Surah Al-Ghashiya ( The Overwhelming )

Surah Al-Ghashiya ( The Overwhelming ) - Chewa Aya count 26

Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)?
Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka,[425]
Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri.
Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala.
Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi).[426]
Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula).
Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola).[427]
Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere
Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse.
Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani?[428]
Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)?
Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire).[429]
Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako),
Share