Surah Al-Imran ( The Famiy of Imran )

Surah Al-Imran ( The Famiy of Imran ) - Chewa Aya count 200

Alif-Lâm-Mîm.
Allah (ndimmodzi), palibe winanso wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye Yekha, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi kuteteza chilichonse.[60]
Kale, kuti (mabukuwo) akhale chotsogolera anthu. Ndipo adavumbulutsa (Qur’an) yolekanitsa pakati pa choonadi ndi chonama.[61] Ndithudi, aja amene sadakhulupirire zizindikiro za Allah, adzakhala ndi chilango chaukali. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wobwezera (chilango mwaukali).
Iye ndi Yemwe amakulinganizani muli m’mimba mmaonekedwe anu mmene akufunira. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
(Anzeruwo amanena): “ E Mbuye wathu! Musaikhotetse mitima yathu pambuyo potiongola. Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu. Ndithudi, Inu Ndinu wopatsa kwambiri.
(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali.
Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”[62]
“Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.”
Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Allah ndi Chisilamu. Ndipo amene adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) sadatsutsane koma pambuyo powabwerera kuzindikira. (Adatsutsana) chifukwa cha dumbo lomwe lidali pakati pawo. Ndipo amene akukana zisonyezo za Allah, (Allah akamulanga pa tsiku la chiweruziro). Ndithu Allah Ngwachangu powerengera.
Ngati (osakhulupirira) atsutsana nawe, nena: “Ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Allah (ndadzipereka kwa Iye) pamodzi ndi amene anditsata.” Ndipo nena kwa onse adapatsidwa buku (Ayuda Ndi Akhrisitu) ndi osadziwa kulemba ndi kuwerenga (Arabu): “Kodi mwagonjera (kwa Allah)?” Ngati agonjera ndiye kuti aongoka. Koma ngati atembenukira kumbali, udindo wako ndikufikitsa uthenga basi. Ndipo Allah akuona akapolo Ake onse.
Zimenezo (kusalabadira malamulo a Allah) nchifukwa chakuti amanena: “Sudzatikhudza Moto koma masiku ochepa basi.” Ndipo zawanyenga pa chipembedzo chawo zomwe adali kupeka (kuti adzakhululukidwa kapena kulangidwa masiku ochepa okha).
Kodi zidzakhala zotani pamene tidzawasonkhanitsa tsiku lopanda chikaiko? Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira pa zomwe udachita. Ndipo iwo sadzaponderezedwa.
Nena “E Mbuye wanga! Mwini ufumu wonse. Mumapereka ufumu kwa yemwe mwamfuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa yemwe mwamfuna. Mumapereka ulemelero kwa yemwe mwamfuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamfuna. Ubwino wonse uli m’manja Mwanu. Ndithudi, Inu ndinu Wokhonza chilichonse.”
(Inu) mumalowetsa usiku mu usana (ndikukhala usana wautali monga m’nyengo yotentha). Ndipo mumalowetsa usana mu usiku (nkukhala usiku wautali monga m’nyengo yachisanu). Mumatulutsa cha moyo m’chakufa; ndipo mumatulutsa chakufa m’chamoyo. Ndipo mumapatsa rizq (chakudya) amene mwamfuna mopanda chiwerengero.”
Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi).
Nena: “Mvereni Allah ndi Mtumiki (wake).” Koma ngati akana, (Allah awakhaulitsa). Ndithudi, Allah sakonda anthu osakhulupirira.
(Kumbukirani) pamene adanena mkazi wa Imran (mayi wa Mariya), m’mapemphero ake): “Mbuye wanga! Ndapereka kwa Inu chimene chili m’mimba mwanga monga “waqf” (wotumikira m’kachisi Wanu). Tero landirani ichi kwa ine. Ndithudi, Inu ndinu Akumva, Wodziwa.”[67]
Choncho pamene adam’bala adati: “Mbuye wanga! Ndabala wamkazi!” Ndipo Allah akudziwa kwambiri chimene wabereka - “Ndipo wamwamuna (yemwe ndimayembekezera kubala) sali ngati wamkazi (amene ndamubala. Sangathe kutumikira moyenera mkachisi Wanu). Ndipo ine ndamutcha Mariya (wotumikira Allah). Ndipo ndikupempha Chitetezo Chanu pa iye ndi ana ake kwa satana wothamangitsidwayo.”
