Dziwani kuti Allah Ngolandira mapemphero oyera, (opanda kuphatikizidwa ndi zina). Koma amene adzipangira athandizi kusiya Allah, (akumanena kuti): “Ife sitikuwapembedza awa, koma tikutero ndi cholinga choti atifikitse pafupi ndi Allah.” Ndithu Allah, adzaweruza pakati pawo (pakati pa okhulupirira Allah, ndi okana) pa zimene akusiyana. Ndithu Allah saongola amene ali wabodza; wokanira zedi (Allah).
Allah akadafuna kupeza mwana, akadasankha yemwe akum’funa mzomwe adalenga. Wapatukana ndi zimenezo! Iye ndi Allah Mmodzi; Wogonjetsa; (Wochita zimene wafuna).
Adalenga thambo ndi nthaka mwamtheradi. Amakulunga usiku mu usana; ndipo amakulunga usana mu usiku. Ndipo dzuwa ndi mwezi wazichita kuti zitumikire monga momwe afunira. Zonsezi zikuyenda kufikira pa nthawi yake imene yaikidwa. Dziwani kuti Iye (Allah) Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri.
Adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi (womwe ndi Adam; tate wa anthu). Ndipo kenako adalenga kuchokera mu mzimu umenewo mnzake, (mkazi wake, Hawa); ndipo adakutsitsirani mitundu isanu ndi itatu ya nyama ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira yaimuna ndi yaikazi, ng’ombe yaimuna ndi yaikazi, mbuzi yaimuna ndi yaikazi ndi nkhosa yaimuna ndi yaikazi. Zonse pamodzi, zisanu ndi zitatu, zomwe mumathandizidwa nazo kwambiri). Amakuumbani m’mimba mwa mayi anu mkaumbidwe kosiyanasiyana, mu mdima utatu; (mu mdima wa mimba, chiberekero ndi mdima wa nembanemba). Ameneyo (adakuchitirani zonsezi), ndi Allah, Mleri wanu; ufumu ngwa Iye. Palibe wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Kodi nanga mukutembunuzidwa bwanji (kusiya Allah?)
Ndipo masautso akampeza munthu, amapempha Mbuye wake ndi kutembenukira kwa Iye (pomwe chikhalirecho adali kumnyoza). Kenako (Mbuye wake) akampatsa mtendere wochokera kwa Iye (waukulu), amaiwala (masautso aja) omwe adali kumpempha Allah kuti amchotsere asadampatse mtenderewo, ndipo kenako ndikumpangira Allah milungu inzake kuti asokeretse ku njira Yake. Nena (iwe Mtumiki kwa yemwe ali ndi chikhalidwe chotere): “Sangalala ndi kukanira kwako (mtendere wa Allah) kwa nthawi yochepa. Ndithu iwe ndi mmodzi wa anthu aku Moto.”
Kodi yemwe akudzichepetsa (kwa Allah ndi kumpembedza) pakati pa usiku uku akugwetsa nkhope pansi ndi kuimilira, kuopa tsiku la chimaliziro ndi kuyembekezera chifundo cha Mbuye wake, (kodi angafanane ndi yemwe amapempha Allah akakhala pa mavuto pokha, akakhala pa mtendere ndikumuiwala?) Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki {s.a.w}): “Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Ndithu ndi eni nzeru amene amalingalira.
Nena: “Ine ndalamulidwa kuti ndimpembedze Allah momuyeretsera mapemphero Ake (posamphatikiza ndi aliyense pa mapemphero, kapena kupemphera mwa chiphamaso).”
Koma amene aopa Mbuye wawo, iwo adzakhala nazo Nyumba zikuluzikulu zimene zamangidwa mosanjikizana, mitsinje ikuyenda pansi pake. Ili ndi lonjezo lochokera kwa Allah. Allah saphwanya lonjezo.
Kodi amene Allah watsekula chifuwa chake povomereza Chisilamu, kotero kuti iye akuyenda mkuunika kwa Mbuye wake, (angafanane ndi yemwe akunyozera kupenyetsetsa zisonyezo za Allah?) Kuonongeka kwakukulu kuli pa ouma mitima yawo posakumbukira Allah (ndi kulabadira Qur’an). Iwo ali m’kusokera koonekera.
