Akukufunsa za chuma cholandidwa pa nkhondo (mmene chingagawidwire). Nena: “Chuma cholanda pa nkhondo ndi cha Allah ndi Mtumiki (ndiamene ali olamula kagawidwe kake); choncho, muopeni Allah ndipo yanjanani mwachibale pakati panu. Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ngati mulidi okhulupirira.”[189]
Ndithu okhulupirira, enieni ndi amene akuti Allah akatchulidwa mitima yawo imadzadzidwa ndi mantha; pamenenso Ayah Zake zikuwerengedwa kwa iwo zimawaonjezera chikhulupiliro, ndipo amayadzamira kwa Mbuye wawo Yekha basi; (sakhulupirira nyanga ndi mizimu ya anthu akufa).[190]
Awa (okhala ndi makhalidwe otere) ndi amene ali okhulupirira mwachoonadi. Iwo adzapeza ulemelero (wapamwamba) kwa Mbuye wawo, ndi chikhululuko ndi zopatsidwa zaulemu.
(Kumbukirani, E inu okhulupirira!) Pamene Allah anakulonjezani gulu limodzi mwa magulu awiri kuti likhale lanu (kuti mumenyane nalo). Koma inu mukufuna lopanda mphamvu kuti likhale lanu (kuti ndilo mumenyane nalo). Koma Allah akufuna kuchitsimikiza choonadi ndi mawu Ake ndi kudula mizu ya osakhulupirira, (pomenyana ndi gulu lamphamvulo, omwe ndi ankhondo a Chikuraishi).
Ndipo Allah sadachite ichi koma kuti chikhale nkhani yabwino (yosangalatsa), ndi kuti mitima yanu ikhazikike ndi chimenecho. Ndipo palibe chipulumutso (chothandiza) koma chimene chachokera kwa Allah. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.[192]
Izi ndi chifukwa chakuti iwo anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki wake (iwo podziika mbali ina kusiya komwe kudali Allah). Amene anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Allah ndi wolanga kwambiri (amalanga ndi chilango choopsa).
Ndipo amene adzawatembenuzire msana kuthawa pa tsikulo - osati kutembenuka (kwa ndale) kofuna kumenyana kapena kukalowa m’gulu (la Asilamu ena) - ndiye kuti adziitanira mkwiyo wochokera kwa Allah; ndipo malo ake ndi ku Jahannam, kumeneko ndi ku malo koipa kubwererapo.
Inu simudawaphe (ndi mphamvu zanu) koma Allah ndi Yemwe anawapha; siudawagende pamene udagenda koma Allah ndi amene anawagenda (pofikitsa mchenga m’maso mwawo, wachita zimenezi) kuti awachitire zabwino Asilamu powapatsa dalitso labwino lochokera kwa Iye. Ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[193]
E inu amene mwakhulupirira muvomereni Allah (pa zimene akukulamulani) ndiponso muvomereni Mtumiki Wake pamene akukuitanirani ku chimene chingakupatseni moyo (wabwino wa pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro). Ndipo dziwani kuti Allah amatchinga pakati pa munthu ndi mtima wake (amautembenula mmene akufunira). Ndipo dziwani kuti kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.[195]
Ndipo muope mazunzo (a Allah a pano pa dziko lapansi) omwe sangagwere okhawo amene adzichitira zoipa mwa inu (koma adzawagweranso amene akusiya kuletsa zoipa) ndipo dziwani kuti Allah Ngolanga kwambiri.[196]
Ndipo dziwani kuti chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (oyesedwa ndi Allah kuti aone mmene mungagwiritsire nazo ntchito). Ndi kuti kwa Allah kuli malipiro aakulu.
E inu amene mwakhulupirira! Ngati muopa Allah, adzakupatsani chilekanitso (cholekanitsa pakati pa choonadi ndi chachabe), ndiponso akufafanizirani zoipa zanu ndi kukukhululukirani. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino waukulu.[198]
Kuti Allah alekanitse oipa ndi abwino, ndi kuti awayike ena mwa oipawo pamwamba pa anzawo, potero nkuwaunjika oipawo mulu umodzi, kenako nawaponya ku Jahannam. Iwowa ndi anthu otaika.
Nena kwa osakhulupirira kuti: “Ngati asiya (zochita zawo zoipa), adzakhululukidwa zimene zidatsogola. Koma ngati abwereza (kuwazunza Asilamu, tiwalanga) ndithudi njira ya Allah yomwe idachitika kwa anthu akale inadutsa (powalanga akasiya kutsata malamulo a Allah).
۞ Ndipo dziwani kuti chilichonse chimene mwapeza monga chuma cholanda ku nkhondo, gawo limodzi mwa magawo asanu ndi cha Allah ndi Mtumiki, ndi a chibale (a Mtumiki), amasiye, masikini ndi munthu wa pa ulendo (amene asowedwa choyendera pa ulendo. Tsatilani malamulowa) ngatidi mwakhulupirira Allah ndi chimene tachivumbulutsa kwa kapolo Wathu pa tsiku lachilekanitso (lolekanitsa pakati pa choona ndi chabodza), tsiku limene magulu awiri adakumana (tsiku la nkhondo ya Badr, gulu la nkhondo la Asilamu ndi gulu la nkhondo la osakhulupirira). Ndipo Allah Ngokhoza kuchita chilichonse.
