Surah Yunus ( Jonah )

Surah Yunus ( Jonah ) - Chewa Aya count 109

Alif-Lam-Ra. Izi ndi Ayah za m’buku lanzeru. (Lokamba zanzeru zokhazokha).
Kodi nchodabwitsa kwa anthu kuti tamuvumbulutsira (chivumbulutso) munthu wochokera mwa iwo (yemwe ndi Muhammad {s.a.w}) kuti: “Chenjeza anthu ndipo awuze nkhani yabwino amene akhulupirira kuti iwo adzapeza ulemelero waukulu kwa Mbuye wawo?” Osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wa matsenga (mfiti) wowonekera.’’[214]
Ndithu Mbuye wanu ndi Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zonse za m’menemo) m’masiku asanu ndi limodzi; (masiku omwe palibe yemwe akuwadziwa kutalika kwake koma Iye Yekha), kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, kukhazikika kwake akukudziwa ndi Iye Yekha basi). Amayendetsa zinthu (za zolengedwa Zake). Palibe muomboli (woombola wina) koma pambuyo pa chilolezo Chake (Allah). Uyo ndiye Allah Mbuye wanu; choncho mupembedzeni Iye. Kodi simungakumbukire (kuti mafanowo si milungu)?
Kobwerera kwanu nonsenu ndi kwa Iye. Ili ndilonjezo la Allah loona. Ndithu Iye ndi Yemwe adayamba kulenga (zolengedwa), ndiponso ndi Yemwe adzazibwereza (pambuyo pa imfa) kuti adzawalipire amene adakhulupirira ndi kumachita zabwino mwa chilungamo. Ndipo amene sadakhulupirire, akapeza zakumwa za madzi owira ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.
Iye (Allah) ndiYemwe adapanga dzuwa kukhala lowala, ndi mwezi kukhala wounika; ndipo adaukonzera mbuto (masitesheni) kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero chake. Allah sadalenge zimenezo koma mwachoonadi (ndi cholinga cha nzeru). Akufotokoza Ayah (Zake) kwa anthu ozindikira.[215]
Iwowo (onse) malo awo ndi ku Moto chifukwa cha zomwe adazipeza (m’njira zosayenera).
Mapemphero awo m’menemo adzakhala kunena: “Subuhanaka Lahuma’ Ulemelero ndi Wanu, E Inu Allah!” Ndipo kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala kunena: “Salaam (alayikum’) Mtendere (ukhale pa inu).” Ndipo duwa yawo yomaliza (idzakhala kuyamika ponena kuti) “Alham’du Lillah Rabil a’lamin’. Kuyamikidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zolengedwa.”[216]
Ndipo Allah akadakhala kuti akuwapatsa anthu zoipa mwachangu (zomwe iwo akuzifulumizitsa) monga mmene amawapatsira mwachangu zabwino (akamupemphamo, ndiye kuti) ikadalamulidwa nthawi yawo (yowaonongera koma Allah amawamvera chisoni), koma amene saopa kukumana Nafe tikuwasiya akuyumbayumba m’zoipa zawo.
Kenako takupangani inu (Asilamu) kukhala olowa m’malo mwawo pa dziko pambuyo pawo kuti tione mmene mungachitire (zabwino kapena zoipa).
Nena: “Allah akadafuna, sindikadakuwerengerani Qur’aniyi ndiponso sakadakudziwitsani Qur’aniyo, ndidakhala pakati panu moyo wanga (zaka zambiri) isadavumbulutsidwe, (simudandimve ndikunena chilichonse cha utumiki). Kodi mulibe nzeru?”
Ndipo iwo akupembedza milungu yina kusiya Allah, yomwe singathe kuwapatsa masautso (ngati atasiya kuipembedza) ndiponso siyingathe kuwapatsa chithandizo (ngati atalimbika kuipembedza) ndipo akunena: “Iwo (mafanowo) ndi aomboli athu kwa Allah.” Nena: “Kodi mukumuuza Allah zomwe sakudziwa kumwamba ndi pansi? Wapatukana Allah Ndipo watukuka kuzimene akum’phatikiza nazo.”
