Surah Ya-seen

Surah Ya-seen - Chewa Aya count 83

Ndikulumbira Qur’an (iyi yomwe yakonzedwa mwaluso) yodzazidwa ndi mawu anzeru.
Ndithu iwe (Muhammad {s.a.w}) ndimmodzi wa atumiki (amene Allah adawatuma kwa anthu kuti akawasonyeze chiongoko).
(Qur’an iyi) nchivumbulutso cha Mwini Mphamvu zoposa; (palibe chokanika kwa Iye) Wachisoni chosatha.
Kuti uwachenjeze anthu omwe makolo awo sadachenjezedwe; choncho iwo ngoiwala (zomwe zili zofunika kuchitira Allah ndi kudzichitira okha pamodzi ndi anthu ena).
Ndithu Ife taika magoli m’makosi mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti mitu yawo yayang’ana mmwamba; (siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana).
Ndipo tawaikira chotsekereza patsogolo pawo ndi chotsekereza pambuyo pawo, ndipo (maso awo) tawaphimba, tero iwo saona (zapatsogolo ndi pambuyo pawo).
Ndithu kuchenjeza kwako kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa (Allah) Wachifundo chambiri ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya chikhululuko (chochokera kwa Allah pa machimo ake) ndi malipiro aulemu.
Ndithu Ife tidzaukitsa akufa, ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo), ndipo chinthu chilichonse tachilemba m’kaundula wopenyeka (wofotokoza chilichonse).
Ndipo pereka kwa iwo (iwe Mneneri) fanizo la (nkhani ya) eni mudzi pamene atumiki (a Allah) adaudzera mudziwo (kuti akaaongole eni mudziwo).
(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu ngati ife; (Allah) Wachifundo chambiri sadavumbulutse chilichonse (kwa munthu); inu simuli kanthu koma mukunena bodza.”
(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.”
“Ndipo palibe china pa ife, koma kufikitsa mwachimvekere (uthenga wa Allah).”
(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza tsoka chifukwa cha inu; ngati simusiya (ulaliki wanuwo wofuna kutichotsa ku chipembedzo chathu) tikugendani ndi miyala; ndipo kuchokera kwa ife chikukhudzani chilango chowawa.”
(Atumiki) adati: “Tsoka lanu lili ndi inu (chifukwa cha kukana kwanu ndi kupitiriza kupembedza mafano). Kodi mukakumbutsidwa (ndi mawu omwe m’kati mwake muli mtendere wanu mukuti takudzetserani masoka; ndi kumatiopseza ndi chilango chowawa)? Koma inu ndi anthu olumpha malire.”
“Atsateni omwe sakupemphani malipiro (pa kukulangizani kwawo), ndipo iwo ngoongoka.”
“Kodi nchiyani chingandiletse ine kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa Iye ndi komwe inu nonse mudzabwerera.”.
“Kodi ndidzipangire milungu kusiya Iye (Allah)? Chipulumutso chawo sichingandipindulire chilichonse ngati (Allah) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira zoipa; ndipo siingandipulumutse.”
“Ndithu ine ngati nditatero ndiye kuti ndili mchisokero choonekera poyera”.
“Ndithu ine ndakhulupirira Mbuye wanu choncho ndimvereni.”
Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa m’Munda wamtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga akadadziwa!”
“Momwe Mbuye wanga wandikhululukira ndikundichita kukhala mmodzi wa opatsidwa ulemu (akadakhulupirira).”
Ndipo anthu ake sitidawatsitsire ankhondo ochokera kumwamba pambuyo pake (kuti awaononge). Ndipo pachizolowezi chathu sititsitsa (ankhondo kumwamba tikafuna kuononga, koma Mngelo mmodzi amakwanira).
(Kuonongeka kwawo) kudali mkuwe umodzi, ndipo nthawi yomweyo adali akufa (izi zidachitika pamene mngelo Gabuliyele adawakuwira mkuwe wamphamvu).
Alemekezeke (Allah), Amene adalenga zinthu zonse, chachimuna ndi chachikazi, kuchokera m’zimene nthaka ikutulutsa, ndi iwo omwe ndi zina zimene (anthu) sakudziwa.
Ndiponso chisonyezo chawo ndiusiku. M’menemo timachotsamo usana (womwe umabisa usiku), ndipo (anthu) amangozindikira ali mu mdima.
