Surah Al-Anbiya ( The Prophets )

Surah Al-Anbiya ( The Prophets ) - Chewa Aya count 112

Mitima yawo ikunyozera (osalabadira za kudza kwa Qiyâma). Ndipo akunenezana mobisa amene adzichitira zoipa; (akuuzana motere): “Kodi uyu (Muhammadiyu) ndi ndani, simunthu monga inu? Kodi mukuudzera ufiti pomwe mukuuona?”
(Mneneri Muhammad{s.a.w}) adati: “Mbuye wanga akudziwa zimene zikunenedwa kumwamba ndi pansi; ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa.
Koma (osakhulupirira) adati: “(Izi zimene akufotokozazi) ndi maloto opanda pake.” (Ndipo nthawi zina amati:) “Koma zimenezi wazipeka.” (Penanso amati:) “Koma iyeyu ndi mlakatuli. Chonchotu, atibweretsere chizizwa monga mmene adatumiziridwa (aneneri) oyamba.”
Sadakhulupirire apatsogolo pawo, eni midzi imene tidaiononga (ngakhale kuti zozizwitsa adaziona); nanga iwo akhulupirira?
Ndipo sitidawatume patsogolo pako, (iwe Mtumiki,) koma anthu, (osati angelo); tidawavumbulutsira (chivumbulutso Chathu.) Choncho, afunseni eni kudziwa ngati inu simukudziwa (nkhani zakale).
Kenako tidawatsimikizira lonjezo (la kuwathangata pa adani awo), ndipo tidawapulumutsa iwo ndi amene tidawafuna (mwa omwe adawatsata), ndipo olumpha malire (a Allah) Tidawaononga.
Ndithu tatumiza kwa inu buku lomwe m’kati mwake muli ulaliki wanu (malangizo kwa inu). Kodi simukuzindikira?
Kukuwa kwawoko sikudathe, kufikira tidawapanga ngati (mbewu) zokololedwa, mpaka kupuma kwawo kudazima (adafa).
Tikadafuna kupanga choti tiziseweretsa (sitidakapanga zomwe mukuzionazi) tikadapanga mwazomwe tili nazo, tikadakhala oti tichite (zachibwana).
Koma (chimene timachita ndi ichi), timachiponya choona pa chachabe ndi kuchiswa bongo bwake, ndipo chachabecho chimachoka. Ndipo chilango chili pa inu chifukwa cha zomwe mukunena (kumnamizira Allah).
Kapena adzipangira milungu yochokera m’nthaka youkitsa akufa, (kotero kuti aichita kukhala milungu yawo mmalo mwa Allah)?
Kukadakhala kuti ilipo m’menemo milungu ina (kuthambo ndi pansi) kupatula Allah, (ziwirizi) zikadawonongeka, wapatukana Allah Mbuye wa Arsh (Mpando Wachifumu) ndi zimene akunena (osakhulupirira).
Kapena adzipangira milungu ina m’malo mwa Iye? Nena: ‘“Bweretsani umboni wanu (pa zimenezi), (izi ndikuuzani) ndichikumbutso kwa awa ali pamodzi ndi ine, ndiponso ndichikumbutso kwa amene adalipo patsogolo panga.” Koma ambiri a iwo sadziwa za choonadi, tero iwo akunyozera.
Ndipo sitidatume patsogolo pako mtumiki aliyense koma tidali kumzindikiritsa kuti palibe mulungu wina wompembedza mwachoonadi, koma Ine; choncho ndilambireni.
Ndipo (osakhulupirira) akuti: “(Allah) Wachifundo chambiri wadzipangira mwana.” Allah wapatukana (ndi zimenezo) koma (awa angelo) ndi akapolo (a Allah) amene alemekezedwa.
(Allah) akudziwa zapatsogolo pawo (angelowo) ndi zapambuyo pawo, ndipo (angelowo) sangaombole (aliyense) koma yekhayo (Allah) wamuyanja, ndipo iwo, chifukwa chomuopa, amanjenjemera.
Ndipo thambo tidalipanga monga tsindwi losungidwa (kuti lisagwe). Koma iwo akuzitembenukira kumbali zizindikiro zake.
Ife sitidawachite anthu amene adalipo patsogolo pako kukhala okhala nthawi yaitali. Nanga ukafa, kodi iwo adzakhala okhala nthawi yaitali?
