E inu anthu! Kumbukirani chisomo cha Allah chomwe chili pa inu (pomthokoza). Kodi alipo Mlengi wina osati Allah amene angakupatseni rizq kuchokera kumwamba ndi pansi? Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi, koma Iye. Nanga mukutembenuzidwira kuti?
E inu anthu! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ngakhale mdyerekezi uja wamkulu (Iblis), asakunyengeni pa za Allah.[339]
Amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake), pa iwo padzakhala chilango chaukali; koma amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, iwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu.
Ndipo Allah adakulengani ndi dothi; kenako ndi dontho la umuna; kenako adakupangani amuna ndi akazi. Ndipo mkazi aliyense satenga mimba ndiponso sabala koma kupyolera m’kudziwa Kwake (Allah). Ndipo amene wapatsidwa moyo, sapatsidwa moyo wautali ndiponso sachepetsedwa moyo wake, koma zonsezo zili m’buku (la Allah). Ndithu zimenezo kwa Allah nzosavuta.
Amalowetsa usiku mu usana, ndi kulowetsa usana mu usiku; dzuwa ndi mwezi adazichita kuti zigonjere (malamulo Ake). Zonse zikuyenda (usana ndi usiku) kufikira nthawi yake yodziwika. Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanu, Mwini ufumu. Ndipo amene mukuwapembedza, osati Iye, alibe ngakhale khoko la chipatso cha kanjedza.
E inu anthu! Inu ndiosaukira (chinthu chilichonse) kwa Allah; koma Allah Ngwachikwanekwane (sasaukira chilichonse kwa inu); Wotamandidwa (ndi zolengedwa zonse).
Ndipo amoyo ndi akufa safanana (amene mitima yawo ili ndi moyo pokhala ndi chikhulupiliro, ndi amene mitima yawo ili yakufa posakhala ndi chikhulupiliro, ngosafanana). Ndithu Allah akumumveretsa amene wam’funa; koma iwe sungathe kumumveretsa amene ali m’manda.
Ndithu Ife takutuma mwachoona kuti unene nkhani yabwino (yokalowa ku Munda wamtendere kwa amene akhulupirira), ndi kuti uchenjeze (za chilango cha Moto kwa amene sadakhulupirire). Ndipo palibe m’badwo uliwonse koma mchenjezi adapitamo.
Ndipo mwa anthu ndi nyama zokwawa, ndi ziweto, nchimodzimodzinso; nzosiyana maonekedwe ake (utoto wake). Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Allah mwa akapolo Ake. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri.
Ndithu amene akuwerenga buku la Allah uku nkumapemphera Swala moyenera napereka m’zimene tawapatsa mwanseri ndi moonetsera, iwo akuyembekezera malonda osaonongeka.
Kenako tidawapatsa buku (Qur’an) amene tidawasankha mwa akapolo Athu, koma alipo ena mwa iwo odzichitira okha chinyengo (pochulukitsa machimo), ena mwa iwo ngaapakatikati; ndipo ena mwa iwo ngopikisana pochita zabwino mwa chifuniro cha Allah. Kuteroko ndiwo ubwino waukulu.
Koma amene sadakhulupirire, wawo ndi moto wa Jahannam sikudzaweruzidwa kwa iwo kuti afe, ngakhale chilango chake sichidzachepetsedwa pa iwo. Umo ndimmene tikumlipirira aliyense wokanira (mtendere wa Allah).
Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala osiyirana pa dziko lapansi (akufa ena, ena nkulowa m’malo mwawo). Ndipo amene sadakhulupirire, kuipa kwa kusakhulupirirako kuli kwa iye mwini. Ndipo kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse kwa Mbuye wawo, koma mkwiyo basi. Ndiponso kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse, koma kutayika basi.
Nena: “Kodi mwawaona aphatikizi anu (awa) amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah? Tandionetsani, ndimbali iti ya nthaka adalenga; kapena iwo ali ndi gawo m’thambo; (gawo lakulenga thambo?) Kapena tidawapatsa buku (Qur’an iyi isadadze) kotero kuti ali ndi umboni wapoyera wochokera m’menemo (wotsimikizira chipembedzo chawo chamafano)? Koma ochita zoipa salonjezana ena kwa ena china chake koma zachinyengo basi.
Chifukwa cha kudzikweza pa dziko ndi kuchita chiwembu choipa. Ndipo chiwembu choipa sichingamuzinge aliyense koma mwini (yemwe) wachitayo. Kodi akuyembekeza china chosakhala machitidwe (a Allah) amene adawapititsa pa anthu akale. Koma supeza kusintha pa machitidwe a Allah. Ndipo supeza kutembenuka pa machitidwe a Allah.