Surah Al-Layl ( The Night )

Surah Al-Layl ( The Night ) - Chewa Aya count 21

Ndikulumbilira usiku pamene ukuphimba (chilichonse).
Ndithu zochita zanu nzosiyanasiyana.[446]
Tsono yemwe akupereka (pa njira ya Allah) ndikumamuopa (Mbuye wake ndikupewa zoletsedwa),[447]
Ndikumavomereza zinthu zabwino; (komwe kuli kukhulupirira Allah mwanzeru),[448]
Choncho timufewetsera njira yompititsa ku zabwino.[449]
Koma uyo achite umbombo ndikuganiza za kuti iye payekha ngokwana;
Choncho timufewetsera njira yompititsa ku mavuto (a muyaya).
Ndipo chuma chake sichidzamthandiza (chilichonse) akadzagwera ku Moto.
Ndithu Ife ndi amene timawalongosolera anthu njira yabwino ndi njira yoipa.
Ndipo ndithu moyo womaliza ndi moyo woyamba uli m’manja mwathu.
Basi, ndikukuchenjezani za Moto woyaka mwa mphamvu.
Yemwe amatsutsa (choona) ndi kunyoza (zisonyezo za Allah).
Koma yemwe akuopa Allah kwambiri akatalikitsidwa ndi Moto.
Amene akupereka chuma chake ndi cholinga chodziyeretsa.
Ndipo palibe aliyense kwa iye, amene adamchitira za chifundo zomwe zikulipidwa.[450]
Koma (akuchita zimenezi) kufuna chikondi cha Mbuye wake Wapamwambamwamba.
Ndipo posachedwa adzasangalala.[451]
Share