Surah Al-Hashr ( The Gathering )

Surah Al-Hashr ( The Gathering ) - Chewa Aya count 24

Zonse za kumwamba ndi za pansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa ku khalidwe losayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Ngopambana (salephera kanthu), Ngwaluntha (m’kakonzedwe Kake ndi m’zochita Zake).
Ndipo kukadapanda kuti Allah adawalembera (pachiyambi) kusamuka (m’nyumba zawo), akadawalanga pa dziko pompano; koma chilango cha Moto chili pa iwo tsiku lachimaliziro.
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adamtsutsa Allah ndi Mthenga Wake, (kutsutsa kopyola muyeso); ndipo amene akutsutsa Allah (sangapulumuke ku chilango Chake). Ndithu Allah Ndiwolanga mwaukali.
Sim’dadule mtengo uliwonse wa zipatso za kanjedza, (inu Asilamu), kapena kuusiya uli chiimire ndi thunthu lake koma nchifuniro cha Allah ndi kuti awayalutse otuluka m’malamulo Ake.[354]
Ndipo chuma chimene wapereka Allah kwa Mtumiki Wake chochokera kwa iwo (Bani Nadhiri), chimenecho inu simudathamangitse mahachi kapena ngamira (pakuchipeza), koma Allah amapereka mphamvu kwa atumiki Ake zogonjetsera amene wamfuna. Ndipo Allah ali ndi Mphamvu (pa) chilichonse.
(Chiperekedwe) kwa osauka osamuka omwe adatulutsidwa m’nyumba zawo ndi (kusiya) chuma chawo chifukwa chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake) ndi kupulumutsa (chipembedzo cha) Allah ndi Mthenga Wake (pogwiritsira ntchito matupi awo ndi chuma chawo); iwowa ndi (Asilamu) owona.
Ndipo (okhulupirira) amene adadza pambuyo (pa Amuhajirina ndi Answari) akunena kuti: “Mbuye wathu tikhululukireni ndi anzathu amene adatitsogolera pa chikhulupiliro, ndipo musaike m’mitima mwathu njiru ndi chidani kwa amene adakhulupirira. E Mbuye wathu! Inu ndinu Wodekha, Wachisoni chosatha.”
Kodi wawaona amene achita uchiphamaso? Amene akunena kwa anzawo amene sadakhulupirire pakati pa anthu a mabuku: “Ndithu ngati (mukakamizidwa) kutuluka mu mzinda wa Madina, ndithudi tidzatuluka nanu pamodzi ndipo sitingamvere aliyense za inu mpaka muyaya; ngati mutamenyedwa nkhondo (ndi Asilamu) tidzakuthandizani. Koma Allah akuikira umboni kuti iwo ndionama (pa zimene alonjeza).
Ndithu inu (Asilamu) mukuopedwa kwambiri m’mitima mwawo kuposa mmene akumuopera Allah. Zimenezo nchifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira (chilichonse).
Fanizo (la Ayuda a Banu Nadhiri) lili ngati (amene adatsutsa mwa Ayuda a Qainuka) amene awatsogolera (kupeza mavuto) posachedwapa, adalawa chilango (pa dziko lapansi) cha zochita zawo (ndi kuswa mapangano). Ndipo iwo adzalandira chilango (china) chowawa kwambiri, (pa tsiku la chiweruziro).
Fanizo la achinyengo (achiphamaso pakuwanyenga Banu Nadhiri kuti amupandukire Mneneri wa Allah) lili ngati satana (ponyenga munthu kusiya chikhulupiliro). Adati kwa Iye: “Mkane (Allah).” Ndipo pamene adamkana, (satana) adati: “Ine sindili ndi iwe; ndithu ine ndikuopa Allah, Mbuye wa zolengedwa.”
Choncho mapeto a onse awiriwo, kudali kukalowa ku Moto ndi kukhala m’menemo nthawi yaitali. Iyi ndiyo mphoto ya anthu onyenga (ochenjelera anzawo).
E inu amene mwakhulupirira! Muopeni Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zimene waletsa) ndipo alingalire munthu aliyense zamawa zimene watsogoza. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngodziwa zimene mukuchita (ndipo adzakulipirani pa zimenezo).
Ndipo musakhale monga amene aiwala (zoyenera kuchitira) Allah; choncho (naye Allah) wawaiwalitsa mitima yawo (powachotsera kuzindikira zimene zingawathandize). Amenewa ndiwo olakwa kwakukulu (otuluka ku chilamulo cha Allah).
Iye ndi Allah, Amene palibenso wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, Wodziwa zamseri ndi zooneka. Iye Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha.
Iye ndi Allah, Amene palibenso wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, Mfumu, Woyera, Mwini mtendere, Wotsimikizira (aneneri Ake mphamvu yochitira zozizwitsa,) Msungi wa chilichonse (yemwe akuona zochita za akapolo Ake;) Wamphamvu zopambana, Mgonjetsi Wotukuka muulemelero; Wamkulukulu. Wayeretsedwa Allah kuzimene akumuphatikiza nazo.
Iye ndi Allah; Mlengi wa (zinthu, palibe chomfanizira); Muumbi wa chilichonse, Mkonzi wa maonekedwe a zinthu, Ake ndi maina abwino, zonse za kumwamba ndi pansi zikumulemekeza Iye ndi kumyeretsa ku makhalidwe osayenerana ndi ulemelero Wake. Iye Ngopambana ndiponso Wanzeru zakuya.
Share