Surah Al-Jumu'ah ( Friday )

Surah Al-Jumu'ah ( Friday ) - Chewa Aya count 11

Zonse zakumwamba ndi dziko lapansi zikulemekeza Allah; Mfumu, Woyera, Wamphamvu zopambana ndi nzeru zakuya (ndi kumyeretsa ku makhalidwe osayenerana ndi ulemelero Wake).
Iye ndiAmene adatumiza kwa Ummiyyina (osadziwa kulemba ndi kuwerenga), Mtumiki wochokera mwa iwo kuti awawerengere ndime Zake ndi kuti awayeretse (ku uchimo ndi kumakhalidwe oipa) ndi kuwaphunzitsa Qur’an ndi mawu anzeru (a mtumiki) ndithu kale adali osokera kowonekera (Mtumiki {s.a.w} asadadze kwa iwo).[361]
Ndipo (adamtumizanso) kwa ena mwa iwo, omwe sadakumane nawo, ndipo Iye (Allah) Ngopambana (pa chinthu chilichonse ndi Wamphamvu zoposa ndiponso) Ngwanzeru zakuya.
Umenewo ndiwo ubwino wa Allah akuupereka kwa amene wamfuna (mwa akapolo Ake); ndipo Allah yekha ndi Mwini ubwino waukulu.
Fanizo la (Ayuda) amene adawasenzetsa Taurat (pokakamizidwa kuti atsatire zophunzitsa za bukulo, koma osatsatira), ali ngati bulu amene akusenza mabuku akuluakulu anzeru, (koma osathandizika nawo). Taonani kuipa fanizo la anthu amene atsutsa zisonyezo za Allah. Ndipo Allah saongola anthu achinyengo.[362]
Ndipo sangailakelake mpang’ono pomwe chifukwa cha (zoipa) zimene manja awo atsogoza! Ndipo Allah akudziwa bwino za (anthu) osalungama.
Ndipo akaona malonda kapena masewero, akubalalika kunka ku zimenezo ndi kukusiya uli chiimire (ukuchita khutuba ndi anthu ochepa). Nena (kwa iwo): “Zimene zili kwa Allah nzabwino kwa inu kuposa masewero ndi malonda. Ndipo Allah Ngwabwino kwambiri kuposa opatsa onse.”
Share