ane zimenezo). Allah ndiye woyenera kuyang’ana za awiriwo. Choncho musatsate zilakolako ndi kusiya chilungamo. Ngati mukhotetsa (umboni), kapena kupewa (kupereka umboni) ndithudi nkhani zonse zomwe mukuchita Allah akuzidziwa.
E inu amene mwakhulupirira! Khulupirirani Allah ndi Mtumiki Wake, ndi buku lomwe analivumbulutsa pa Mtumiki Wake, ndi mabuku omwe adawavumbulutsa kale. Ndipo amene akane Allah, angelo Ake, mabuku Ake, atumiki Ake ndi tsiku lachimaliziro, ndiye kuti wasokera; kusokera konkera nako kutali.
Ndithudi, amene adakhulupirira, kenako nkusakhulupirira, nadzakhulupiriranso, kenako nkusakhulupiriranso, naonjezera kusakhulupirira, Allah sadzawakhululukira, ndipo sadzawawongolera m’njira (yabwino).
Auze achiphamaso kuti adzapeza chilango chowawa.
Omwe amaachita osakhulupirira kukhala abwenzi awo kusiya Asilamu. Kodi akufuna kupeza ulemelero kwa iwo? Ndithudi ulemelero wonse ngwa Allah; (suli m’manja mwa anthu).
Ndithudi Iye wakuvumbulutsirani m’buku (ili) kuti mukamva ma Ayah (ndime) a Allah akukanidwa ndi kuchitiridwa chipongwe, musakhale pamodzi nawo mpaka alowe m’zokamba zina. (Ngati mutakhala nawo) ndiye kuti mukhala chimodzimodzi ndi iwo. Ndithudi, Allah adzawasonkhanitsa achiphamaso ndi osakhulupirira onse m’moto wa Jahannam.
(A chiphamaso) omwe akukuyembekezerani (kuti mavuto akugwereni), ngati mutapeza kupambana kochokera kwa Allah, amakuuzani: “Kodi sitidali nanu limodzi?” Koma ngati osakhulupirira atapeza gawo (lopambana), amanena (kwa osakhulupirira): “Kodi Sitidayandikire kukugonjetsani pamene tidali m’gulu lankhondo la okhulupirira koma timakutsekerezani kwa okhulupirira?” Koma Allah adzaweruza pakati panu tsiku la chiweruziro. Ndipo Allah sangawaikire njira osakhulupirira pa okhulupirira (kuti awagonjetse kotheratu).
Ndithu achiphamaso akufuna kunyenga Allah koma Iye awalanga (chifukwa cha chinyengo chawocho). Ndipo akaimilira kupemphera Swala, amaimilira mwaulesi ndikungoonetsa anthu (kuti akupemphera). Ndipo satchula Allah koma pang’ono pokha.
Akungoyendayenda pakati pa awa ndi awa (pakati pa Asilamu ndi osakhulupirira). Iwo sali mbali iyi kapena mbali inayo. Ndipo amene Allah wamlekelera kuti asokere sungampezere njira yolungama.
E inu amene mwakhulupirira! Musawachite osakhulupirira kukhala abwenzi anu kusiya okhulupirira (Asilamu), kodi mukufuna kuti Allah akhale ndi umboni woonekera pa inu (kuti ndinu oyipa?)
Ndithu achiphamaso adzakhala pansi penipeni pa Moto; ndipo sudzampeza mthandizi woimira iwo.
Kupatula amene alapa (pambuyo pa uchiphamaso wawo); nakonza (makhalidwe awo) nadziphatika kwa Allah; namuyeretseranso Allah chipembedzo chawo. Choncho iwo ali pamodzi ndi okhulupirira. Ndipo Allah adzapatsa okhulupirira malipiro akulu.
Allah sangakulangeni ngati mumthokoze ndi kumkhulupirira. Ndithudi, Allah Ngolandira kuthokoza kwanu, ndiponso Ngodziwa.
۞ Allah sakonda kutulutsa mawu ofalitsa kuipa (kwa anthu) kupatula yekhayo wachitiridwa zoipa. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[151]
Ngati mungaonetse chabwino, kapena kuchibisa, kapena kukhululukira zoipa, (zoterozo ndizo zofunika), ndithu Allah Ngokhululuka ndiponso Ngokhoza.
Ndithudi amene sakhulupirira Allah ndi atumiki Ake, ndikumafuna kulekanitsa pakati pa Allah ndi atumiki Ake, ndikumanena kuti: “Ena tikuwakhulupirira, koma ena tikuwakana,” ndikumafunanso kukhonza njira yapakati pa zimenezo,[152]
Iwowo ndiosakhulupirira enieni. Ndipo osakhulupirira tawakonzera chilango choyalutsa.
