Surah Al-Muddaththir ( The One Enveloped )

Surah Al-Muddaththir ( The One Enveloped ) - Chewa Aya count 56

Imilira ndipo uwachenjeze (anthu za chilango cha Allah).
Ndipo Mbuye wako (Yekha) umkulitse (pomulemekeza).
Ndipo nsalu zako uziyeretse (ndi madzi ku uve).
Ndiponso zoipa (monga mafano ndi zina zonse ) zipewe.
Usapatse (anthu) ncholinga choti ulandire zambiri.
Chifukwa cha Mbuye wako, pirira (ku malamulo Ake poleka zomwe waletsa ndi kuchita zimene walamula).
Ndi ana okhala nawo (paliponse).
Ndipo ndamkonzera (ulemelero), kumkonzera (kwabwino).
Kenako ali ndi dyera kuti ndimuonjezere (zina popanda kuthokoza).
Ndidzamkakamiza kuchilango chovuta; (kukwera phiri la ku Moto limene sakatha kulikwera).
Iye adalingalira (mu mtima mwake) ndi kukonza bwino (chonena chonyoza Qur’an).
Choncho waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)!
Ndiponso waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)!
Kenako adayang’anayang’ana (nkhope za anthu).
Kenakonso adachita tsinya ndikukwinya nkhope (kwambiri ndi mkwiyo).
Kenakonso adanyoza choonadi ndi kudzikweza (posachivomereza),
Adati: “Sichina ichi (Qur’an) koma ndi matsenga amene adalandiridwa (kuchokera kwa amatsenga akale),
Posachedwa ndimlowetsa ku ‘Saqara.’
Nanga ndi chiyani chingakudziwitse za ‘Saqara?’
(Ndi moto umene) siusiya (mnofu) ndiponso siusiya (fupa),
Kumeneko kuli khumi ndi asanu ndi anayi (alonda oyang’anira Motowo.)
Ndipo sitidaike oyang’anira ku Moto (kukhala anthu) koma angelo; ndipo sitidaike chiwerengero chawo koma ndimayesero kwa amene sadakhulupirire, kuti atsimikize amene adapatsidwa mabuku (zimene Qur’an ikunena za chiwerengero cha angelo a ku Moto) ndiponso kuti chionjezeke chikhulupiliro kwa amene akhulupirira, ndikuti asapeneke amene adapatsidwa mabuku pamodzi ndi okhulupirira. Ndiponso kuti amene m’mitima mwawo muli matenda (matenda achinyengo) komanso osakhulupirira anene: “Kodi Allah akulinganji pa fanizo limeneli?” Momwemo Allah akumulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo akumuongola amene wamfuna ndipo palibe amene angadziwe magulu a nkhondo a Mbuye wako kupatula Iye mwini. (Kutchula moto ndi zam’kati mwake) sichina koma ndichenjezo kwa anthu.
Sichoncho; ndikulumbilira mwezi,
Ndithu uwo, (moto wa Jahannam) ndi chimodzi mwa malodza akulu,
Kwa yemwe wafuna mwa inu kutsogola (pochita zabwino zokamthandiza tsiku louka kwa akufa) kapena kutsalira (ndi za m’dziko).
Kupatula akudzanja lamanja (Asilamu amene adadzimasula okha potembenukira kwa Allah).
(Iwo) adzakhala m’minda (yosasimbika kukongola kwake) akufunsana wina ndi mnzake,
(Kuti): “Nchiyani chakulowetsani ku Moto?”
Adzanena: “Sitidali m’gulu la omwe adali kupemphera (Swala).
Koma tinkangomira (m’zachabe ndi zabodza) pamodzi ndi omira (m’menemo).
Kodi ali ndi chiyani iwo pakuti azinyozera chenjezoli (limene lili Qur’an?)
(Akuyenda mothamanga kuti asamve chenjezoli) ngati kuti iwo ndi mbidzi zothawa,
Ati akufuna aliyense mwa iwo apatsidwe kalata zotambasulidwa (zimene zitsimikize uthenga wa Mneneri Muhammad{s.a.w}).
Sichoncho! Ndithu ichi (Qur’an) ndichikumbutso (chokwanira).
Choncho amene wafuna achikumbukire (amene sakufuna ndizake)!
Ndipo sangakumbukire pokhapokha Allah atafuna. Iye ndiye Amene ali woyenera kumuopa, ndiponso ndiye Mwini kukhululukira (amene akumuopa).
Share