Munthu walengedwa ndi chikhalidwe chokonda zinthu (zake zonse) mwachangu. Posachedwapa ndikusonyezani zisonyezo Zanga; choncho musandifulumizitse (kukubweretserani chilango changa).
Ndipo (osakhulupirira) akuti: “Kodi malonjezo awa adzakwaniritsidwa liti, ngati mukunena zoona?”
Chikhala kuti amene sadakhulupirire akudziwa chilango chimene chidzawapeza panthawi yomwe sangathe kutchinjiriza Moto kunkhope zawo ndi kumisana yawo ndipo kuti sadzathandizidwa, (sakadanena zimenezi.)
Koma (Qiyâma) idzawadzera mwadzidzidzi ndi kuwadzidzimutsa; kenako sadzatha kuibweza kapena kupatsidwa danga (kuti achite zomwe sadachite.)
Kapena ali nayo milungu yowatchinjiriza m’malo mwa Ife? (Milunguyo) siingathe kudzithandiza yokha (nanga ndiye ingathe kuthandiza ena?) Ndipo (milungu) imeneyo siidzasamalidwa ndi Ife.
Ndipo kukadawakhudza kumenya kumodzi kwa chilango cha Mbuye wako, ndithudi, (akadadzichepetsa nthawi yomweyo). Akadanena: “Tsoka kwa ife ndithu tidali osalungama.”
Ndipo tsiku la Qiyâma tidzaika masikero achilungamo, choncho mzimu uliwonse sudzachitidwa chinyengo pa chilichonse. Ngakhale (chinthucho) chili cholemera ngati njere ya mpiru, tidzachibweretsa; ndipo tikukwana (kukhala akatswiri) pa chiwerengero.
Ndipo ndithu Mûsa ndi Harun tidawapatsa (buku) losiyanitsa pakati pa choonadi ndi chonama, ndiponso muuni ndi ulaliki kwa anthu oopa (Allah).
(Akumbutse anthu) pamene adauza bambo wake ndi anthu ake, “Nchiyani mafano awa omwe inu nthawi zonse mukupitiriza kuwapembedza.”
Adati: “Tidapeza makolo athu akuwapembedza. (Choncho nafenso Tikuwapembedza).”
(Iwo) adati: “Kodi watibweretsera choonadi, kapena iwe ndi m’modzi mwa osereula?”
(Iye) adati: (“Iyayi, ine siwosereula), koma Mbuye wanu, ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka amene adalenga zimenezi; ine pa zimenezi, ndine m’modzi wochitira umboni.”
“Ndipo ndikulumbilira Allah, ndiwachitira chiwembu mafano anuwo pambuyo ponditembenukira misana kupita komwe mukupita.”
Choncho adawaphwanya (mafanowo) zidutswazidutswa kupatula lalikulu lawo (sadaliswe) kuti iwo alibwelere (ndi kulifunsa zimene zachitika).
(Iwo parnene adafika kumafano awo) adati: “Ndani wachita ichi pa milungu yathu? Ndithu iye ndi m’modzi wa ochita zoipa.”
(Iye) adati: “(Iyayi), koma wachita ichi ndi mkulu wawoyu. Choncho afunseni (kuti akuuzeni zenizeni) ngati amatha kuyankhula.”
Kenako adazyolitsa mitu yawo (ndikubwerera kuumbuli wawo) nanena kuti: “Ndithu iwe ukudziwa kuti izi siziyankhula (nchifukwa ninji ukutichita chipongwe)?”
(Iye) adati: “Kodi mukupembedza zomwe sizingakuthandizeni chilichonse, kusiya Allah, zomwenso sizingakupatseni masautso?”
(Iwo) adati: “Mtentheni; ndipo pulumutsani milungu yanu, ngati inu mungathe kuchita zimenezi.”
Ndipo (akumbutse za) Daud ndi Sulaiman, pamene ankaweruza mlandu wa munda, pomwe mbuzi za anthu zidadya ndi kuonongaononga usiku mmenemo ndipo Ife tidali mboni pa kuweruza kwawo.
Tero tidamzindikiritsa za mlanduwo Sulaiman (kuposa tate wake Daud). Yense wa iwo tidampatsa kuweruza ndi kudziwa; ndipo tidagonjetsa mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Daud zikulemekeza (Allah); ndipo Ife ndi ochita chimene tafuna.
