E iwe Mneneri (s.a.w)! Nchifukwa ninji ukudziletsa chimene Allah wakuloleza kuchita? Ukufuna kukondweretsa akazi ako (nchifukwa Chake wachita izi?) Koma Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo kumbuka pamene Mneneri (s.a.w) adauza wina mwa akazi ake nkhani mwachinsinsi, choncho (mkaziyo) pamene adaiulula, Allah adamdziwitsa (Mtumiki) za kuululidwa kwa nkhaniyo, (ndipo Mtumiki) adaifotokoza mbali ina ya nkhaniyo, koma mbali ina adaisiya. Pamene adamfotokozera (mkazi wake) zankhaniyo adati: “Ndani wakuuza zimenezi?” (Mtumiki {s.a.w}) adati: “Wandiuza Wodziwa kwambiri ndiponso Wodziwa zazing’ono ndi zazikulu (Amene sichibisika kwa Iye chobisika chilichonse.)
E inu amene mwakhulupirira! Dzitchinjirizeni inu ndi mawanja anu ku Moto umene nkhuni zake ndi anthu ndi miyala; oyang’anira ake ndi angelo ouma mtima, amphamvu, sanyoza Allah pa zimene Wawalamula, ndipo amachita (zokhazo) zimene alamulidwa.[369]
(Adzawauza osakhulupirira pa tsiku la chiweruziro) E inu amene simdakhulupirire! Musadandaule lero, ndithu mukulipidwa pa zimene mumachita (padziko lapansi).
E iwe Mneneri! Limbana ndi akafiri (osakhulupirira) ndi Amunafikina (Achiphamaso), aumire mtima. Ndipo malo awo ndi ku Jahannam, taonani kuipa kobwerera (kwawo)!
Allah wapereka fanizo la osakhulupirira monga mkazi wa Nuh ndi mkazi wa Luti. Awiriwa adali pansi pa akapolo Athu awiri abwino, koma adali osakhulupirika kwa amuna awo, (ndipo amuna awo) sadawateteze kalikonse ku chilango cha Allah, ndipo kudanenedwa kwa iwo “Lowani ku Moto pamodzi (ndi ena) olowa.”
Ndiponso Allah wapereka fanizo la amene akhulupirira monga mkazi wa Firiauna (Farawo) pamene adanena: “Mbuye wanga! Ndimangireni kwa inu Nyumba mu Jannah, ndipo ndipulumutseni kwa Firiauna ndi zochita zake, ndiponso ndipulumutseni kwa anthu oipa (ndi amtopola.)”
Ndi (fanizo lina la wokhulupirira monga) Mariya mwana wa Imran amene adasunga umaliseche wake; ndipo tidauzira mmenemo Mzimu Wathu ndipo adavomereza mawu a Mbuye wake (omwe adali zolamula Zake ndi zoletsa Zake) ndi mabuku Ake (amene adavumbulutsidwa kwa Aneneri Ake); ndipo adali mmodzi wa opitiriza kudzichepetsa (ndi kumvera Allah).