Surah An-Naba' ( The Great News )

Surah An-Naba' ( The Great News ) - Chewa Aya count 40

Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa.[373]
Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira).[374]
Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala?[375]
Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)?
Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi).
Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito).
Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake).
Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo;
Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba;
Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa);
Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama).
Ndi minda yothothana nthambi za mitengo.
Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale.
Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu.
Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo.
Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu.[376]
Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo);
Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto);
Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo.
Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu.
Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango.
Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana.
Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu.
Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira.[378]
Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero);
Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola.
Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi).
Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi).
Share