Surah Al-Furqan (The Criterion )

Surah Al-Furqan (The Criterion ) - Chewa Aya count 77

Watukuka Mwini kupereka madalitso, Yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo Wake kuti ikhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse.
Ndipo m’malo mwa Iye (Mulungu weniweni, osakhulupirira) adzipangira milungu yomwe siilenga chilichonse koma iyo ndiyomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza. Ndiponso ilibe mphamvu zoperekera irnfa ndi moyo, ngakhale kuukitsa akufa.
Ndipo osakhulupirira akunena: “Ichi sikanthu (Qur’an imene Muhammad {s.a.w} wadza nayo) koma ndi chonama chimene wachipeka, ndipo pachimenechi amthandiza anthu ena (eni mabuku).” Kunena zoona, iwo (osakhulupirira) adza ndi chinyengo ndi bodza (pazonena zawozi). [292]
Ndipo (osakhulupirira) akunena: “Iyi (Qur’an) ndi nthano za anthu akale zomwe (Muhammad {s.a.w}) adazilembetsa. Choncho zikulakatulidwa kwa iye m’mawa ndi madzulo (kuti aloweze).”
Nena: “Adaivumbulutsa Yemwe akudziwa zobisika za m’thambo ndi m’nthaka. Ndithu Iye ali Wokhululuka; Wachisoni, (nchifukwa chake sakukulangani mwachangu pazimene mukunenazi).”
Ona momwe akukuponyera mafanizo (omwe sali oyenerana nawe, nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa wamisala, wabodza, wophunzitsidwa ndi anthu ena) choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yoongoka yokunenera).
Watukuka Mwini kupereka madalitso ambiri, Yemwe akafuna, akuchitira zabwino kuposa zimenezi, (adzakupatsa pa tsiku lachimaliziro) Minda yamtendere yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; ndipo adzakupangira nyumba zikuluzikulu zachifumu.
Koma akutsutsa zanthawi ya Qiyâma. ndipo tawakonzera Moto woyaka (iwo) amene akutsutsa zanthawi ya Qiyâma (ya chimaliziro).
(Motowo) ukadzawaona (naonso nkuuona) kuchokera pa malo apatali, (iwo) adzamva mkwiyo wa Motowo ndi mkokomo wake.
Ndipo akadzaponyedwa m’menemo, pamalo opanika uku manja atanjatidwa chakukhosi, pamenepo adzaitana imfa (kuti iwafike, afe apumule ku masautsowo).
(Tidzawauza): “Lero musaitane imfa imodzi, koma itanani imfa zambiri (ndipo simupeza mpumulo koma mazunzo okhaokha).”
Nena (kwa osakhulupirira): “Kodi izi ndizo zabwino, kapena munda wamuyaya umene alonjezedwa oopa Allah kuti udzakhale mphoto (yabwino) kwa iwo ndi kobwerera (kotamandika)?”
“M’menemo adzapeza chilichonse chomwe adzafune. Adzakhala nthawi yaitali. Mtenderewu ndi lonjezo lochokera kwa Mbuye wako pa iwo lomwe adampempha kuti adzawakwaniritsire.”
Ndipo (kumbuka) tsiku limene adzawasonkhanitse (awa osakhulupirira) ndi omwe adali kuwapembedza (monga Isa (Yesu), Uzairi ndi angelo) kusiya Allah; adzanena (Allah kuuza amene ankalambiridwawo): “Kodi ndinu mudasokeretsa anthu angawa, kapena ndi okha adasokera njira.”
Adzanena: “E ulemelero ukhale kwa inu! Sizidali zoyenera kwa ife kudzikonzera atetezi mmalo mwa Inu, (nanji kuuza anthu kuti azitipembedza). Koma mudawasangalatsa iwo ndi makolo awo kufikira adaiwala malangizo (Anu). Ndipo adali anthu oonongeka.”
(Allah adzati): “Ndithu yakutsutsani (milungu yanuyo) pa zimene mwanena (kuti iwo adakusokeretsani). Ndipo simutha kudzichotsera (chilango) ngakhale (kupeza) chithandizo.” Ndipo, ndithudi amene achite zoipa mwa inu, tidzamulawitsa chilango chachikulu.
۞ Ndipo amene alibe chiyembekezo chakukumana Nafe akunena: “Bwanji angelo satumidwa kwa ife? Kapena timuone Mbuye wathu (kuti atitsimikizire kuti ndiwedi Mtumiki wake”? Ndipo Allah akunena): “Ndithu adzitukumula mmitima mwawo ndipo anyoza; kunyoza kwakukulu.”
Tsiku lowaona angelo, sikudzakhala chisangalalo tsiku limenelo kwa ochimwa, (koma lidzakhala tsiku lochoka moyo wawo). Ndipo adzanena (tsiku limenelo): “Ha! Allah atitchinjirize kwambiri.” (Koma mawu awa, sadzathandiza chilichonse).
Ndipo tidzaidzera ntchito iliyonse (yabwino) imene adachita, ndipo tizaichita monga fumbi louluka (ponseponse, yopanda phindu chifukwa cha kusakhulupirira Allah kwawo.)
Anthu a ku Munda wamtendere tsiku limenelo adzakhala ndi mokhala mwabwino, ndi pamalo pampumulo wabwino.
Ndipo akumbutse za tsikulo pomwe thambo lidzang’ambika ndikudzetsa mitambo (yomwe idzachititsa chimdima ponseponse). Ndipo angelo adzatsika ambirimbiri.
“E tsoka langa! Ndikadapanda kumchita uje kukhala bwenzi wanga. (nkadapulumuka lero).”
