Surah Al-Mursalat ( Those sent forth )

Surah Al-Mursalat ( Those sent forth ) - Chewa Aya count 50

Ndikulumbilira mphepo yomwe ikuomba motsatizana.
Ndi mphepo yobalalitsa mitambo ndi mvula.
Ndi ma Ayah osiyanitsa pakati pachoona ndi chonama;
Ndi angelo opereka chivumbulutso kwa aneneri.
Kuti chichotse madandaulo kapena chikhale chenjezo;
Ndithu zimene mukulonjezedwa (kuti chimaliziro chidzakhalapo) zidzachitikadi (popanda chipeneko),
Pamene nyenyezi zidzafafanizidwa (kuwala kwake ndi kuchotsedwa m’malo mwake).
Ndi pamenenso mapiri adzachotsedwa m’malo mwake ndi kuperedwa (kukhala fumbi).
Ndi pamene atumiki adzasonkhanitsidwa pa nthawi yake, (kuti apereke umboni ku mibadwo yawo).
Kodi nditsiku lanji azichedwetsera (zinthu zikuluzikulu kuti zidzachitike)?
Nditsiku loweruza (pakati pa zolengedwa).
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).
Kodi sitidawaononge (anthu) akale (chifukwa cha machimo awo, monga anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu)?
Kenako titsatiza ena (okana Allah m’kuonongekako monga tidawachitira oyamba),
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).
Kodi sitidakulengeni kuchokera ku madzi onyozeka, (madzi ambewu ya munthu)?
Kenako tidawaika pamalo okhazikika (kuti chilengedwe chake chikwanire pamenepo),
Mpaka nyengo yodziwika (imene tidaipima kuti mwana abadwe).
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).
(Kudzanenedwa kwa okana tsiku la chimaliziro:) Pitani kuzimene mudali kuzitsutsa zija.
Simthunzi (wamtendere) ndiponso siwotchinjiriza ku malawi a Moto.”
Ndithu motowo umaponya mphalikira (mbaliwali) zazikulu ngati nyumba,
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (zimenezi).
Ndipo sadzapatsidwa chilolezo (choyankhulira) kuti apereke madandaulo awo.
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (za tsiku limenelo).
(Adzauzidwa kuti): Ili ndi tsiku loweruza (pakati pa abwino ndi oipa takusonkhanitsani inu (otsutsa Muhammad {s.a.w}), ndi akale (otsutsa aneneri akale).
Ngati muli ndi ndale (yodzipulumutsira ku chilango Changa) ndichiteni ndaleyo!
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo la Allah).
Ndithu oopa (Allah tsiku limenelo) adzakhala mu mthunzi ndi mitsinje,
Ndipo adzakhala ndi zipatso zomwe azidzazifuna.
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani, imwani mokondwa chifukwa cha zabwino zomwe mudali kuchita (mu moyo wa dziko lapansi).
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah)
Idyani, sangalalani pang’ono m’kanthawi kochepa; ndithu inu ndinu ochimwa (chifukwa chakumphatikiza Allah ndi zolengedwa).
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah).
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Weramani, (pembedzani Allah).” sawerengera.
Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (malamulo a Allah).
Kodi ndi nkhani iti imene adzaikhulupirira pambuyo pa Iyi (Qur’an)?
Share