Surah Al-'alaq ( The Clot )

Surah Al-'alaq ( The Clot ) - Chewa Aya count 19

Werenga! (Iwe Mneneri (s.a.w), zomwe zikuvumbulutsidwa) mdzina la Mbuye wako Yemwe adalenga (zolengedwa zonse).[460]
Adalenga munthu kuchokera ku magazi owundana.[461]
Werenga! Ndipo Mbuye wako ndi Wopereka kwambiri.[462]
Yemwe waphunzitsa (munthu kulemba) ndi cholembera.
Waphunzitsa munthu zinthu (zambiri) zomwe (iye) sadali kuzidziwa.
Zoona ndithu koma munthu akupyola malire (podzikweza).
Palibe chikaiko, (iwe Mneneri (s.a.w) kobwerera (onse) nkwa Mbuye wako basi; (adzawaukitsa).[463]
Tandiuza (za woletsayo) ngati akutsutsa (zimene wadza nazo Mneneri) ndikunyoza (chikhulupiliro ndi ntchito yabwino)?
Kodi sakudziwa kuti Allah akuona (machitidwe ake. Ndipo adzamlipira)?
Ayi ndithu ngati sasiya timukoka tsitsi lapatsumba (tiligwira mwamphamvu tsumba lake ndikukamponya ku Moto).
Basi aliitane gulu lakelo, (la amene amakhala nawo pabwalo kuti amthandize pano pa dziko kapena tsiku lachimaliziro),
Nafe tiitana azabaniya (angelo a ku Moto).
Ayi ndithu usamumvere (pa zimene akukuletsazo); koma gwetsa nkhope yako pansi, ndipo dziyandikitse kwa Mbuye wako.
Share