Surah As-Saff ( The Row )

Surah As-Saff ( The Row ) - Chewa Aya count 14

Zonse zakumwamba ndi zapansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe osayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Yekha Ngopambana pa chilichonse; Wanzeru zakuya.
Ndithu Allah amakonda amene akumenya nkhondo pa njira Yake (yofalitsa chipembedzo Chake), ali pa mzere (umodzi) uku ali monga chomanga, chomangika mwamphamvu.[359]
Ndipo kumbuka (iwe Mneneri{s.a.w}) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti: “Ndichifukwa ninji mukundivutitsa ine pomwe mukudziwa kuti ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu?” Ndipo pamene adapitiriza kupandukira choonadi, Allah adaipinda mitima yawo (kuti isalandire chiongoko); ndipo Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo Chake.
Ndiponso (kumbuka) pamene adanena (Mtumiki) Isa (Yesu) mwana wa Mariya, kuti: “E inu ana a Israelil! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu, amene ndikuchitira umboni zimene zidadza patsogolo panga za buku la Chipangano chakale (Torah) ndipo ndikuuzani nkhani yabwino ya mthenga amene adzadze pambuyo panga, dzina lake Ahamad (Muhammad{s.a.w}).” Koma pamene adawadzera (Mtumiki wolonjedzedwayo) ndi zisonyezo zowonekera poyera (kuti iye ndi Mtumiki wa Allah). Adati: “Awa ndi matsenga owonekera.”
Iye ndi amene adatuma Mtumiki Wake (Muhammad{s.a.w}) ndi chiongoko ndi chipembedzo choona, kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse, ngakhale kuti ophatikiza Allah ndi mafano zikuwaipira.
Ndizina zomwe mukuzifuna. Thandizo (lonse) lichokera kwa Allah ndi kugonjetsa kumene kuli pafupi; ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira.
E inu amene mwakhulupirira! Khalani othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah (pamene Mtumiki akukuitanani kuti mumthangate) monga momwe adanenera Isa (Yesu) mwana wa Mariya powauza otsatira ake: “Ndani adzandithangata pa ntchito ya Allah (yofalitsa chipembedzo Chake)? Otsatira ake adanena: “Ife ndife othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah.” Choncho gulu lina la ana a Israyeli lidakhululupirira, ndipo gulu lina silidakhululupirire, tero tidawapatsa mphamvu amene adakhulupirira pa adani awo, ndipo adali opambana.
Share