(Kumbukirani) pamene mudali mbali ya chigwa yoyandikira (mzinda wa Madina) pomwe iwo (ankhondo a Chikuraishi) adali mbali ya kutali ya tsidya lina (la chigwacho) pomwe aulendo amalonda adali cha kumunsi kwanu. Ngati mukadapangana nthawi yokumanirana (kuti mukumane nthawi yakutiyakuti), mukadasiyana posunga chipangano (chifukwa cha kuopa kuchuluka kwa adani anuwo). Koma (mwakumana mosayembekezera ndi ankhondo a adaniwo) kuti Allah akwaniritse chinthu chomwe nchofunika kuti chichitike, kuti awonongeke amene waonongeka (posankha kusakhulupirira) ndi umboni woonekera (umene adaukana kuutsata), ndi kuti akhale ndi moyo amene wakhala ndi moyo (amene watsata njira ya Chisilamu) ndi umboninso woonekera. Ndithudi Allah Ngwakumva zonse, Ngodziwa kwambiri.[202]
Ndipo mumvereni Allah ndi Mtumiki Wake, musakangane (kuopera kuti) mungakhale olephera (ndi kutaya mtima), ndikuchoka mphamvu zanu. Koma pitirizani kupirira. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi anthu opirira.
Ndipo musakhale ngati anthu amene anatuluka m’nyumba zawo modzikweza ndi modzionetsera kwa anthu, ndikuwasekereza anthu kuyenda pa njira ya Allah. Koma Allah ndi Wodziwa kwambiri zimene akuchita.
(Kumbukirani) pamene achiphamaso ndi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo amanena: “Anthu awa chipembedzo chawo (cha Chisilamu) chawanyenga.” Komatu amene akuyadzamira kwa Allah ndithudi Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
(Khalidwe lawo awa lili ) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi omwe adalipo patsogolo pawo. Anazikana zizindikiro za Allah, choncho Allah anawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndithudi Allah Ngwamphamvu, Wolanga moopsa.
Ndipo akonzekereni mmene mungathere ndi mphamvu zanu (zonse zomenyera nkhondo), ndiponso poikiratu mahatchi odikira nkhondo kuti muwaopseze nazo adani a Allah ndi adani anu (amene mukuwadziwa) ndiponso (ndi) ena omwe (inu) simukuwadziwa. Koma Allah akuwadziwa. Ndipo chilichonse mungapereke pa njira ya Allah chidzalipidwa kwa inu modzadza ndipo simuzaponderezedwa.
Ngati afuna kukunyenga pa chimvanochi, ndithudi, Allah akukwanira kwa iwe (kukuteteza). Iye ndi Yemwe anakuthangata ndi chipulumutso chake ndi okhulupirira.
Ndipo (Allah) analuzanitsa pakati pa mitima yawo (poika chikondi pakati pawo). Ngati ukanapereka zonse za m’dziko lapansi (ncholinga choti uwaluzanitse mitima yawo mwa iwe wekha) sukadatha kuluzanitsa pakati pa mitima yawo. Koma Allah adaluzanitsa pakati pawo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
Sichoyenera kwa Mneneri kukhala ndi akayidi mpaka amenye nkhondo (kwambiri) ndi kugonjetseratu maiko molimba (ndi pamene atha kukhala ndi akayidi). Mukufuna zinthu za m’dziko pomwe Allah akufuna (mupeze mphoto ya) tsiku lachimaliziro! Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
Pakadapanda lamulo la Allah limene linatsogolera kale (lokulolezani chuma chopeza ku nkhondo), chilango chachikulu chikanakugwerani, chifukwa cha zimene munatenga (ku-nkhondo ya Badri).
E iwe Mneneri! Uza akaidi a pankhondo amene ali m’manja mwanu kuti ngati Allah aona chabwino chilichonse m’mitima mwanu, adzakupatsani zoposa zimene mwalandidwa ndipo adzakukhululukirani; Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
Ndithu anthu amene anakhulupirira nasamuka kwawo ndi kumenyana pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi moyo wawo; ndiponso amene anawalandira (iwo) ndi kuwapatsa malo ndi kuwathandiza, awa ndiabale otchinjirizana wina ndi mnzake. Ndipo anthu amene akhulupirira koma nasiya kusamuka (kudza ku Madina), palibe udindo pa inu wa kuwateteza kufikira nawonso atasamuka (kudza ku Madina). Ngati atakupemphani chithandizo cha chipembedzo athandizeni, kupatula (akaputana ndi anthu) amene pakati panu ndi iwo pali chipangano, (pamenepo musawathandize pomenyana ndi osakhulupirirawo omwe muli nawo chipangano). Ndipo Allah Ngowoona zomwe muchita.
Amene akhulupirira nasamuka, namenya nkhondo panjira ya Allah (pamodzi nanu), ndiponso amene anawalandira (osamukawo), nawapatsa malo ndi kuwathandiza, iwo ndi omwe ali okhulupirira mwa choonadi. Iwo adzapeza chikhululuko ndi zopatsidwa za ulemu.
Ndipo aja akhulupirira pambuyo (pa Amuhajirina ndi Answari), nawonso nasamukira (ku Madina kukakhala pamodzi ndi Mtumiki ndi Asilamu anzawo), namenyanso nkhondo pamodzi nanu, iwo ndi amene ali mwa inu. Koma achibale chakubadwana, ndiamene ali oyenera (kulowerana mmalo pa chuma) ena ndi ena, mmene zilili) m’buku la Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse.