Surah Al-A'raf (The Heights )

Surah Al-A'raf (The Heights ) - Chewa Aya count 206

Alif-Lâm-Mîm-Sad.
(Iyi Qur’an ndi) buku (lopatulika) lomwe lavumbulutsidwa kwa iwe. Choncho chifuwa chako chisabanike ndi ilo (poopa kufikitsa mawu ake kwa anthu kuti angakuyese wabodza;) kuti uwachenjeze nalo (otsutsa) ndi kuti likhale chikumbutso kwa okhulupirira (kuti aonjezere chikhulupiliro chawo).[178]
Ndimidzi yambiri imene tidaiononga ndipo chilango Chathu chidaidzera nthawi ya usiku, kapena usana iwo atagona tulo tamasana (akupumula monga momwe zinawachitikira anthu a Loti ndi anthu a Shuaib).
Ndipo sikunali kulira kwawo pamene chinawafika chilango chathu koma kunena (ndi kuvomereza): “Ndithudi, ife tinali ochita zoipa.” (Koma kuvomereza kwawoko sikunawapindulire kanthu).
Tsono tidzawauza mozindikira bwino-bwino (chilichonse chimene ankachita). Ndipo sitidali kutali (nawo pamene ankachita zochita zawo).
Ndipo sikero (yoyezera zochita za anthu) tsiku limenelo idzakhala yoona (yopanda chinyengo). Choncho, amene idzalemere miyeso yake (ya zabwino), iwowo ndiwo opambana.
Ndithudi tinakupatsani mphamvu yokhalira pa dziko, ndipo takupangirani m’menemo zinthu zofunika pa moyo wanu. Koma kuyamika kwanu mpang’ono.
(Allah) adati: “Nchiyani chakuletsa kumgwadira pamene ndakulamula?” (Satana) anati: “Ine ndine wabwino kuposa iye. Ine munandilenga ndi moto koma iye mudamulenga ndi dongo.”
(Allah) adati: “Choncho, choka m’menemo ndi kutsikira pansi. Sikofunika kwa iwe kudzitama m’menemo. Tuluka, ndithu iwe ndiwe mmodzi wa onyozeka.”[179]
(Satana) adati: “Ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwa (akapolo anu ku imfa).”
(Allah) adati: “Ndithudi iwe ndi mmodzi wa opatsidwa nthawi.”
Iye (chifukwa cha njiru yake yoopsa pa Adam) adati: “Tsono chifukwa chakuti mwandichita ine kukhala wopotoka, ndidzawakhalira (akapolo Anu ndi kuwabisalira) pa njira Yanu yoongoka (ndi cholinga chowasokeretsa).”
(Allah) adati: “Tuluka m’menemo, uli wonyozeka ndi wothamangitsidwa. Amene adzakutsata iwe mwa iwo, ndithudi, (ndikamponya ku Moto). Ndipo ndikaidzadzitsa Jahannam ndi inu nonse.”
(Kenako Allah adanena kwa Adam) “E iwe Adam! Khala ndi mkazi wako m’Munda wamtendere (sangalalani ndi zomwe zili m’menemo), idyani paliponse pamene mwafuna. Koma mtego uwu musawuyandikire kuopera kuti mungakhale m’gulu la odzichitira okha zoipa.”
Ndipo adawalumbilira onse awiri kuti: “Ndithudi, ine ndine mmodzi mwa olangiza (ndikukufunirani zabwino).”
Iwo (Adam ndi mkazi wake) adati (modzichepetsa): “E Mbuye wathu! Tadzichitira tokha zoipa, ngati simutikhululukira ndi kuchita nafe chifundo ndiye kuti tikhala mwa otaika.”
(Allah) adati: “Tsikani pansi uku pali chidani pakati panu. Ndipo padziko lapansi ndipokhala panu ndi kusangalala kwanu mpaka m’nthawi yoikidwayo.”
(Allah) adatinso: “Muzikakhala moyo pamenepo, ndipo muzikafa pamenepo; ndipo momwemo mudzatulutsidwa (mutauka kwa akufa).”
