Surah Abasa ( He frowned )

Surah Abasa ( He frowned ) - Chewa Aya count 42

Adachita tsinya (Mneneri) ndi kuyang’ana kumbali.[384]
Chifukwa chakuti adamdzera wakhungu (kudzamfunsa zokhudzana ndi chipembedzo chake pamene iye adali kuyankhula ndi atsogoleri Achiquraishi).
Nanga chingakudziwitse nchiyani kuti mwina iye angadziyeretse (pomvera ulaliki wako watsopano)?
Koma amene wadzikwaniritsa (ndi chuma chake ndi mphamvu zake),
Ameneyo ndi yemwe ukumchitira chidwi.
Koma amene wakudzera uku akuthamanga (kufuna maphunziro ndi chiongoko),
Ndipo iye akuopa (Allah mu mtima mwake).
Za iye, iwe sukusamala, (ukuyikira chidwi kwa wina).
Sichoncho! Ndithudi iyi (Qur’an) ndi chikumbutso (chenjezo).[385]
Basi, amene wafuna alangizika (ndi Qur’an, ndipo amene sakufuna msiye).
(Malangizowa akuchokera) mmakalata olemekezeka (kwa Allah);
Apamwamba ndiponso oyeretsedwa (kumbiri iliyonse yopunguka);
Omwe ali m’manja mwa Alembi (Angelo).
Waonongeka (watembeleredwa) munthu. Nkotani kusayamika kwake kotereku.
Kuchokera mchinthu chanji chimene iye adamulenga.
Kuchokera ku dontho lamadzi (onyozeka) adamulenga, namkonzeratu mkalengedwe kosiyanasiyana.
Kenako adamfewetsera njira (yotulukira m’mimba mwa mai ake).
Ndipo amamchititsa kuti amwalire namukumbula m’manda,
Kenako akadzafuna adzamuukitsa (pambuyo pa imfa).
Ayi ndithu (munthu) sanakwaniritsebe zimene adamulamula Mbuye wake (Allah chingakhale wakhala nthawi yaitali pa dziko lapansi).
Ndithu Ife timagwetsa mvula yambiri (kuchokera ku mitambo).
Ndipo timameretsa m’menemo njere (ya chakudya cha anthu ndi zina zimene amasunga mnkhokwe),
Ndi mzitona (wabwino) ndi (zipatso za) kanjedza,
Ndi minda yothothana nthambi za mitengo,
Ndi zipatso (zodyedwa ndi anthu) ndi msipu (wodyedwa ndi nyama);
(Tazimeretsa zimenezo kuti) zikondweretse inu ndi ziweto zanu.
Choncho likadzafika lipenga logonthetsa mkhutu (ndi kuumitsa makosi).
Munthu aliyense mwa iwo, tsiku limenelo adzakhala ndi zakezake zotangwanika nazo. (Sadzalabadira za anzake).
Tsiku limenelo nkhope zina zidzakhala zowala;[387]
Zosekelera ndi zachimwemwe (chifukwa cha nkhani yabwino ya ku Munda wamtendere.)
Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zokutidwa ndi fumbi.
Share