أَلَمْ يَأْتِكُمْ نَبَؤُا۟ ٱلَّذِينَ مِن قَبْلِكُمْ قَوْمِ نُوحٍۢ وَعَادٍۢ وَثَمُودَ ۛ وَٱلَّذِينَ مِنۢ بَعْدِهِمْ ۛ لَا يَعْلَمُهُمْ إِلَّا ٱللَّهُ ۚ جَآءَتْهُمْ رُسُلُهُم بِٱلْبَيِّنَٰتِ فَرَدُّوٓا۟ أَيْدِيَهُمْ فِىٓ أَفْوَٰهِهِمْ وَقَالُوٓا۟ إِنَّا كَفَرْنَا بِمَآ أُرْسِلْتُم بِهِۦ وَإِنَّا لَفِى شَكٍّۢ مِّمَّا تَدْعُونَنَآ إِلَيْهِ مُرِيبٍۢ ﴿٩﴾
Kodi siidakudzereni nkhani ya omwe adalipo patsogolo panu? Anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu? Ndi omwe adadza pambuyo pawo? Omwe palibe akuwadziwa kupatula Allah. Atumiki awo adawadzera ndi umboni oonekera. Koma adabwezera manja awo kukamwa kwawo (kusonyeza kutsutsa), ndipo adati: “Ndithu ife tikuzikana zimene mwatumizidwa nazo, ndipo ife tili mchikaiko pa zimene mukuitanira, ndiponso mchipeneko.”