E inu ana a Adam! Ndithu tatsitsa kwa inu chovala chobisa umaliseche wanu ndi chodzikongoletsera nacho. Koma chovala choopa nacho Allah (pakudziyeretsa ku zoletsedwa) chimenecho ndicho chabwino koposa. Zimenezo ndi zizindikiro za (chisomo cha) Allah kuti iwo akumbukire.[180]
Nena: “Mbuye wanga walamula chilungamo; ndiponso (wandiuza kuti ndikuuzeni kuti) lungamitsani nkhope zanu (kwa Iye) m’nthawi ya Swala iliyonse, ndipo mpembedzeni Iye Yekha momuyeretsera chipembedzo monga Iye adakulengani pachiyambi, momwemonso mudzabwerera kwa Iye.”
Nena: “Ndani waletsa zokongoletsa za Allah (zovala), zomwe Iye (Allah) adawatulutsira akapolo Ake ndi zakudya zabwino?” Nena: “Zinthu zimenezo nzololedwa kwa amene akhulupirira (Asilamu) pamoyo wa pa dziko lapansi. (Zidzakhala) zawozawo tsiku la chimaliziro. M’menemo ndi momwe tikulongosolera Ayah (Zathu) kwa anthu ozindikira.”[181]
M’badwo ulionse uli ndi nthawi yakeyake (yofera). Ndipo nthawi yawo ikadza sangaichedwetse ngakhale ola limodzi, ndiponso sangaifulumizitse.
Kodi ndani woipitsitsa koposa munthu wopekera bodza Allah kapena wotsutsa zivumbulutso Zake? Iwo gawo (lachakudya chimene) adawalembera liwafika (pano pa dziko lapansi ngakhale kuti ngosakhulupirira mwa Allah). Kufikira pomwe adzawadzera atumiki Athu (angelo kudzatenga miyoyo yawo), nawapatsadi imfa uku akunena: “Kodi zili kuti zija munkazipembedza kusiya Allah?” Adzati: “Zatisowa.” Ndipo adzadzichitira okha umboni kuti iwo adali okana (Allah).
(Allah) adzati (pa tsiku la chiweruziro): “Lowani ku Moto pamodzi ndi mibadwo imene idamuka kale (inu musanabwere) yochokera m’ziwanda ndi mu anthu. M’badwo uliwonse pamene uzikalowa, udzatembelera unzake, kufikira pamene onse adzasonkhana m’menemo. Adzanena apambuyo kwa oyambilira awo: “Mbuye wathu! Awa, adatisokeretsa. Apatseni chilango cha Moto chochuluka.” (Allah) adzanena: “Aliyense mwa inu akhala ndi chilango chochuluka; koma izi inu simukudziwa.”[183]
Moto wa Jahannam ndi mphasa yawo; ndipo pamwamba pawo adzakhala ndi (chofunda cha Moto) chowaphimba. Umo ndimomwe Tikuwalipirira anthu osalungama.
Ndipo tidzachotsa kusakondana (komwe kudali) m’mitima mwawo; (adzakhala okondana ngakhale pa dziko lapansi adali odana), uku pansi ndi patsogolo pawo mitsinje ikuyenda; ndipo adzanena (m’kuthokoza kwawo): “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Yemwe adatitsogolera ku ichi (chomwe chatidzetsera mtendere). Sitikadaongoka pakadapanda Allah kutiongola. Atumiki a Mbuye wathu adadza ndi choonadi.” Ndipo adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Uwu ndi Munda wamtendere umene mwapatsidwa chifukwa cha zomwe mudali kuchita.”
Anthu a ku Munda wamtendere adzaitana anthu aku Moto (adzanena kuti): “Ndithudi ife tapeza zimene Mbuye wathu adatilonjeza kuti nzoona. Kodi nanunso mwapeza zomwe Mbuye wanu adakulonjezani kuti nzoona?” (Anthu a ku Moto) adzanena: “Inde.” Choncho wolengeza pakati pawo adzalengeza kuti: “Matembelero a Allah ali pa anthu ochita zoipa.”
“Omwe ankaletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah nafuna kuikhotetsa njirayo (kuti ioneke yokhota pamaso pa anthu), omwenso sadakhulupirire za tsiku lachimaliziro.”
Ndipo pakati pawo (pa anthu a ku Munda wamtendere ndi a ku Moto) padzakhala chotchinga. Ndipo pamwamba pachikweza padzakhala anthu ena (ofanana ntchito zawo zabwino ndi zoyipa) omwe akazindikira onse (a ku Jannah ndi ku Moto), ndi zizindikiro zawo. Ndipo akawaitana anthu a ku Jannah (kuti): “Salaamun Alayikum (mtendere ukhale pa inu).” Koma asanailowe uku ali ndi chikhulupiliro (kuti ailowa).