Tsopano amene akhulupirira Allah ndi atumiki Ake, napanda kulekanitsa pakati pa aliyense wa iwo (koma nkuwakhulupirira onse), iwo adzawapatsa malipiro awo. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.
Anthu amene adapatsidwa buku (Ayuda) akukupempha (iwe Mtumiki) kuti uwatsitsire buku kuchokera kumwamba. Ndithudi, adampemphanso Mûsa zazikulu kuposa zimenezi pomwe adati: “Tiwonetse Allah poyera.” Choncho udawagwira moto wamphenzi chifukwa cha kuipitsa kwao (motowo udachotsa miyoyo yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Zitatero Allah adawapatsa moyo kachiwiri). Kenako iwo adapanga thole (mwana wang’ombe monga mulungu wawo) pambuyo powafikira chisonyezo choonekera. Koma tidawakhululukira zimenezo, ndipo tidampatsa Mûsa chisonyezo choonekera poyera.[153]
Ndipo tidatukula phiri la Al-Tur pamwamba pawo (Ayudawo) polandira pangano lawo; tidati kwa iwo: “Lowani pachipata (cha dziko ili la Sham) mutawerama.” Tidatinso kwa iwo: “Musalumphe malire pa nkhani ya Sabata.” Ndipo tidalandira kwa iwo pangano lokhwima.[154]
Choncho (tidawalanga) chifukwa chakuswa mapangano awo, ndi kukana kwawo zisonyezo za Allah, ndi kupha kwawo aneneri popanda choonadi, ndi kunena kwawo kwakuti: “Mitima yathu yakutidwa (siingathe kuzindikira zomwe ukunena iwe Muhammad {s.a.w}).” (Ai, Siinakutidwe ndi chilichonse), koma Allah waidinda zidindo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo; tero sakhulupirira koma pang’ono pokha.
Chifukwanso cha kusakhulupirira kwawo ndi kumnamizira kwawo Mariya bodza lalikulu (kuti wabala Isa (Yesu) m’njira ya chiwerewere);
Ndikuyankhula kwawo (kwakuti): “Ife tamupha Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, Mtumiki wa Allah; pomwe sadamuphe ndipo sadampachike pa mtanda. Koma adasokonezedwa (ndi munthu wina namuganizira kuti ndi Isa (Yesu). Ndithudi, amene akutsutsana pankhaniyi (Ayuda ndi Akhrisitu) ali m’chikaiko pa iyo; alibe kudziwa kotsimikizika, koma akungotsatira zongoganizira. Ndipo, sadamuphe mosimikiza (kuti ndi iye).
Koma Allah adamkweza kwa Iye ndipo Allah Ndimwini mphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Palibe aliyense mwa anthu omwe adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) koma kuti azamkhulupirira iye (Yesu kuti sadali mulungu) imfa yake (Yesuyo) isadadze (izi zizachitika pamene Yesuyo azabwerenso padziko lapansi kumapeto kwa dziko). Nayenso (Yesu) pa siku la chiweruziro adzaikira umboni pa iwo (kuti iye adali chabe kapolo wa Allah).
Chifukwa chakuchita kwawo zoipa, awo Ayuda, tidaletsa kwa iwo zinthu zabwino (zakudya) zomwe zidali zovomerezeka kwa iwo; ndiponso chifukwa cha kutsekereza kwawo anthu ambiri kuyenda panjira ya Allah.
Ndi kudya kwawo riba (katapira) pomwe adaletsedwa kuti asadye; ndiponso chifukwa chakudya kwawo chuma cha anthu mwachinyengo. Ndipo osakhulupirira mwa iwo tawakonzera chilango chopweteka.
Koma mwa iwo amene azama pa maphunziro, ndi okhulupirira (onsewo) akukhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulutsidwa patsogolo pako. Ndipo omwe akupitiriza kupemphera Swala, ndi kupereka Zakaati, ndi kukhulupirira Allah komanso tsiku lachimaliziro, iwo tidzawapatsa malipiro aakulu.
Ndithudi, takuvumbulutsira (chivumbulutso) monga momwe tidamuvumbulutsira Nuh (Nowa) ndi aneneri amene anadza pambuyo pake. Ndipo tidamuvumbulutsiranso Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi mbumba yake. Ndipo (tidamuvumbulutsiranso) Isa (Yesu), Ayyub (Yobu), Yunus (Yona), Haarun (Aroni) ndi Sulaiman, ndipo Daud tidampatsa Zabur (Masalimo).