۞ Ndipo dzuwa; limayenda m’njira ndi m’nthawi yake imene idakonzedwa kwa ilo. Chikonzero chimenecho ncha (Allah) Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
Ndiponso mwezi; tidaukonzera malo oimirapo mpaka kukafika pomwe umabwerera ndi kukhala wochepa ndi wokhota monga nthambi ya mtengo wa kanjedza, youma komanso yokhota.[341]
Nkosatheka kwa dzuwa kukumana ndi mwezi (njira yake); nawonso usiku sungathe kupambana usana (pakudza nthawi yausana isadathe, koma zimasinthana). Ndipo chilichonse mwa izo chimasambira m’njira yake (imene Allah adachikonzera).
Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo (chosonyeza madalitso Athu pa iwo). Ndithu tidaukweza mtundu wawo mchombo chodzazidwa (ndi zonse zamoyo).
Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza m’madzi, ndipo sangapezeke wowathandiza, ndiponso sangapulumutsidwe.
Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha chifundo Chathu pa iwo ndi kuti asangalale kufikira nthawi yawo (yofera).
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo panu ndi zomwe ziri pambuyo panu kuti muchitiridwe chifundo.” (Iwo akunyoza malangizowo).
Ndipo palibe chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo (zosonyeza umodzi Wake ndi kukhoza Kwake) chomwe chidawadzera popanda kuchinyoza (ndi kuchikana).
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (amphawi) zimene Allah wakupatsani.” Osakhulupirira amanena kwa okhulupirira: “Kodi tidyetse yemwe Allah akadafuna akadamdyetsa; (titsutsane ndi cholinga cha Allah)? Ndithu inu simuli kanthu koma muli m’kusokera koonekeratu.”
Ndipo akunena (mwachipongwe kwa okhulupirira): “Kodi lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro), lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”
Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa akufa); iwo adzangozindikira akutuluka m’manda kunka kwa Mbuye wawo uku akuthamanga.
Adzati: “Kalanga ife! Kodi ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza): “Izi ndi zimene adalonjeza (Allah), Wachifundo chambiri ndi zimene adanena atumiki moona.”
Ndithu anthu aku Jannah (Munda wamtendere) lero akhala wotanganidwa ndi chisangalalo.
M’menemo apeza (mtundu uliwonse) wa zipatso ndiponso apeza chilichonse chimene akuchifuna.
“Mtendere (pa iwo)!” Limeneli ndi liwu lochokera kwa Mbuye (wawo), Wachisoni chosatha.
Ndipo tikadafuna, tikadawasintha kukhala ndi maonekedwe a nyama pamalo pawo pomwepo (pamene adali), kotero kuti sakadatha kuyenda (kunka patsogolo) ngakhale kubwerera pambuyo.
Ndipo amene tikumtalikitsira moyo wake, timam’bwezeranso pambuyo m’kalengedwe kake (ndi kukhala ngati mwana). Kodi bwanji saganizira mwanzeru?
Ndipo sitidamphunzitse (Mtumiki {s.a.w}) ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa iye (kukhala mlakatuli). Qur’an sichina, koma ndichikumbutso ndi buku lomwe likulongosola chilichonse.
Kuti liwachenjeze amene ali moyo, ndi kuti litsimikizike liwu (la chilango) pa osakhulupirira.
Ndi kuti tazichita kukhala zowatumikira? Zina mwa izo amazikwerapo; ndipo zina mwa izo amazidya.
Ndipo m’menemo (m’nyama) muli zowathandiza (zambiri) ndiponso zakumwa. Nanga bwanji sathokoza?
(Koma) siingathe kuwathandiza; ndipo iwo (kwa milunguyo) ndi asilikali amene akonzedwa kulondera (mafanowo ndi kuwatumikira).
Mawu awo (onyoza Allah ndi okutsutsa iwe) asakudandaulitse. Ndithu Ife tikudziwa zimene akubisa ndi zimene akuzionetsera poyera.
Ndipo akutiponyera fanizo (lotsutsa kukhoza Kwathu kuukitsa akufa) ndi kuiwala chilengedwe chake (chochokera kumadzi opanda pake). Akunena: “Ndani angaukitse mafupa pomwe ali ofumbwa?”
Ndithu machitidwe Ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika (nthawi yomweyo).
Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pa chinthu chilichonse; ndipo kwa Iye (ndiko) mudzabweerera nonse.
Share