Surah Al-A'raf (The Heights ) - Aya 57

Surah Al-A'raf (The Heights ) - Chewa - Aya 57 Aya count 206

وَهُوَ ٱلَّذِى يُرْسِلُ ٱلرِّيَٰحَ بُشْرًۢا بَيْنَ يَدَىْ رَحْمَتِهِۦ ۖ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَقَلَّتْ سَحَابًۭا ثِقَالًۭا سُقْنَٰهُ لِبَلَدٍۢ مَّيِّتٍۢ فَأَنزَلْنَا بِهِ ٱلْمَآءَ فَأَخْرَجْنَا بِهِۦ مِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِ ۚ كَذَٰلِكَ نُخْرِجُ ٱلْمَوْتَىٰ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ ﴿٥٧﴾
Ndipo Iye ndi Yemwe amatumiza mphepo kuti ikhale nkhani yosangalatsa patsogolo pa chifundo Chake (mvula), kufikira mphepoyo itasenza mitambo yolemera yomwe tikuitumiza ku dziko lakufa. Ndipo kupyolera mwa iyo tikutsitsa madzi ndipo ndimadzio tikutulutsa mitundu yonse ya zipatso. Momwemo ndimo tidzawaukitsira akufa. (Zonsezi) nkuti inu mukumbukire. [185]
Share