Ndipo maso awo akakatembenuzidwa (kuyang’ana) ku mbali ya anthu a ku Moto, adzanena: “Mbuye wathu musatiike pamodzi ndi anthu ochita zoipa. (Tikhululukireni zolakwa zathu. Tilowetseni ku Jannah).”
Naonso anthu a ku Moto adzaitana a ku Jannah (ndikuwauza kuti): “Tatipungulirani madzi kapena chinthu chimene Allah wakupatsani.” (Anthu a ku Jannah) adzanena kuti:“Ndithu Allah waletsa kupereka zonse ziwirizo kwa osakhulupirira.”
Omwe adachita chipembedzo chawo kukhala zinthu zopanda pake ndiponso masewero; ndipo udawanyenga moyo wa m’dziko. Choncho, lero Ifenso tiwaiwala (tiwaleka ku Moto) monga momwe adakuiwalira kukumana ndi tsiku lawo ili, ndi chifukwa chakukana kwawo zivumbulutso Zathu.
Kodi chiliponso chomwe akudikilira osati zotsatira zake (za bukulo)? Ndipo tsiku lakudza zotsatira zake, adzanena amene kale sadalilabadire: “Ha! Atumiki a Mbuye wathu adadzadi ndi choonadi (tsopano tikuvomereza). Kodi tingakhale nawo ife aomboli oti atiombole (kwa Mbuye wathu), kapena tingabwezedwe kuti tikachite (zabwino) osati zija tinkachita?” Zoonadi adziononga okha, ndipo zawasowa zabodza zomwe adali kupeka.
Ndithudi, Mbuye wanu ndi Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi. Kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu). Amauchita usiku kuti uvindikire usana, zimatsatana mwamsangamsanga. Ndipo dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi nzofewetsedwa, (zikuyenda mogonjera) ndi Lamulo Lake. Dziwani kuti kulenga ndi kulamula Nkwake. Ndithudi, watukuka Allah Mbuye Wazolengedwa (zonse).
Ndipo m’nthaka yabwino umatuluka mmera wake (mwachangu) mwachilolezo cha Mbuye wake. Ndipo nthaka yomwe ili yoipa siitulutsa (mmera wake) koma movutikira. M’menemo ndi momwe Tikuchifotokozera chivumbulutso momveka kwa anthu oyamika.[186]
Akuluakulu a mwa anthu ake adati: “Ndithu ife tikukuona kuti uli m’kusokera koonekera (potiletsa izi zomwe tidawapeza nazo makolo athu).”
(Iye) adati: “E anthu anga! Palibe kusokera mwa ine. Koma ine ndine Mtumiki wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa!”
“Ndikufikitsa kwa inu uthenga wa Mbuye wanga. Ndiponso ndikukulangizani; ndipo ndikudziwa zochokera kwa Allah zomwe inu simukuzidziwa.”
“Kodi mukudabwa kukudzerani ulaliki wochokera kwa Mbuye wanu kudzera mwa munthu wa mwa inu, (yemwe wadza) kuti akuchenjezeni ndi kuti muope (Allah), ndikutinso muchitiridwe chifundo?”
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Palibe uchidzete mwa ine. Koma ine ndine Mtumiki wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa.”
“Ndikufikitsa kwa inu uthenga wa Mbuye wanga. Ndipo ine ndine mlangizi wanu (wokufunirani zabwino), wokhulupirika.”
“Kodi mukudabwa pokudzerani ulaliki kuchokera kwa Mbuye wanu kupyolera mwa munthu wochokera mwa inu kuti akuchenjezeni? Kumbukirani (mtendere wa Allah) pamene adakuikani kukhala amlowam’malo pambuyo pa anthu a Nuh, ndipo akuonjezerani m’kalengedwe kukhala a misinkhu itali-itali ndi amphamvu. Kumbukiraninso mtendere wa Allah (pothokoza) kuti mupambane.”
Ndipo kwa Asamudu tidamtumiza m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Gwadirani Allah; inu mulibe mulungu wina koma Iye basi. Chizindikiro chochokera kwa Mbuye wanu chadza kwa inu. Iyi ndi ngamira ya Allah monga chisonyezo chanu (chizizwa chanu), choncho, isiyeni izidya m’dziko la Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopera kuti chingakugwereni chilango chowawa kwambiri.”