Choncho Mbuye wake adamulandira, kulandira kwabwino; namkulitsa, kukulitsa kwabwino. Adampatsa Zakariya kuti amulere. Nthawi iliyonse Zakariya akamulowera mchipinda mwake (mwa Mariya) m’kachisimo, amampeza ali ndi chakudya. Amati: “Iwe Mariya! Ukuzipeza kuti izi?” (Iye) amati: “Izi zikuchokera kwa Allah. Ndipo Allah amampatsa yemwe wamfuna popanda chiyembekezo (mwini wakeyo).”[68]
Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.”
(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndidzakhala bwanji ndi mwana pomwe ukalamba wandifikira, nayenso mkazi wanga ndichumba.” (Mngelo adati): “Ndimomwemo; Allah amachita chimene wafuna.”
(Iye) adati: “Mbuye wanga! Ndipatseni chizindikiro!” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu koma momangolozera (ndi chala) basi. Ndipo tamanda Mbuye wako, kutamanda kwambiri ndiponso umlemekeze (popemphera) madzulo ndi m’mawa.”
(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah.
Iye adzayankhula ndi anthu ali mchikuta ndi kuukulu (wake). Ndipo adzakhala mmodzi wa anthu abwino.”
(Mariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingakhale ndi mwana bwanji pomwe sadandikhudze munthu aliyense (wamwamuna)?” (Mngelo) adati: “Ndi momwemo. Allah amalenga chimene wafuna. Akafuna chinthu amanena kwa icho: ‘Chitika,’ ndipo chimachitikadi.”
“Ndipo (ndikhala) wotsimikizira zomwe zidalipo patsogolo panga (rn’buku la) Taurat. Ndipo ndadza kuti ndikulolezeni zina mwa zomwe zidaletsedwa kwa inu. Ndipo ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu (zotsimikizira uthenga wanga). Choncho, opani Allah ndi kundimvera (ine).”
“Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu; choncho mupembedzeni. Iyi ndiyo njira yoongoka.”
Koma pamene Isa (Yesu) adazindikira mwa iwo kusakhulupirira adati: “Ndani akhale athandizi anga kwa Allah (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?” Ophunzira ake adati: “Ife ndife athandizi a Allah (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Allah; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu ndi odzipereka kwa Allah (Asilamu).”
“Mbuye wathu! Tazikhulupirira zimene mwavumbulutsa, ndipo tamtsata Mtumikiyo. Choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboniwo.”
Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna kupha Isa (Yesu), koma Allah adachiwononga chiwembu chawocho. Allah Ngokhoza bwino zedi poononga ziwembu za anthu a chiwembu.
(Kumbukirani) pamene Allah adati: “Iwe Isa (Yesu)! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako yokhala ndi moyo (Ayuda sachita kanthu kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine ndiponso ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (iwe) ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo ndidzaweruza pakati panu pa zomwe mudali kusiyana.
Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam; adamulenga ndi dothi namuuza kuti: “Khala munthu.” Ndipo adakhaladi.[72]
Nena: “Inu eni buku (la Allah, Ayuda ndi Akhrisitu!) Idzani ku liwu lolingana pakati pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze aliyense koma Allah (Mmodzi Yekha), ndiponso tisamphatikize ndi chilichonse ndipo ena mwa ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m’malo mwa Allah.” Ngati atembenuka ndi kunyoza, nenani: “Ikirani umboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera malamulo a Allah).”
Ndithu anthu omwe ali oyenera kudzilumikiza ndi Ibrahim ndi amene adamutsata (m’nyengo yake) ndi Mtumiki uyu (Muhammad {s.a.w}) ndi amene amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo Allah ndi Mtetezi wa okhulupirira.
Ndipo gulu lina la amene adapatsidwa buku lidati (kwa anzawo): “Khulupirirani chomwe chavumbulutsidwa kwa Asilamu kumayambiliro kwa usana, ndipo chikaneni kumalekezero kwake (kwa usana) mwina angabwelere (kusiya Chisilamu).[73]
Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.”
Sichoncho (monga momwe akunenera)! Koma amene akukwaniritsa lonjezo lake napewa machimo (ndiyemwe ayenera kukhala wokondedwa kwa Allah). Ndithudi, Allah amakonda opewa machimo.
Ndithu anthu amene akusinthanitsa chipangano cha Allah ndi malumbiliro awo, (ndi zinthu za) mtengo wochepa, iwo alibe gawo labwino pa tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah sadzawayankhula (ndi mawu abwino); ndipo sadzawayang’ana (ndi diso la chifundo) pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso sadzawayeretsa (kumachimo awo); ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka.
