Surah Al-Ahzab ( The Combined Forces )

Surah Al-Ahzab ( The Combined Forces ) - Chewa Aya count 73

E iwe Mneneri! Muope Allah, ndipo usamvere osakhulupirira ndi achiphamaso. Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri; Wanzeru zakuya (m’zoyankhula ndi m’zochita Zake).[316]
Ndipo tsata zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako (pozigwiritsa ntchito). Ndithu Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita.
Ndipo yadzamira kwa Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Msungi ndi Mtetezi (wako).
Aitaneni ndi maina a atate awo. Kutero ndichilungamo kwa Allah. Koma ngati simukuwadziwa atate awo, (aitaneni ngati) ndiabale anu pachipembedzo; ndiponso ndi anzanu. Palibe uchimo kwa inu pa zimene mwazichita molakwitsa (mosazindikira). Koma (pali uchimo) pa zimene mitima yanu yachita mwadala. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
Mneneri ngofunika kwambiri kwa okhulupirira kuposa moyo wawo, (matupi awo ndi chuma chawo); ndipo akazi ake ndi amayi awo (amayi a Asilamu; nkoletsedwa kuwakwatira pambuyo pa imfa yake). Ndipo achibale pakati pawo ngoyenera (kulandira zamasiye pamalamulo a) m’buku la Allah kuposa Asilamu ena ngakhalenso Amuhajirina (amene adasamuka ku Makka kupita ku Madina chifukwa cha chipembedzo cha Chisilamu). Kupatula ngati mutachita zabwino kwa anzanu (sikolakwika). Izi zidalembedwa kale m’buku.[317]
Ndipo (akumbutse) pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri onse pangano lawo. Ndi kwa iwe, ndi kwa Nuh, Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano lamphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah).
Kuti (Allah) adzafunse owona (aneneri) (tsiku la chimaliziro) pa zimene adanena (kwa anthu awo zakufikitsa uthenga woonadi kwa iwo). Ndipo Allah wawakonzera (osakhulupirira) chilango chopweteka.
Pamene adakudzerani cha kumtunda kwanu, ndi kunsi kwanu (kumtunda kwa dambo ndi kumunsi kwake), pamene maso adangoti tong’oo chammbali ndipo mitima idafika kum’mero (chifukwa cha mantha ndi kunjenjemera) uku mukumganizira Allah maganizo osiyanasiyana.
Panthawi imeneyo okhulupirira adayesedwa mayeso aakulu. Adanjenjemeretsedwa kunjenjemera kwambiri.
Ndipo pamene ankanena achiphamaso (achinyengo) ndi omwe m’mitima mwawo muli matenda: “Palibe chomwe adatilonjeza Allah ndi Mtumiki Wake koma chinyengo basi.”
Ndipo pamene gulu lina mwa iwo lidanena: “E inu nzika za mu Yathiriba (Madina)! Palibe njira kwa inu yokhalira (pa nkhondo yogonjayi). Choncho bwererani (ku nyumba zanu; msiyeni Muhammad alimbane yekha ndi adani ake).” Ndipo gulu lina la nkhondo lochokera mwa iwo limapempha chilolezo kwa Mneneri (s.a.w) ( chobwelera ku Madina) ponena (kuti): “Ndithu nyumba zathu nzamaliseche (zopanda chitetezo).” Koma izo sizamaliseche. Sakufuna china, koma kuthawa basi.
Ndipo akadawalowera (magulu ankhondo a adaniwo), mbali zonse (za Mzindawo), kenako nkupemphedwa kuti atuluke m’Chisilamu ndi kumenyana ndi Asilamu, akadachita zimenezo; ndipo sakadayembekezera koma nthawi yochepa basi.
Ndipo ndithu (awa amene adathawa pabwalo la nkhondo), adali atamulonjeza kale Allah (kuti iwo) sadzatembenuza misana (kuthawa). Ndipo lonjezo la Allah nlofunsidwa. (Choncho iwo adzafunsidwa pa zomwe adalonjeza kwa Allah).
