يُنَادُونَهُمْ أَلَمْ نَكُن مَّعَكُمْ ۖ قَالُوا۟ بَلَىٰ وَلَٰكِنَّكُمْ فَتَنتُمْ أَنفُسَكُمْ وَتَرَبَّصْتُمْ وَٱرْتَبْتُمْ وَغَرَّتْكُمُ ٱلْأَمَانِىُّ حَتَّىٰ جَآءَ أَمْرُ ٱللَّهِ وَغَرَّكُم بِٱللَّهِ ٱلْغَرُورُ ﴿١٤﴾
(Achinyengo) adzaitana okhulupirira ponena kuti: “Kodi sitidali nanu limodzi (pa dziko ndi kumatsagana nanu?” (Okhulupirira) adzati: “Inde! (Mudali nafe monga momwe mukunenera). Koma inu munadziononga nokha ndipo mumayembekezera (kuti okhulupirira awapeze mavuto ndi kuonongeka); mudakaikira (zinthu za chilengedwe chanu); choncho zikhulupiliro zanu zonama zidakunyengani pomwe mudali angwiro mpaka lamulo la Allah (imfa) lidakupezani, komanso adakunyengani onyenga (satana) za Allah.