Ndipo ndithudi anthu kalero (m’nthawi ya Adam) adali mpingo umodzi (opembedza Allah), koma adasiyana (pambuyo pake). Ndipo pakadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako, lomwe lidatsogola (lakuti adzawalanga tsiku la Qiyâma), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo m’zomwe adali kusiyana.[218]
Ndipo akunena: “Kukadakhala kuti chinatsitsidwa kwa iye chizindikiro (chotsimikizira uneneri wake) chochokera kwa Mbuye wake (chomwe takhala tikuchipempha nthawi ndi nthawi).” Nena (kwa iwo): “Ndithu kudziwa zobisika nkwa Allah Yekha. Choncho dikirani (chiweruzo cha Allah) inenso pamodzi nanu ndine mmodzi wa odikira.”
Ndipo tikawalawitsa anthu mtendere pambuyo pa masautso omwe adawakhudza, pompo iwo amayamba kuzichitira ndale Ayah Zathu. Nena: “Allah ngwachangu kwambiri poononga ndale (zawo).” Ndithu amithenga athu (angelo) akulemba ziwembu zanu (zonse) zimene mukuchita.
Koma akawapulumutsa, pompo akuyamba kudzitukumula ndi kuononga pa dziko popanda chowayenereza (kutero). E inu anthu! Ndithu kuononga kwanu kukubweretserani masautso inu nokha. Ndipo chisangalalo (chake) cha moyo wa dziko lapansi (nchochepa). Kenako kobwerera kwanu ndi kwa Ife, ndipo tidzakuuzani zomwe munkachita.
Ndipo Allah akuitanira (anthu Ake) ku Nyumba yamtendere. Ndipo amamuongolera kunjira yolungama amene wamfuna (ngati ali wotheka kuongoka).
Ndipo omwe achita zabwino, adzapata (malipiro) abwino ndi zoonjezera. Ndipo fumbi silikavindikira nkhope zawo. Ndiponso kunyozeka sikukawapeza. Iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere; mmenemo akakhala nthawi yaitali.
Ndipo amene akolola zoipa (kuchokera m’zochita zawo zoipa) mphoto ya choipa ndiyofanana ndi icho; ndipo kunyozeka kudzawapeza; sadzakhala ndi aliyense wotha kuwateteza ku chilango cha Allah. Nkhope zawo zidzakhala ngati zaphimbidwa ndi zidutswa za usiku wa m’dima, (zidzakhala zakuda kwambiri); awo ndiwo anthu a ku Moto. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali.
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse. Kenako tidzawauza amene ankaphatikiza (Allah ndi mafano kuti): “Imani pompo inu pamodzi ndi aphatikizi anuwo.” Ndipo tidzawasiyanitsa pakati pawo; koma aphatikizi awowo adzati: “Simudali kutipembedza ife (koma mudali kupembedza zilakolako zanu).”
“Allah akukwanira kukhala mboni pakati pathu ndi pakati panu. Ndithu ife sitidali kuzindikira za mapemphero anu. (Sitinkazindikira kuti inu mukutipembedza).”
Nena: “Kodi ndani akukupatsani (zopatsa) kuchokera kumwamba (povumbwitsa mvula), ndi pansi (pomeretsa mmera)? Nanga ndani amakupatsani kumva ndi kupenya? Nanga ndani amene akutulutsa chamoyo kuchokera m’chakufa, ndi kutulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo? Nanga ndani akukonza zinthu zonse?” Anena: “Ndi Allah.” Choncho, nena: “Kodi bwanji simukumuopa?”
Uyo ndi Allah, Mbuye wanu Woona; nanga pali chiyani pambuyo poleka choonadi, sikusokera basi? Kodi nanga mukutembenuzidwa chotani (kusiya choonadi)?
Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) amene angayambitse kulenga zolengedwa; kenako (zitafa) ndikuzibweza?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuyambitsa zolengedwa kenaka ndi kuzibweza (pambuyo poonongeka). Nanga mukunamizidwa chotani (kusiya chikhulupiliro)?”
Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) woongolera kuchoonadi?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuongolera ku choonadi. Kodi amene akutsogolera ku choonadi sindiye woyenera kwambiri kutsatidwa kapena (woyenera kutsatidwa ndi) yemwe sakutha kudziongola pokhapokha atawongoledwa ndi wina wake? Nanga mwatani kodi, kodi mukuweruza bwanji?”
Ndipo ambiri a iwo satsatira (china) koma zoganizira basi, (osati chomwe afufuza ndikuchizindikira ndi nzeru zawo). Ndithu choganizira sichithandiza ngakhale pang’ono ku choonadi. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene akuchita.
Ndipo sikotheka Qur’an iyi kukhala yopekedwa, yosachokera kwa Allah (monga momwe munenera). Koma (yachokera kwa Allah) kutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake, ndi kulongosola za buku (lakale). Palibe chikaiko m’menemo (kuti) yachokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
Kapena akunena kuti waipeka? Nena: “Tabwerani ndi sura (imodzi) yofanana ndi iyo, ndipo itanani amene mungathe (kuwaitana kuti akuthandizeni) kupatula Allah, ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’aniyi waipeka Muhammad {s.a.w}).”
Koma atsutsa zomwe sakuzizindikira (m’mene zilili) ngakhale tanthauzo lake (la kuona kwake kapena kunama kwake) lisanawafike. Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo. Choncho, taona momwe mathero a anthu ochimwa adalili.
Ndipo ngati apitiriza kukutsutsa, nena: “Ine ndili ndi ntchito yanga, inunso muli ndi ntchito yanu. Inu mwatalikirana nazo zimene ndikuchita, inenso ndatalikirana nazo zimene mukuchita!”
Ndipo mwa iwo alipo ena amene akumvetsera kwa iwe, (koma osati ndi cholinga choti adziwe). Kodi iwe ungathe kuwamveretsa agonthi, chikhalirecho nzeru alibe?
Ndipo alipo ena mwa iwo amene akukutong’olera maso (kukuyang’ana monyoza). Kodi iwe ungathe kuwatsogolera akhungu, chikhalirecho sali openya?
Ndithu Allah sachitira anthu choipa chilichonse. Koma anthu akudzichitira okha zoipa. (Adapatsidwa nzeru, koma sazigwiritsa ntchito).
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe adzawasonkhanitsa (onse) ngati kuti sadakhale (pa dziko lapansi) koma ola limodzi la usana (atathedwa nzeru). Adzazindikirana pakati pawo; (koma aliyense sadzalabadira mnzake). Ndithu aonongeka amene adatsutsa za kukumana ndi Allah ndipo sadali oongoka.
Ndipo ngati tingakusonyeze (pompano pa dziko lapansi) zina mwa zomwe tikuwalonjeza ndikuwachenjeza nazo, kapena kukubweretsera imfa (usadazione zimenezo), kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kenako Allah ndi mboni pa zomwe akuchita.
Ndipo fuko lililonse lili ndi Mtumiki ndipo akazabwera Mtumiki wawo (tsiku la chiweruziro), kudzaweruzidwa pakati pawo mwa chilungamo ndipo sadzaponderezedwa.
Ndipo akunena (osakhulupirira): “Kodi lonjezo ili lidzachitika liti ngati mukunena zoona?”
Nena: “Ndilibe mphamvu mwandekha pa (kudzichotsera) vuto ngakhale (kudzibweretsera) thandizo. (Nanga za zimenezo ndingadziweponji)? Koma chimene Allah wafuna (ndi chomwe chimachitika). M’badwo uli wonse uli ndi nthawi yake (yofera). Nthawi yawo (yofera) ikadza sangathe kuichedwetsa ola limodzi ngakhale kuifulumizitsa.”
