Surah Adh-Dhariyat ( The Wind that Scatter )

Surah Adh-Dhariyat ( The Wind that Scatter ) - Chewa Aya count 60

. Ndikulumbilira mphepo imene ikubalalitsa mitambo ya mvula.
Ndi imene imasenza mitolo yolemera (ya madzi).
Ndi awo amene amagawa rizq (limene Allah amalipereka kwa amene wamfuna).
Ndithu zimene mukulonjezedwa nzoonadi, (zidzachitika).
Ndipo, ndithu malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi.
Ndikulumbilira thambo lomwe njira zake zambiri nzoikidwa mwaluso.
Ndithu inu muli m’mau otsutsana, (pa zimene mukunena).
(Kupyolera m’mawu amenewa) akuchotsedwa ku icho (chikhulupiliro chalonjezo loona) amene adachotsedwa (ku chikhulupilirocho).
Aonongeka abodza (amene akunena za tsiku lachiweruziro mongoganizira.)
Iwo amene akubira mu umbuli, osalabadira (za tsiku lachimaliziro).
Akufunsa (mwachipongwe ponena kuti) “Lidzakhala liti tsiku lamalipiro?”
(Adzawauza kuti): “Lawani chilango chanu ichi chimene munkachifulumizitsa (kuti chikufikeni).”
Ndithu oopa (Allah) adzakhala (akusangalala) m’minda ndi mu akasupe okongola,
Nthawi yausiku amagona pang’ono. (Amadzuka nachita mapemphero mochulukitsa).
Ndipo m’chuma chawo mudali gawo (lodziwika) la opempha ndi osapempha (mwa osauka).
M’nthaka muli zizindikiro kwa otsimikiza, (zosonyeza kuti Allah alipo).
Ndipo kumwamba kuli zokuthandizani (pa moyo wanu), ndi zimene mukulonjezedwa.
Pamene adalowa kwa iye ndi kunena kuti: “Salaam,” (“Mtendere”)! Iye adayankha: “Salaam,” (“Mtendere) inu ndinu anthu osadziwika (achilendo).”
Adatembenukira kwa akunyumba ake (mwakachetechete), ndipo adadza ndi nyama ya mwana wa ng’ombe yonona (yowotcha).
Naipereka kwa iwo (koma sadadye); iye adanena (modabwa): “Kodi bwanji simukudya?”
Mumtima mwake adadzazidwa mantha ndi iwo. Iwo adati: “Usaope,” ndipo adamuuza nkhani yabwino ya kubala mwana wodziwa.
Adadza mkazi wake ndi mkuwe (pamene adamva nkhani yabwino ija). Adadzimenya kunkhope (ndi dzanja lake kusonyeza kudabwa ndi kusatheka). Ndipo adati: (“Ine ndine) nkhalamba (ndiponso) chumba; (ndingabereke bwanji)?”
Iwo adati: “Momwemo, Mbuye wako wanena. Iye Ngwanzeru zakuya (pa chilichonse chimene akulamula); Ngodziwa; (palibe chimene chingabisike kwa Iye).
۞ (Ibrahim) adati: “Kodi nkhani yanu ndiyotani E inu otumidwa?”
“Yoikidwa chizindikiro cha aliyense wochimwa kuchokera kwa Mbuye wako.”
Ndipo tidasiya pamenepo chizindikiro (chosonyeza kuonongeka kwa eni mudziwo kuti chikhale lingaliro) kwa amene akuopa chilango chopweteka.
M’nkhani ya Mûsa (muli phunziro) pamene tidamtuma kwa Farawo uku atalimbikitsidwa ndi chisonyezo choonekera.
Koma Farawo adanyoza (kukhulupirira Mûsa) chifukwa chotama nyonga zake, ndipo adati: “Uyu ndi wamatsenga kapena wamisala.”
Ndipo m’nkhani ya Âdi (muli phunziro) pamene tidawatumizira chimphepo (chamkuntho) chopanda chabwino mkati mwake.
Ndipo m’nkhani ya Samudu (muli chisonyezo) pamene kudanenedwa kwa iwo kuti: “Sangalalani (mnyumba zanu) mpaka nthawi yaikika.”
Naonso anthu a Nuh (tidawaononga) kale chifukwa iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah).
Thambo tidalimanga mwamphamvu (ndi luntha); ndipo tingathe kuchita zochuluka (kuposa zimenezi.)
Ndipo nthaka tidaiyala; taonani kukonza bwino Ife amene tidakonza nthaka!
Ndipo m’chinthu chilichonse talenga ziwiriziwiri kuti inu mulingalire (ndi kukhulupirira mphamvu Zathu).
Ndipo musadzipangire mulungu wina wompembedza ndi kumuphatikiza ndi Allah. Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera poyera kwa inu wochokera kwa Iye.
Momwemo (ndimo idalili mibadwo yakale pamodzi ndi aneneri awo); palibe Mthenga amene adawadzera anthu akale, anthu akowa kulibe, popanda kumnena kuti: “Ndiwamatsenga kapena wamisala.”
Kodi adalangizana za mawuwa pakati pawo? Iyayi, koma iwo ndianthu opyola malire.
Choncho apatukire iwo (amakani), iwe suli wodzudzulidwa (pakuleka kwawo kuyankha kuitana).
Ndithu Allah ndi Amene amapereka rizq; Iye ndi Mwini mphamvu zoposa; Wolimba, (salaphera kanthu).
Ndithu amene adzichitira okha chinyengo (pokana ndi kutsutsa) ali nalo gawo la chilango monga gawo la anzawo (a mibadwo yakale); choncho asandifulumizitse (kutsitsa chilango nthawi yake isanafike)!
Share