“Ndipo kumbukirani pamene (Allah) adakupangani kukhala amlowammalo pambuyo pa mtundu wa Âdi. Ndipo adakukhazikani pa dziko (mwa ubwino). Mukudzimangira nyumba zikuluzikulu mchigwa, ndiponso kusema ndi kuboola mapiri kukhala nyumba. Choncho kumbukirani mtendere wa Allah, ndipo musaononge pa dziko pofalitsa chisokonezo.”
Adanena akuluakulu omwe adali odzitukumula mwa anthu ake kuuza omwe adaponderezedwa kwa amene adakhulupirira mwa iwo: “Kodi muli ndi chitsimikizo kuti Swalih ngotumizidwa ndi Mbuye Wake (wapatsidwa utumiki)?” (Iwo) Adati: “Ndithu ife tikukhulupirira zomwe watumidwa nazo (kuzifikitsa kwa ife).”
Choncho adaipha (adaizinga) ngamira ndi kunyoza lamulo la Mbuye wawo, nati: “E iwe Swaleh! Tibweletsere (chilango) chimene wakhala ukutilonjeza ngati ulidi mmodzi wa otumidwa.”
Choncho, chivomerezi chidawagwira mwadzidzidzi, adapezeka ali akufa chigwadire m’nyumba zawo.
Tero, Swalih adawasiya (nkupita kwina kwake) uku akunena: “E anthu anga! Ndidafikitsadi uthenga wa Mbuye wanga kwa inu. Ndipo Ndidakuchenjezani ndi kukulangizani. Koma inu simufuna alangizi.”
Nayenso Luti (tidamtuma, ndipo kumbuka) pamene adati kwa anthu ake: “Kodi mukuchita chonyansa chomwe sadakutsogolereni aliyense kuchichita mwa anthu akale m’zolengedwa zonse?”
Kuyankha kwa anthu ake sikudali kwa mtundu wina koma kuti: “Apirikitseni m’mudzi wanu. Ndithu iwowo ndi anthu odziyeretsa. (Choncho akhaliranji m’mudzi wa uve? Akakhale ndi anzawo ochita zaukhondo).”
Koma tidampulumutsa iye ndi banja lake, kupatula mkazi wake; adali m’gulu la otsalira m’mbuyo (adaonongeka).
“Ndipo musamawakhalire anthu pa njira iliyonse mowabisalira ndi kumawaopseza, ndi kuwatsekereza kuyenda pa njira ya Allah amene amkhulupirira Iye, ndi kufuna kuikhotetsa njirayo (kuti anthu asaitsate). Ndipo kumbukirani pamene mudali ochepa nakuchulukitsani. Ndipo onani momwe adalili mapeto a owononga.”
Choncho chivomerezi chidawaononga mwadzidzidzi motero adapezeka akufa chigwadire mnyumba zawo.
(Pamene nthawi yakuonongeka kwawo idayandikira, Shuaib adatuluka m’mudzimo pamodzi ndi aja adakhulupirira) nawasiya oipawo (kunka kutali) uku akunena: “E inu anthu anga! Ndinafikitsadi uthenga wa Mbuye wanga ndipo ndinakuchenjezani ndiye nchotani ndidandaule za anthu okanira.”
Ndipo palibe pamene tidamtuma mneneri aliyense m’mudzi uliwonse (nkumukana) koma tinkawalanga eni mudziwo ndi masautso ndi mavuto kuti afatse (ndi kulambira Allah; koma ayi adakanika).
Kenako tinasintha pamalo pa choipa pobweretsapo chabwino, (tidawachotsera masautso ndi mavuto ngakhale sadali okhulupirira) mpaka anachuluka, ndi kuchulukanso chuma chawo; anayamba kunena kuti: “Masautso ndi mavuto adawakhudzaponso makolo athu. (Zoterezi sizachilendo kwa ife).” Choncho tidawaononga mwadzidzidzi asakudziwa.
Kodi anthu a m’mizinda (iyo momwe muli anthu oipa) ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango chathu sichingawadzere usiku iwo ali mtulo?
Kapena anthu a m’mizindayo ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango Chathu sichingawafike masana uku iwo akusewera?
Kodi akudziika pa chitetezo ku chilango cha Allah? Sangadziike pa chitetezo ku chilango cha Allah kupatula anthu otayika basi.
