Surah Al-Inshiqaq (The Splitting Asunder)

Surah Al-Inshiqaq (The Splitting Asunder) - Chewa Aya count 25

Pamene thambo lidzang’ambike (kusonyeza mapeto ake),
Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero,
Ndiponso pamene nthaka idzatambasulidwe (pogumuka mapiri ake ndikuchoka zitunda zake),
Ndi kutaya zomwe zidali mkati mwake ndi kukhala yopanda kanthu,[405]
Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero. (Choncho zikadzachitika zimenezi ndiye kuti munthu adzalandira mphoto ya zochita zake).[406]
E iwe munthu! Ndithudi iwe ukubwerera kwa Mbuye wako (ndi zochita zako zabwino kapena zoipa), kubwerera kotsimikizika, ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira za zochitachita zako).
Tsono amene adzapatsidwe kaundula wa zochita zake kudzanja la manja,[407]
Ndipo adzabwerera kwa anthu ake (okhulupirira) ali wokondwa.
Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wa zochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake (chifukwa chomunyoza),
Basi, iye adzaitana imfa (kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira);
Kamba kakuti iye adali wokondwa; (kukondwa kwa machimo) pamodzi ndi anthu ake (osaganizira za mathero ake).
Ndithudi, amaganiza kuti sadzabwerera (kwa Allah ndiponso sadzawerengedwa).
Chifukwa ninji (asabwelere)? Ndithu Mbuye wake adali kumuona. (Choncho alipidwa zimene adachita).
Choncho ndikulumbilira kufiira kwa dzuwa (pamene likulowa).
Ndi usiku ndi zimene wasonkhanitsa,[409]
Ndithudi mudzachoka apa kunka apa (pa moyo uno mpakana umene uli nkudza).
Kodi nchiyani chikuwaletsa iwo (okanira) kukhulupirira (Allah ndi kuuka kumanda, zisonyezo zake zitaonekera poyera)?
Ndipo ikawerengedwa kwa iwo Qur’an, sagwetsa pansi nkhope zawo (modzichepetsa).
Koma amene sadakhulupirire akutsutsa basi (chifukwa cha makani ndi kudzikweza).
Ndipo Allah akudziwa (bwinobwino) zimene akuzisonkhanitsa.
Share