Surah Al-Qiyamah ( The Resurrection )

Surah Al-Qiyamah ( The Resurrection ) - Chewa Aya count 40

Ndikulumbiliranso mzimu wodzidzudzula (pa cholakwa chimene wachita. Ndithu mudzaukitsidwa; mafupa anu omwazikana atasonkhanitsidwa.)
Kodi munthu akuganiza kuti Ife (Amene tidamlenga kuchokera popanda chilichonse) sitidzatha kusonkhanitsa mafupa ake (ofumbwa)?
Iyayi, Ife tikhoza (kutisonkhanitsa) ndi kutilongosola bwino timizere takunsonga kwa zala zake. (Mafupa ake ndiye osanena)!
Koma munthu akufuna kuti apitirize kuchimwa (mmasiku akudza) mtsogolo mwake.
Akufunsa (mwa chipongwe): “Kodi lidzakhala liti tsiku la chimaliziro?”
Pamene maso adzangoti tong’oo (ndi mantha),
(Adzauzidwa): “Iyayi, (iwe munthu) palibe pothawira (pako)!”
Tsiku limenelo munthu adzauzidwa zochita zake zimene adazitsogoza ndi zimene adazichedwetsa.
Ngakhale atapereka madandaulo ake (otani kuti apulumuke nawo sadzapulumuka).
Usaigwedezere (Qur’an) lirime lako (pamene ikuvumbulutsidwa) kuti uifulumilire (kuiwerenga ndi kuisunga mu mtima).
Ndithu ndiudindo wathu kuisonkhanitsa (mu mtima mwako) ndi kukhazikitsa kawerengedwe kake (palirime lako).
Choncho pamene tikukuwerengera iwe tsatira kuwerenga kwakeko (uku uli chete).
Kenako, ndithu ndiudindo Wathu kulongosola (zimene siukumvetsa),
Ndipo mukusiya moyo wa tsiku lachimaliziro.
Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zoziya (zokhwinyata).
Sichoncho! Pamene mzimu udzafika pa nthitimtima, (pomwe pakumana mafupa am’mapewa).
Ndipo ndikunenedwa ndani angamchiritse!
Ndipo (iye mwini wake), nkutsimikiza kuti ndithu uku ndikusiyana (ndi dziko lapansi),
Ndipo miyendo idzasanjikizana; (iyi ndi nthawi yochoka mzimu).
Tsiku limenelo koperekedwa (anthu onse) nkwa Mbuye wako.
Ndipo sadakhulupirire komanso sadapemphere Swala (zisanu),
Koma (m’malo mwake) adatsutsa ndi kunyoza.
Kuonongeka nkwako (iwe wotsutsa)! Kuonongeka zedi!
Kodi munthu akuganiza kuti angosiidwa chabe? (Sadzaweruzidwa)?
Kodi sadali dontho la umuna umene udafwamphukira (m’chiberekero)?
Kenako adakhala nthinthi (ntchintchi) ya magazi, ndipo adamlenga ndi kumlinganiza (monga munthu).
Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa?
Share