Iyo ndi midzi (ikuluikulu) yomwe tikukusimbira iwe zina mwa nkhani zake. Ndithudi, adawadzera atumiki awo ndi zizindikiro (zoonekera poyera zosonyeza kuti iwo ndi atumiki a Allah). Koma sadali oti nkukhulupirira pa zomwe adazitsutsapo kale. Umo ndi mmene Allah amadindira ndi kuitseka mitima ya osakhulupirira (kotero kuti sangathandizike ndi malangizo a mtundu uliwonse).
Ndipo ambiri a iwo sitidawapeze akukwaniritsa lonjezo lililonse koma tidawapeza ambiri a iwo ali opandukira (chilamulo cha Allah).
Ndipo Mûsa adati: “E iwe Farawo! Ndithu ine ndine mthenga wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.”
“Ndikofunika kwa ine kuti ndisamnenere Allah chilichonse koma choonadi basi. Ndithu ndakudzerani ndi chizindikiro choonekera kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho, aleke ndinke nawo ana a Israyeli.”
(Farawo) adati: “Ngati wadza ndi chizindikiro, bwera nacho (tichione), ngati iwe ulidi mmodzi wa onena zoona.”
Nduna za mwa anthu a Farawo zidati: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa (kwambiri zamatsenga).”
(Iwo) adati (kwa Farawo): “Muleke pang’ono iye ndi m’bale wakeyu (usawaphe); ndipo tumiza osonkhanitsa m’mizinda kuti akusonkhanitsire (amatsenga onse akuluakulu).”
“Kuti akubweretsere wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri.”
(Farawo) adati: “Inde, ndipo mudzakhala mwa oyandikitsidwa (mudzakhala nduna zanga).”
(Amatsenga) adati: “E iwe Mûsa! Kodi uyamba kuponya ndiwe (matsenga ako pamaso pa anthu), kapena ife tikhale oyambilira kuponya?”
Choncho, choonadi chidatsimikizika, ndipo zidapita pachabe zomwe ankachita.
Ndipo amatsenga adadzigwetsa uku akulambira (Allah).
“Ndithudi, nditseteka manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa; (kudula dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wa kumanzere, kapena dzanja la kumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja). Kenako ndikupachikani nonsenu.”
“Komatu palibe choipa chimene waona mwa ife kupatula kuti takhulupirira zizindikiro za Mbuye wathu pamene zatidzera. E Mbuye wathu! Titsanulireni chipiliro, ndipo tipatseni imfa uku tili Asilamu (ogonjera Inu).”
Ndipo nduna za mwa anthu a Farawo zidati (kwa Farawo): “Kodi umuleka Mûsa ndi anthu ake kuti abwere ndi chisokonezo m’dziko, ndi kuti akusiye iwe ndi milungu yako (yomwe adatilangiza makolo athu kuti tipembedze pamodzi ndi iwe)? (Farawo) Adati: “Tipha ana awo achimuna ndikuwasiya amoyo (ana awo) achikazi. Ndithudi ife pa iwo tili ndi mphamvu zowagonjetsera.”
(Adali chonchi): Ubwino ukawadzera, amati: “Ubwinowu nchifukwa cha zochita zathu zabwino.” Ndipo choipa chikawadzera, amakankhira kwa Mûsa ndi amene adali naye. (Amati iye ndiye wadzetsa tsokalo chifukwa choisambula milungu yawo). Dziwani kuti tsoka lawo limachokera kwa Allah (chifukwa cha zochita zawo zoipa). Koma ambiri a iwo sazindikira.
Ndipo adati (kwa Mûsa): “Chisonyezo chilichonse chimene ungatibweretsere kuti utilodze nacho (siupindula kanthu). Ifetu sitikukhulupirira.”
Ndipo tidawaolotsa ana a Israyeli pa nyanja (ndi kupulumuka ku masautso a Farawo), nadza kwa anthu omwe adali kupembedza mafano awo. (Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Nafenso tipangire mulungu (wamafano) monga milungu yomwe ali nayo iwo.” (Mneneri Mûsa) adati: “Ndithudi, inu ndinu anthu osazindikira.”
Adati: “Kodi ndikufunireni mulungu wina kusiya Allah chikhalirecho Iye wakuchitirani zabwino zoposa pa zolengedwa zonse?”
Ndipo tidamlonjeza Mûsa masiku makumi atatu (kuti achite mapemphero kuti kenako timpatse Taurat). Ndipo tidawakwaniritsa ndi masiku khumi; chomwecho lidakwanira pangano la Mbuye wake (lopita kukampatsa Tauratiyo) m’masiku makumi anayi. Ndipo Mûsa adati kwa m’bale wake Harun: “Lowa m’malo mwanga pa (kuwatsogolera) anthu angawa. Ndipo konza; usatsate njira ya oononga.”
Pamene Mûsa adafika kumalo achipangano Chathucho, ndipo Mbuye wake namulankhula, (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Dzionetseni kwa ine kuti ndikuoneni.” Allah adati: “Sungathe kundiona; koma yang’ana phirilo (lomwe lili patsogolo pako). Ngati likhazikika pamalo pake (popanda kusweka), ukhoza kundiona.” Choncho Mbuye wake pamene adadzionetsa kwa phirilo, adalichita kukhala loswekasweka ndipo Mussa adagwa ndi kukomoka. Pamene adatsitsimuka adati: “(Ha! Ndikutsimikizadi kuti) Inu ndinu Wolemekezeka. Ndalapa kwa Inu, ndipo ndine woyamba mwa okhulupirira (izi).”
(Allah) adati: “E iwe Mûsa! Ndithu Ine ndakusankha iwe mwa anthu onse, (kukusankhira) uthenga Wanga ndi kuyankhulana Nane. Choncho landira chimene ndakupatsa, ndipo khala m’modzi wa anthu othokoza.”
Ndipo tidamlembera m’mapale (m’masileti) maphunziro aulaliki wa mtundu uliwonse wofotokoza chinthu chilichonse: “Choncho, atenge mwa mphamvu ndi kuwalamulira anthu ako kuti awagwire mwa ubwino wake. Posachedwapa ndidzakusonyezani midzi ya oipa oswa malamulo athu (momwe idaonongekera. Ndipo ndikulowetsani inu m’menemo).”
Ndipo pambuyo pake (popita kukalandira Taurat), anthu a Mûsa adaumba (fano la) thole (mwana wa ng’ombe) kuchokera mu zodzikongoletsera zawo (zibangiri zawo za siliva ndi golide); yemwe adali ndi thupi ndi kumatuluka mawu (koma wopanda moyo). Kodi sakuona kuti ilo (fano lawolo) silikuwalankhula ndiponso silikuwaongolera njira (yabwino?) Koma adalipanga basi (kuti likhale mulungu wawo wa fano) potero adali kudzichitira okha zoipa.
Ndipo pamene Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya, wodandaula (pomva zomwe zidachitikazo), adati: “Umlowam’malo wanu womwe mudandichitira pambuyo panga, ngoipa zedi. Kodi mudalifulumilira lamulo la Mbuye wanu; (mudachita zanuzanu musanadziwe chimene angakulamulireni Mulungu wanu)? Ndipo adawaponya pansi mapalewo (momwe mudalembedwa malamulo a chipembedzo chake). Nagwira mutu wa M’bale wake nkuukokera kwa iye. (kufuna kummenya chifukwa cha mkwiyo umene adali nawo. M’bale wakeyo) adati: “E iwe mwana wa mayi anga! Ndithu anthu (awa) adandiyesa wofooka, potero (sadamvere malangizo anga). Adatsala pang’ono kundipha. Choncho usawakondweretse adani (ndi chilango chako) pa ine, ndipo usandiike pamodzi ndi anthu oipa.”
(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi m’bale wanga ndipo tilowetseni m’chifundo Chanu. Inu Ndinu Achifundo kuposa achifundo onse.”
Ndipo Mûsa adasankha anthu ake makumi asanu ndi awiri (70 omwe adali amakhalidwe abwino) kuti akafike kumalo a chipangano chathu (chimene tidamuuza kuti akabwere nawo pa phiripo kuti akapemphe chikhululuko pa machimo awo omwe adachitidwa ndi anzawo oipa). Ndipo pamene chivomerezi chachikulu chidawafika (adatsala pang’ono kufa). (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ngati mukadafuna mukadawaononga iwo ndi ine kale (pamaso pa anzawo onse kuti adzionere okha kuti amwalira ndi mphamvu za Allah, osati pakuwapha ine). Kodi mutiononga chifukwa cha zochita za mbuli zathu? Izi sichina koma ndi mayesero anu. Kupyolera m’mayeserowo mumamlekelera kusokera amene mwamfuna, ndi kumtsogolera amene mwamfuna. Inu ndiye Mtetezi wathu; choncho, tikhululukireni ndi kutimvera chifundo. Inu ndinu Abwino mwa okhululuka onse.”
