وَإِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِۦ يَٰقَوْمِ لِمَ تُؤْذُونَنِى وَقَد تَّعْلَمُونَ أَنِّى رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيْكُمْ ۖ فَلَمَّا زَاغُوٓا۟ أَزَاغَ ٱللَّهُ قُلُوبَهُمْ ۚ وَٱللَّهُ لَا يَهْدِى ٱلْقَوْمَ ٱلْفَٰسِقِينَ ﴿٥﴾
Ndipo kumbuka (iwe Mneneri{s.a.w}) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti: “Ndichifukwa ninji mukundivutitsa ine pomwe mukudziwa kuti ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu?” Ndipo pamene adapitiriza kupandukira choonadi, Allah adaipinda mitima yawo (kuti isalandire chiongoko); ndipo Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo Chake.