Lemekeza dzina la Mbuye wako Wapamwambamwamba (ndikuliyeretsa ku zinthu zosayenera).[417]
Amene adalenga (chilichonse) ndikuchikonza bwinobwino (mkalengedwe kolingana).
Amene adalamuliratu (chilichonse zochita zake) ndi kuchiongolera.[418]
Ndi Yemwenso akumeretsa msipu.
Ndipo nausandutsa kukhala wouma ndi wodera.
Tikulakatulira (chivumbulutso Chathu) ndipo siuyiwala.[419]
Kupatula chimene wafuna Allah (kuti uchiiwale); ndithu Iye amadziwa zoonekera ndi zimene zimabisika.
Ndipo tikufewetsera (njira yochitira zinthu) zabwino.[420]
Choncho akumbutse (wanthu powalalikira) ngati kukumbutsa kuthandiza.[421]
(Palibe chikaiko ulalikiwo) aukumbukira (ndikuthandizidwa nawo) amene akuopa Allah.
Ndipo wamavuto ambiri, (wamakani ndi wokanira), adzitalikitsa ndi ulalikiwo.[422]
Amene adzalowa ku moto waukulu (umene wakonzedwa kuti udzakhale malipiro ake).
Ndipo sakafa m’menemo (ndikupumula kumazunzo), ndiponso sakakhala ndi moyo (wamtendere).
Ndithu wapambana amene wadziyeretsa (ku machimo),[423]
Ndikukumbukira dzina la Mbuye wake (ndi mtima wake, ndi lirime lake) uku akumapemphera.
Koma inu mukukonda kwambiri moyo wa dziko lapansi.
Pamene moyo wa tsiku lachimaliziro ndiwabwino kwambiri ndiponso wamuyaya.
Ndithu izi (mukuuzidwa m’Qur’an) zilipo m’mabuku oyamba, akale,[424]
Mabuku a Ibrahim ndi Mûsa.