Surah As-Saaffat ( Those Ranges in Ranks )

Surah As-Saaffat ( Those Ranges in Ranks ) - Chewa Aya count 182

Ndikulumbira (angelo) amene amandanda m’mizere yondondozana, (popembedza ndi kugonjera Mbuye wawo).
Ndi omwe amalalika ulaliki (wa Allah ndi kumtamanda mochulukira).
Ndithu tidalikongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi chokongoletsa cha nyenyezi (zowala).
Ndi kuti lisungidwe ku satana aliyense wogalukira (lamulo la Allah).
Kuti asamvere (zomwe zikunenedwa ndi) gulu lolemekezeka (la angelo). Ndipo akugendedwa (ndi kupirikitsidwa) mbali zonse.
Kuthamangitsidwa mwamphamvu; ndipo chilango chonkerankera patsogolo chili pa iwo.
Kupatula amene wazembetsa mawu (akumwamba), ndipo chikumtsatira iye chenje cha moto chowala kwambiri.
Tawafunsa (otsutsa zouka ku imfa): “Kodi iwo ngovuta kuwalenga kuposa zimene tidalenga, (monga: thambo, nthaka, nyenyezi ndi zina zotere)?” Ndithu Ife tidawalenga kuchokera ku dongo lonyata.
Koma iwe (Mneneri) ukudabwa (za kutsutsa kwawo kuuka ku imfa pomwe zisonyezo zilipo zambirimbiri), ndipo akukuchitira chipongwe (kudabwa kwako).
Ndipo akachiona chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah,) amachichitira chipongwe.
Ndipo osakhulupirira amanena: “Palibe chilipo apa, koma ndi matsenga woonekera poyera.”
“Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, tidzatulutsidwanso (kuchokera m’manda tili amoyo)?”
Nena (iwe Mneneri): “Inde (mudzaukitsidwa inu pamodzi ndi makolo anu) uku inu muli onyozeka.”
Ndipo adzanena (okanawo): “Kalanga ife! Kuonongeka nkwathu! Ili nditsiku lija lamalipiro!”
(Kudzanenedwa kwa angelo): “Asonkhanitseni amene adali osalungama pamodzi ndi akazi awo (okana Allah) ndi milungu yawo imene amaipembedza,”
“Koma aimikeni pano chifukwa iwo afunsidwa (za chikhulupiliro chawo ndi zochita zawo):”
“Kodi nchifukwa ninji inu (opembedza mafano) simukupulumutsana (monga mumanenera pa dziko lapansi kuti mudzapulumutsana)?”
Koma iwo pa tsikulo adzagonjera ndi kudzipereka (ku lamulo la Allah).
Ndipo (ofooka) adzanena (kwa odzikweza): “Inu mumatidzera kumbali komwe timakuganizira kuti nkwabwino (ndi kutichotsako kunka nafe ku njira yopotoka).
“Ndipo tidalibe nyonga zokuponderezerani inu, koma mudali anthu opyola malire (ndi kutuluka ku choonadi cha Allah).”
“Choncho mawu a Mbuye wathu (onena za chilango) atsimikizika pa ife; ndithu ife tichilawa (chilango).”
“Tidakusokeretsani; nafenso tidali osokera. (Choncho musatidzudzule).”
Ndithu (chilango chonga chimenecho) ndimomwe timawachitira olakwira (Allah).
Ndipo ankanena: “Kodi ife tisiye kupembedza milungu yathu chifukwa cha zonena za mlakatuli, wopenga?”
Iyayi koma adawadzera ndi choonadi (Mthenga wawo Muhammad yemwe siwamisala kapena wolakatula zopeka) ndipo adawatsimikizira za atumiki.
Zipatso (zamtundu uliwonse); ndipo iwo adzalandira ulemu (waukulu),
Adzakhala pa makama (a mtengo wapatali) uku akuyang’anizana.
