Surah As-Sharh ( The Opening Forth)

Surah As-Sharh ( The Opening Forth) - Chewa Aya count 8

Kodi sitidachiphanule chifuwa chako (pokupatsa chiongoko ndi chikhulupiliro ndi nzeru zambiri)?
Ndipo takuchotsera mtolo wako (pa ntchito yolalikira pokuthandiza ndi kukufewetsera zinthu zako).
Ndipo takukweza kutchulidwa kwako.[455]
Ndipo ndithu pali chovuta palinso zabwino (Zambiri).
Ndithu pali chovuta palinso zabwino (zambiri).
Basi, ukamaliza ntchito (yolalikira ndi Jihâd) limbikira kupemphera.[456]
Ndipo khala wolakalaka (zabwino zomwe zili) kwa Mbuye wako.
Share