Surah Al-Bayyinah ( The Clear Evidence )

Surah Al-Bayyinah ( The Clear Evidence ) - Chewa Aya count 8

Amene adakanira (Allah ndi Mthenga Wake) mwa omwe adapatsidwa buku ndi opembedza mafano sadali olekana (ndi umbuli wawo ndi kusalabadira kwawo choona) mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo choonekera poyera.[466]
(Yemwe ndi) Mtumiki wochokera kwa Allah akuwawerengera makalata oyeretsedwa (ku zonama).[467]
Omwe mkati mwake muli malamulo oongoka (ofotokoza za choona).[468]
Sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe chidawafikira chisonyezo (chosonyeza kuti Muhammad (s.a.w) ndi mthenga wa Allah yemwe adalonjezedwa mmabuku awo).
Ndipo sadalamulidwe (china) koma kuti ampembedze Allah (Mmodzi yekha) ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona (ndi kusiya njira zonama) ndi kuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka (cha pachuma chawo); chimenecho (ndicho) chipembedzo choongoka.[469]
Ndithu amene sadakhulupirire (Mneneri) (s.a.w) pakati pa anthu a mabuku ndi opembedza mafano adzalowetsedwa ku Jahannam ndikukhala m’menemo nthawi yaitali; iwowo ndiwo zolengedwa zoipa.
Share