Surah Al-Waqi'ah ( The Event )

Surah Al-Waqi'ah ( The Event ) - Chewa Aya count 96

Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino).
Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu).
Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro).
(Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale.
Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide,
Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi).
Anyamata osasintha adzakhala akuwazungulira iwo (ndi kuwatumikira).
Uku atatenga matambula ndi maketulo (odzaza ndi zakumwa za ku Jannah), ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa zochokera mu akasupe oyenda;
Ndi akazi ophanuka maso mokongola,
(Kukongola kwawo) ndiye ngati ngale zosungidwa bwino mzigoba zake.
Kukhala mphoto chifukwa cha zimene amachita (zabwino padziko lapansi).
Anthu akudzanja lamanja. Taonani kukula malipiro a anthu akudzanja lamanja!
(Adzakhala m’mithunzi ya) mitengo ya masawu yopanda minga.
Ndi mitengo ya nthochi yobereka kwambiri.
Ndi m’mithunzi yotambasuka kwambiri, yosachoka,
Zopezeka mnyengo zonse, ndiponso zosaletsedwa (kwa amene akuzifuna).
Ndithu tidzawalenga (akazi okhulupirira) m’kalengedwe kapamwamba.
Okondedwa ndi amuna awo; ofanana misinkhu,
Gulu lalikulu lochokera ku m’badwo woyamba.
Ndiponso gulu lalikulu lochokera ku mibadwo yotsiriza.
Anthu akudzanja lakumanzere. Taonani chilango choopsa kwa anthu akudzanja lakumanzere!
Adzakhala mu mvuchi wamoto ndi m’madzi owira.
Ndithu iwo amakhala kalelo mosangalala (samalabadira kumvera Allah),
Ndipo amapitiriza kuchita machimo aakulu (polinga kuti palibe kuuka ku imfa).
“Kodi ndi makolo athu akale (adzaukitsidwanso!)”
Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo). Ndithudi, amibadwo yoyamba ndi mibadwo yomaliza (omwe inu muli m’gulu lawo),
Mudzadya (ku Jahannam) mtengo wa Zakkum, (mtengo wowawa wopezeka mu Jahannam).
Mudzakhutitsa mimba zanu ndi umenewu (chifukwa cha njala yadzaoneni).
Adzamwa monga mmene imamwera ngamira yodwala matenda aludzu!
Tandiuzani za madzi (ambewu ya munthu) amene mumawathira m’chiberekero,
Kodi inu ndiamene mumawalenga (madziwo ndi kumayang’anira mkusinthasintha kwake kuti akhale cholengedwa) kapena Ife ndiamene timawalenga?
Tikadafuna tikadazitembenuza (mbewu zimenezo kukhala zouma isanakwane nthawi yake yozithyola) choncho mukadakhala mukudandaula.
(Uku mukunena:) “Ndithu ife tangotaya chuma chathu (padera);”
“Koma ife tamanidwa (phindu la khama lathu).”
Ife taupanga kuti ukhale chikumbutso (cha Moto watsiku lachimaliziro akauona), ndikuti ukhale chothandiza kwa anthu apaulendo (amene akuyenda m’chipululu).
Choncho, pitiriza kulemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.
Ndikulumbilira motsimikiza, mmene mumatsikira nyenyezi (pomwe zikulowa).
Ndithu kulumbira uku, mukadakhala olingalira, nkwakukulu kwabasi (pazimene kukusonya).
Ndithu iyi ndi Qur’an yolemekezeka (ndipo mkati mwake muli zithandizo zambiri).
Chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.
Kodi mwakuchita kukanira kukhala kuthokoza kwanu pa zimene wakupatsani?
Mmaona bwanji (mzimu wa mmodzi wa inu) ukafika kummero (panthawi ya imfa).
Ngati (amene yamfikira imfayo) adali mmodzi wa woyandikitsidwa (kwa Allah;)
Kobwerera kwake ndi kumpumulo ndi mtendere ndi kupatsidwa zonunkhira ndiponso Munda wamtendere.
(Kudzanenedwa kwa iye:) “Mtendere ukhale pa iwe, amene udali m’gulu la anthu akudzanja lakumanja (anthu abwino).”
Share