Uku zikuwazungulira zikho zodzazidwa ndi zakumwa zochokera m’kasupe woyenda nthawi zonse.
(M’zakumwazo) mulibe zopweteketsa mutu (kwa ozimwa) ndiponso iwo sadzaledzera nazo.
Ndipo kwa iwo kudzakhala akazi oyang’ana iwo okha, ophanuka maso (okongola).
Onga ngati dzira (la nthiwatiwa) losungidwa (m’mapiko).
Adzanena wonena mmodzi wa iwo: “Ine ndidali ndi mnzanga (wopembedza mafano amene amatsutsana nane za chipembedzo ndi zophunzitsa za Qur’an yolemekezeka).”
“Zakuti tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, (tidzaukanso) ndi kulandira malipiro (pa zochita zathu)?”
(Wokhulupirira) adzanena (kwa anzake: “Inu anthu a kumtendere) kodi simungasuzumire (nane ku moto kuti timuone)?”
Adzanena: “Ndikulumbilira Allah! Udatsala pang’ono kuti undiononge (ndikadakuvomera paja pa dziko lapansi).”
“Ndipo pakadapanda chisomo cha Mbuye wanga, ndikadakhala mmodzi mwa opezeka ku Moto.”
“Kodi zili choncho kuti sitidzafanso (tizingosangalala m’Munda wamtendere).”
Ndithu izi (zimene Allah waika m’Munda wamtendere) ndiko kupambana kwakukulu.
Kodi zimenezo ndilo phwando labwino kapena mtengo wa Zaqqum (wowawa kwambiri womwe anthu a ku Moto azikadya)?
Ndithu Ife taupanga (mtengo umenewu) kukhala mayeso ndi chilango cha anthu ochimwa (podzichitira okha chinyengo ndi kupembedza mafano.)
Umenewu ndimtengo omwe umatuluka pakatikati pa Jahannam (adaulenga kuchokera ku Moto).
Ndithu iwo akadya mtengowo ndi kudzaza mimba zawo ndi zipatso zake (pakuti sakapeza chakudya china kupatula zipatso za mtengowo).
Kenako, ndithu kuwawa kwa mtengowo kosakanikirana ndi madzi owira kuzakhala pa iwo.
Kupatula akapolo a Allah, oyeretsedwa (iwo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere).
Ndithu Nuh adatiitana, (ndipo tidamuyankha mayankho abwino), taonani kukhala bwino Ife Oyankha.
Ndipo tidazichita zidzukulu zake kukhala zotsala (pa dziko, oipa ataonongeka).
Ndipo tidamsiira mbiri yabwino kwa mibadwo yodza pambuyo pake.
Kumbuka pamene adadza kwa Mbuye wake ndi mtima wabwino (wogonjera malamulo).
“Kodi maganizo anu ngotani pa Mbuye wa zolengedwa zonse?”
Ndipo adanena: “Ine ndine wodwala!”
(Ibrahim) adapita mozemba ku mafano awo, ndipo adawauza (mwachipongwe:) “Bwanji simukudya (chakudya chomwe chaikidwa patsogolo panupo)?”
Atatero adawatembenukira ndi kuwamenya (mwamphamvu) ndi dzanja lamanja.
(Pamene adamva eni mafanowo) adadza kwa iye akuthamanga.
Anati: “Kodi mukupembedza (miyala) imene mwasema?”
“Chikhalirecho Allah ndiye adakulengani ndi zimene mukuchita!”
Adafuna kumchita chiwembu (kuti amuphe ndi moto), koma tidawachita kukhala onyozeka.
Ndipo (Ibrahim) adati: “Ndithu ine ndikupita kwa Mbuye wanga, Iye andiongolera.”
“E Mbuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale (mmodzi) mwa olungama!”
Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (mwanayo ndi Ismaila).
Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana nsinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (owona ochokera kwa Allah omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Allah). Nanga ukuti bwanji?” (Mwana wabwino) adanena: “Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamulidwa. Ngati Allah afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira.”
Pamene adagonjera onse awiri (chofuna cha Allah), ndipo (Ibrahim) adam’goneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha).
“Ndithu wavomereza maloto! (Choncho usamuphe mwana wakoyo).” Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino.
Ndipo tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apereke nsembe).
Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).
M’menemo ndi mornwe timawalipirira ochita zabwino.
Ndiponso tidamuuza nkhani yabwino (yoti akhala ndi mwana wotchedwa) Isihaqa; mneneri; wam’gulu la olungama.
Ndipo ndithu tidawachitira zabwino Mûsa ndi Haruna, (powapatsa uneneri ndi madalitso ambiri).
Ndipo tidawathangata (powagonjetsera adani awo), ndipo iwo adali opambana.
Ndipo tidawapatsa (Mûsa ndi Haruna) buku losonyeza poyera (malamulo).
Ndiponso tidawasiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pawo).
(Kumbuka) pamene adanena kwa anthu ake: “Bwanji simuopa (Allah)?”
“Mukupembedza (fano lotchedwa) Ba’la ndi kusiya (kupembedza) Wabwino zedi mwa olenga onse.”
Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).
(Kumbuka) pamene adathawira m’chombo chodzazidwa (ndi katundu).
Choncho adachita mayere, ndipo adali m’gulu la omgwera (mayerewo).
Kukadapanda kuti iye adali m’modzi mwa otamanda ndi kulemekeza Allah).
Akadakhala m’mimba mwake mpaka tsiku loukitsidwa (zolengedwa ku imfa).
Ndipo (atachira) tidamtuma ku anthu okwana zikwi zana limodzi (100,000) kapena kupambana apa.
Ndipo adakhulupirira (ndi kuvomereza ulaliki wake); choncho tidawapatsa chisangalalo kufikira nthawi (ya imfa yawo).
Choncho afunse: “Kodi Mbuye wako ndiye woyenera ana aakazi, ndipo iwo aamuna? (Pomwe iwo akabereka mwana wamkazi amanyansidwa naye)!”
Kodi nchiyani chakupezani (kuti muweruze mopanda chilungamo); nanga mukuweruza bwanji (zimenezi)?
Kodi bwanji simukumbukira, (mwaiwala zisonyezo Zake zodabwitsa ndi kupatukana kwake ndi zimenezo)?
Kapena inu muli ndi umboni woonekera (wochokera kumwamba)?
Tabweretsani buku lanulo (momwe mwalembedwa zimenezi) ngati mukunena zoona.
Ndipo adapeka chibale pakati pa Iye (Allah) ndi ziwanda; (pomwe ziwanda nzobisika kwa iwo). Ndithu ziwanda zimadziwa kuti iwo osakhulupirira akaonekera (kwa Allah kuti aweruzidwe)!
Walemekezeka Allah! Ndi kupatukana ndi zimene akumnamizira!
Koma akapolo a Allah oyeretsedwa (ali kutali ndi zimene akusimba osakhulupirirazi).
Ndithu inu (osakhulupirira) ndi zimene mukuzipembedza (kusiya Allah),
Kupatula yemwe (Allah adadziwa kuti) ngolowa ku Jahannam.
Ndipo (angelo adanena): “Aliyense mwa ife ali ndi malo ake odziwika.”
“Ndipo ndithu (ena mwa) ife ngondanda m’mizere (ya mapemphero nthawi zonse).”
“Ndipo (ena mwa) ife ngolemekeza (Allah nthawi zonse ndi kumtamanda ndi kumpatula ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero wake).”
Koma (pamene lidawadzera bukulo), adalikana; choncho posachedwa adziwa (zotsatira zake).
Mbuye wako, Mwini ulemelero, wapatukana ndi zimene akumnamizira (osakhulupirira).
Ndipo kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.
Share