Iye ndi Oyamba (adalipo chilichonse chisadayambe); Wamuyaya (zonse zikadzatha); Woonekera (mzisonyezo pa chinthu chilichonse), Wobisika mkati kwambiri (saonedwa ndi maso pamoyo uno), Iye Ngodziwa chilichonse (kunja ndi mkati mwake).
Iye ndi Amene adalenga kumwamba ndi pansi (ndi zonse zammenemo) m’masiku asanu ndi limodzi kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu monga momwe Iye adziwira polongosola ufumu Wake). Akudziwa chilichonse cholowa m’nthaka ndi chimene chikutuluka m’menemo; ndi chilichonse chimene chikutsika kuchokera kumwamba ndi chimene chikukwera kumeneko. Ndipo Iye ali nanu paliponse pamene muli. Ndithu Allah amaona chilichonse chimene mukuchita, (sichibisika chilichonse kwa Iye).
Usiku amawulowetsa mu usana, ndipo usana amawulowetsa mu usiku. (Choncho kumasiyana kutalika kwake); ndipo Iye Ngodziwa zobisika za m’zifuwa (ndi zoganiza za m’mitima).
Khulupirirani Allah ndi Mthenga Wake, ndipo perekani (pa njira ya Allah m’chuma chimene Allah wakupatsani uchiyang’anira. Choncho mwa inu amene akhulupirira (mwa Allah ndi mthenga Wake) ndikupereka (zimene awapatsa) iwo ali ndi malipiro aakulu (kwa Allah).
Iye ndi Amene akuvumbulutsa kwa kapolo Wake Ayah (ndime) zofotokoza mwatsatanetsatane kuti akutulutseni mum’dima (wa kusokera) ndi kukuikani ku chiongoko cha kuunika. Ndipo ndithu Allah Ngoleza kwa inu, Ngwachisoni.
Kodi ndichifukwa chiani simukupereka pa njira ya Allah (chuma chanu) pamene Allah Ndimwini wa zosiyidwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Sali ofanana mwa inu amene adapereka chuma (panjira ya Allah) pamodzi ndi kumenya nkhondo usadagonjetsedwe (mzinda wa Makka), iwowo ndiomwe ali ndi ulemelero waukulu kuposa amene apereka chuma chawo ndi kumenya nkhondo pambuyo. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino (ngakhale ali osiyana ulemelero wawo); ndipo Allah akudziwa zonse zimene muchita. (Choncho aliyense adzalipidwa molingana ndi zimene amachita).
Basi lero sililandiridwa dipo lochokera kwa inu (limene mungalipereke kuti mudzipulumutse ku chilango ngakhale likhale lamtengo wotani). Ndiponso sililandiridwa dipo lochokera kwa osakhulupirira (amene adalingana nanu n’kusakhulupirira kwawo Allah) malo anu nonsenu ndi ku Moto basi. Amenewa ndi malo okuyenerani. Kumeneko ndiko kobwerera koipa kwabasi!
Kodi siidakwane nthawi kwa okhulupirira kuti mitima yawo idzichepetse pokumbukira Allah ndi zomwe zidavumbulutsidwa za chowonadi (Qur’an yolemekezeka)? Ndi kuti asakhale monga omwe adapatsidwa buku kale (Ayuda ndi Akhrisitu) amene nthawi yawo yosiyana ndi aneneri awo idali yaitali. Choncho mitima yawo idauma ndipo ambiri a iwo adatuluka m’chilamulo (cha Allah).
Ndithu amene akupereka sadaka amuna ndi akazi, ndi kumamkongoza Allah ngongole yabwino (Allah) adzawaonjezera malipiro pa zimenezi. Ndipo ali ndi malipiro aulemu.
Ndipo amene akhulupirira Allah ndi aneneri Ake, iwowo ndiwo owona (pa chikhulupiliro); ndi ofera pa njira ya Allah (onsewo) azapeza malipiro awo ndi kuwala kwawo kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire ndi kutsutsa zisonyezo zathu iwowo ndi eni a ku Jahena.
Chitani changu (pa zinthu zokupatitsani) chikhululuko chochokera kwa Mbuye wanu ndi Munda wamtendere womwe mulifupi mwake muli ngati kutambasuka kwa kumwamba ndi pansi; wakonzedwera amene akhulupirira Allah ndi aneneri Ake; umenewo ndi ubwino wa Allah womwe akuupereka kwa amene wamfuna. Allah ndi Mwini ubwino waukulu.
Silipezeka tsoka lililonse panthaka (monga chilala) ngakhale pamatupi anu koma lidalembedwa kale m’buku (la Allah) tisadalilenge ndi kulipereka. Ndithu zimenezo kwa Allah nzofewa.
(Takudziwitsani zimenezi) kuti musadandaule ndi chimene chakudutsani, ndi kutinso musakondwere monyada ndi chimene wakupatsani. Allah sakonda aliyense wodzitama, wonyada.
Ndipo ndithu tidatuma Nuh ndi Ibrahim ndi kukhazikitsa uneneri m’mbumba yawo ndi mabuku (achiongoko). Ena mwa iwo adayenda pa njira yolungama, koma ambiri a iwo adapatuka pa njira yolungamayo.
Kenako tidatsatiza pambuyo pawo ndi atumiki Athu ndipo tidasatiza ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndipo tidampatsa Injili ndipo tidaika kufatsa ndi chifundo m’mitima ya omwe adamtsatira. Koma kusakwatira, adakuyambitsa okha; sitidawalamule zimenezo koma (adayambitsa zimenezo) chifukwa chofuna chikondi cha Allah; koma sadazisunge moyenera. Choncho amene adakhulupirira pakati pawo tidawapatsa malipiro awo, koma ambiri a iwo ngopandukira malamulo.
(Allah akupatsani zonsezi) kuti adziwe amene adapatsidwa buku (omwe sadamkhulupirire Mtumiki{s.a.w}) kuti iwo sangathe kudzisankhira okha chilichonse mu mtendere wa Allah. Ndipo ndithu ubwino wonse uli m’manja mwa Allah Yekha. Amapatsa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wochuluka.