Ndipo amene adzatembenuke pambuyo pa lonjezoli, (Allah adzawalanga chifukwa chakuti) iwo ngopandukiradi chilamulo cha Allah.
Ndipo amene angafune chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mmodzi mwa (anthu) otaika.
M’menemo adzakhala nthawi yaitali; ndipo sichidzapeputsidwa chilango kwa iwo, ndiponso sadzapatsidwa danga.
Nena: “Allah wanena zoona. Choncho tsatirani chipembedzo cha Ibrahim yemwe adali wolungama; sadali mwa ophatikiza Allah ndi mafano.”
Ndithudi, nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu (kuti azipempheramo) ndiyomwe ili pa Bakka (ku Makka); yodalitsidwa ndiponso ndichiongolo kwa anthu onse.[75]
M’menemo muli zizindikiro zoonekera (zozindikiritsa kupatulika kwake ndi ukale wake); ndi pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira; ndipo amene akulowamo amakhala m’chitetezo; ndipo Allah walamula anthu kuti akachite Hajj ku nyumbayo amene angathe kukonzekera ulendo wonka kumeneko. Ndipo yemwe angakane, (osapitako pomwe ali nazo zomuyenereza), ndithudi, Allah Ngwachikwanekwane pa zolengedwa Zake.
Nena: “E inu amene mudapatsidwa buku! chifukwa chiyani mukuzikana zizindikiro za Allah pomwe Allah ndi Mboni wa zonse zimene mukuchita?”
Nena: “ E inu amene mudapatsidwa buku! Chifukwa chani mukutsekereza anthu amene akhulupirira kuyenda pa njira ya Allah? Mukufuna kuti ikhote pomwe inu ndinu mboni (kuti ndi njira ya Allah yopanda choipa)? Komatu Allah sanyalanyaza zomwe mukuchita.”
Patsikulo nkhope zina zidzakhala zowala pomwe nkhope zina zidzakhala zakuda. Tsono amene nkhope zawo zidzakhala zakuda, (adzauzidwa): “Kodi mudakana ( Allah) pambuyo pa chikhulupiliro chanu? Choncho, lawani chilango (chopweteka) chifukwa cha zomwe mudali kuzikana.”
Tsono (anthu odala) omwe nkhope zawo zidzawale, adzakhala m’chifundo cha Allah. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali.
Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah).[78]
Sangakuvutitseni (adani anuwo, makamaka Ayuda) koma ndi timasautso (tochepa); ngati (atayesera) kukuthirani nkhondo, akufulatirani (kuthawa); ndipo kenako sangapulumutsidwe.
Adindidwa chidindo chakunyozeka paliponse pamene angapezeke kupatula (akagwira) chingwe (cha chipembedzo) cha Allah, kapena chingwe cha anthu (pothandizidwa ndi anthu ena. Koma paokha sangakhale ndi nyonga). Abwerera ndi mkwiyo wa Allah; ndipo chidindo chaumphawi chadindidwa pa iwo. Izi nchifukwa chakuti iwo sadali kukhulupirira mawu a Allah, ndipo amapha aneneri popanda choonadi. Izi nchifukwa chakutinso adanyoza ndi kulumpha malire.
Ndipo chabwino chilichonse chimene angachite sadzakanidwa nacho, (koma adzawalipira malipiro abwino). Ndipo Allah Ngodziwa za amene akuopa Iye.[79]
Fanizo la chimene akupereka mwaulere pa moyo uwu wa dziko lapansi, chili ngati mphepo yomwe mkati mwake muli chisanu chaukali, chagwera pa munda wa anthu omwe adadzichitira okha zoipa, n’kuuonongeratu. Si Allah amene adawachitira zoipa, koma iwo okha adadzichitira zoipa.[80]
(Kumbukira) pamene unachoka m’mawa kusiya banja lako kuti uwakonzere Asilamu malo omenyanira (nkhondo). Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[83]
(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi.
Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani).
Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
(Kuchita izi) nkuti adule gawo la osakhulupirira (kuti ena a iwo aphedwe) kapena awasambule ndi kuti abwelere ali olephera.[85]
Ndipo chimkereni mwachangu chikhululuko cha Mbuye wanu (kupyolera m’zochita zanu zabwino), ndi Munda (Wake) umene Kutambasuka kwake (mulifupi) kuli ngati kumwamba ndi pansi, (womwe) wakonzedwa kuti ukhale wa oopa Allah.[87]
Zidapita njira za zilango zambiri zosiyanasiyana zomwe adapatsidwa amene adalipo patsogolo panu. Tero tayendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a anthu otsutsa.
Uku ndi kulengeza poyera kwa anthu (onse); komanso chiongoko ndi ulaliki kwa (anthu) oopa Allah!
Ndipo musafooke (pomenya nkhondo), ndiponso musadandaule (ndi mavuto amene akupezani) pakuti ndinu apamwamba, ngati mulidi okhulupirira.
Ngati mwavulazidwa, naonso anthuwo avulazidwanso molingana. Ndipo amenewo ndimasiku, timawapatsa anthu mosinthanasinthana. (Ichi chachitika) kuti Allah aonetse poyera amene akhulupirira (moona; choncho sadathawe konse); ndi kuti awachite ena mwa inu kukhala Shuhadaa (ofera pankhondo yoyera). Komatu Allah sakonda anthu ochita zoipa.[89]
Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe Allah asadawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo cha Allah mwa inu ndi kuwaonetseranso poyera opirira (pa nkhondo ya Allah)?
Munthu aliyense sangafe pokhapokha mwa chilolezo cha Allah, (ndi kukwanira) nthawi yake yolembedwa. Ndipo amene akufuna mphoto ya pa dziko la pansi, timpatsa pompo; ndipo amene akufuna Mphoto ya tsiku lachimaliziro tidzampatsa konko. Ndipo, tidzawalipira (zabwino) othokoza.[92]
(Anthu olungamawa) kunena kwawo sikudali kwina koma ankati: “Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kupyola malire kwathu m’zinthu zathu. Ndipo limbikitsani mapazi athu (panjira Yanu) ndipo tithandizeni ku anthu osakhulupirira.”
Komatu Allah ndiye Mbuye wanu. Iye Ngwabwino kwabasi kuposa athandizi (ena onse).
Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa.
Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira.[94]
Kumbukirani pamene mudali kuthawa mwa liwiro popanda kumvera aliyense; pomwe Mtumiki adali kukuitanani, ali pambuyo panu. Ndipo (Allah) Adakupatsani madandaulo pa madandaulo. (Motero wakukhululukirani) kuti musadandaule pa zomwe zakudutsani, ngakhalenso (pa masautso) omwe akupezani. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita.
Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.”[95]
Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa.
Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi).
Ndipo ngati mumwalira kapena kuphedwa (n’chimodzimodzi), ndithudi nonsenu mudzasonkhanitsidwa kwa Allah.
Chifukwa cha chifundo chochokera kwa Allah, uli woleza mtima kwa iwo, (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}). Ndipo ukadakhala waukali, wouma mtima, ndithudi, akadakuthawa pamaso pako. Choncho akhululukire ndi kuwapemphera chikhululuko (kwa Allah); ndipo chita nawo upo pa zinthu. Ndipo ngati watsimikiza, tsamira kwa Allah (basi, ndi kuchita chimene watsimikiza kuchichita). Ndithudi, Allah amakonda oyadzamira Kwake (odalira Iye).
Nkosatheka kwa Mtumiki kuchita chinyengo. Ndipo amene achite chinyengo adzadza pa tsiku lachimaliziro ndi zomwe adazichitira chinyengo. Kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zomwe adachita. Ndipo sadzaponderezedwa.
Kodi amene akutsata chokondweretsa Allah angalingane ndi yemwe wabwerera ndi mkwiyo wochokera kwa Allah, ndipo Jahannam nkukhala malo ake? Taonani kuipa kumalo obwerera!
Pamene sautso lidakupezani lomwe inu mudawathira nalo (adani anu) lochulukirapo kawiri, mudanena: “Lachokera kuti (sautso) ili?” Nena: “Ilo lachokera kwa inu eni (chifukwa cha kunyoza lamulo lomwe adakuuzani). Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.”
Ndipo sautso lomwe lidakupezani tsiku lomwe adakumana magulu awiri ankhondo, lidali mwa chilolezo cha Allah ndikutinso awaonetsere poyera okhulupirira.
Ndi kuwadziwitsa amene adachita uchiphamaso. Iwo adauzidwa: “Bwerani, menyani (nkhondo) pa njira ya Allah kapena mwatsekereze (adani kwa ife).” Adati: “Tikadadziwa kuti pali kumenyana, ndithudi, tikadakutsatani (koma kumeneko kuli kuphedwa kokhakokha basi).” Iwo tsiku limenelo adali pafupi ndikusakhulupirira kuposa chikhulupiliro (ngakhale kuti masiku onse amasonyeza Chisilamu mwa chiphamaso). Akunena ndi milomo yawo zomwe sizili m’mitima mwawo. Koma Allah akudziwa bwinobwino (zonse) zomwe akubisa.
