Surah Al-Hijr ( The Rocky Tract )

Surah Al-Hijr ( The Rocky Tract ) - Chewa Aya count 99

۞ Alif-Lâm-Râ. Izi ndi Aaya (ndime) za m’buku (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika,) ndi Qur’an yomveka bwino.
Nthawi zambiri omwe sadakhulupirire (pamene adzakhala m’Moto) adzalakalaka kuti akadakhala okhulupirira (pamoyo wa pa dziko lapansi).
Asiye azidya (chakudya monga momwe zidyera nyama) ndi kusangalala; ndipo chiyembekezo chiziwatangwanitsa ndi kuwanyenga; posachedwa adziwa (kuti zimene amaziyembekezerazo nzabodza).
Ndipo sitidaononge mudzi uliwonse (m’midzi yochita zoipa) koma udali ndi nthawi yake (youwonongera) yodziwika.
Ndipo palibe mtundu wa anthu umene ungaitsogolere nthawi yake (yofera) kapena kuichedwetsa (itakwana kale).
Ndipo (osakhulupirira) akunena (mwachipongwe) “E iwe amene wavumbulutsiridwa ulaliki! Ndithudi ndiwe wamisala.”
“Bwanji iwe osatibweretsera angelo (kuti akuchitire umboni) ngati uli mmodzi waonena zoona?”
(Allah akuwauza:) “Ife sititsitsa angelo pokhapokha kutatsimikizika (tikawatuma kukapereka chilango kwa anthu). Ndipo pamenepo sangapatsidwe nthawi.”
Koma saikhulupirira Qur’aniyi chikhalirecho mafanizo a anthu oyamba awadutsa (ndipo aona momwe tidawaonongera).
Ndipo tikadawatsekulira (awa osakhulupirira) khomo lakumwamba ndipo nkukhala akukwera m’menemo (ndi kutsika monga momwe amafunira kuti zimenezo zikhale chozizwitsa cha Mtumiki),
Akadati: “Ndithu maso athu aledzera; (iyayi) koma ndife anthu olodzedwa (tikuona zomwe sindizo).”[245]
Ndithudi, kumwamba tidaikako “Buruji” (njira momwe zikuyendamo nyenyezi) ndipo tidakukongoletsa kwa okuwona.
Ndipo tidakuteteza kwa satana aliyense wopirikitsidwa (kumwambako akafuna kukamvetsera zimene zikunenedwa kumeneko).
Kupatula amene amamvetsera mobera; ndipo pompo chinsakali chamoto choonekera chimamtsata.
Ndipo mmenemo takupangirani zinthu zoyendetsa moyo (wanu zakudya ndi zakumwa ndi zina zotere) ndiponso (tidakupatsani ana ndi ziweto) zomwe inu simungathe kuzidyetsa. (Ife ndife amene tikuzikonzera chakudya chawo, osati inu).
Ndipo palibe chinthu chilichonse koma gwero lake likuchokera kwa Ife; ndipo sitichitsitsa koma mwamlingo wodziwika (osati mwachisawawa).
Ndipo timazitumiza mphepo zitasenza madzi, ndipo madziwo tikuwatsitsa kuchokera kumitamboyo; kenako tikukumwetsani madziwo (tikukumwetseraninso ziweto zanu, mitengo yanu ndi zina), ndipo inu si amene mukuwasunga (madziwo).
Ndipo ndithudi, Ife ndife omwe timapereka moyo, ndi kupereka imfa. Ndiponso Ife ndi Amlowam’malo (a chinthu chilichonse chimene chikusiidwa chopanda mwini).
Ndipo ndithu tikuwadziwa mwa inu amene atsogola (amene adafa kale), ndipo ndithu tikuwadziwanso amene atsalira (ali ndi moyobe ndi amene sanabadwe).
Ndipo ndithu palibe chikaiko, Mbuye wako ndi Yemwe adzawasonkhanitsa (pambuyo pa imfa kuti adzawaweruze). Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa chilichonse.
Ndipo ndithu tidamlenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera, osinthika mtundu;
Ndipo (kumbuka) pamene Mbuye wako adauza angelo (kuti): “Ndithu Ine ndilenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
Adati: “Sindingamuweramire munthu yemwe mwam’lenga ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
(Allah) adati: “Choncho choka m’menemo; ndithu iwe ndiwe wopirikitsidwa (ku chifundo Changa).”
(Iblis) adati: “Mbuye wanga choncho ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwe kwa akufa.”
(Allah) adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi mwa opatsidwa nthawi (danga).”
Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (ikadzafika nthawi imeneyo, udzafa).”
(Satana) adati: “Mbuye wanga! Pakuti mwanena kuti ndine wosokera, choncho ndikawakometsera za m’dziko (kufikira kuti akakulakwireni), ndithu ndikawasokeretsa onse.”
(Allah) adati: “Iyi ndinjira yoongoka yobwerera kwa Ine (ndipo adzandidzera akadzafuna).”
Ndithudi owopa Allah adzakhala m’minda ndi akasupe (omwe adzakhala patsogolo pawo).
(Ndipo tidzawauza) “Lowani m’menemo mwamtendere, mosatekeseka.”
Ndipo tidzawachotsera mfundo za chidani zomwe zidali m’mitima mwawo; (adzakhala) mwachibale, (mokondana,) atakhala pa mipando yachifumu atayang’anizana nkhope.
Auze akapolo anga kuti ndithu Ine ndine Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.