Ndipo (tidavumbulutsanso chivumbulutso) kwa atumiki omwe takusimbira kale nkhani zawo komanso kwa atumiki ena omwe sitinakusimbire (nkhani zawo); ndipo Allah adayankhula ndi Mûsa mwachindunji.
(Iwo ndi) atumiki omwe adauza nkhani zabwino (kwa anthu abwino) ndi kuwachenjeza (oipa) kuti anthu asadzakhale ndi mtsutso pa Allah pambuyo pa (kudza kwa) atumikiwa. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Koma Allah akuikira umboni zimene wakuvumbulutsira kuti (nzoona), adavumbulutsa mwanzeru Zake. Nawonso angelo akuikira umboni. Ndipo Allah akukwana kukhala mboni.
Ndithu amene sadakhulupirire, nawatsekereza (anthu) kuyenda pa njira ya Allah, ndithudi asokera; kusokera kwakukulu.
Ndithudi, amene sadakhulupirire, namachita zoipa, sali Allah owakhululukira iwowo ndi kuwaongolera njira.
Kupatula njira yomka ku Jahannam, mmenemo akakhala muyaya. Ndipo zimenezo nzopepuka kwa Allah.
E inu anthu! Ndithu Mtumiki wakudzerani ndi choonadi chochokera kwa Mbuye wanu. Choncho khulupirirani; ndi bwino kwa inu kutero. Koma ngati mukana, (dziwani kuti) zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri Ngwanzeru zakuya.
E inu anthu a buku! Musamalumphe malire pa chipembedzo chanu. Ndipo musamamnenere Allah koma zowona (zokhazokha). Ndithu Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndi mtumiki wa Allah (ndiponso ndi munthu wolengedwa) ndi liwu Lake lomwe adaliyika mwa Mariya ndiponso (ali) ndi mzimu (moyo) wochokera kwa Iye (Allah, monga mizimu ina yonse imachokera kwa Iye). Choncho Khulupirirani Allah ndi atumiki Ake. Musamanene: “Utatu wa Mulungu;” siyani, (zikhululupiliro za utatu wa Mulungu), kutero ndibwino kwa inu. Ndithudi, Allah ndi Mulungu m’modzi (basi). Ulemelero wake ngotukuka kutali ndi kukhala ndi mwana. Nzake zonse za kumwamba ndi pansi. Ndipo Allah ndiMtetezi Wokwanira.
Mesiya (Mneneri Isa {Yesu}) sangaone kunyozeka kukhala kapolo wa Allah, ngakhalenso angelo oyandikitsidwa (kwa Allah). Ndipo amene angaone kunyozeka pa ukapolo wake kwa Allah nadzitukumula, onse adzawasonkhanitsa kwa Iye (ndipo kenako nkuwalonga kung’anjo ya Moto).
Koma amene adamkhulupirira (Yesuyo) ndi kuchita zabwino adzawapatsa malipiro ao mokwanira ndi kuwaonjezera mu zabwino Zake. Koma amene adaona kunyozeka (pokhala kapolo wa Allah) nadzitukumula, adzawalanga chilango chowawa; ndipo sadzapeza bwenzi ngakhale mtetezi kupatula Allah.
E inu anthu! Ndithudi, wakudzerani umboni wochokera kwa Mbuye wanu. Ndipo takuvumbulutsirani kuunika koonekera poyera.
Tsono amene akhulupirira Allah ndi kudziphatika kwa Iye, iwo adzawalowetsa ku chifundo ndi kuzabwino zochokera kwa Iye, ndikuwatsogolera kwa Iye njira yoongoka.
Akukufunsa (iwe Mneneri, za malamulo a chuma cha munthu yemwe wafa osasiya mwana kapena kholo). Nena: “Allah akukulamulani pa zayemwe sadasiye mwana ndi kholo (kuti) ngati munthu atamwalira pomwe alibe mwana, koma ali ndi mlongo wake (wa bambo amodzi), choncho (mlongo wakeyo) alandire theka (½) la zomwe wasiya (womwalirayo). Nayenso angalandire chuma (chamlongo wake) ngati alibe mwana. Ndipo ngati iwo ali (alongo) awiri, ndiye kuti adzalandira magawo awiri mmagawo atatu (2/3) a zomwe wasiya. Ndipo ngati ali abale (angapo) amuna ndi akazi, ndiye kuti mwamuna aliyense alandire gawo lolingana ndi la akazi awiri. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani (malamulo Ake) mwatsatanetsatane kuti musasokere. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.