Nena: “Kodi mukuona bwanji, ngati chilango chakecho chitakudzerani usiku kapena usana (mungathe kuthawa)? Nanga bwanji ochimwa akuchifulumizitsa (kuti chidze mwachangu)?”
“Kodi chikadza ndipamene mudzachikhulupirire?” Panthawiyo mudzauzidwa): “Kodi tsopano (ndi pamene mukukhulupirira), chikhalirecho mudali kuchifulumizitsa (kale)?”
Kenako kudzanenedwa kwa amene adachita zoipa: “Lawani chilango chamuyaya! Kodi mungalipidwe zina osakhala zomwe mudazipata (kuchokera m’zochita zanu zoipa)?”
Eti akukufunsa: “Kodi nzoona izo (zimene ukunena)?” Nena: “Inde! Ndikulumbira kwa Mbuye wanga, zimenezo ndi zoona. Ndipo inu simuli olepheretsa (Allah).”
Ndipo kukadakhala kuti munthu aliyense amene adachita zoipa, nkukhala nazo zonse zam’dziko akadapereka zonse kuti adziombole nazo (pamene adzaona kuopsa kwa chilango cha tsikulo). Ndipo akadzachiona chilango, adzayesetsa kubisa madandaulo (awo; koma adzaonekera poyera). Ndipo kudzaweruzidwa mwachilungamo pakati pawo, ndipo iwo sadzaponderezedwa.
Iye (Allah ndi amene) amapereka moyo ndi imfa. Ndipo kwa Iye (nonsenu) mudzabwezedwa.
Nena: “Chifukwa cha ubwino wa Allah ndi chifundo Chake (mwapeza zimenezi), choncho asangalalire zimenezi.” Izi ndizabwino kwambiri kuposa zimene akusonkhanitsa (m’zinthu za dziko lapansi).
Nena: “Kodi mukuona bwanji, rizq lomwe Allah wakutsitsirani? Kenako inu lina mwa ilo mwalichita kukhala loletsedwa (la haramu), ndipo lina mwa ilo kukhala lololedwa (la halali).” Nena: “Kodi Allah adakulolezani (kuchita zimenezo), kapena mukumpekera Allah bodza?”
Ndipo siutanganidwa ndi ntchito iliyonse, ndiponso simuwerenga m’menemo (chinthu chilichonse) cha m’Qur’an ndipo simuchita ntchito ina iliyonse (inu anthu) koma Ife timakhala mboni pa inu pamene mukutanganidwa nayo. Ndipo sichibisika kwa Mbuye wako chinthu chilichonse ngakhale cholemera ngati nyelere, m’nthaka ngakhale kumwamba. Ndipo ngakhale chocheperapo zedi kuposa pamenepo kapena chokulirapo koma chili m’kuku (la Allah) lofotokoza chilichonse.
Ndipo (iwe, Mtumiki) zisakudandaulitse zonena zawo (zomwe akukunenera monyoza). Ndithu ulemelero ndi mphamvu zonse nza Allah. Iye Ngwakumva, Ngodziwa.
Iye (Allah) ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti muzipumamo, ndi (adakupangirani) usana kukhala wowala (kuti mupenye). Ndithu m’zimene muli zisonyezo (zosonyeza chifundo cha Allah pa zolengedwa Zake) kwa anthu akumva.
Ndichisangalalo chochepa basi m’dziko lapansi. Kenako kwa Ife ndiwo mabwelero awo. Kenako tidzawalawitsa chilango chaukali chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.
Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga.
Ngati mutembenuka ndikunyoza, (ndikufuna kwanu). Ine sindinakupempheni malipiro. Malipiro anga kulibe kulikonse (kumene ndingalandire) koma kwa Allah, ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa Asilamu (ogonjera Iye).”
Koma adamutsutsa. Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye m’chombo. Ndipo tidawasankha iwo kukhala otsala (pa dziko anzawo ataonongeka). Ndipo tidawamiza amene adatsutsa Ayah Zathu. Choncho taona momwe mapeto a ochenjezedwa adalili!