Akukondwera pa zimene wawapatsa Allah kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo akufunira mafuno abwino amene sadakumane nawo omwe ali pambuyo pawo, (omwe alipobe pa dziko lapansi) ponena kuti pa iwo sipadzakhala mantha kapena kudandaula.
Omwenso adauzidwa ndi anthu (olembedwa ganyu ndi Akafiri aku Makka) kuti: “Anthu Akusonkhanirani. Choncho aopeni.” Koma (zonenazo) zidawaonjezera chikhulupiliro (Asilamu). Ndipo adati: “Allah akutikwanira, ndipo Iye ndi Mtetezi wabwino koposa.”
Ndithudi, amene asinthanitsa kusakhulupirira ndi chikhulupiliro, sangathe kumvutitsa Allah ndi chilichonse. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chopweteka.
Ndithu Allah wamva liwu (lonyogodola) la omwe (Ayuda) anena kuti: “Allah ngosauka, ndipo ife ndife olemera.” Tazilemba zimene anena, ndipo (talembanso) kupha kwawo aneneri popanda choonadi. Ndipo tidzawauza (tsiku la chiweruziro): “Lawani chilango cha Moto owotcha.”[101]
Ndipo ngati akutsutsa iwe (Mtumiki Muhammad (s.a.w}, sichachilendo) adatsutsidwanso atumiki patsogolo pako omwe adadza ndi zisonyezo zoonekera ndi mabuku anzeru, ndi mabukunso ounika.
Munthu aliyense adzalawa imfa. Ndithudi, mudzalipidwa malipiro anu mokwanira tsiku lachimaliziro. Ndipo amene adzatalikitsidwe ndi Moto nalowetsedwa ku Munda wamtendere, ndiye kuti wapambana, (kupambana kwakukulu), ndipo moyo wapadziko lapansi sulikanthu koma ndichisangalalo chonyenga basi.[104]
Ndithu mudzayesedwa m’chuma chanu ndi miyoyo yanu; ndipo mudzamva masautso ambiri kuchokera kwa omwe adapatsidwa mabuku kale ndiponso kuchokera kwa omwe akuphatikiza Allah ndi zinthu zina (Arab), koma ngati mupirira ndi kudzisunga ku zomwe mwaletsedwa ndi Allah, (ndiye kuti mwachita chinthu chabwino kwambiri) pakuti zinthu izi (ndi zinthu zazikulu) zofunika munthu kuikirapo mtima.
Ndipo (akumbutse) pamene Allah adamanga chipangano ndi amene adapatsidwa buku (ndi kuwauza) kuti ndithudi mudzalifotokoze mwatsatanetsatane (bukulo) kwa anthu, ndipo musadzalibise. Koma Adaliponya kumbuyo kwa misana yawo naligulitsa ndi mtengo wochepa. Taonani kuipa chimene adagula (chimene adasankha)!
Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.”
“E Mbuye wathu! Ndithudi, ife tamva woitana akuitanira ku chikhulupiliro kuti: ‘Khulupirirani Mbuye wanu,’ ndipo takhulupirira. E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kutifafanizira zoipa zathu, ndipo mutenge mizimu yathu tili pamodzi ndi anthu abwino.”
Choncho Mbuye wawo adawavomereza (zopempha zawo ponena kuti): “Ndithudi, ine sindidzasokoneza (khama la) ntchito yabwino kwa ochita ntchito mwa inu, kaya atakhala mwamuna kapena mkazi, (pakuti) inu ndinu amodzi. Choncho amene asamuka (kumidzi yawo mwachifuniro chawo), naapirikitsidwa m’midzi yawo navutitsidwa pa njira Yanga, namenya nkhondo ndikuphedwa, ndithudi, ndiwafafanizira zolakwa zawo. Ndipo ndidzawalowetsa m’Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Amenewo ndimalipiro ochokera kwa Allah, ndipo kwa Allah kuli malipiro abwino.”
Ndichisangalalo chochepa; kenako malo awo ndi kumoto wa Jahannam. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!
Koma amene aopa Mbuye wawo (potsatira zolamulidwa ndi kuleka zoletsedwa) adzapeza Minda yamtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi patsogolo pake). Adzakhala m’menemo nthawi yaitali, ndi phwando lochokera kwa Allah. Ndipo zomwe zili kwa Allah nzabwino kwa anthu abwino (kuposa zosangalatsa za dziko lapansi).
Share