Surah Al-Burooj ( The Big Stars )

Surah Al-Burooj ( The Big Stars ) - Chewa Aya count 22

Ndikulumbilira thambo lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi zikuluzikulu).[411]
Ndi tsiku lolonjezedwa (kuwerengedwa ndi kulipidwa),
Ndi woikira umboni, ndi woikiridwa umboni.[412]
Atembeleredwa eni ngalande zamoto (zomwe adali kuwazunzira okhulupirira Allah, achimuna ndi achikazi).[413]
(Ngalande) za moto wankhuni (zambiri zomwe adali kuzikoleza ndikuotchera okhulupirira),
Pamene iwo adali chikhalire m’mphepete mwa ngalandezo.
Uku iwo akuyang’ana zomwe amawachitira okhulupirira, (pootchedwa ndi moto).
Sadaone choipa chilichonse mwa iwo koma chifukwa choti adakhulupirira Allah mwini mphamvu zonse ndiponso mwini kuyamikidwa,
Ndithu amene ayesa mayeso okhulupirira achimuna ndi achikazi (pa chipembedzo chawo ndi mazunzo ndi chilango cha moto), pambuyo pake osalapa (pa zimenezi), adzalandira chilango cha Jahena ndiponso chilango cha moto wopsereza,[414]
Ndithu kulanga kwa Mbuye wako (kwa anthu achinyengo), ndi kwaukali kwambiri.[415]
Iye, (Mmodzi yekha) ndi amene adayambitsa zolengedwa ndiponso ndi Yemwe adzazibweze (pambuyo poonongeka);
Iye, ndi Wokhululuka (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Wokonda kwambiri (amene akumkonda ndi kumumvera),
Mwini Arsh (Mpando wachifumu), (ndiponso) Wolemekezeka (mmene alili ndi mbiri Zake),
Wochita zimene wafuna, (ndipo chimene wafuna sichikanika).
Firiaun (Farawo) ndi Samudu, (ndi chilango chimene chidawapeza chifukwa chakulimbikira kwawo pa zinthu zopanda pake)?
Yomwe idachokera mu ubawo (chisileti chachikulu) wotetezedwa (ndi manja alionse, osintha kanthu kapena kuonjezerapo).
Share