۞ قَالَ ٱلْمَلَأُ ٱلَّذِينَ ٱسْتَكْبَرُوا۟ مِن قَوْمِهِۦ لَنُخْرِجَنَّكَ يَٰشُعَيْبُ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ مَعَكَ مِن قَرْيَتِنَآ أَوْ لَتَعُودُنَّ فِى مِلَّتِنَا ۚ قَالَ أَوَلَوْ كُنَّا كَٰرِهِينَ ﴿٨٨﴾
۞ Akuluakulu omwe adadzikuza mwa anthu ake, adanena: “Tikupirikitsa, iwe Shuaib m’mudzi mwathu muno ndi amene akhulupirira pamodzi nawe, pokhapokha mutabwerera ku chipembedzo chathu.” (Iye) adati: “Kodi ngakhale kuti tikuchida?”