Nena: “Kuthawa sikungakuthandizeni ngati mukuthawa imfa kapena kuphedwa; choncho (kuthawa kwanuku) simusangalatsidwa (nako) koma pang’ono basi. (Kenako ikatha nthawi ya moyo wanu, mukufa).”
Ndithu Allah akuwadziwa amene akudziletsa mwa inu (kupita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) ndi kuletsanso anthu ena), ndi amene akuuza abale awo: “Bwerani kwa ife; (m’thaweni Muhammad {s.a.w}).” Ndiponso sapita ku nkhondo koma pang’ono pokha.
(Kufikira tsopano chifukwa cha mantha awo) akuganiza kuti magulu a nkhondo (adani) sadapitebe; ndipo magulu amenewo akadadzanso, akadalakalaka akadakhala kuchipululu pamodzi ndi arabu a kuchimidzi ndi kuti azikangofunsa za nkhani zanu. Akadakhala pamodzi ndi inu sadakamenyana (ndi adani) koma pang’ono pokha.[319]
Ndithu muli nacho chitsanzo chabwino mwa Mthenga wa Allah (m’kudzipereka kwake ndi khama lake pa njira ya Allah, ndi kupirira kwake ndi masautso) kwa yemwe akuopa Allah ndi tsiku lachimaliziro, namatchula Allah kwambiri.
Ndipo pamene okhulupirira adaona magulu a nkhondo (a adani atawazinga mbali zonse), adati: “Ichi ndichimene Allah ndi Mtumiki Wake adatilonjeza (kuti tidzapeza masautso, kenako nkupambana), ndipo Allah ndi Mtumiki Wake adanena zoona.” Ndipo (ichi) sichidawaonjezere china, koma chikhulupiliro (mwa Allah) ndi kudzipereka.
Mwa okhulupirira alipo amuna ena amene adakwaniritsa zomwe adamlonjeza Allah (kuti sadzathawa pa nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w), ena mwa iwo adamaliza moyo wawo (nakwaniritsa lonjezo lawo pofera pa njira ya Allah). Ndipo ena mwa iwo akuyembekezerabe (kufera pa njira ya Allah). Ndipo sadasinthe konse (lonjezo lawo).[320]
Kuti Allah awalipire owona chifukwa cha kuona kwawo; ndi kuti awalange achiphamaso ngati atafuna, kapena kuwalandira kulapa kwawo (ngati atalapa). Ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha.
Ndipo Allah adawabweza amene sadakhulupirire uku ali odzazidwa ndi mkwiyo m’mitima mwawo; sadapeze chabwino; (sadagonjetse Asilamu ndi kupeza zimene ankaziyembekezera monga zotola za pa nkhondo). Ndipo Allah adawakwaniritsira okhulupirira nkhondo (powatumizira adani mphepo yamkuntho ndi angelo). Ndipo, Allah Ngwamphamvu, Ngopambana, (sapambanidwa ndi chilichonse).
E iwe Mneneri! Nena kwa akazi ako (m’njira yowalangiza): “Ngati mufuna moyo wa dziko lapansi ndi zosangalatsa zake (ine ndilibe zosangalatsa za m’dziko, ndipo sindingakukakamizeni kuti mukhale ndi ine mu moyo wa umphawi; ngati mufuna) bwerani ndikupatsani cholekanira, chokusangalatsani, kenako ndikusiyeni kusiyana kwabwino (kopanda masautso).”
E inu akazi a Mneneri! Inu simuli monga mmodzi wa akazi ena (omwe siakazi a Mtumiki, paulemelero) ngati muopa Allah. Choncho musalobodole mawu (mowakometsa poyankhulana ndi amuna,) kuti asalakelake (kuchita zoipa ndi inu) yemwe mu mtima mwake muli matenda (achiwerewere). Koma nenani zonena zabwino.
Ndipo khalani mnyumba zanu, ndipo musadzionetsere (kwa amuna) uku mutadzikongoletsa monga mmene ankaonetsera zokongoletsa zawo (akazi) a m’nthawi ya umbuli wakale. Ndipo pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat, mverani Allah ndi Mtumiki Wake. Ndithu Allah akufuna kukuchotserani uve e, inu a kunyumba (ya Mneneri)! Ndi kuti akuyeretseni ndithu.
