Surah Ibrahim ( Abraham )

Surah Ibrahim ( Abraham ) - Chewa Aya count 52

Alif-Lâm-Ra. (Ili ndi) buku lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti uwatulutse anthu mu mdima ndi kuwaika mkuunika - mwalamulo la Mbuye wawo - uwapititse kunjira ya Mwini mphamvu zoposa, Woyamikidwa.
Amene akukondetsa moyo wadziko lapansi kuposa moyo wa pambuyo pa imfa, ndipo amatsekereza (anthu) ku njira ya Allah ndikufuna kuikhotetsa (pomwe njirayo njosakhota). Iwo ali mkusokera kotalikana kwambiri (ndi choonadi).
Ndipo sitidamtume mtumiki aliyense koma ndi chiyankhulo cha anthu ake kuti awafotokozere. Kenako Allah akumsiya kusokera amene wamfuna (chifukwa mwini wake safuna kuongoka). Ndipo amamuongolera yemwe wamfuna, ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Ndipo ndithu tidamtumiza Mûsa ndi zozizwitsa Zathu (tidamuuza): “Achotse anthu ako mu mdima (wa umbuli) ndi kuwaika mkuunika (kwa chikhulupiliro) ndipo uwakumbutse masiku a Allah (a masautso).” Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa yense wopirira, wothokoza.
Ndipo (akumbutse anthu ako) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu pamene adakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe adakuzunzani ndi chilango choipa. Ankazinga (kupha) ana anu aamuna ndi kuwasiya amoyo ana anu aakazi; ndithu m’zimenezi mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu.”
Ndipo (kumbukani) pamene Mbuye wanu adalengeza kuti: “Ngati muthokoza, ndikuonjezerani; ndipo ngati simuthokoza (dziwani kuti) chilango changa nchaukali.”
Ndipo Mûsa adati (kwa anthu ake): “Ngati inu mukana (pakusiya kuthokoza) pamodzi ndi onse a m’dziko, (Allah salabadira chilichonse pa zimenezo), ndithudi Allah Ngwachikwanekwane; Ngotamandidwa.”
Atumiki awo adati: “Kodi mwa Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka muli chikaiko? Iye akukuitanani kuti akukhululukireni machimo anu, ndi kuti (mukakhulupirira) akupatseni nthawi (pokutalikitsirani moyo wanu) kufikira pa nthawi yoyikidwa.” Adati: “Inu sikanthu kena koma ndinu anthu ngati ife. Mungofuna kutitsekereza ku zimene ankazipembedza makolo athu; choncho tibweretsereni umboni woonekera.”
Ndipo amene sadakhulupirire, adanena kwa atumiki awo: “Ndithu tikutulutsani m’dziko lathu, pokhapokha mubwelere m’chipembedzo chathu.” Koma Mbuye wawo (Allah) adawavumbulutsira uthenga (wakuti): “Ndithu tiwaononga ochita zoipa (osakhulupirira).”
“Ndipo tikukhazikani (inu) pambuyo pawo m’dzikomo. Apeza zimenezi omwe aopa kuimilira pamaso pa Ine, ndi kuopa chilango Chnga.”
Ndipo (atumikio) adapempha chithandizo (kwa Allah), ndipo adaonongeka aliyense wodzikuza, wamakani.
(Yemwe) kutsogolo kwake Jahannam ikumdikira, ndipo (kumeneko) adzamumwetsa madzi amafinya (otuluka m’matupi a anthu a ku Moto).
Fanizo la amene sadakhulupirire Mbuye wawo, zochita zawo (zabwino zomwe sadzalipidwa nazo chabwino chilichonse chifukwa chakuti sadazichite pofuna kukondweretsa Allah) zili ngati phulusa lomwe likuulutsidwa ndi mphepo ya mkuntho; ndipo sadzatha kupindula chilichonse pa zimene adachita, uko ndikutaika konka nako kutali (ndi choonadi).
Ndipo onse (adzatuluka m’manda mwawo ndiponso) akaonekera kwa Allah (kuti awalipire). Pamenepo ofooka (omwe adasokera chifukwa chotsatira atsogoleri awo) adzanena kwa omwe ankadzikuza: “Ndithu ife tidali kukutsatirani inu; kodi inu simungathe kutichotsera kanthu kochepa m’chilango cha Allah chi?” (Atsogoleri) adzati: “Allah akadationgolera, tikadakuongolerani; (koma tsopano) ndi chimodzimodzi kwa ife titekeseke ndi chilangochi, kapena tipirire nacho; tilibe pothawira.”