“Ndipo tilembereni zabwino pa dziko lino lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro, ndithudi tibwerera kwa inu!” (Allah) adati: “Chilango changa ndichifikitsa kwa yemwe ndamfuna (mwa anthu oipa); ndipo chifundo Changa chakwanira pa chilichonse (pa abwino ndi oipa). Choncho ndiwalembera (kuti mtendere umenewu udzakhale wawowawo pa tsiku lachimaliziro) amene akupewa (zoletsedwa) ndi kumapereka Zakaat, ndi kumakhulupirira zizindikiro Zathu;”
Ndipo mwa anthu a Mûsa, mudali gulu lomwe linkatsogolera anzawo ku choonadi. Ndipo ndi choonadicho ankachita chilungamo.
Ndipo pamene adauzidwa: “Khalani mu Mzinda uwu (Yerusalemu), ndipo idyani m’menemo paliponse pamene mwafuna, ndipo nenani (polowa mu mzindamo uku mutawerama): “Tifafanizireni machimo athu, (E Inu Mbuye wathu)!” Ndipo lowerani pa chipata (chake) modzichepetsa; tikukhululukirani zolakwa zanu ndipo tiwaonjezera zabwino ochita zabwino.
Tawafunsani nkhani ya mudzi umene udali m’mphepete mwa nyanja; (anthu am’mudziwo) pamene adali kuswa (lamulo la) tsiku la Sabata (lomwe adauzidwa kuti pa tsikuli asamachite usodzi wa nsomba, koma m’malo mwake azichita mapemphero okha). Nsomba zawo zinkawadzera yandayanda patsiku la Sabata, koma patsiku lomwe silidali la Sabata sizidali kuwabwerera (yandayanda). Motero tidawayesa mayeso chifukwa chakuchimwa kwawo.
Ndipo (akumbutse ) pamene gulu lina mwa iwo linkanena (kwa omwe amachenjeza amene adaswa kupatulika kwa tsiku la Sabata pamene adati): “Pali phindu lanji kuwachenjeza anthu omwe Allah awawononga kapena kuwalanga ndi chilango chaukali pompano pa dziko lapansi)? (Iwo) adati: “Kuti tidzakhale ndi chidandaulo kwa Mbuye wathu (ponena kuti tidawachenjeza koma sadatimvere) ndi kutinso mwina angaope (Allah nasiya kuswa lamulo Lake).”
Choncho, pamene sanalabadire zimene anauzidwa ndi kuchenjezedwa, tinawapulumutsa (anthu) omwe amaletsa zoipa, ndipo tidawakhaulitsa amene ankadzichitira okha zoipa ndi chilango choipa kwambiri chifukwa chakupandukila (kwawo) malamulo.
Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako analengeza (kuti) ndithu adzawatumizira iwo (Ayuda) anthu mpaka tsiku la Qiyâma, omwe adzawazunza ndi mazunzo oipa. Ndithu Mbuye wako ngofulumira kulanga, ndipo ndithu palibe chikaiko, Iye Ngokhululuka kwambiri, Ngwachifundo chambiri.
Ndipo tidawalekanitsa pakati pawo (Ayuda), ndi kuwabalalitsa pa dziko lonse kukhala mafuko osiyanasiyana. Ena mwa iwo abwino (olungama) ndipo ena sali choncho (oipa). Tinawayesa mayeso a zabwino ndi zoipa kuti abwelere (koma ayi, sanabwelere).
Choncho, anawatsatira pambuyo (anthu abwinowo), otsatira atsopano omwe analandira buku (la Allah nalowa mmalo mwa iwo koma popanda kulitsata ndi kulilingalira). Ankatenga zinthu zoletsedwa za pa dziko lapansi uku akunena: “Tidzakhululukidwa, (Allah adzatikhululukira).” Ngati zina zonga izo zitawapeza, amazitenganso. Kodi silidatengedwe pangano kwa iwo la m’buku kuti sadzamunenera Allah bodza koma zoona zokhazokha? (Nanga akuneneranji kuti Allah adzawakhululukira pomwe akupitiriza machimo)? Pomwe iwo aphunzira zomwe zili mmenemo. Komatu nyumba ya chimaliziro idzawakhalira bwino amene akuopa (Allah). Nanga bwanji simukuzindikira?
Ndipo amene akugwirisitsa buku (la Allah potsata zophunzitsa zake) ndi kumapemphera Swala, (tidzawalipira zabwino). Ndithu Ife sitipititsa pachabe malipiro a ochita zabwino.