Ndipo lowezani pamtima zimene zikunenedwa m’nyumba zanu; ndime za mawu a Allah ndi (zonena za Mtumiki) zanzeru. Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika kwambiri, ndi zapoyera.
Ndipo (kumbuka) pamene udamuuza yemwe Allah adampatsa mtendere (pomuongolera ku Chisilamu, ndipo) iwenso udampatsa mtendere (pomulera ndi kumpatsa ufulu, yemwe ndi Zaid Bun Haritha, udati kwa iye): “Gwirizana ndi mkazi wako, ndipo wopa Allah.” Ukubisa mu mtima mwako chimene Allah afuna kuchisonyeza poyera (chomwe ndi kuti Allah akulamula kumkwatira mkazi ameneyo akamuleka Zaid Bun Haritha kuti chichoke chizolowezi choti mwana wongomulera chabe nkumuyesa mwana wako weniweni). Ndipo ukuopa anthu (kuti akudzudzula pa zimenezo), pomwe woyenera kumuopa ndi Allah. Choncho pamene Zaid adamaliza chilakolako chake pa mkazi ameneyo, tidakukwatitsa iwe kuti pasakhale masautso pa okhulupirira pokwatira akazi a ana awo akungowalera chabe ngati (anawo) atamaliza zilakolako zawo pa akaziwo, ndipo lamulo la Allah ndilochitika, (palibe chingalepheretse kuti lisachitike).[324]
Palibe tchimo pa Mneneri pa zimene Allah wamulamula. Chimenechi ndichizolowezi cha Allah (njira ya Allah) pa amene adanka kale. Ndipo lamulo la Allah ndi chikonzero (chomwe) chidakonzedwa. (Ndipo sichisinthidwa). [325]
(Aneneri) amene amafikitsa uthenga wa Allah (kwa anthu) uku akumuopa Iye, ndipo samamuopa aliyense koma Allah (yekha). Ndipo Allah Akukwana kukhala wowerengera (zochita za akapolo Ake).[326]
Iye ndi Amene akukuchitirani chifundo (ndi kukufunirani zabwino) nawonso Angelo Ake (akukupemphelerani kwa Allah) kuti akutulutseni mu mdima ndi kukuikani m’kuunika. Ndipo (Iye) Ngwachisoni zedi kwa okhulupirira.
E iwe Mneneri (wa Allah)! Ndithu Ife takutuma (kuti ukhale) mboni (pa anthu ako ndi pa mibadwo yonse). Wonena nkhani zabwino (kwa oopa Allah), ndi mchenjezi (kwa onyoza Allah).
Ndi kuti ukhale woitanira (anthu) kwa Allah kupyolera m’chifuniro Chake. Ndi (kutinso ukhale) nyali younikira (anthu).
Ndipo usawamvere osakhulupirira ndi achiphamaso (pa zimene akufuna kuti uwapeputsire malamulo a Allah), usalabadire masautso awo, ndipo tsamira kwa Allah. Ndipo Allah akukwanira kukhala Mtetezi.
E iwe Mneneri! Ndithu Ife takuloleza (kukhala nawo pamodzi) akazi ako amene wawapatsa chiwongo chawo, ndi chimene dzanja lako lamanja lapeza (omwe ndi akazi ogwidwa pa nkhondo) chomwe Allah wakupatsa, ndi ana achikazi a m’bale wa atate ako, ndi ana achikazi a mlongo wa atate ako, ndi ana achikazi a atsibweni ako, ndi ana achikazi a m’bale wa mayi ako amene adasamuka pamodzi ndi iwe, ndi mkazi wokhulupirira atadzipereka yekha kwa Mneneri ngati Mneneri akufuna kumkwatira, chilolezo ichi ncha iwe wekha, osati okhulupirira onse. Ndithu tikudziwa malamulo amene tawakhazikitsa kwa iwo pa akazi awo, ndi chimene manja awo akumanja apeza; (takuchitira zimenezi iwe wekha Mneneri Muhammad {s.a.w}) kuti pasakhale masautso pa iwe (ngati ukufuna kukwatira mkazi wina chifukwa chofalitsa chipembedzo) ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni chosatha.
