Surah Quraish

Surah Quraish - Chewa Aya count 4

Cholinga chakuwachita Maquraish kuti apitirize chizolowezi chawo,[486]
Apitilize chizolowezi chawo choyenda nthawi ya dzinja (kunka ku Yemen) ndi nthawi yachirimwe (kunka ku Sham kukachita malonda, mosatekeseka ndi mopanda mantha).
Choncho, amupembedze Mbuye wa Nyumba iyi (Al-Kaaba amene adachititsa kuti athe kuyenda maulendo awiriwo).
Yemwe amawadyetsa (nthawi imene Arabu anzawo) ali m’njala, ndipo amawapatsa chitetezo (pomwe anzawo) ali ndi mantha.
Share