Surah Al-Mutaffifin (Those Who Deal in Fraud)

Surah Al-Mutaffifin (Those Who Deal in Fraud) - Chewa Aya count 36

Kuonongeka koopsa kukawapeza opunguza miyeso ya malonda.
Amene amati akamadziyezera zinthu kwa anthu amafuna kulandira miyeso yodzadza.
Koma pamene iwo akamawayesera pa muyeso wa mbale kapena wa sikelo amapungula (choyenera kulandira ogulawo).
Kodi amenewa (akupungula miyeso pamalondawo) sakuganiza kuti adzaukitsidwa;
Pa tsiku lalikulu (ndiponso loopsa)?
Ayi! Ndithu (siyani chinyengo pamalonda ndi kusalabadira kuuka mmanda); zolembedwa za ntchito ya oipa zili mu Sijjin.
Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu oipa).
Ndipo palibe angalitsutse koma yekhayo wopyola malire (pochita zoipa), wa machimo ambiri;
Pamene ma Ayah Athu akuwerengedwa kwa iye (onena za tsiku la malipiro ndikuuka mmanda) amanena kuti: “Izi ndi nthano za anthu akale.”
Iyayi, sichoncho! Koma yaphimbidwa mitima yawo ndi dzimbiri (la machimo) omwe akhala akukolola.[402]
Ayi ndithu iwo (okanira) tsiku limenelo) adzatchingidwa kwa Mbuye wawo; (sadzamuona).
Kenaka adzauzidwa (powaliritsa) “Ichi nchilango chomwe mudali kuchitsutsa (pa dziko lapansi).”
Zoona, ndithu kaundula wa anthu abwino (ochita ntchito zabwino) ali mu Illiyyun.
Ameneyu ndi kaundula (wamkulu) yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu abwino);
Amamuyikira umboni (angelo) amene ayandikitsidwa (kwa Allah).
Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (zimene Allah wawapatsa monga mtendere ndi ulemelero).
Adzamwetsedwa vinyo (woyeretsedwa) wotsekeredwa ndi zitsekerero zolimba;
Komalizira kwake (kwa vinyoyo) kuzikatuluka fungo la misk; kuti akapeze zimenezi, apikisane opikisana.[403]
Ndipo chosakanizira cha vinyoyo ndi madzi a Tasnim.
(Tasnim ameneyo) ndi kasupe amene azikamwa amene ayandikitsidwa (kwa Allah.)
(Okhulupirira) akadutsa pafupi ndi iwo ankakodolerana maso (mwachipongwe);
Ndipo akabwerera kwa anzawo amabwerera akusangalala (ndi kunyozedwa kwa okhulupirira);
Ndipo (nthawi zonse) akawaona Asilamu amanena: “Ndithu awa ndi osokera (chifukwa chomkhulupirira Mtumiki).” (s.a.w)
Sanatumizidwe (Akafiri) kukhala ayang’aniri kwa okhulupirira (ndikuwaweruza zakulungama ndi kusokera).
Basi lero okhulupirira awaseka osakhulupirira (powabwezera chipongwe chawo chimene ankachita pa dziko lapansi),[404]
Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (mtendere umene Allah wawapatsa).
Kodi alipidwa osakhulupirira pa zomwe ankachita zija (pa dziko lapansi)?
Share