Ndipo satana adzanena chiweruzo chikadzalamulidwa (oipa kulowa ku Moto, abwino kulowa ku Munda wamtendere): “Ndithu Allah adakulonjezani lonjezo loona (ndipo wakwaniritsa). Nane ndidakulonjezani, koma sindidakukwaniritsireni. Ndidalibe mphamvu pa inu (yokukakamizirani kunditsata) koma ndimangokuitanani basi, ndipo munkandiyankha. Choncho musandidzudzule, koma dzidzudzuleni nokha. Sindingathe kukuthangatani ndiponso inu simungathe kundithangata. Ndithu ine ndidakukana kundiphatikiza kwanu ndi Allah kale. Ndithu ochita zoipa adzapeza chilango chowawa.”[242]
Ndipo amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, adzalowetsedwa ku Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda, adzakhala m’menemo nthawi yaitali mwachilolezo cha Mbuye wawo. Kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala: “Mtendere!”
Umapereka zipatso zake nthawi iliyonse mwachifuniro cha Mbuye wake. (Umo ndi momwe liwu labwino lilili, limabwera ndi zabwino). Ndipo Allah amaponyera anthu mafanizo kuti akumbukire.
(Yomwe ndi) Jahannam; adzailowa; taonani kuipa malo okhazikikapo!
Ndipo wakupatsani mu zonse zomwe mwampempha (ndi zimene simudam’pemphe). Ngati mutayesa kuwerenga madalitso a Allah, simungathe kuwawerenga. Ndithu munthu ngwachinyengo chachikulu, ngosathokoza.
Ndipo (kumbukani) pamene Ibrahim adanena: “Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa mtendere; ndipo ndipatuleni ine ndi ana anga ku machitidwe opembedza mafano.”
“Mbuye wanga! Ndithu (mafano) awa asokeretsa anthu ambiri. Choncho amene wanditsata, ndithu iyeyo ali mwa ine (mudzamulipira chabwino monga mwandilonjeza), ndipo amene wandinyoza (mutha kumukhululukira) ndithu Inu Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni.”
“Mbuye wanga! Ndithu ine ndaikhazika ina mwa mbumba yanga (mwana wanga Ismail) pachigwa ichi (cha Makka) chopanda zomera pa Nyumba Yanu Yopatulika (Al-Ka’ba); Mbuye wathu (aloleni) kuti akhale opemphera Swala; choncho ichiteni mitima ya anthu kukhala yopendekera kwa iwo (akonde kudzakhala malo amenewo), ndipo apatseni zipatso kuti athokoze.”
“Mbuye wanga! Ndichiteni kukhala wopemphera Swala pamodzi ndi mbumba yanga. Mbuye wathu! Landirani zopempha zanga.”
“Mbuye wathu! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi amene akhulupirira, (makamaka) patsiku la chiwerengero (Qiyâma)!”
(Adzakhala) akuyenda mothamanga mitu ili m’mwamba ndipo maso awo osatha kuphethira, ndipo m’mitima mwawo muli mopanda kanthu (mopanda ganizo lililonse chifukwa cha kudzadzidwa ndi mantha).
Ndipo achenjeze anthu za tsiku lomwe chilango chidzawadzera; ndipo amene ankadzichitira okha zoipa adzakhala akunena: “Mbuye wathu! Tichedwetseni kanthawi kochepa (tipatseninso mwawi kuti tibwelere pa dziko); tikayankhe kuitana Kwanu ndi kuwatsata atumiki.” (Adzauzidwa): “Kodi simunkalumbira kale kuti inu simudzachoka (pa dziko)?”
“Chikhalirecho mudakhala m’malo mommuja mwa omwe adadzichitira okha zoipa; ndipo kudaonekeratu poyera kwa inu mmene tidawachitira (powaononga); ndipo tidakufotokozerani mafanizo (osiyanasiyana koma inu mudatsutsa).”
Ndithudi, adachita ziwembu zawo, koma ziwembu zawo zili kwa Allah (akuzidziwa bwinobwino); ndipo ziwembu zawozo angakhale zitatha kuchotsetsa mapiri (sangamchite kanthu Mtumiki Muhammad (s.a.w} popeza Allah wamteteza).
Choncho usaganize kuti Allah Ngwakuswa lonjezo Lake kwa atumiki Ake. Ndithu Allah ndi mwini mphamvu (salephera chilichonse), Ngobwezera chilango mwaukali.
(Likumbukireni) tsiku lomwe nthaka iyi idzasinthidwa kukhala nthaka ina (yachilendo), ndi thambonso (lidzakhala lina), ndipo iwo (anthu onse adzatuluka m’manda mwawo) adzaonekera pamaso pa Allah Mmodzi Wamphamvu (zopanda malire).
Share