Allah wavumbulutsa nkhani yabwino zedi yomwe ndi buku logwirizana nkhani zake; (losasemphana). Lobwerezabwereza (malamulo ake). Makungu a omwe amaopa Mbuye wawo amanjenjemera ndi ilo. Kenako makungu awo ndi mitima yawo zimakhazikika pokumbukira Allah. Buku limeneli ndi chiongoko cha Allah; ndi ilo, akumuongola amene wamfuna. Ndipo amene Allah wamulekelera kuti asokere (chifukwa chonyozera kwake choona), sangakhale ndi womuongola (ndi ompulumutsa ku chionongeko).
Kodi yemwe adzakhala akudzitchinjiriza ndi nkhope yake (uku manja atanjatidwa) ku chilango choipa pa tsiku la Qiyâma, (angafanane ndi yemwe adzakhala mchisangalalo mminda ya mtendere?” Ndipo kudzanenedwa kwa oipa: “Lawani zoipa za zochita zanu.”
Choncho Allah adawalawitsa kunyozeka pa moyo wa pa dziko lapansi; koma ndithu chilango cha tsiku la chimaliziro nchachikulu zedi (kuposa chilango cha m’dziko lapansi) akadakhala akudziwa!
Allah wapereka fanizo la munthu wotumikira mabwana awiri omwe ngokangana pa za iye, ndi munthu yemwe akutumikira bwana mmodzi. Kodi awiriwa ngofanana? Kuyamikidwa konse nkwa Allah! Koma ambiri a iwo sadziwa.
Kodi Allah sali Wokwanira kwa kapolo Wake? Koma akukuopseza ndi zina zosakhala Iye! Ndipo yemwe Allah wam’lekelera kuti asokere, ndithu alibe womuongola.
Ndithu ife takuvumbulutsira buku ili chifukwa cha anthu (onse) kuti Tiwafotokozere choona. Choncho amene waongoka, zabwino zake nza iye mwini. Koma amene wakhota, ndiye kuti akudzikhotetsa yekha. (Ndipo zoipa za kukhotako zidzakhala pa iye yekha). Ndipo iwe si muyang’anili wawo.
Ndipo pamene Allah Yekha akutchulidwa, mitima ya amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro imanyansidwa; koma akatchulidwa amene sali Iye, iwo amakondwa.
Pamene munthu mavuto amkhudza, amatipempha (uku ali wodzichepetsa); koma tikampatsa mtendere wochokera kwa Ife, amanena kuti: “Ndapatsidwa mtendere uwu chifukwa chakudziwa kwanga (njira zoupezera).” (Sichoncho) koma mtendere umenewu ndi mayeso; koma ambiri a iwo sadziwa!
Ndipo ndithu kwavumbulutsidwa kwa iwe, ndi kwa amene adalipo patsogolo pako (mawu awa:) “Ngati umphatikiza (Allah ndi milungu yabodza), ndithu ntchito zako zionongeka, ndipo ukhala mwa oluza (otaika).”
Koma sadamlemekeze Allah, kulemekeza koyenerana Naye, pomwe pa tsiku la Qiyâma nthaka yonse (idzakhala) chofumbata Chake mmanja; ndipo thambo lidzakulungidwa ndi dzanja Lake lamanja. Walemekezeka Allah. Ndipo watukuka ku zimene akum’phatikiza nazozi.
Ndipo amene adakanira, adzakusidwa kunka ku Jahannam ali magulumagulu kufikira pomwe adzaifikira, makomo ake adzatsekulidwa, ndipo alonda ake adzawauza: “Kodi sadakudzereni aneneri ochokera mwa inu okulakatulirani zisonyezo za Mbuye wanu, ndi kukuchenjezani za kukumana kwanu ndi tsiku lanuli?” Adzayankha (nati): “Inde, adatidzera; koma lidatsimikizika liwu la chilango pa okanira.”