Ndipo tidamphunzitsa (Daud) kapangidwe ka chovala chapankhondo chifukwa cha inu kuti chikutetezeni mkumenyana kwanu; kodi simungakhale othokoza?
Ndipo (tidamugonjetseranso) asatana omwe ankamubilira m’madzi (ndikumtolera ngale), ndipo ankachita ntchito zina kuonjezera pa zimenezi; ndipo Ife tidali owasunga (owateteza).
Ndipo akumbutsenso za Ayubu pamene adakuwira Mbuye wake (kuti): “Ndithu mavuto andikhudza, pomwe Inu ndi Achifundo kuposa achifundo!”
Choncho tidavomera (pempho lake); ndipo tidamchotsera mavuto omwe adali nawo, ndipo tidampatsa ana ake ofanana ndi omwe adali nawo kale ndikuonjezeranso ena onga iwo, (zonsezi monga) chifundo chochokera kwa Ife, (ndikuti zikhale) chikumbutso kwa ochita mapemphero.
Ndipo (mtchulenso) Thun-Nun (Yunusu), pamene adachoka uku atakwiya, ndipo ankaganiza (kuti tamuloleza kusamuka) ndikuti sititha kumchita kanthu. Choncho adaitana mu mdima (mammimba mwa nsomba imene idamumeza, kuti): “Ndithu palibe mulungu wina wopembezedwa mwachoonadi koma Inu; mwayeretsedwa; ndithu ine ndidali m’modzi wa odzichitira zoipa.”
Ndipo (akumbutse za) Zakariya pamene adaitana Mbuye wake (kuti): “Mbuye wanga! Musandisiye ndekha; ndithu Inu ndinu wabwino kuposa alowa mmalo onse.”
Ndipo (atchulire za Mariya) yemwe adauteteza umaliseche wake (podzisunga); ndipo tidauzira mwa iye Mzimu Wathu, ndipo tidamchita iye ndi mwana wake kukhala chizizwa (cha Allah) kwa zolengedwa zonse.
Koma iwo adaswa chinthu chawochi pakati pawo (tero adakhala mipingo yosiyanasiyana). Onse adzabwerera kwa Ife.
Ndipo nkosatheka kwa eni mudzi umene tidauononga chifukwa cha machimo awo kuti asabwelere kwa Ife; (koma ndithu abwerera).
Kufikira pamene Yaajuju ndi Maajuju adzatsekulilidwa (mpanda wawo), ndipo iwo adzakhala akuthamanga kuchokera m’phiri lililonse.
Ndipo lonjezo la choonadi lidzafika; pamenepo maso a omwe sadakhulupirire, adzatong’oka uku akunena: “Tsoka pa ife! Ndithu tidali osalabadira (za chinthu) ichi; koma tidali oipa, (odzichitira tokha zoipa.)”
Mmenemo iwo adzakhala akubuula ndipo iwo mmenemo sadzamva (chifukwa makutu adzagontha).
(Kumbukirani) tsiku lomwe tidzakulunga thambo monga momwe amakulungira makalata okhala ndi malembo m’kati mwake; monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso (kuzilenga kachiwiri. Ndipo aliyense adzalipidwa pa zomwe adali kuchita) ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife. Ndithu Ife ndi Ochita (zomwe tikunena.)
Ndipo ndithu tidalemba m’zaburi (mu Masalimo buku la Daud) pambuyo polemba mu chikumbutso (Lauhil-Mahafudh) kuti: “Dziko (lapansi) adzalilowa akapolo Anga abwino.”
Ndithu pazimenezi (nkhani za aneneri), pali miyambo kwa anthu, opembedza (Allah).
Nena: “Ndithu kukuvumbulutsidwa kwa ine kuti mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; nanga inu mudzagonjera (zofuna Zake polowa m’Chisilamu)?”
Koma ngati anyozera, nena: “Ndalengeza (uthenga) kwa inu mofanana (popanda tsankho); sindidziwa kuti zomwe mukulonjezedwa zili pafupi kapena zili kutali.”
“Ndipo sindikudziwa, mwina kuchedwetsa chilango chanu ndi mayeso akukuyesani ndikukusangalatsani ndi zokoma (za m’dziko) mpaka Idzakwane nthawi yoikidwayo.”
Adati: “E Mbuye wanga! Weruzani moona.” “Ndipo Mbuye wathu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukusimbazo.”
Share