Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi yantchito),
Ndi usiku pamene ukuvindikira.
Sadakusiye Mbuye wako (iwe Mneneri) (s.a.w) ndiponso sadakude.[452]
Ndithu moyo watsiku lirimkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu.
Ndithu posachedwapa akupatsa Mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondwera.[453]
Kodi sadakupeze uli wa masiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino?
Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)?[454]
Ndiponso adakupeza uli wosauka nakulemeretsa?
Basi, wamasiye usamchitire nkhanza.
Ndiponso wopempha usamukalipire.
Tsono mtendere wa Mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino).