Surah Al-Fajr ( The Dawn )

Surah Al-Fajr ( The Dawn ) - Chewa Aya count 30

Ndikulumbilira kuyera kwa m’bandakucha; (pamene usiku uthawa).
Ndi masiku khumi (a mwezi wa Dhul-Hijjah omwe ngopatulika kwa Allah).[430]
Ndi Shaf’i ndi Witri: (nambala yogawika ndi yosagawika).[431]
Ndi usiku pamene ukupita (chifukwa cha kuyenda kwa dziko kodabwitsa).
Kodi m’zimene zatchulidwazi simuli kulumbira kokwanira, kwa munthu wa nzeru?
Kodi sudadziwe momwe Mbuye wako adawalangira Âdi (anthu a mneneri Hûd).
Aku Irama; ataliatali ngati zipilala.[432]
Ndi Asamudu, (anthu a mneneri Swaleh) amene adali kudula matanthwe ku chigwa (chotchedwa Wadi Qura ndi kumamanga nyumba zikuluzikulu)?
Komanso Firiauna (Farawo) mwini magulu ankhondo (omwe amalimbikitsa ufumu wake monga momwe zichiri zimalimbikitsira tenti)?
Ndipo adachulukitsa m’menemo kuononga (pamwamba pa kuononga).[433]
Choncho Mbuye wako adawathira ndi mitundu ya zilango (zoopsa).
Ndithu Mbuye wako ali tcheru (ndi zochita za anthu. Ndipo akuwasungira kuti adzawalipire).[434]
Pamene munthu Mbuye wake akumuyesa (mayeso) ndikumulemekeza ndi kumpatsa mtendere (wachuma, ulemelero ndi mphamvu) amanena monyada: Mbuye wanga wandilemekeza (chifukwa zimenezi nzondiyenera ine).
Sichoncho ayi, (monga momwe mukuganizira) koma inu simuchitira za ufulu ana amasiye!
Sichoncho! (Siyani machitidwe amenewa); nthaka ikadzapondedwa (ndikuifafaniza).
Ndikubwera Mbuye wako (mmabweredwe omwe akuwadziwa Iye Mwini) ndi angelo ali mmizeremizere.
Adzanena: Kalanga ine! Ndikadatsogoza zabwino pa za moyo wanga uno!
Motero patsikuli, palibe wina amene adzalange monga momwe (Allah) adzalangire.[436]
Ndiponso sanganjate aliyense monga kunjata kwa iye (Allah).
Bwerera kwa Mbuye wako uli wokondwera (ndi zomwe wapatsidwa), ndipo uli woyanjidwa (ndi Allah pa zomwe udatsogoza).[438]
Ndipo lowa m’munda Wanga (mnyumba ya mtendere wa muyaya).
Share