Pambuyo pake tidawatumiza atumiki (ambiri) kwa anthu awo. Adawadzera ndi zisonyezo zoonekera poyera koma sadali okhulupirira zimene ena adazitsutsa kale, (adatsatira njira zomwezo za anzawo). Umo ndi momwe tikudindira zidindo m’mitima ya anthu opyola malire.
Mûsa adati: “Mukutero pa choonadi pamene chakudzerani? Kodi matsenga ali chonchi? Ndipo amatsenga sangapambane (ngakhale zitatani).”
Ndipo Farawo adati: “Ndibweretsereni wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri (zamatsenga).”
Ndipo pamene amatsenga adadza, Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zomwe mufuna kuponya (kuti musonyeze ukatswiri wanu kwa anthu).”
Ndipo tidavumbulutsa kwa Mûsa ndi m’bale wake mawu Athu (oti): “Apangireni nyumba anthu anu mu Eguputo ndipo nyumba zanu zichiteni kukhala misikiti (pakuti simungathe kukhala ndi misikiti yoonekera), ndipo pempherani Swala. Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira (kuti Allah awapatsa zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).”
(Angelo adamuuza kuti:) “Tsopano (ndipamene ukukhulupirira), pomwe kale udanyoza ndikukhala mmodzi wa oononga!”
“Choncho lero tikupulumutsa (polisunga) thupi lako, kuti ukhale chisonyezo kwa amene akudza m’mbuyo mwako (kuti adziwe kuti sudali mulungu). Koma ndithu anthu ambiri salabadira zisonyezo Zathu.”
Ndipo ngakhale kuti chisonyezo chamtundu uliwonse chiwadzere (sangakhulupirirebe), mpaka aone chilango chopweteka.
Kodi udalipo mudzi (ndi umodzi womwe pakati pa midzi mwa yomwe tidaiwononga), umene udalapa ndi kukhulupirira (pambuyo poona chilango kotero kuti) chikhulupiliro chake nkuuthandiza pa nthawi imeneyo, osati kupatula anthu a Yunus okha? Pamene adakhulupirira, tidawachotsera chilango choyalutsa m’moyo wa padziko lapansi, ndipo tidawasangalatsa kufikira nthawi yawo (yofera).
Ndipo Mbuye wako akadafuna (kuwakakamiza anthu mwamphamvu kuti akhulupirire), onse ali m’dziko lapansi akadakhulupirira (sipakadatsala ndi mmodzi yemwe. Koma Allah safuna kukakamiza anthu mwamphamvu). Nanga kodi iwe uwakakamiza anthu kuti akhale okhulupirira?
Nena: “Yang’anani nchiyani chikupezeka kumwamba ndi pansi!” Ndipo zisonyezo zonsezi ndi machenjezo onsewa sangawakwanire (ndi kuwapindulira kanthu) anthu osakhulupirira.
Kodi chiliponso chimene akudikira posakhala (kuwadzera) monga masiku (azilango zomwe zidawapeza) amene adapita kale (iwo asadafike)? Nena: “Dikirani nanenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”
“Ndiponso (ndauzidwa kuti): ‘Lungamitsa nkhope yako kuchipembedzo momuyeretsera Allah mapemphero Ake, ndipo usakhale mmodzi mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).’
‘Ndipo (kuti), usapembedze chimene sichingakupindulitsire zabwino, kapena kukubweretsera masautso, kusiya Allah. Ngati utero ndiye kuti iwe ndi mmodzi wa oipa.”
Ndipo ngati Allah atakukhudza ndi masautso, palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni zedi.
Nena: “E inu anthu! Choonadi chakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene waongoka, (zabwino zake) zili pa iye mwini. Ndipo amene wasokera, ndithu zotsatira za kusokera zili pa iye mwini. Ndipo ine sindili muyang’aniri pa inu, (udindo wanga ndi kuchenjeza basi).”
Ndipo (andiuza kuti): “Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira kufikira Allah adzaweruze. Iye Ngoweruza bwino kuposa aweruzi onse.”
Share