Ndipo(akumbutse) pamene tidalizula phiri ndikulinyamula pamwamba pawo monga denga (kapena mtambo umene wawavindikira) natsimikiza kuti liwagwera, (tidawauza): “Landirani, mwamphamvu malamulo amene takupatsani, ndipo kumbukirani zomwe zili m’menemo (pozitsata ndi kuzichita); kuti inu muope.”
Ndipo (kumbukirani) pamene Mbuye wako adawatulutsa ana a Adam m’misana ya atate awo ndi kuwachititsa umboni okha (powauza kuti): “Kodi Ine sindine Mbuye wanu?” Iwo adati: “Inde tikuikira umboni (kuti Inuyo ndiye Mbuye wathu).” (Allah adawauza kuti): “Kuopera kuti mungadzanene tsiku louka kwa akufa: “Ife sitidali kuzindikira chipanganochi.”
Kapena mungadzati: “Makolo athu ndi amene adapembedza mafano kale, ndipo ife tidali ana odza pambuyo pawo (choncho tidawatsatira pazimene ankachita). Kodi nanga mutiononga chifukwa cha zomwe adachita oipa?”
M’menemo ndi momwe tikulongosolera mokwanira zivumbulutso kuti mwina iwo angabwelere (kwa Allah).
Amene Allah wamuongola ndiye woongoka. Ndipo amene wamulekelera kusokera (chifukwa chakusatsatira kwake malangizo a Allah), iwo ndiwo otaika (oonongeka).
Ndipo mwa amene tidawalenga, alipo anthu oongolera (anzawo) ku choonadi. Ndipo kupyolera mchoonadicho akuchita chilungamo.
Ndipo amene atsutsa zivumbulutso zathu, tiwalekelera pang’onopang’ono, kenako nkuwakhaulitsa kuchokera momwe iwo sakudziwa.
Ndipo ndiwapatsa kanthawi. Ndithu kukhaulitsa kwanga nkokhwima.
Nena: “Ine ndekha ndilibe mphamvu yodzibweretsera chabwino kapena kudzichotsera choipa, koma chimene Allah wafuna. Ndikadakhala kuti ndikudziwa za mseri, ndikadadzichulukitsira zabwino, ndipo choipa sichikadandikhudza. Ine sindili chilichonse koma mchenjezi ndi wouza anthu okhulupirira nkhani zabwino.”
Iye ndi Yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi, napanga mwa iye mkazi wake kuti adzikhala naye. Pamene adamkumbatira, adakhala ndi pakati popepuka nayenda napo (mosalemedwa). Koma pamene (pakatipo) padalemera (patangotsala pang’ono kuti abereke) anampempha Allah, Mbuye wawo (kuti): “Ngati mutipatsa mwana wabwino, ndithu tidzakhala mwa othokoza kwambiri.”
Choncho, pamene adawapatsa mwana wabwino (yemwe adapempha) adamchitira Allah anzake (mafano) pa chimene adawapatsacho. Koma Allah watukuka kuzimene akumphatikiza nazozo.
Kodi akumphatikiza (Allah) ndi zinthu zomwe sizilenga chilichonse pomwe izo zikulengedwa?
Ndipo sizingathe kuwathandiza ngakhale kudzithandiza zokha (podzibweretsera zabwino ndi kudzichotsera zoipa).
Ngati (milungu yamafanoyo) mutaiitanira ku chiongoko, siingakutsatireni (chifukwa chakuti siimva kapena kuzindikira chilichonse). Nchimodzimodzi kwa inu kuiitana kapena kukhala chete (palibe chimene ingadziwe).
“Ndithu Mtetezi wanga ndi Allah, Yemwe wavumbulutsa buku (ili lopatulika). Ndipo Iye amawateteza ochita zabwino.”
Koma anzawo (omwe ali oipa) amawalimbikitsa m’machimo, ndipo kenako saleka (kupitiriza machimowo).
Ngati siudawabweretsere chozizwitsa, akunena: “Bwanji wosachibweretsa pa iwe wekha? Nena: “Ndithudi ndikutsatira zimene zikuvumbulitsidwa kwa ine kuchokera kwa Mbuye wanga. (Sindichita chinthu mwa ine ndekha). Iyi (Qur’an) ndi umboni (waukulu pa zoyankhula zanga) kuchokera kwa Mbuye wanu. (Izo) ndi chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira.”
Share