Pamene adalowa kwa iye ndikunena: “Salaman (Mtendere!)” (Iyenso adawayankha: “Mtendere ukhalenso pa inu.” Ndipo Pamene adaona kuti akana chakudya) Adati: “Ndithu ife tikukuopani.”
Iwo adati: “Usaope! Ife tikukuuza nkhani yabwino ya (kuti ubala) mwana wanzeru kwambiri.”
Iye adati: “Ha! Mukundiuza nkhani iyi pomwe ukalamba wandifikira? Kodi nkhani yabwinoyi mukundiuza mnjira yotani?”
Iwo adati: “Takuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi; choncho, usakhale mwa otaya mtima.”
Iye adati: “(Ine sinditaya mtima ndi chifundo cha Allah. Ndipo) palibe angataye mtima ndi chifundo cha Allah, koma wosokera basi (yemwe sazindikira ukulu wa Allah).”
Iye adati: “Nanga cholinga chanu china nchiyani, E inu otumidwa?”
Ndipo pamene atumikiwo adawadzera anthu a Luti (ali mmaonokedwe amunthu)
(Luti) adati: “Ndithudi, inu ndi anthu osadziwika (sitikudziwani).”
Iwo adati: “Inde, ife takudzera ndi zomwe (iwo) adali kuzikaikira, (zomwe ndi chilango chawo).”
“Ndipo tadza kwa iwe ndi (chinthu) choonadicho, ndithu ife ndi owona (pazimene tinenazi).”
“Choncho, choka ndi banja lako mkati mwa usiku; ndipo iwe udziwatsata pambuyo pawo; tsono aliyense wa inu asayang’ane kumbuyo (akamva mkokomo wachilango chochokera kumwamba, kuopa kuti angafe), ndipo yendani (mwachangu) kunka komwe mukulamulidwa.”
Ndipo adadza (kwa Luti) anthu a m’mudziwo akusangalala (poona kuti kwadza alendo okongola kuti achite nawo zadama).[246]
(Mneneri Luti) adati: “Ndithu awa ndialendo anga; choncho musandiyalutse (pochita nawo zadama).”
“Muopeninso Allah, ndipo musandichititse manyazi (pamaso pawo).”
Iwo adati (kwa Mneneri Luti): “Kodi sitidakuletse kulandira anthu (achilendo)?”
Iye adati: “Awa (akazi onsewa ali ngati) ana anga. Ngati inu ndinu ochita (chimene chalamulidwa, akwatireni; musachite zauve ndi alendowa).”
Ndikulumbira moyo wako, ndithu iwo m’kuledzera kwawo (ndi zoipa) akungoyumbayumba.
Choncho mkuwe wa chilango udawagwira pamene dzuwa linkatuluka.
Choncho (midziyo) tidaigadabula kumwamba kukhala pansi, (pansi kukhala kumwamba); ndipo tidawavumbwitsira mvula yamiyala (yotentha) ya moto.
Ndithudi, (m’nkhani iyi) muli malingaliro (aakulu) kwa anthu olingalira zinthu.
Ndipo (midzi) iyi (yomwe tidaiwononga chotereyi), ili chikhalire m’njira moyenda anthu (ndipo iwo akuona zizindikiro zake).
Ndipo ndithu anthu a m’nkhalango (anthu a Mneneri Shuaib) adali ochita zoipa kwabasi.
Choncho, tidawalanga. Ndipo (maiko) awiriwa ali m’njira zoonekera, (momwe Aquraish amadutsa pa maulendo awo).
Iwo adali kujoba nyumba m’mapiri mwamtendere (ankaboola mapiri kuwasandutsa nyumba zawo).
Sichidawathandize (chuma) chomwe ankachipeza (ngakhalenso zimene ankazichita).
Sitidalenge thambo ndi nthaka ndi (zonse) zapakati pake koma (kulimbikitsa) choonadi. Ndipo palibe chikaiko, Qiyâma idza. Choncho mkhululukire kukhululuka kwabwino (aliyense wokuchitira zoipa).
Ndithudi, Mbuye wako, Iye ndi Mlengi wa zonse, Wodziwa kwambiri.
Ndipo ndithu takupatsa (Ayah izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga kawirikawiri, (Sûrat Al-Fatihah), ndi Qur’an yolemekezeka.
Usatong’olere maso ako (kuyang’ana) zimene tawasangalatsa nazo mitundumitundu ya mwa iwo (monga chuma cha anthu osakhulupirira). Usawadandaulirenso iwo ndipo tsitsa phiko lako kwa okhululupirira, (uwafungatire).
Ndipo nena: “Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera (sindikubisa chilichonse kuopera kuti chingakutsikireni chilango).”
Monga momwe tidatsitsira (chilango) kwa amene adadzigawa m’magulu.
Omwe aichita Qur’an kukhala magawomagawo; (zina nkuzikhulupirira, zina nkuzitsutsa).
(Allah akudzilumbilira kuti:) Pali Mbuye wako, tidzawafunsa onse (tsiku la Qiyâma).
Choncho, lengeza zimene ukulamulidwa, ndipo uwapewe opembedza mafano, (usaope chilichonse kwa iwo).
Ndithu Ife tikukwanira kukuteteza ku (zoipa za) achipongwe.
(Koma pirira), lemekeza Mbuye wako pamodzi ndi kumtamanda (ndi rnbiri Zake zabwino) ndipo khala mwa olambira (Allah.)
Share