Ukhoza kumchedwetsa (posagona m’nyumba mwake) amene wam’funa pakati pa iwo ndi kumuyandikitsa kwa iwe amene wam’funa. Ndipo amene wam’funa mwa amene udawapatuka, palibe tchimo pa iwe. Kuchita izi kuchititsa kuti maso awo atonthole (mitima yawo ikondwe) ndipo asadandaule; ndi kuyanjana nacho chimene wawapatsa onse. Ndipo Allah akudziwa zimene zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Ngoleza, (salanga mwachangu).
Pambuyo (pa akazi awa amene uli nawo) nkosaloledwa kwa iwe kukwatira akazi ena, (poonjezera pa chiwerengero cha akazi amene uli nawo). Ndiponso usasinthe (ofanana ndi chiwerengero chawo), (zonsezi nzoletsedwa kwa iwe) ngakhale kuti ubwino wawo utakusangalatsa, kupatula chimene dzanja lako lakumanja lapeza; ndipo Allah ndi M’yang’aniri wa chinthu chilichonse.
E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba za Mneneri pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kukadya, osati kukhala nkuyembekezera kupsa kwa chakudya. Koma mukaitanidwa, lowani. Ndipo mukamaliza kudya, balalikani; ndiponso musakambe nkhani zocheza. Chifukwa kutero kumavutitsa Mneneri. Ndipo iye amakuchitirani manyazi (kuti akutulutseni); koma Allah alibe manyazi ponena choona. Ndipo inu mukamawafunsa (akazi ake) za ziwiya, afunseni uku muli kuseri kwa Chotsekereza. Zimenezo ndi zoyera zedi ku mitima yanu ndi mitima yawo. Sikoyenera kwa inu kumvutitsa Mtumiki wa Allah, ndiponso nkosayenera kwa inu kukwatira akazi ake pambuyo pa imfa yake mpaka muyaya. Ndithu kutero ndi tchimo lalikulu kwa Allah.[330]
Chilichonse chimene mungachionetse kapena kuchibisa Allah achidziwa. Ndithu chifukwa chakuti Allah Ngodziwa chilichonse.
Ndithu Allah akumtsitsira madalitso Mneneri; nawonso angelo Ake (akumpemphelera chifukwa cha zochita zake zabwino). E inu amene mwakhulupirira! Mpemphereni madalitso ndi kumpemphera mtendere (chifukwa chokusonyezani njira yolungama).
Ndithu amene akumukwiyitsa Allah ndi kumuvutitsa Mtumiki Wake (ponyozera malamulo ake) Allah wawatembelera pa dziko lapansi (mpaka) pa tsiku la chimaliziro, ndipo wawakonzera chilango chosambula.
Ngati sasiya (machitidwe awo oipa) achiphamaso (achinyengo), ndi amene m’mitima mwawo muli matenda (a chiwerewere), ndi ofalitsa mbiri zoipa mu mzinda, tikukhwirizira kwa iwo (kuti uwathire nkhondo). Kenako sadzakhala m’menemo pamodzi ndi iwe, koma nthawi yochepa.
Anthu akukufunsa za (kudza kwa) nthawi (ya tsiku la chitsiriziro). Nena: “Kuzindikira kwa nthawiyo kuli ndi Allah (Yekha). Nanga nchiyani chikudziwitse kuti nthawi ya chimaliziro iri pafupi?”
Tsiku limene nkhope zawo zikatembenuzidwa ku Moto (zikutenthedwa), uku akunena: “Kalanga ife! Tikadamumvera Allah ndi kumveranso Mtumiki (s.a.w), (sibwenzi tili m’chilangomu).”
E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah (pokwaniritsa malamulo Ake, ndi kusiya zoletsedwa), ndipo nenani mawu olungama.
Share