“Ndithu adandisokeretsa kufikira ndidasiya ulaliki (wa Allah) utandidzera. Zoonadi, satana amataya munthu (akaona kuti wamgwetsa m’chionongeko).”
Ndipo Mtumiki (adasuma kwa Mbuye wake) adati: “E Mbuye wanga! Ndithu anthu anga aisandutsa Qur’aniyi kukhala chinthu chosiidwa, (sakuiwerenga. Ndiponso sakutsata ziphunzitso zake).”
Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji Qur’an yonse siidavumbulutsidwe nthawi imodzi kwa iye? Momwemo (ukuoneramo, tikuitumiza pang’onopang’ono) kuti tiulimbikitse mtima wako ndi iyo, ndipo taiyala, mkayalidwe kabwino.
Ndipo sangakubweretsere fanizo lililonse koma tikubweretsera choonadi (choyankha fanizolo ndi kukudziwitsa) ndi kumasulira kwabwino.
Ndipo onse tidawaponyera mafanizo; ndiponso onse tidawaononga motheratu (pamene adakana kutsatira malamulo athu).
Ndipo ndithu iwo (Aquraish, m’maulendo awo) adafika pa mudzi (Sodomu ndi Gomora) womwe mvula yoipa (ya sangalabwi) idawavumbwa. Kodi sadali kuuona? Koma sadali kuyembekezera zakuuka ku imfa.
Ndipo akakuona (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}), amangokuchitira chipongwe: “Kodi uyu ndi yemwe Allah wamtuma kuti akhale mtumiki?”
Kodi wamuona yemwe wachichita chilakolako chake (chimene akuchikonda) kukhala mulungu wake? Kodi iweyo ungathe kukhala muyang’aniri wa iye (kotero kuti ungamkakamize chomwe safuna)?
Kodi sudaone momwe Mbuye wako wautambasulira mthunzi? Akadafuna, akadauchita kuti ukhale wokhazikika (wosasinthasintha). Ndipo talichita dzuwa kukhala chisonyezo chake. [294]
Kenaka tikuufumbata kwa Ife m’kufumbata kwapang’onopang’ono (kufikira wonse wutachoka).
Ndipo Iye ndi amene wakuchitirani usiku kukhala monga chovala, ndipo tulo monga mpumulo, ndipo usana wauchita kukhala monga nthawi youka (kuimfa).
Ndiponso ndithu tikuigawa (mvulayi) pakati pawo kuti akumbukire, ndipo anthu ambiri akukana (kuthokoza Allah) koma kupitiriza kusakhulupirira.
Ndipo tikadafuna, tikadatuma mchenjezi wawowawo m’mudzi uliwonse, (koma tatuma Muhammad {s.a.w} kuti akhale mchenjezi wa onse).
Choncho usawamvere osakhulupirira koma limbana nawo ndi iyo (Qur’an); kulimbana kwakukulu.
Ndipo Iye ndiye adalenga munthu ndi madzi ndiponso adamchitira chibale cha magazi ndi chibale cha ukwati. Ndipo Mbuye wako ali Wokhoza chilichonse.
Ndipo (ena mwa anthu) akupembedza zina zake kusiya Allah, zomwe sizingawathandize ndiponso sizingawadzetsere masautso (atasiya kuzipembedza). Ndipo wosakhulupirira ndi mthandizi wa zoipa poukira Mbuye wake.
Ndipo Ife sitidakutume koma kuti ukhale wouza nkhani zabwino (okhulupirira); ndi wochenjeza (osakhulupirira).
Nena: “Sindikupemphani malipiro pa zimenezi (zomwe ndikukuphunzitsani) koma amene afuna ayende pa njira yopita kwa Mbuye wake, (popanda chopereka).”
Ndipo tsamira kwa (Allah) Wamoyo, Wamuyaya Yemwe saafa. Ndipo mulemekeze pomtamanda ndi mbiri Zake. Ndipo Iye akukwana kudziwa bwinobwino machimo a akapolo Ake.
Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zimene zikupezeka mkati mwake. (Adazilenga) m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, m’kukhazikika kodziwa Yekha). Iye Ngwachifundo chambiri; mufunseni wodziwa za Iye.
Ndipo akauzidwa (kuti): “Mulambireni (Allah) Wachifundo chambiri.” Amati: “Ndani Wachifundo chambiri? Kodi tilambire Yemwe iwe ukutilamula?” (Mawu amenewa) adawaonjezera iwo mwano.
Ndipo Iye ndi Yemwe adapanga usiku ndi usana kuti zizitsatana (ndikusinthana). (Izi zingapindulitse) kwa amene afuna kukumbukira kapena (amene) afuna kuthokoza.
Ndi omwe amapititsa nthawi ina ya usiku uku akulambira ndi kuimilira chifukwa cha kulemekeza Mbuye wawo.
Chilango chidzawonjezeredwa kwa iye tsiku la Qiyâma, ndipo adzakhala m’chilango muyaya uku ali wonyozeka.
Iwo adzalipidwa zipinda (za pamwamba ku Jannah) chifukwa cha mavuto omwe adawapirira. Ndipo akalandira m’menemo ulemu ndi mtendere.
Akakhala m’menemo nthawi yaitali; akongolerenji malo okhazikika ndi kukhalamo.
Nena: “Ndithu Mbuye wanga sakadalabadira chilichonse pa inu pakadapanda mapemphero anu, (akadakulangani pompano pa dziko lapansi.) Komabe inu mwatsutsa (uthenga wa aneneri). Choncho chilango chidzakugweranibe.”
Share